Malembo Oyera
Helamani 3


Mutu 3

Anefi ochuluka asamukira ku dziko la kumpoto—Amanga nyumba za simenti ndi kusunga zolemba zambiri—Makumi a zikwi atembenuka ndi kubatizidwa—Mawu a Mulungu amatsogolera anthu ku chipulumutso—Nefi mwana wa Helamani akhala pa mpando wa chiweruzo. Mdzaka dza pafupifupi 49–39 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika mu chaka cha makumi anayi ndi zitatu cha ulamuliro wa oweruza, padalibe mkangano pakati pa anthu a Nefi kupatula kunyada pang’ono kumene kudali mu mpingo, kumene kudayambitsa kusagwirizana pang’ono pakati pa anthu, zomwe zidathetsedwa mu mpingo mu kutha kwa dzaka makumi anayi ndi zitatu.

2 Ndipo padalibe mkangano pakati pa anthu m’chaka cha makumi anayi ndi zinayi; Ngakhalenso padalibe mikangano yaikulu m’chaka cha makumi anayi ndi zisanu.

3 Ndipo zidachitika mu cha makumi anayi ndi zisanu ndi chimodzi, inde, padali mikangano yambiri ndi kusagwirizana kwambiri; m’mene mudali wochuluka kwambiri amene adachoka m’dziko la Zarahemula, ndipo adapita ku dziko la kumpoto kuti akalandire dzikolo.

4 Ndipo adayenda ulendo wautali kwambiri, kotero kuti adafika pamadzi aakulu ndi mitsinje yambiri.

5 Inde, ndipo ngakhale iwo adafalikira m’madera wonse a dzikolo, m’mbali zonse zomwe sizidachitidwe bwinja ndi zopanda mitengo, chifukwa cha wokhalamo ambiri amene adalandira dzikolo.

6 Ndipo tsopano palibe gawo la dziko limene lidali bwinja, kupatula la matabwa; koma chifukwa cha kukula kwa chiwonongeko cha anthu amene adakhala m’dzikolo lidatchedwa bwinja.

7 Ndipo pakukhala matabwa ochepa pa dzikolo, komabe anthu amene adapita adakhala aluso kwambiri pa ntchito ya simenti; kotero adamanga nyumba za simenti, momwe ankakhalamo.

8 Ndipo zidachitika kuti iwo adachulukana ndi kufalikira, ndipo adapita patsogolo kuchokera ku dziko la kummwera kupita ku dziko la kumpoto, ndipo adafalikira mpaka kuti adayamba kuphimba nkhope ya dziko lonse lapansi, kuchokera ku nyanja ya kummwera mpaka nyanja kumpoto, kuchokera ku nyanja kumadzulo mpaka kunyanja kummawa.

9 Ndipo anthu amene adali m’dziko lakumpoto adakhala m’mahema, ndi m’nyumba za simenti, ndipo adalora mtengo uliwonse umene ungamere pankhope pa dzikolo kuti ukule, kuti m’kupita kwa nthawi iwo akakhale ndi matabwa omangira nyumba zawo, inde, mizinda yawo, ndi makachisi awo, ndi masunagoge awo, ndi malo opatulika awo, ndi mitundu yonse ya zomanga zawo.

10 Ndipo zidachitika pamene matabwa adali ochepa kwambiri m’dziko la kumpoto, iwo adatumiza ambiri mwa njira yotumizira pamadzi.

11 Ndipo kotero iwo adapangitsa anthu m’dziko la kumpoto kuti athe kumanga mizinda yambiri, yonse yamitengo ndi simenti.

12 Ndipo zidachitika kuti adalipo ambiri a anthu a Amoni, amene adali Alamani mwa kubadwa, adapitanso ku dzikoli.

13 Ndipo tsopano pali zolemba zambiri zosungidwa za zochitika za anthu awa, ndi ambiri a anthu awa, zomwe ziri zapadera ndi zazikulu kwambiri, zokhudza iwo.

