Malembo Oyera
Mormoni 4


Mutu 4

Nkhondo ndi kuphana zipitilira—wankhaza alanga oipa—Kuipa kwakukulu kupambana kuposa kale mu Israeli yense—Amayi ndi ana aperekedwa nsembe ku mafano—Alamani ayamba kusesa Anefi pamaso pawo. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 363–375.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti mu chaka cha mazana atatu ndi makumi asanu ndi limodzi mphambu zitatu Anefi adapita ndi ankhondo awo kukamenyana ndi Alamani, kunja kwa dziko la Bwinja.

2 Ndipo zidachitika kuti ankhondo a Anefi adabwenzedwanso kachiwiri ku dziko la Bwinja. Ndipo pamene iwo adali otopabe, ankhondo atsopano Achilamani adabwera pa iwo; ndipo adali ndi nkhondo yoopsya; kotero kuti Alamani adalanda mzinda wa Bwinja, ndi kupha ambiri mwa Anefi, ndi kutenga ambiri ukaidi.

3 Ndipo otsalawo adathawa ndi kukaphatikizana ndi okhala ku mzinda wa Teyankumu. Tsopano mzinda wa Teyankumu udali kumalire ndi gombe la nyanja; ndipo udali pafupi ndi mzinda wa Bwinja.

4 Ndipo zidali chifukwa ankhondo a Anefi adapita kwa Alamani moti adayamba kukanthidwa; pakuti kupanda pamenepo, Alamani sakadakhala ndi mphamvu pa iwo.

5 Koma, taonani, ziweruzo za Mulungu zidzafikira oipa; ndipo ndi kudzera mwa oipa m’mene oipa amalangidwa; pakuti ndi oipa amene amavundula mitima ya ana a anthu m’kukhetsa mwazi.

6 Ndipo zidachitika kuti Alamani adapanga zokonzekera kubwera motsutsana ndi mzinda wa Teyankumu.

7 Ndipo zidachitika m’chaka cha mazana atatu ndi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinayi Alamani adabwera motsutsana ndi mzinda wa Teyankumu, kuti akathenso kulanda mzinda wa Teyankumu.

8 Ndipo zidachitika kuti iwo adabwenzedwa ndi kuthamangitsidwa ndi Anefi. Ndipo pamene Anefi adaona kuti adawathamangitsa Alamani adayamba kudzitamandira mu mphamvu zawo; ndipo adapita mu mphamvu zawo zokha, ndi kutenganso mzinda wa Bwinja.

9 Ndipo tsopano zinthu zonsezi zidachitidwa, ndipo kudali zikwizikwi zophedwa ku mbali zonse ziwiri, onse Anefi ndi Alamani.

10 Ndipo zidachitika kuti zaka mazana atatu ndi makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu n’chimodzi zidatha, ndipo Alamani adabweranso kachiwiri pa Anefi kunkhondo; ndipo Anefi sadalapebe pa zoipa zomwe adachita, koma adalimbikira m’zoipa zawo mosalekeza.

11 Ndipo ndizosatheka kuti lilime lilongosole, kapena kuti munthu alembe kalongosoledwe kabwino ka zochitika zoopsya za mwazi ndi kuphana kumene kudali pakati pa anthu, onse Anefi ndi Alamani; ndipo mtima uliwonse udaumitsidwa, mpaka kuti adakondwera mu kukhetsa mwazi mosalekeza.

12 Ndipo kudalibe kuipa kwakukulu kotere pakati pa ana onse a Lehi, kapena ngakhale pakati pa nyumba ya Israeli yonse, molingana ndi mawu a Ambuye, monga zidalili pakati pa anthu awa.

13 Ndipo zidachitika kuti Alamani adalanda mzinda wa Bwinja, ndipo izi chifukwa choti chiwerengero chawo chidaposa chiwerengero cha Anefi.

14 Ndipo iwo adagubiranso motsutsana ndi mzinda wa Teyankumu, ndipo adathamangitsa okhalamo kunja kwake, ndipo adatenga ambiri ukaidi onse azimayi ndi ana, ndipo adawapereka iwo ngati nsembe ku milungu yawo yamafano.

15 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha mazana atatu ndi makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu ndi ziwiri, Anefi pokhala okwiya chifukwa Alamani adapereka nsembe azimayi awo ndi ana awo, kuti adapita motsutsana ndi Alamani mwa mkwiyo waukulu kwambiri, kotero kuti adawagonjetsa kachiwiri Alamani, ndi kuwathamangitsa iwo kunja kwa maiko awo.

16 Ndipo Alamani sadabwerenso kachiwiri motsutsana ndi Anefi mpaka chaka cha mazana atatu ndi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu.

17 Ndipo mu chaka chimenechi iwo adabwera motsutsana ndi Anefi mwa mphamvu zawo zonse; ndipo adali osawerengeka chifukwa cha kukula kwa chiwerengero chawo.

18 Ndipo kuchokera pa nthawi imeneyi kupita chitsogolo Anefi sadapeze mphamvu pa Alamani, koma adayamba kupululutsidwa ndi iwo ngati mame pamaso pa dzuwa.

19 Ndipo zidachitika kuti Alamani adatsikira motsutsana ndi mzinda wa Bwinja; ndipo kudamenyedwa nkhondo yoopsya kwambiri mu mzinda wa Bwinja, mumenemo iwo adagonjetsa Anefi.

20 Ndipo iwo adathawa kachiwiri pamaso pawo, ndipo adabwera ku mzinda wa Boazi; ndipo kumeneko iwo adaima motsutsana ndi Alamani ndi kulimba mtima kwakukulu, kotero kuti Alamani sadawagonjetse mpakana iwo atabweranso kachiwiri.

21 Ndipo pamene iwo adabwera kachiwiri, Anefi adathamangitsidwa ndi kuphedwa ndi kupha kwakukulu kwambiri, azimayi awo ndi ana awo adaperekedwanso nsembe kwa mafano.

22 Ndipo zidachitika kuti Anefi adathawanso kuchoka pamaso pawo, kutenga onse okhalamo limodzi nawo, onse am’matauni ndi m’mamidzi.

23 Ndipo tsopano ine, Mormoni, poona kuti Alamani adali pafupi kulanda dzikolo, kotero ndidapita ku phiri la Shimu, ndi kunyamula zolemba zonse zimene Amaroni adazibisa kwa Ambuye.

Print