Malembo Oyera
Mormoni 5


Mutu 5

Mormoni atsogoleranso ankhondo Achinefi mu nkhondo za mwazi ndi kuphana—Buku la Mormoni lidzabwera kuti lidzatsimikizire Israeli yense kuti Yesu ndiye Khristu—Chifukwa cha kusakhulupilira kwawo, Alamani adzabalalika, ndipo Mzimu udzasiya kulimbana nawo—Iwo adzalandira uthenga wabwino kuchokera kwa Amitundu mu masiku otsiriza. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 375–384.

1 Ndipo zidachitika kuti ndidapita pakati pa Anefi, ndipo ndidalapa kulumbiro limene ndidapanga loti sindidzawathandizanso; ndipo iwo adandipatsanso ulamuliro wa ankhondo awo, pakuti ankandiona ine ngati kuti ndikadatha kuwapulumutsa ku masautso awo.

2 Koma taonani, ndidalibe chiyembekezo, pakuti ndinkadziwa ziweruzo za Ambuye zimene zikuyenera kudza pa iwo; pakuti iwo sadalape ku mphulupulu zawo, koma adalimbana ndi miyoyo yawo opanda kuitanira Munthu uyo amene adawalenga iwo.

3 Ndipo zidachitika kuti Alamani adabwera motsutsana nafe pomwe ife tidathawira ku mzinda wa Yordani; koma taonani, adathamangitsidwa kuti iwo sadatenge mzindawo pa nthawi imeneyo.

4 Ndipo zidachitika kuti adabweranso motsutsana nafe, ndipo ife tidatetezabe mzindawu. Ndipo kudalinso mizinda ina imene idatetezedwa ndi Anefi, imene malinga ake adawadula iwo kuti sakadatha kulowa m’dziko limene lidali patsogolo pathu, kuti awononge okhala mu dziko lathu.

5 Koma zidachitika kuti maiko ena aliwonse amene ife tidadutsamo, ndi okhalamo m’menemo sadasonkhanitsidwe, adawonongedwa ndi Alamani, ndi matauni awo, ndi midzi yawo, ndi mizinda idayatsidwa ndi moto; ndipo motero zaka mazana atatu ndi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu n’zinayi zidapita.

6 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha mazana atatu ndi makumi asanu ndi atatu Alamani adabweranso motsutsana nafe ku nkhondo, ndipo ife tidaima motsutsana nawo molimba mtima; koma zonse zidali chabe, pakuti chachikulu chidali chiwerengero chawo mpaka adapondaponda anthu Achinefi pansi pa mapazi awo.

7 Ndipo zidachitika kuti tidayambanso kuthawa, ndipo iwo amene kuthawa kwawo kudali kwachangu kuposa Alamani adathawa, ndipo iwo amene kuthawa kwawo sikudapose Alamani adasesedwa ndi kuwonongedwa.

8 Ndipo tsopano taonani, ine, Mormoni, sindikufuna kukhumudwitsa miyoyo ya anthu mukuwaponyera pamaso pawo zochitika zoopsya zotere za mwazi ndi kuphana monga zidaonekera pamaso panga; koma ine, podziwa kuti zinthu izi zikuyenera ndithu kudziwika, ndipo kuti zinthu zonse zimene zili zobisika zikuyenera kuvumbulutsidwa pa madenga-anyumba—

9 Ndiponso kuti chidziwitso cha zinthu izi chikuyenera kubwera kwa otsalira a anthu awa, ndiponso kwa Amitundu, amene Ambuye anena kuti adzabalalitsa anthu awa, ndipo anthu awa adzawerengedwa ngati opanda ntchito pakati pawo—kotero ndikulemba nkhani yofupikitsidwa pang’ono, kuwopa kupereka nkhani yonse ya zinthu zimene ine ndaziona, chifukwa cha lamulo limene ndalandira, ndiponso kuti inu musakhale ndi chisoni chachikulu kwambiri chifukwa cha zoipa za anthu awa.

10 Ndipo tsopano taonani, ichi ndikuyankhula kwa mbewu yawo, ndiponso kwa Amitundu amene ali osamala za nyumba ya Israeli, amene amazindikira ndi kudziwa kumene madalitso awo amachokera.

