Malembo Oyera
Helamani 4


Mutu 4

Opanduka a Chinefi ndi Alamani aphatikizana ndi kutenga dziko la Zarahemula—Zigonjetso za Anefi zikudza chifukwa cha kuipa kwawo—Mpingo ucheperachepera, ndipo anthu akhala ofooka ngati Alamani. Mdzaka dza pafupifupi 38–30 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika m’chaka cha makumi asanu ndi chinayi mudali kusagwirizana kwambiri mu mpingo, ndipo mudalinso mkangano pakati pa anthu, kotero kuti mudali kukhetsa mwazi kochuluka.

2 Ndipo gawo lopandukiralo lidaphedwa ndi kuthamangitsidwa m’dzikolo, ndipo lidapita kwa mfumu ya Alamani.

3 Ndipo zidachitika kuti adayesetsa kuti autse Alamani kuti amenyane ndi Anefi; koma taonani, Alamani adachita mantha kwambiri, kotero kuti sadamvere mawu a ogalukirawo.

4 Koma zidachitika m’chaka cha makumi asanu ndi zisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza, kumeneko kudali opanduka amene adapita kuchokera kwa Anefi kupita kwa Alamani; ndipo iwo adapambana ndi enawo mukuwautsa iwo ku mkwiyo motsutsa Anefi; ndipo adakonzekera nkhondo chaka chonsecho.

5 Ndipo mu chaka cha makumi asanu ndi zisanu ndi ziwiri iwo adabwera motsutsana ndi Anefi ku nkhondo, ndipo iwo adayamba ntchito yakupha; inde, kotero kuti mu makumi asanu ndi mphambu zisanu ndizitatu a ulamuliro wa oweruza adapambana mu kutenga dziko la Zarahemula; inde, komanso maiko onse, kufikira ku dziko limene lidali pafupi ndi dziko la Chuluka.

6 Ndipo Anefi ndi magulu ankhondo a Moroniha adayendetsedwa ngakhale ku dziko la Chuluka;

7 Ndipo kumeneko iwo adalimbitsa linga motsutsana ndi Alamani, kuchokera ku nyanja ya kumadzulo, ngakhale mpaka kummawa; iwo pokhala ulendo wa tsiku limodzi kwa Mnefi, pa mzere umene iwo adali atalimbitsa ndi kuika ankhondo awo kuti ateteze dziko lawo la kumpoto.

8 Ndipo kotero ogalukira awo a Anefi, mothandizidwa ndi gulu lankhondo lochuluka la Alamani, adali atapeza chuma chonse cha Anefi chomwe chidali m’dziko la kummwera. Ndipo zonsezi zidachitika mu dzaka makumi asanu ndi zisanu ndi zitatu ndiponso zisanu ndi zinayi za ulamuliro wa oweruza.

9 Ndipo zidachitika m’chaka cha makumi asanu ndi limodzi cha ulamuliro wa oweruza, Moroniha adapambana ndi magulu ankhondo ake pakutenga zigawo zambiri za dziko; inde, adatenga mizinda yambiri imene idagwa m’manja mwa Alamani.

10 Ndipo zidachitika m’chaka cha makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu imodzi cha ulamuliro wa oweruza iwo adapambana ngakhale kubwenzeretsa theka la chuma chawo chonse.

11 Tsopano kutaika kwakukulu uku kwa Anefi, ndi kupha kwakukulu kumene kudali pakati pawo sikukadachitika chikadapanda kukhala chifukwa cha kuipa kwawo ndi chonyansa chawo chimene chidali pakati pawo; inde, ndipo chidalinso mwa iwo amene adadzinenera kukhala a Mpingo wa Mulungu.

12 Ndipo chidali chifukwa cha kunyada kwa mitima yawo, chifukwa cha chuma chawo chochuluka, inde, chidali chifukwa cha kupondereza kwawo kwa osauka, kumana chakudya chawo kwa anjala, kumana zovala zawo kwa amaliseche, ndi kukantha abale awo odzichepetsa pa tsaya, kupanga m’nyozo kwa icho chimene chidali chopatulika, kukana mzimu wa uneneri ndi wa vumbulutso, kupha, kuononga, kunama, kuba, kuchita chigololo, kuwuka mu mikangano ikuluikulu, ndi kupatukira kupita ku dziko la Nefi, pakati pa Alamani—

13 Ndipo chifukwa cha kuipa kwawo kwakukulu, ndi kudzitamandira kwawo mu mphamvu zawo, adasiyidwa mu mphamvu zawo; kotero iwo sadachite bwino, koma adasautsidwa ndi kukanthidwa, ndi kuthamangitsidwa patsogolo pa Alamani, mpaka iwo atataya pafupifupi maiko awo wonse.

