Malembo Oyera
Helamani 9


Mutu 9

Atumiki apeza wamkulu wa oweruza atafa pa mpando oweruzira—Aikidwa m’ndende ndipo pambuyo pake amasulidwa—Mwa kutsogozedwa kwakudzodzedwa Nefi azindikiritsa Seyantumu monga wakupha—Nefi avomerezedwa ndi ena monga mneneri. Mdzaka dza pafupifupi 23–21 Yesu asadabadwe.

1 Taonani, tsopano zidachitika kuti pamene Nefi adayankhula mawu awa, anthu ena amene adali pakati pawo adathamangira kumpando wa chiweruzo; inde, adalipo asanu amene adapita, ndipo adanena mwa iwo okha, pamene adali kupita:

2 Taonani, tsopano ife tidzadziwa motsimikizika ngati munthu uyu ali mneneri ndipo Mulungu wamulamulira iye kuti anenere zinthu zodabwitsa motero kwa ife. Taonani, sitikukhulupilira kuti ali; inde, sitikukhulupilira kuti ndi mneneri; komabe, ngati chinthu ichi chimene wanena chokhudza oweruza wamkulu chili choona, kuti iye wafa, pamenepo ife tidzakhulupilira kuti mawu ena amene iye wayankhula ali owona.

3 Ndipo zidachitika kuti adathamanga ndi mphamvu zawo, ndikukalowa ku mpando wa chiweruzo; ndipo taonani, oweruza wamkulu adali atagwa pansi, ndipo adagona m’mwazi wake.

4 Ndipo tsopano taonani, pamene adaona ichi adazizwa kwambiri, kotero kuti adagwa pansi; pakuti sadakhulupilire mawuwo amene Nefi adayankhula okhudza oweruza wamkulu.

5 Koma tsopano, pamene adaona adakhulupilira, ndipo mantha adadza pa iwo kuopa kuti ziweruzo zonse zimene Nefi adayankhula zikuyenera kubwera pa anthu; kotero iwo adanjenjemera, ndipo adagwa pansi.

6 Tsopano, pomwepo pamene oweruzayo adaphedwa—iye atabayidwa ndi m’bale wake ataziphimba ndi chovala cha chinsinsi, ndi kuthawa, ndipo antchito adathamanga ndikukauza anthu, akukweza mfuu wakupha pakati pawo;

7 Ndipo taonani, anthuwo adadzisonkhanitsa pamodzi kumalo a mpando wa chiweruzo—ndipo taonani, m’kudabwitsika kwawo adaona anthu asanu amene adagwa pansi aja.

8 Ndipo tsopano taonani, anthuwo sadadziwe kalikonse kokhudzana ndi khamulo limene lidasonkhana pamodzi m’munda wa Nefi; kotero adati pakati pa iwo okha, Anthu awa ndi amene adapha oweruzayo, ndipo Mulungu adawakantha kotero kuti sakadatha kutithawa.

9 Ndipo zidachitika kuti adawagwira, ndi kuwamanga, ndi kuwaponya mu ndende. Ndipo kumeneko kudali chilengezo chotumizidwa kunja kuti oweruza adaphedwa, ndipo kuti adamupha adatengedwa ndipo adaponyedwa m’ndende.

10 Ndipo zidachitika kuti mawa lake anthu adasonkhana pamodzi kukalira ndi kukasala kudya, pa kuikidwa kwa oweruza wamkulu amene adaphedwa.

11 Ndipo motero, nawonso oweruza aja amene adali m’munda wa Nefi, ndipo adamva mawu ake, adasonkhananso pamanda.

12 Ndipo zidachitika kuti adafunsa mwa anthu, nanena, Ali kuti asanu amene adatumidwa kukafunsa zokhudza oweruza wamkulu ngati adamwalira? Ndipo iwo adayankha nati: Zokhudzana ndi awa asanu amene mukunena kuti mudawatuma, sitikuwadziwa; koma alipo asanu amene ali akupha, omwe tidawaponya m’ndende.

13 Ndipo zidachitika kuti oweruzawo adafuna kuti abweretsedwe; ndipo adabweretsedwa, ndipo taonani, iwo adali asanu amene adatumidwa; ndipo taonani, oweruzawo adawafunsa kuti adziwe zokhudza nkhaniyi, ndipo adawauza zonse zimene adachita, kuti:

14 Tidathamanga ndipo tidafika ku malo a mpando wa chiweruzo, ndipo pamene tidaona zinthu zonse ngakhale monga Nefi adachitira umboni, tidadabwa kwambiri kotero kuti tidagwa pansi; ndipo pamene tidatsitsimuka m’kudabwitsika kwathu, taonani, adatiponya m’ndende.

15 Tsopano, za kuphedwa kwa munthu uyu, ife sitidziwa amene adachita; ndipo izi zokha zomwe tikudziwa, tidathamanga ndipo tidabwera molingana ndi momwe mudafunira, ndipo taonani adali atafa, molingana ndi mawu a Nefi.

16 Ndipo tsopano zidachitika kuti oweruzawo adafotokoza nkhaniyo kwa anthu, ndipo adafuula motsutsa Nefi, kuti: Taonani, ife tikudziwa kuti Nefi uyu akuyenera kuti adagwirizana ndi wina kuti aphe oweruza, ndipo kenako kuti iye athe kulengeza kwa ife, kuti athe kutitembenuzira ife ku chikhulupiliro chake, kuti iye athe kudzikweza yekha kuti akhale munthu wamkulu, osankhidwa ndi Mulungu, ndi mneneri.

17 Ndipo tsopano taonani, ife timubweretsa poyera munthu uyu, ndipo adzavomereza kulakwa kwake ndi kutidziwitsa ife wakupha weniweni wa oweruzayu.

