Malembo Oyera
Mormoni 6


Mutu 6

Anefi asonkhana ku dziko la Kumora pa kumenyana komaliza—Mormoni abisa zolemba zopatulika mu phiri la Kumora—Alamani apambana, ndipo fuko la Anefi liwonongedwa—Mazana a Zikwi aphedwa ndi lupanga. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 385.

1 Ndipo tsopano ndikumaliza zolemba zanga zokhudzana ndi chiwonongeko cha anthu anga, Anefi. Ndipo zidachitika kuti ife tidaguba chitsogolo pamaso pa Alamani.

2 Ndipo ine, Mormoni, ndidalemba kalata kwa mfumu ya Alamani, ndipo ndidafuna kwa iye kuti atilore ife kuti tisonkhanitse pamodzi anthu athu ku dziko la Kumora, pafupi ndi phiri limene linkatchedwa Kumora, ndipo kumeneko tikathe kumenyana nawo.

3 Ndipo zidachitika kuti mfumu ya Alamani idandilora ine chinthu chimene ndidafuna.

4 Ndipo zidachitika kuti tidagubira ku dziko la Kumora, ndipo tidakhoma mahema athu mozungulira phiri la Kumora; ndipo lidali dziko la madzi ambiri, mitsinje, ndi akasupe; ndipo kuno tidali ndi chiyembekezo chopeza mwayi pa Alamani.

5 Ndipo pamene dzaka mazana atatu ndi makumi asanu ndi atatu mphambu zinayi zidatha, tidasonkhanitsa onse otsalira a anthu athu ku dziko la Kumora.

6 Ndipo zidachitika kuti pamene tidasonkhanitsa anthu athu onse ku dziko la Kumora, taonani ine, Mormoni, ndidayamba kukalamba; ndipo podziwa kuti kudali kulimbana komaliza kwa anthu anga, ndipo nditalamulidwa ndi Ambuye kuti ndisalore kuti zolemba, zimene zinkaperekedwa kuchokera kwa makolo athu, zimene zidali zopatulika, kuti zigwere m’manja mwa Alamani, (pakuti Alamani adzaziwononga) kotero ndidapanga zolembazi kuchokera ku mapale a Nefi, ndipo ndidabisa mu phiri la Kumora zolemba zonse zimene zidaperekedwa kwa ine ndi dzanja la Ambuye, kupatula mapale ochepawa amene ndidapereka kwa mwana wanga Moroni.

7 Ndipo zidachitika kuti anthu anga, ndi akazi awo ndi ana awo, tsopano adaona ankhondo Achilamani akugubira kufupi nawo; ndipo ndi mantha oopsya a imfa amene amadzadza pazifuwa za onse oipa, adayembekezera kuwalandira iwo.

8 Ndipo zidachitika kuti adabwera kudzamenyana nafe, ndipo munthu aliyense adadzadzidwa ndi mantha chifukwa chakukula kwa chiwerengero chawo.

9 Ndipo zidachitika kuti adagwera pa anthu anga ndi lupanga, ndi mauta, ndi mivi, ndi nkhwangwa, ndi zida zankhondo zamitundu yonse.

10 Ndipo zidachitika kuti anthu anga adakhapidwa, inde, ngakhale zikwi khumi amene adali ndi ine, ndipo ine ndidavulazidwa mkatimo; ndipo iwo adandidutsa ine moti sadayike chimaliziro ku moyo wanga.

11 Ndipo pamene iwo adadutsa ndi kukhapa anthu anga onse kupatula makumi awiri ndi anayi a ife, (m’modzi mwa iwo adali mwana wanga Moroni) ndipo ife populumuka imfa ya anthu athu, tidaona m’mawa mwake, pamene Alamani adabwelera ku misasa yawo, kuchokera pamwamba pa phiri la Kumora, zikwi khumi za anthu anga amene adakhapidwa potsogoleredwa kutsogolo ndi ine.

12 Ndipo tidaonanso zikwi khumi za anthu anga amene adatsogoleredwa ndi mwana wanga Moroni.

13 Ndipo taonani, zikwi khumi za Gigidona zidagwa, ndipo iyenso adali mkatimo.

14 Ndipo Lama adagwa ndi zikwi khumi zake; ndi Giligala adagwa ndi zikwi khumi zake; ndi Limuha adagwa ndi zikwi khumi zake; ndi Jenemu adagwa ndi zikwi khumi zake; ndi Kumeniha adagwa ndi zikwi khumi zake, ndi Moroniha, ndi Antionamu, ndi Shibulomu, ndi Semu, ndi Yosi, adagwa ndi zikwi khumi zawo aliyense.

15 Ndipo zidachitika kuti kudali khumi ena amene adagwa ndi lupanga, ndi zikwi khumi zawo aliyense; inde, ngakhale anthu anga onse, kupatula adalipo makumi awiri amene adali ndi ine, ndiponso ochepa amene adathawira ku maiko akum’mwera, ndi ochepa amene adathawira kwa Alamani, adagwa; ndipo minofu yawo, ndi mafupa awo, ndi mwazi zili pa nkhope ya dziko lapansi, atasiyidwa ndi m’manja mwa iwo amene adawapha kuti awolele pa nthaka, ndi kunyenyeka ndi kubwelera kwa kholo lawo dothi.

16 Ndipo mtima wanga udang’ambika ndi kuwawidwa, chifukwa cha kuphedwa kwa anthu anga, ndipo ndidalira:

17 O inu owoneka bwino, kodi mudachokeranji mu njira za Ambuye! O inu owoneka bwino, kodi mudakaniranji kuti Yesu, amene adaima ndi manja otsegula kuti akulandireni!

18 Taonani, ngati mudakapanda kuchita izi, simukadagwa. Koma taonani, inu mwagwa, ndipo ine ndikulira kutaika kwanu.

19 O inu ana aamuna ndi aakazi owoneka bwino, inu azibambo ndi azimayi, inu amuna ndi akazi, inu owoneka bwino, zatheka bwanji kuti mugwe!

20 Koma taonani, inu mwapita, ndipo chisoni changa sichingathe kupangitsa kubwelera kwanu.

21 Ndipo tsiku likudza posachedwa limene chokufa chanu chidzavala chosafa, ndipo matupi awa amene ali kuwola tsopano m’kuvunda akuyenera posachedwa kukhala matupi osavunda; ndipo mukuyenera kudzaima pamaso pa mpando wa chiweruzo wa Khristu, kuti mudzaweruzidwe molingana ndi ntchito zanu; ndipo ngati zili kuti ndinu olungama, ndiye ndinu odalitsidwa ndi makolo anu amene adatsogola pamaso panu.

22 O kuti inu mudalapa chiwonongeko chachikulu ichi chisadafike pa inu. Koma taonani, inu mwapita, ndipo Atate, inde, Atate wa Muyaya wakumwamba, akudziwa nyengo yanu; ndipo achita kwa inu molingana ndi chilungamo chake ndi chifundo.

Print