14 Koma taonani, gawo limodzi mwa zana la zochitika za anthu awa, inde, nkhani ya Alamani ndi ya Anefi, ndi nkhondo zawo, ndi mikangano, ndi kusagwirizana, ndi maulaliki awo, ndi mauneneri awo, ndi manyamulidwe awo, ndi mamangidwe a ngalawa zawo, ndi mamangidwe a makachisi awo, ndi masunagoge ndi malo opatulika awo, ndi kulungama kwawo, ndi kuipa kwawo, ndi kupha kwawo, ndi kuba kwawo, ndi kulanda kwawo, ndi mitundu yonse ya zonyansa ndi zadama, sizingakwanire mu ntchito iyi.

15 Koma taonani, kuli mabuku ambiri ndi zolemba zambiri za mtundu uliwonse, ndipo zasungidwa makamaka ndi Anefi.

16 Ndipo zaperekedwa kuchokera ku m’badwo umodzi kupita ku umzake ndi Anefi, ngakhale mpaka pamene iwo agwa mu kulakwitsa ndipo adaphedwa, kulandidwa, ndi kusakidwa, ndi kuthamangitsidwa, ndi kuphedwa, ndi kumwazikana pa nkhope ya dziko lapansi, ndi kusakanizikana ndi Alamani mpaka iwo sadzatchedwanso Anefi, kukhala oipa, ndi opulukira, ndi ankhanza, inde, ngakhale kukhala Alamani.

17 Ndipo tsopano ndibweleranso ku nkhani yanga; kotero, zimene ine ndayankhula zadutsa patakhala mikangano yaikulu, ndi zisokonezo, ndi nkhondo, ndi kusagwirizana, pakati pa anthu a Nefi.

18 Chaka cha makumi anayi ndi zisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza chidatha;

19 Ndipo zidachitika kuti kudali kukadali mkangano waukulu m’dziko, inde, ngakhale mu chaka cha makumi anayi ndi zisanu ndi ziwiri, ndiponso m’chaka cha makumi anayi ndi zisanu ndi zitatu.

20 Komabe Helamani adakhala pa mpando wa chiweruzo ndi chilungamo ndi kupanda tsankho; inde, iye adasamalira kusunga malamulo olembedwa, ndi ziweruzo, ndi malamulo a Mulungu; ndipo iye adachita cholungama pamaso pa Mulungu kosalekeza; ndipo adayenda m’njira za atate ake, kotero kuti adachita bwino m’dzikolo.

21 Ndipo zidachitika kuti adali ndi ana amuna awiri. Iye adapereka kwa wamkulu dzina la Nefi, ndipo kwa wamng’ono, dzina la Lehi. Ndipo iwo adayamba kukula mwa Ambuye.

22 Ndipo zidachitika kuti nkhondo ndi mikangano idayamba kutha, mu mlingo wochepa, pakati pa anthu a Anefi, ku mapeto a chaka cha makumi anayi ndi mphambu zisanu ndi zitatu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

23 Ndipo zidachitika m’chaka cha makumi anayi ndi zisanu ndi zinayi cha ulamuliro wa oweruza, mudali mtendere wopitirilabe wokhazikitsidwa m’dzikomo, monse kupatulapo magulu achinsinsi amene Gadiyantoni wachifwamba adakhazikitsa m’madera okhazikika kwambiri a dzikolo, amene pa nthawiyo sadali odziwika kwa iwo amene adali pa mutu wa boma; kotero sadawonongedwe m’dzikolo.

24 Ndipo zidachitika kuti m’chaka chomwecho kudali kuchita bwino kwakukuru mu mpingo, mwakuti adaliko dzikwi amene adadzilowetsa wokha ku mpingo ndipo adabatizidwa m’kulapa.

25 Ndipo kuchita bwino kwa mpingo kudali kwakukulu, ndipo madalitso ochuluka amene adatsanuliridwa pa anthu, kotero kuti ngakhale akulu ansembe ndi aphunzitsi adadabwa koposera muyeso.

