Malembo Oyera
Mormoni 3


Mutu 3

Mormoni afuula kulapa kwa Anefi—Iwo apeza kupambana kwakukulu ndi ulemelero mu mphamvu zawo—Mormoni akana kuwatsogolera iwo, ndipo mapemphero ake a iwo akhala opanda chikhulupiliro—Buku la Mormoni limaitana mafuko khumi ndi awiri a Israeli kuti akhulupilire uthenga wabwino. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 360–362.

1 Ndipo zidachitika kuti Alamani sadabwerenso kudzamenyana kufikira dzaka khumi zina zitapita. Ndipo taonani, ndidapempha anthu anga, Anefi, mukukonzekeretsa maiko awo ndi zida zawo za nkhondo motsutsana ndi nthawi ya nkhondo.

2 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adati kwa ine: Fuula kwa anthu awa—Lapani inu, ndi kubwera kwa ine, ndi kubatizidwa, ndi kumanganso mpingo wanga, ndipo inu mudzapulumutsiwa.

3 Ndipo ine ndidafuula kwa anthu awa, koma kudali kwachabe; ndipo iwo sadazindikire kuti adali Ambuye amene adawapulumutsa iwo, ndi kuwapatsa iwo mwayi wolapa. Ndipo taonani iwo adaumitsa mitima yawo motsutsana ndi Ambuye Mulungu wawo.

4 Ndipo zidachitika kuti potsatira kutha kwa zaka khumi zimenezi, kupanga, mu dzaka zonse, dzaka mazana atatu ndi makumi asanu ndi limodzi kuchokera pa kubwera kwa Khristu, mfumu ya Alamani idatumiza chikalata kwa ine, chimene chidadziwitsa ine kuti iwo adali kukonzekera kubwera kachiwiri kudzamenyana nafe.

5 Ndipo zidachitika kuti ine ndidachititsa anthu anga kuti adzisonkhanitse okha pamodzi ku dziko la Bwinja, ku mzinda umene udali kumalire, kudzera njira yopapatiza imene imalondolera kum’mwera.

6 Ndipo kumeneko tidaikako ankhondo athu, kuti tithe kuimitsa ankhondo Achilamani, kuti iwo asalande dziko lathu lililonse; kotero tidamanga malinga motsutsana nawo ndi ankhondo athu onse.

7 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha mazana atatu ndi makumi asanu ndi khumi n’chimodzi Alamani adabwera ku mzinda wa Bwinja kudzamenyana nafe; ndipo zidachitika kuti mu chaka chimenechi tidawagonjetsa iwo, kufikira kuti iwo adabwelera ku maiko awo kachiwiri.

8 Ndipo mu chaka cha mazana atatu ndi makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu ziwiri iwo adabweranso kachiwiri ku nkhondo. Ndipo tidawagonjetsa kachiwiri, ndi kupha chiwerengero chachikulu cha iwo, ndipo okufa awo adaponyedwa m’nyanja.

9 Ndipo tsopano, chifukwa cha chinthu chachikulu chimenechi chimene anthu anga, Anefi, adachichita, adayamba kudzitamandira mu mphamvu zawo, ndipo adayamba kulumbilira kumwamba kuti iwo adzabwenzera okha pa mwazi wa abale awo amene adaphedwa ndi adani awo.

10 Ndipo iwo adalumbilira kumwamba, ndiponso pa mpando wachifumu wa Mulungu, kuti iwo adzapita ku nkhondo motsutsana ndi adani awo, ndipo adzawachotsa iwo pa nkhope yadzikolo.

11 Ndipo zidachitika kuti ine, Mormoni, ndidakanitsitsa kuchokera pa nthawi imeneyi kupita chitsogolo kukhala wamkulu ndi otsogolera anthu awa, chifukwa cha zoipa ndi zonyansa zawo.

12 Taonani, ndidawatsogolera iwo, posatengera kuipa kwawo ndidawatsogolera nthawi zambiri ku nkhondo, ndipo ndidali nawo chikondi, molingana ndi chikondi cha Mulungu chimene chidali mwa ine, ndi mtima wanga onse; ndi moyo wanga udatsanulira m’pemphero kwa Mulungu wanga tsiku lonse chifukwa cha iwo; komabe, kudali kopanda chikhulupiliro, chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo.

13 Ndipo katatu ndawapulumutsa iwo kuchoka m’manja mwa adani awo, ndipo iwo sadalape machimo awo.

14 Ndipo pamene iwo adalumbira mwa zonse zomwe zidaletsedwa iwo ndi Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, kuti adzapita kunkhondo ndi adani awo, ndi kubwenzera okha pa mwazi wa abale awo, taonani mawu a Ambuye adabwera kwa ine nati:

15 Kubwenzera choipa ndi kwanga, ndipo ndidzabwenzera; ndipo chifukwa choti anthu awa sadalape nditatha kuwapulumutsa, taona, adzadulidwa pa nkhope ya dziko lapansi.

16 Ndipo zidachitika kuti ndidakanitsitsa kupita motsutsana ndi adani anga; ndipo ndidachita ngakhale monga Ambuye adandilamulira, ndipo ndidaima ngati ongowonelera ku zochitika ku dziko lapansi zinthu zimene ndidaziona ndi kuzimva, molingana ndi maonetsedwe a Mzimu umene udachitira umboni wa zinthu zilinkudza.

17 Kotero ndikukulemberani inu, Amitundu, ndiponso kwa inu, nyumba ya Israeli, pamene ntchito idzayambika, kuti mudzakhala pafupi kukonzekera kubwelera ku dziko la cholowa chanu.

18 Inde, taonani, ndikukulemberani inu onse akumalekezero a dziko lapansi; inde, kwa inuyo, mafuko khumi ndi awiri a Israeli, amene mudzaweruzidwa molingana ndi ntchito zanu ndi khumi ndi awiri amene Yesu adawasankha kukhala ophunzira ake mu dziko la Yerusalemu.

19 Ndipo ndikulemberanso kwa inu otsalira a anthu awa, amenenso mudzaweruzidwa ndi khumi ndi awiri amene Yesu adawasankha mu dziko ili ndipo iwo adzaweruzidwa ndi khumi ndi awiri ena amene Yesu adawasankha mu dziko la Yerusalemu.

20 Ndipo zinthu izi Mzimu wandionetsera kwa ine; kotero ndikuzilemba kwa inu nonse. Ndipo pa chifukwa ichi ndikulembera kwa inu, kuti mukathe kudziwa kuti mukuyenera nonse kuima pamaso pa mpando wa chiweruzo wa Khristu, inde, munthu aliyense amene ali wa banja la anthu la Adamu; ndipo mukuyenera kuima kuti muweruzidwe ku ntchito zanu, kaya ndi zabwino kapena zoipa;

21 Ndiponso kuti mukathe kukhulupilira uthenga wabwino wa Yesu Khristu, umene udzakhale pakati panu; ndiponso kuti Ayuda, anthu apangano a Ambuye, adzakhala ndi mboni ina kupatula iye amene adamuona ndi kumumvera, Khristu ameneyo, amene iwo adamupha, adali Khristu yemweyo ndi Mulungu yemweyo.

22 Ndipo ndikufuna kuti ndikulimbikitseni nonse akumalekezero a dziko lapansi kuti mulape ndi kukonzekera kuima pamaso pa mpando wa chiweruzo wa Khristu.

Print