Malembo Oyera
Helamani 1


Buku la Helamani

Nkhani ya Anefi. Nkhondo ndi mikangano yawo, ndi kusagwirizana kwawo. Ndiponso mauneneri a ambiri a aneneri oyera, asadabwere Khristu, molingana ndi zolemba za Helamani, amene adali mwana wa Helamani, ndiponso molingana ndi zolemba za ana ake, ngakhale mpaka kufikira pa kudza kwa Khristu. Ndiponso ambiri a Alamani atembenuka. Nkhani ya kutembenuka kwawo. Nkhani ya kulungama kwa Alamani, ndi kuipa ndi zonyansa za Anefi, molingana ndi zolemba za Helamani ndi ana ake aamuna, ngakhale kutsika mpaka pa kubwera kwa Khristu, limene likutchedwa Buku la Helamani, ndi zina zotero.

Mutu 1

Pahorani wachiwiri akhala mkulu wa oweruza ndipo aphedwa ndi Kishkumeni—Pakumeni akhala pa mpando wa chiweruzo—Koriyantumuri atsogolera magulu ankhondo a Alamani, atenga Zarahemula, ndipo apha Pakumeni—Moroniha agonjetsa Alamani ndi kutenganso Zarahemula, ndipo Koriyantumuri aphedwa. Mdzaka dza pafupifupi 52–50 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano taonani, zidachitika kumayambiliro a chaka cha makumi anayi a ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, kudayamba kukhala vuto lalikulu pakati pa anthu a Anefi.

2 Pakuti taonani, Pahorani adamwalira, ndipo adatsikira kulichete; choncho kudayamba kukhala mkangano waukulu wokhudzana ndi ndani amene akuyenera kukhala pampando wa chiweruzo pakati pa abale, womwe adali ana a Pahorani.

3 Tsopano awa ndi maina awo a amene adalimbirana mpando wa chiweruzo, amene adachititsanso anthu kulimbana: Pahorani, Paanchi, ndi Pakumeni.

4 Tsopano awa sadali onse a ana aamuna a Pahorani (popeza adali nawo ambiri), koma awa ndiwo amene adapikisana pampando wa chiweruzo; kotero, iwo adachititsa magawo atatu pakati pa anthu.

5 Komabe, zidachitika kuti Pahorani adasankhidwa ndi mawu a anthu kuti akhale oweruza wamkulu ndi bwanamkubwa pa anthu a Nefi.

6 Ndipo zidachitika kuti Pakumeni, pamene adaona kuti sakadatha kupeza mpando wa chiweruzo, iye adagwirizana ndi mawu a anthu.

7 Koma taonani, Paanchi, ndi gawo ilo la anthu amene adali kufuna kuti akhale bwanamkubwa wawo, adali wokwiya kwambiri; kotero, iye adali pafupi kukopa anthu awo kuti adzuke mu kuwukira motsutsa abale awo.

8 Ndipo zidachitika pamene iye adali pafupi kuchita ichi, taonani, iye adagwidwa, ndipo adayesedwa monga mwa mawu a anthu, ndipo adaweruzidwa kuti aphedwe; pakuti iye adauka mu kuwukira ndipo adafuna kuwononga ufulu wa anthu.

9 Tsopano pamene anthu aja amene adali kufuna kuti iye akhale bwanamkubwa wawo adaona kuti adaweruzidwa kuti aphedwe, kotero adakwiya, ndipo taonani, iwo adatuma m’modzi Kishkumeni, ngakhale ku mpando wa chiweruzo wa Pahorani, ndipo adapha Pahorani pamene adakhala pa mpando wa chiweruzo.

10 Ndipo adatsatiridwa ndi antchito a Pahorani; koma taonani, kuthawa kwa Kishkumeni kudali kwa liwiro kotero kuti palibe munthu akadatha kumupeza iye.