26 Ndipo zidachitika kuti ntchito ya Ambuye idapita patsogolo ku kubatiza ndi kuyanjanitsa ku mpingo wa Mulungu, miyoyo yambiri, inde, ngakhale makumi a zikwi.

27 Motero tingathe kuona kuti Ambuye ndi achifundo kwa wonse amene akufuna, mu kuona mtima kwa mitima yawo, kuitanira pa dzina lake loyera.

28 Inde, kotero tikuona kuti chipata cha kumwamba chili chotsegukira kwa wonse; ngakhale kwa iwo amene adzakhulupilira dzina la Yesu Khristu, amene ali Mwana wa Mulungu.

29 Inde, tikuona kuti aliyense amene angathe kufuna kuti agwire mawu a Mulungu, womwe ali amoyo ndi amphamvu, womwe adzagawanitsa kuchenjera konse ndi misampha ndi machenjelero a mdyerekezi, ndi kutsogoza munthu wa Khristu mu njira yolunjika ndi yopapatiza kudutsa phompho lamuyaya la chisoni lomwe lakonzedwa kuti limeze woyipa—

30 Ndi kufikitsa miyoyo yawo, inde, miyoyo yawo yosafa, pa dzanja lamanja la Mulungu mu ufumu wa kumwamba, kudzakhala pansi ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, ndi makolo athu woyera wonse, kuti asatulukenso.

31 Ndipo mu chaka chimenechi kudali kusangalala kosalekeza m’dziko la Zarahemula, ndi m’madera onse ozungulira, ngakhale m’dziko lonse limene lidali la Anefi.

32 Ndipo zidachitika kuti kudali mtendere ndi chisangalalo chachikulu kumapeto kwa chaka cha makumi anayi ndi zisanu ndi zinayi; inde, ndipo kudalinso mtendere wokhazikika ndi chisangalalo chachikulu m’chaka cha makumi asanu cha ulamuliro wa oweruza.

33 Ndipo m’chaka cha makumi asanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza mudalinso mtendere, kupatula kunyada kumene kudayamba kulowa mu mpingo—osati mu mpingo wa Mulungu, koma m’mitima ya anthu amene adadzinenera kukhala a Mpingo wa Mulungu—

34 Ndipo iwo adzikuza mu kunyada, ngakhale ku mazunzo a ambiri a abale awo. Tsopano ichi chidali choipa chachikulu, chimene chidapangitsa gawo lodzichepetsa kwambiri la anthu kuvutika mazunzo aakukulu, ndi kudutsa mu masautso ambiri.

35 Komabe iwo adasala kudya ndi kupemphera kawirikawiri, ndipo adakula molimbika ndi mwamphamvu mu kudzichepetsa kwawo, ndi kukhazikika ndi kulimba mu chikhulupiliro cha Khristu, mu kudzaza miyoyo yawo ndi chisangalalo ndi chitonthozo, inde, ngakhale ku chiyeretso ndi kuyeretsedwa kwa mitima yawo, kuyeretsedwa kumene kumadza chifukwa cha kupereka mitima yawo kwa Mulungu.

36 Ndipo zidachitika kuti chaka chamakumi asanu ndi ziwiri chidatha mu mtenderenso, kupatulapo kudali kunyada kwakukulu kumene kudalowa m’mitima ya anthu; ndipo chidali chifukwa cha chuma chawo chochuluka kwambiri ndi kuchita bwino kwawo m’dzikolo; ndipo kudakula pa iwo tsiku ndi tsiku.

37 Ndipo zidachitika mu chaka cha makumi asanu ndi zitatu cha ulamuliro wa oweruza, Helamani adamwalira, ndipo mwana wake wamkulu Nefi adayamba kulamulira m’malo mwake. Ndipo zidachitika kuti adakhala pa mpando wachiweruzo ndi chilungamo ndi kupanda tsankho; inde, adasunga malamulo a Mulungu, ndi kuyenda m’njira za atate ake.