14 Koma taonani, Moroniha adalalikira zinthu zambiri kwa anthu chifukwa cha uchimo wawo, ndiponso Nefi ndi Lehi, womwe adali ana aamuna a Helamani, adalalikira zinthu zambiri kwa anthu, inde, ndipo adanenera zinthu zambiri kwa iwo za mphulupulu zawo, ndi chimene chingawadzere ngati salapa machimo awo.

15 Ndipo zidachitika kuti adalapa, ndipo monga momwe adalapa iwo adayamba kuchita bwino.

16 Pakuti pamene Moroniha adaona kuti adalapa adayesetsa kuwatsogolera iwo kuchoka dera ndi dera, ndi kuchoka mzinda ndi mzinda, ngakhale mpaka iwo atalandiranso theka limodzi la chuma chawo ndi theka limodzi la maiko awo wonse.

17 Ndipo kotero adamaliza makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu imodzi cha ulamuliro wa oweruza.

18 Ndipo zidachitika m’chaka cha makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri cha ulamuliro wa oweruza, kuti Moroniha sakadatha kupezanso chuma pa Alamani.

19 Choncho iwo adasiya madongosolo awo kuti atenge otsala a mayiko awo, pakuti adali ochuluka kwambiri Alamani kotero kuti kudakhala kosatheka kuti Anefi apeze mphamvu zambiri pa iwo; kotero Moroniha adagwiritsa ntchito ankhondo ake wonse m’kusunga zigawo izo zimene iye adatenga.

20 Ndipo zidachitika, chifukwa cha kukula kwa chiwerengero cha Alamani, Anefi adali mu mantha aakulu, kuwopa angathe kugonjetsedwa, ndi kupondelezedwa, ndi kuphedwa, ndi kuwonongedwa.

21 Inde, iwo adayamba kukumbukira mauneneri a Alima, ndiponso mawu a Mosiya; ndipo iwo adaona kuti iwo adali anthu osamvera, ndi kuti iwo adapeputsa malamulo a Mulungu;

22 Ndipo kuti iwo adali atasintha ndi kupondereza pansi pa mapazi awo malamulo a Mosiya, kapena icho chimene Ambuye adamulamulira iye kuti apereke kwa anthu; ndi iwo adaona kuti malamulo awo adali atayipitsidwa, ndipo adasanduka anthu oipa, kotero kuti adali oipa ngakhale monga ngati kwa Alamani.

23 Ndipo chifukwa cha kusaweruzika kwawo mpingo udali utayamba kucheperachepera; ndipo adayamba kusakhulupilira mzimu wa uneneri ndi mzimu wa chivumbulutso; ndipo ziweruzo za Mulungu zidawayang’ana pankhope.

24 Ndipo iwo adaona kuti adakhala ofooka, monga ngati kwa abale awo, Alamani, ndipo kuti Mzimu wa Ambuye sudawasungenso iwo; inde, udachoka kwa iwo chifukwa Mzimu wa Ambuye sukhala m’kachisi wosayera—

25 Kotero Ambuye adaleka kuwasunga ndi mphamvu yake yozizwitsa ndi yosayerekezeka, pakuti iwo adagwa mu mkhalidwe wa kusakhulupilira ndi kuipa koopsya; ndipo adaona kuti Alamani adali ochuluka kwambiri kuposa iwo, ndipo pokhapokha atagwiritsitsa kwa Ambuye Mulungu wawo akuyenera kuwonongeka kosapeweka.

26 Pakuti taonani, iwo adaona kuti mphamvu ya Alamani idali yaikulu monga mphamvu yawo, ngakhale munthu kwa munthu. Ndipo kotero adagwa mu kulakwitsa kwakukulu uku; inde, kotero adakhala ofooka, chifukwa cha kulakwitsa kwawo, mu nthawi ya zaka zosachuluka.

Print