11 Ndipo iye adapita kwa iwo amene adamutuma iye, ndipo onse adalowa mu pangano, inde, kulumbira pa Mlengi wawo wosatha, kuti sadzauza aliyense kuti Kishkumeni adapha Pahorani.

12 Kotero, Kishkumeni sadadziwike mwa anthu a Nefi, pakuti adadzibisa pa nthawi yomwe adapha Pahorani. Ndipo Kishkumeni ndi agulu lake, amene adapanga naye pangano, adadzisakaniza okha mwa anthu, mwanjira yakuti iwo wonse sadapezeke; koma wonse amene adapezedwa adaweruzidwa kuti aphedwe.

13 Ndipo tsopano taonani, Pakumeni adasankhidwa, monga mwa mawu a anthu, kuti akhale oweruza wamkulu ndi bwanamkubwa pa anthu, kulamulira m’malo mwa m’bale wake Pahorani; ndipo kudali monga mwa ufulu wake. Ndipo zonsezi zidachitidwa m’chaka cha makumi anayi cha ulamuliro wa oweruza; ndipo chidali ndi mathero.

14 Ndipo zidachitika mu chaka cha makumi anayi ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza, kuti Alamani adasonkhanitsa pamodzi gulu lankhondo losawerengeka la anthu, ndipo adawapatsa iwo malupanga, ndi zikwanje, ndi mauta, ndi mivi, ndi zisoti zotetezera ku mutu, ndi za pachifuwa, ndi zishango zamtundu uliwonse.

15 Ndipo iwo adabweranso kuti akathe kupanga nkhondo molimbana ndi Anefi. Ndipo iwo adalondoledwa ndi munthu yemwe dzina lake adali Koriantumuri; ndipo iye adali chidzukulu cha Zarahemula; ndipo adali ogalukira kuchokera pakati pa Anefi; ndipo adali munthu wamkulu ndi wamphamvu.

16 Kotero, mfumu ya Alamani, imene dzina lake lidali Tubaloti, amene adali mwana wa Amoroni, poganiza kuti Koriantumuri, pokhala munthu wamphamvu, akhonza kuyima motsutsana ndi Anefi, ndi mphamvu zake komanso ndi nzeru zake zazikulu, kotero kuti potumiza iye akuyenera kupeza mphamvu pa Anefi—

17 Kotero adawautsa iwo ku mkwiyo, ndipo adasonkhanitsa pamodzi ankhondo ake, ndipo adasankha Koriyantumuri kukhala mtsogoleri wawo, ndipo adapangitsa kuti agube pansi ku dziko la Zarahemula kukamenyana ndi Anefi.

18 Ndipo zidachitika kuti chifukwa cha mikangano yambiri ndi zovuta zambiri m’boma, kuti sadasunge alonda okwanira m’dziko la Zarahemula; pakuti adayesa kuti Alamani sakadayerekeza kubwera pakati pa maiko awo kuti akaukire mzinda waukulu uja wa Zarahemla.

19 Koma zidachitika kuti Koriyantumuri adagubira patsogolo pa gulu lake lalikulu lankhondo, ndipo adafika pa anthu a mzindawo, ndipo kuguba kwawo kudali ndi liwiro lalikulu kwambiri kotero kuti padalibe nthawi kuti Anefi asonkhanitse pamodzi ankhondo awo.

20 Chotero Koriyantumuri adapha alonda pakhomo la mzindawo, ndipo adaguba ndi gulu lake lonse lankhondo kulowa m’mzindawo, ndipo adapha aliyense amene adawatsutsa, kufikira kuti iwo adalanda mzinda wonsewo.

21 Ndipo zidachitika kuti Pakumeni, yemwe adali oweruza wamkulu, adathawa pamaso pa Koriyantumuri, ngakhale mpaka ku makoma a mzindawo. Ndipo zidachitika kuti Koriyantumuri adamumenyetsa iye ku khoma, kufikira kuti adafa. Ndipo motero adatha masiku a Pakumeni.