18 Ndipo zidachitika kuti asanuwo adamasulidwa pa tsiku loika malirowo. Komabe, iwo adadzudzula oweruzawo m’mawu amene iwo adayankhula motsutsana ndi Nefi; ndipo adalimbana nawo m’modzi m’modzi, kotero kuti adawakhazika chete iwo.

19 Komabe, iwo adapangitsa kuti Nefi atengedwe ndi kumangidwa ndi kubweretsedwa pamaso pa khamulo, ndipo adayamba kumufunsa iye m’njira zosiyanasiyana, kuti amukole, kuti akamuyimbe mlandu wa imfa—

20 Nati kwa iye: Wachita mgwirizano; munthu uyu ndi ndani amene wachita kupha uku? Tsopano tiuze, ndipo vomereza kulakwa kwako; kuti, Taonani, ndalama ndi izi; ndipo tikupatsa moyo wako ngati ungatiuze, ndi kuvomereza pangano lomwe udapangana naye.

21 Koma Nefi adati kwa iwo, O wopusa inu, wosadulidwa mtima inu, akhungu inu, ndi anthu osamva inu, kodi mukudziwa kuti Ambuye Mulungu wanu adzakulolerani mpaka liti kuti mupitilire m’njira yanu yauchimo iyi?

22 O inu mukuyenera kuyamba kulira ndi kubuula, chifukwa cha chiwonongeko chachikulu chimene pa nthawi ino chikukudikirani inu, pokhapokha inu mudzalape.

23 Taonani inu mukunena kuti ine ndagwirizana ndi munthu kuti aphe Seezoramu, mkulu wa oweruza wathu. Koma onani, ndikunena kwa inu, kuti ichi n’chifukwa ine ndachitira umboni kwa inu kuti inu mukathe kudziwa zokhudza chinthu ichi; inde, ngakhale kuti ukhale umboni kwa inu, kuti ndidadziwa za zoipa ndi zonyansa zimene zili mwa inu.

24 Ndipo chifukwa ndachita ichi, mukunena kuti ndapangana ndi munthu kuti achite ichi; inde, popeza ndakuonetsani chizindikiro ichi, mwandikwiyira, ndipo mukufuna kuwononga moyo wanga.

25 Ndipo tsopano taonani, ndidzakuwonetsani chizindikiro china, ndipo muone ngati muchinthu ichi mukufuna kundiwononga.

26 Taonani Ine ndikunena kwa inu: Pitani ku nyumba ya Seyantumu, yemwe ali m’bale wa Seezoramu, ndipo kaneneni kwa iye—

27 Kodi Nefi, mneneri wonamizira, amene akunenera zoipa zochuluka motere zokhudza anthu awa, wagwirizana ndi iwe, m’mene mudapha Seezoramu, amene ali m’bale wako?

28 Ndipo taonani, adzanena kwa inu, Ayi.

29 Ndipo mudzati kwa iye: Kodi wapha m’bale wako?

30 Ndipo adzaimilira ndi mantha, osadziwa choti anene. Ndipo taonani, adzakana kwa inu; ndipo adzachita ngati akudabwa; komabe, iye adzanena kwa inu kuti iye ndi osalakwa.

31 Koma taonani, mudzamuyang’anitsitsa, ndipo mudzapeza mwazi m’mphepete mwa chovala chake.

32 Ndipo pamene mudzaona ichi, mudzati, Kodi mwazi uwu wachokera kuti? Sitikudziwa kuti ndi mwazi wa m’bale wako?

33 Ndipo pamenepo adzanjenjemera, ndikudzaoneka otumbululuka, ngati kuti imfa yafika pa iye.

34 Pamenepo mudzati, Chifukwa cha mantha awa ndi kutumbululuka kumene kwakugwera pa nkhope, taona, ife tikudziwa kuti iwe ndi olakwa.

35 Ndipo pamenepo mantha aakulu adzamugwera; ndipo pamenepo adzavomereza kwa inu, ndipo sadzakananso kuti adachita kupha uku.

36 Ndipo kenako adzanena kwa inu, kuti ine, Nefi, sindikudziwa kalikonse zokhudza nkhaniyo koma kuti idapatsidwa kwa ine ndi mphamvu ya Mulungu. Ndipo pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine munthu oona mtima, ndipo kuti ine ndidatumidwa kwa inu kuchokera kwa Mulungu.

37 Ndipo zidachitika kuti iwo adapita ndipo adachita, ngakhale monga momwe Nefi adanenera kwa iwo. Ndipo taonani, mawu amene iye adanena adali oona; pakuti molingana ndi mawuwo adakana; komanso molingana ndi mawuwo adavomereza.

38 Ndipo adabweretsedwa kuti atsimikizire kuti iye mwini adali wakupha yemweyo, mwakuti asanuwo adamasulidwa, ndipo nayenso Nefi.

39 Ndipo padali ena a Anefi amene adakhulupilira mawu a Nefi; ndipo padalinso ena amene adakhulupilira chifukwa cha umboni wa asanuwo; pakuti adatembenuka ali m’ndende.

40 Ndipo padali ena mwa anthuwo; amene adanena kuti Nefi adali mneneri.

41 Ndipo adaliponso ena omwe adati: Taonani, iye ndi mulungu; pakuti pokhapokha atakhala mulungu sakadatha kudziwa zinthu zonsezi. Pakuti, taonani, watiuza maganizo a mitima yathu, ndiponso watiuza zinthu; ndipo ngakhale iye wabweretsa ku chidziwitso chathu wakupha weniweni wa mkulu wa oweruza wathu.

Print