Malembo Oyera
Mormoni 2


Mutu 2

Mormoni atsogolera ankhondo Achinefi—Mwazi ndi kuphana zisesa dziko—Anefi adandaula ndi kulira mwa chisoni cha olangidwa—Tsiku lawo la chisomo lidutsa—Mormoni atenga mapale a Nefi—Nkhondo zipitilira. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 327–350.

1 Ndipo zidachitika kuti m’chaka chomwecho kudayamba kukhala nkhondo kachiwiri pakati pa Anefi ndi Alamani. Ndipo posatengera kuti ndidali wamng’ono, ndidali wamkulu msinkhu; kotero anthu a Nefi adandisankha ine kukhala mtsogoleri wawo, kapena mtsogoleri wa ankhondo awo.

2 Kotero zidachitika kuti m’chaka cha khumi ndi zisanu n’chimodzi ndidapita patsogolo pa ankhondo Achinefi, motsutsana ndi Alamani; kotero dzaka mazana atatu ndi makumi awiri ndi mphambu zisanu n’chimodzi zidatha.

3 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha mazana atatu ndi makumi awiri ndi mphambu zisanu ndi ziwiri Alamani adabwera pa ife mwa mphamvu zazikulu kwambiri, kufikira kuti iwo adachititsa mantha ankhondo anga; kotero iwo sadamenyane, ndipo adayamba kuthawira chaku maiko akumpoto.

4 Ndipo zidachitika kuti tidafika ku mzinda wa Angola, ndipo tidalanda mzindawo, ndi kupanga zokonzekera kudziteteza tokha motsutsana ndi Alamani. Ndipo zidachitika kuti tidalimbitsa mzindawo ndi mphamvu zathu; koma posatengera za malinga athu onse Alamani adabwera pa ife ndipo adatithamangitsa ife kuchoka mu mzindawo.

5 Ndipo iwo adatithamangitsanso ife kuchoka mu dziko la Davide.

6 Ndipo tidaguba ndi kufika ku dziko la Yoswa, limene lidali mu malire kumadzulo kwa gombe la nyanja.

7 Ndipo zidachitika kuti tidawasonkhanitsa anthu athu mwachangu monga kudalili kothekera, kuti tithe kuwasonkhanitsa iwo pamodzi mu gulu limodzi.

8 Koma taonani, dzikolo lidali lodzadza ndi achifwamba ndi Alamani; ndipo posatengera za chiwonongeko chachikulu chimene chidali pa anthu anga, iwo sadalape pa zochita zawo zoipa; kotero kudali mwazi ndi kuphana kuzungulira pa nkhope ya dziko lonselo, konse kumbali ya Anefi ndiponso kumbali ya Alamani; ndipo kudali kusintha kotheratu kwakukulu kuzungulira dziko lonselo.

9 Ndipo tsopano, Alamani adali ndi mfumu, ndipo dzina lake lidali Aroni; ndipo iye adabwera motsutsana nafe ndi ankhondo okwana zikwi makumi anayi ndi zinayi. Ndipo taonani, ndidatsutsana naye ndi zikwi makumi anayi ndi ziwiri. Ndipo zidachitika kuti ndidamugonjetsa iye ndi ankhondo anga mpaka adathawa pamaso panga. Ndipo taonani, zonsezi zidachitika, ndipo dzaka mazana atatu ndi makumi atatu zidatha.

10 Ndipo zidachitika kuti Anefi adayamba kulapa ku zoipa zawo, ndipo adayamba kulira ngakhale monga kudaneneledwera ndi Samueli mneneri; pakuti taonani palibe munthu amene akadasunga icho chimene chidali chake, pakuti akuba, ndi achifwamba, ndi akupha anthu, ndi matsenga, ndi ufiti umene udali mudzikolo.

11 Choncho kudayamba kukhala maliro ndi kudandaula mu dziko lonselo chifukwa cha zinthu izi, ndipo makamaka pakati pa anthu a Nefi.

12 Ndipo zidachitika kuti pamene ine, Mormoni, ndidaona kudandaula kwawo ndi maliro awo ndi chisoni chawo pamaso pa Ambuye, mtima wanga udayamba kukondwera mkati mwanga, podziwa zifundo ndi kuleza mtima kwa Ambuye, kotero poganiza kuti iye adakhala wachifundo kwa iwo kuti adzakhalenso anthu olungama.

13 Koma taonani ichi chisangalalo changachi chidali pachabe, pakuti chisoni chawo sichidali cha kulapa, chifukwa cha ubwino wa Mulungu; koma chidali maka chisoni cha olangidwa, chifukwa choti Ambuye sangalore nthawi zonse kuti adzisangalala mu uchimo.

14 Ndipo iwo sadabwere kwa Yesu ndi mitima yosweka ndi mizimu yolapa, koma adatembelera Mulungu, ndipo adafuna kuti afe. Komabe iwo akadalimbana ndi lupanga pa moyo wawo womwe.