22 Ndipo tsopano pamene Koriyantumuri adawona kuti adali atatenga mzinda wa Zarahemula, ndipo atawona kuti Anefi adathawa pamaso pawo, ndipo adaphedwa, ndi kutengedwa, ndi kuponyedwa m’ndende, ndipo adalanda malo a linga lamphamvu m’dziko lonselo, mtima wake udalimba kotero kuti adali pafupi kupita kukamenyana ndi dziko lonselo.

23 Ndipo tsopano sadachedwe m’dziko la Zarahemula, koma adaguba ndi gulu lankhondo lalikulu, ngakhale kupita ku mzinda wa Chuluka; pakuti adatsimikiza mtima kupita ndi kupyoza ndi lupanga njira yake, kuti akatenge mbali za kumpoto kwa dzikolo.

24 Ndipo, poganiza kuti mphamvu zawo zazikulu zidali pakati pa dzikolo, kotero adaguba, osawapatsa iwo nthawi ya kudzisonkhanitsa pamodzi kupatula m’magulu ang’onoang’ono; ndipo moteremu iwo adagwa pa iwo ndi kuwagwetsera pansi.

25 Koma taonani, kuguba uku kwa Koriyantumuri kudutsa pakati pa dziko kudapatsa Moroniha mwayi waukulu pa iwo, pakusaganizira za kukula kwa chiwerengero cha Anefi amene adaphedwa.

26 Pakuti, taonani, Moroniha adaganiza kuti Alamani sakadayerekeza kubwera pakati pa dzikolo, koma kuti adzaukira mizinda yozungulira m’malire monga adali kuchitira; kotero Moroniha adali atapangitsa kuti magulu ankhondo awo amphamvu ayenera kusunga zigawo izo zozungulirana ndi malire.

27 Koma taonani, Alamani sadawopsedwe monga mwa chikhumbo chake, koma iwo adali atabwera pakati pa dzikolo, ndipo adali atatenga mzinda waukulu umene udali mzinda wa Zarahemla, ndipo adali kuguba kudutsa madera akuluakulu a dzikolo, akupha anthu ndi kupha kwakukulu, wonse akazi, ndi ana, kutenga midzi yambiri ndi malinga ambiri.

28 Koma pamene Moroniha adazindikira izi, pomwepo adatumiza Lehi ndi gulu lankhondo mozungulira kuti awatchingire iwo asadabwere ku dziko la Chuluka.

29 Ndipo adachita motero; ndipo adawatchingira asadafike kudziko la Chuluka; ndi kupereka kwa iwo nkhondo, kotero kuti adayamba kubwelera m’mbuyo ku dziko la Zarahemula.

30 Ndipo zidachitika kuti Moroniha adawatsatira iwo m’kubwelera kwawo, ndipo adamenya kwa iwo nkhondo, moti idakhala nkhondo yamwazi ochuluka; inde, wochuluka adaphedwa, ndipo pakati pa chiwerengero chimene chidaphedwa Koriyantumuri adapezekaponso.

31 Ndipo tsopano, taonani, Alamani sakadatha kubwelera njira iliyonse, kapena kumpoto, kapena kumwera, kapena kummawa, kapena kumadzulo, pakuti adazingidwa pa dzanja lirilonse ndi Anefi.

32 Ndipo motero Koriyantumuri adagwetsera Alamani pakati pa Anefi, mpaka kuti iwo adali mu mphamvu ya Anefi, ndi iye mwini adaphedwa, ndipo Alamani adadzipereka wokha m’manja mwa Anefi.

33 Ndipo zidachitika kuti Moroniha adatenganso mzinda wa Zarahemula, ndipo adapangitsa kuti Alamani amene adatengedwa ukaidi kuti achoke m’dzikolo mu mtendere.

34 Ndipo kotero chidatha chaka cha makumi anayi ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza.