Mutu 7
Mormoni aitana Alamani a m’masiku otsiriza kuti akhulupilire mwa Khristu, kuvomereza uthenga wabwino wake, ndi kupulumutsidwa—Onse amene amakhulupilira mu Baibulo adzakhulupiliranso mu Buku la Mormoni. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 385.
1 Ndipo tsopano, taonani, ndikufuna kuyankhula zinthu zina kwa otsalira a anthu awa amene apulumuka, ngati kungatheke kuti Mulungu athe kuwapatsa mawu anga, kuti iwo adziwe zinthu za makolo awo; inde, ndikuyankhula kwa inu, inu otsalira a nyumba ya Israeli; ndipo awa ndiwo mawu amene ndikuyankhula:
2 Mukudziwa kuti ndinu a nyumba ya Israeli.
3 Mukudziwa kuti mukuyenera kubwera kolapa, kupanda apo simungapulumutsidwe.
4 Mukudziwa kuti mukuyenera kutula pansi zida zanu zankhondo, ndi kusakondweranso m’kukhetsa mwazi, ndi kusazitenganso, kupatula akhale kuti Mulungu wakulamulani.
5 Mukudziwa kuti mukuyenera kubwera ku chidziwitso cha makolo anu, ndi kulapa machimo anu onse ndi mphulupulu, ndi kukhulupilira mwa Yesu Khristu, kuti iye ndi Mwana wa Mulungu, ndipo kuti iye adaphedwa ndi Ayuda, ndipo ndi mphamvu ya Atate iye waukanso, pamene iye wapeza chigonjetso pa manda; ndiponso mwa iye mbola ya imfa yamezedwa.
6 Ndipo iye akubweretsa chiukitso cha okufa, kumene munthu akuyenera kuukitsidwa kuti akaime pamaso pa mpando wake wa chiweruzo.
7 Ndipo wabweretsa chiwombolo cha dziko lapansi, kumene iye amene apezeka osalakwa pamaso pake pa tsiku lachiweruzo chapatsidwa kwa iye kukakhala pamaso pa Mulungu mu ufumu wake, kukaimba mosalekeza matamando ndi oyimba akumwamba, kwa Atate, ndi kwa Mwana, ndi kwa Mzimu Woyera, amene ndi Mulungu m’modzi, mu chikhalidwe cha chimwemwe chimene chilibe mapeto.
8 Kotero lapani, ndi kubatizidwa mu dzina la Yesu, ndi kugwiritsitsa pa uthenga wabwino wa Khristu umene udzaikidwa pamaso panu, osati mu zolemba izi zokha komanso mu zolemba zimene zidzabwere kwa inu ndi Amitundu kuchokera kwa Ayuda, zolemba zake zidzabwera kuchokera kwa Amitundu kwa inu.
9 Pakuti taonani, izi zalembedwa ndi cholinga choti inu mukathe kukhulupilira zimenezo, ndipo ngati mukhulupilira zimenezo mudzakhulupiliranso zimenezi; ndipo ngati mukhulupilira zimenezi muzadziwa zokhudzana ndi makolo anu, ndiponso ntchito zodabwitsa zimene zidachitidwa ndi mphamvu ya Mulungu pakati pawo.
10 Ndipo mudzadziwanso kuti ndinu otsalira a mbewu ya Yakobo; kotero mukuwerengedwa pamodzi ndi anthu a chipangano choyamba; ndipo ngati mungakhale kuti mwakhulupilira mwa Khristu, ndi kubatizidwa, koyamba ndi madzi, kenako ndi moto ndipo ndi Mzimu Woyera, kutsatira chitsanzo cha Mpulumutsi wathu, molingana ndi icho chimene iye watilamula ife, zidzakhala bwino ndi inu mu tsiku la chiweruzo. Ameni.