Malembo Oyera
Mormoni 1


Buku la Mormoni

Mutu 1

Amaroni alangiza Mormoni zokhudzana ndi zolemba zopatulika—Nkhondo iyambika pakati pa Anefi ndi Alamani—Anefi Atatu atengedwa—Kuipa, kusakhulupilira, matsenga ndi ufiti zipambana. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 321–326.

1 Ndipo tsopano, ine Mormoni, ndikupanga zolemba za zinthu zonse zimene ine ndaziona ndi kuzimva, ndipo ndikuzitchula kuti Buku la Mormoni.

2 Ndipo pafupi ndi nthawi imene Amaroni adabisa zolembazi kwa Ambuye, iye adabwera kwa ine, (ine pokhala wa dzaka pafupifupi khumi, ndipo ndidayamba kuphunzira zinthu zina potsatira kaphunziridwe ka anthu anga) ndipo Amaroni adati kwa ine: Ndikuona kuti ndiwe mwana wodziletsa, ndipo ndiwe wachangu pakumvera.

3 Kotero, pamene uli pafupifupi dzaka makumi awiri ndi zinayi ndikufuna kuti udzakumbukire zinthu zimene iwe waziona zokhudzana ndi anthu awa; ndipo pamene iwe udzakhala msinkhu umenewo udzapite ku dziko la Antumu, ku phiri limene lidzatchedwe Shimu; ndipo kumeneko ine ndabisako kwa Ambuye zozokotedwa zopatulika zonse zokhudzana ndi athu awa.

4 Ndipo taona, udzatenge mapale a Nefi kwa wekha, ndipo otsalawo udzawasiye m’malo amene aliwo; ndipo udzazokote pa mapale a Nefi zinthu zonse zimene iwe waziona zokhudzana ndi anthu awa.

5 Ndipo ine, Mormoni, pokhala chidzukulu cha Nefi, (ndipo dzina la atate anga lidali Mormoni) ndidakumbukira zinthu zimene Amaroni adandilamula.

6 Ndipo zidachitika kuti ine, pokhala wadzaka khumi ndi chimodzi, ndidatengedwa ndi atate anga kudziko la kum’mwera, ngakhale dziko la Zarahemula.

7 Dziko lonse lidakhala lophimbidwa ndi zomangamanga, ndipo anthu adali ochuluka pafupifupi, monga ngati udali mchenga wa kunyanja.

8 Ndipo zidachitika kuti mu chaka chimenechi kudayamba kukhala nkhondo pakati pa Anefi, amene adali ophatikizana Anefi ndi Ayakobe ndi Ayosefe ndi Azoramu; ndipo nkhondo imeneyi idali pakati pa Anefi, ndi Alamani ndi Alemueli ndi Aismaeli.

9 Tsopano Alamani ndi Alemueli ndi Aismaeli ankatchedwa Alamani, ndipo magulu awiriwa adali Anefi ndi Alamani.

10 Ndipo zidachitika kuti nkhondoyo idayamba kuchitika kumalire a Zarahemula, pafupi ndi madzi a Sidoni.

11 Ndipo zidachitika kuti Anefi adasonkhanitsa pamodzi chiwerengero chachikulu cha amuna, ngakhale kupitilira chiwerengero cha zikwi makumi atatu. Ndipo zidachitika kuti m’chaka chomwechi adakhala ndi nkhondo zingapo, m’mene Anefi adagonjetsa Alamani ndipo adapha ambiri mwa iwo.

12 Ndipo zidachitika kuti Alamani adasiya zolinga zawo, ndipo kudakhazikitsidwa mtendere mu dzikolo; ndipo mtenderewo udakhalabe kwa nthawi ya pafupifupi dzaka zinayi, komwe kudalibe kukhetsa mwazi.

13 Koma kuipa kudapambana pa nkhope ya dziko lonselo, kotero kuti Ambuye adachotsa ophunzira awo okondedwa, ndipo ntchito ya zozizwitsa ndi machilitso idasiyika chifukwa cha kusaweruzika kwa anthuwo.

14 Ndipo kudalibe mphatso zochokera kwa Ambuye, ndipo Mzimu Woyera sudafike pa aliyense, chifukwa cha kuipa kwawo ndi kusakhulupilira.

15 Ndipo ine, pokhala wadzaka khumi ndi zisanu ndipo pokhala wa malingaliro atcheru, kotero ndidayenderedwa ndi Ambuye, ndipo ndidalawa ndi kudziwa ubwino wa Yesu.

16 Ndipo ndidayesetsa kulalikira kwa anthu, koma pakamwa panga padatsekedwa, ndipo ndidaletsedwa kuti ndilalikire kwa iwo; pakuti taonani iwo adagalukira motsutsana ndi Mulungu wawo mwadala; ndipo ophunzira okondedwa adachotsedwa m’dzikolo, chifukwa cha mphulupulu zawo.

17 Koma ine ndidakhalabe pakati pawo, koma ndidaletsedwa kulalikira kwa iwo, chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo; ndipo chifukwa cha kuuma kwa mitima kwawoko dziko lidatembeleredwa chifukwa cha iwo.

18 Ndipo achifwamba a Gadiyantoni amenewa, amene adali pakati pa Alamani, adadzadza m’dzikolo, mpakana kuti okhalamo m’menemo adayamba kubisa chuma chawo mnthaka; ndipo chidakhala chotelera chifukwa Ambuye adatembelera dzikolo, kufikira kuti sadathe kuchisunga, kapena kuchibwenzeretsanso.

19 Ndipo zidachitika kuti kudali zamatsenga, ndi ufiti, ndi chitaka; ndipo mphamvu ya oipayo idakhazikika pa dziko lonselo, ngakhale kufikira pokwaniritsa mawu onse a Abinadi, ndiponso Samueli Mlamani.