15 Ndipo zidachitika kuti chisoni changa chidabweleranso kwa ine, ndipo ndidaona kuti tsiku la chisomo lidawadutsa, konse kuthupi ndi kuuzimu; pakuti ndidaona zikwizikwi za iwo zikugwa mu kupanduka poyera motsutsana ndi Mulungu wawo, ndipo kuunjika ndowe pa nkhope ya dzikolo. Ndipo motero dzaka mazana atatu ndi makumi anayi ndi mphambu zinayi zidatha.

16 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha mazana atatu ndi makumi anayi ndi mphambu zisanu Anefi adayamba kuthawa pamaso pa Alamani; ndipo adathamangitsidwa kufikira atabwera ngakhale ku dziko la Yashoni, zisadatheke kuti awayimitse iwo mu kuthawa kwawoko.

17 Ndipo tsopano, mzinda wa Yashoni udali kufupi ndi dziko limene Amaroni adabisako zolemba kwa Ambuye, kuti zisakathe kuwonongedwa. Ndipo taonani ine ndidapita molingana ndi mawu a Amaroni, ndipo ndidatenga mapale a Nefiwo, ndikulembapo molingana ndi mawu a Amaroni.

18 Ndipo pamapale a Nefiwo ndidalembapo nkhani yonse ya zoipa ndi zonyansa; koma pamapale awa sindidafune kulembapo nkhani yonse ya zoipa ndi zonyansa zawo, pakuti taonani, zochitika zoipa ndi zonyansa zakhala zikupitilira pamaso panga kuyambira pamene ndidadziwa mokwanira njira za munthu.

19 Ndipo tsoka kwa ine chifukwa cha kuipa kwawo; pakuti mtima wanga wadzadzidwa ndi chisoni chifukwa cha kuipa kwawo, masiku anga onse, komabe, ndikudziwa kuti ndidzakwezedwa patsiku lotsiriza.

20 Ndipo zidachitika kuti mu chaka chimenechi anthu a Nefi adasakidwa ndi kuthamangitsidwa. Ndipo zidachitika kuti tidathamangitsidwa kufikira titafika chakumpoto kwa dziko limene linkatchedwa Semu.

21 Ndipo zidachitika kuti tidamanga malinga a mzinda wa Semu, ndipo tidasonkhanitsa anthu athu monga m’mene kudalili kothekera, kuti mwina tingathe kuwapulumutsa iwo kuchiwonongeko.

22 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha mazana atatu ndi makumi anayi ndi mphambu zisanu ndi chimodzi iwo adayamba kubweranso kwa ife.

23 Ndipo zidachitika kuti ndidayankhula kwa anthu anga, ndipo ndidawalimbikitsa iwo mwa mphamvu zazikulu, kuti ayime molimba mtima pamaso pa Alamani ndi kumenyera akazi awo, ndi ana awo, ndi nyumba zawo, ndi makomo awo.

24 Ndipo mawu anga adautsira iwo mphamvu zinazake, kufikira kuti sadathawe pamaso pa Alamani, koma adaima ndi kulimba mtima motsutsana nawo.

25 Ndipo zidachitika kuti tidalimbana ndi ankhondo zikwi makumi atatu kutsutsana ndi ankhondo zikwi makumi asanu. Ndipo zidachitika kuti tidaima pamaso pawo molimba mtima kotero kuti iwo adathawa pamaso pathu.

26 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adathawa ife tidawatsatira iwo ndi ankhondo athu, ndipo tidakumana nawo kachiwiri, ndipo tidawagonjetsa; komabe mphamvu ya Ambuye siidali nafe; inde, tidasiyidwa kwa ife tokha, pokuti Mzimu wa Ambuye sudakhale mwa ife; kotero tidakhala ofooka monga abale athuwo.

27 Ndipo mtima wanga udachita chisoni chifukwa cha tsoka lalikulu limeneli la anthu anga, chifukwa cha zoipa zawo ndi zonyansa zawo. Koma taonani, tidapitabe motsutsana ndi Alamani ndi achifwamba a Gadiyantoni, kufikira tidatenganso dziko la cholowa chathu.

28 Ndipo dzaka mazana atatu ndi makumi anayi ndi mphambu zisanu ndi zinayi zidapita. Ndipo mu chaka cha mazana atatu ndi makumi asanu tidapanga chigwilizano ndi Alamani ndi achifwamba a Gadiyantoni, mu chimene ife tidagawana maiko a cholowa chathu.

29 Ndipo Alamani adatipatsa ife dziko lakumpoto, inde, ngakhale ku njira yopapatiza imene imatsogolera ku dziko la kum’mwera. Ndipo ife tidawapatsa Alamani maiko onse akum’mwera.

Print