11 Pakuti ndidziwa kuti otere adzakhala ndi chisoni chifukwa cha tsoka la nyumba ya Israeli; inde, iwo adzakhala ndi chisoni chifukwa cha kuwonongedwa kwa anthu awa; iwo adzakhala ndi chisoni kuti anthu awa sadalape kuti athe kukumbatiridwa m’mikono ya Yesu.

12 Tsopano zinthu izi zalembedwera kwa otsalira a nyumba ya Yakobo; ndipo zalembedwa monga momwemu, chifukwa ndizodziwika kwa Mulungu kuti zoipa sizidzabweretsa izi kwa iwo; ndipo zikuyenera kubisidwa kwa Ambuye kuti zidzabwere mu nthawi yake yoyenera.

13 Ndipo ili ndi lamulo lomwe ine ndidalandira; ndipo taonani, izo zidzabwera molingana ndi lamulo la Ambuye, pamene iye adzawone koyenera, mu nzeru zake.

14 Ndipo taonani, izo zidzapita kwa Ayuda osakhulupilira; ndipo pachifukwa ichi izo zidzapita—kuti akathe kukopeka kuti Yesu ndiye Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo; kuti Atate akathe kubweretsa, kudzera mwa Wokondedwa yekhayo, cholinga chake chachikulu ndi chamuyaya, mu kubwenzeretsa Ayuda, kapena onse a nyumba ya Israeli, ku dziko lawo lacholowa, limene Ambuye Mulungu wawo adawapatsa iwo, m’kukwanilitsa pangano lake.

15 Ndiponso kuti mbewu ya anthu awa ikathe kukhulupilira uthenga wake wabwino mokwanira, umene udzapite kwa iwo kuchokera kwa Amitundu; pakuti anthu awa adzamwazikana, ndipo adzakhala okuda, aumve, ndi anthu onyansa, kupitilira kufotokoza kwa icho chimene chidakhalapo pakati pathu, inde, ngakhale icho chimene chidakhalapo pakati pa Alamani, ndipo izi chifukwa cha kusakhulupilira kwawo ndi kupembedza mafano.

16 Pakuti taonani, Mzimu wa Ambuye wasiya kale kulimbana ndi makolo awo; ndipo iwo ali opanda Khristu ndi Mulungu mu dziko lapansi; ndipo iwo akuthamangitsidwa monga ngati mankhusu pamaso pa mphepo.

17 Iwo adali anthu okondweretsa, ndipo adali ndi Khristu ngati m’busa wawo, inde, ankatsogoleredwa ngakhale ndi Mulungu Atate.

18 Koma tsopano, taonani, akutsogoleredwa ndi Satana, ngakhale monga mankhusu amatengedwa pamaso pa mphepo, kapena monga bwato uku ndi uko pa mafunde, opanda thanga kapena nangula, kapena opanda chilichonse chimene angathe kuwongolera, ndipo ngakhale monga chili, chonchonso iwo ali.

19 Ndipo taonani, Ambuye asungira madalitso awo, amene akadatha kuwalandira mu dzikolo, kwa Amitundu amene adzakhale m’dzikolo.

20 Koma taonani, zidzachitika kuti iwo adzathamangitsidwa ndi kubalalitsidwa ndi Amitundu; ndipo atatha kubalalitsidwa ndi Amitundu, taonani, kenako Ambuye adzakumbukira pangano limene iwo adapanga kwa Abrahamu ndi kwa onse a nyumba ya Israeli.

21 Ndiponso Ambuye adzakumbukira mapemphero a wolungama, amene ayikidwa kwa iye chifukwa cha iwo.

22 Ndipo kenako, O inu Amitundu, mungaime bwanji pamaso pa mphamvu ya Mulungu, kupatula mutalapa ndi kubwelera ku njira zanu zoipa?

23 Kodi inu simukudziwa kuti muli m’manja mwa Mulungu? Kodi inu simukudziwa kuti iye ali ndi mphamvu zonse, ndipo pa lamulo lake lalikulu dziko lapansi lidzapindidwa pamodzi ngati mpukutu?

24 Kotero, lapani inu, ndi kudzichepetsa nokha pamaso pake, kuopa iye adzabwera mu chilungamo motsutsana nanu—kuopa otsalira a mbewu ya Yakobo adzapita pakati panu monga mkango, ndi kukung’ambani inu mzidutswa, ndipo sikudzakhala okupulumutsani.

Print