Malembo Oyera
Helamani 16


Mutu 16

Anefi amene akhulupilira Samueli abatizidwa ndi Nefi—Samueli sangaphedwe ndi mivi ndi miyala ya osalapa Achinefi—Ena aumitsa mitima yawo, ndipo ena aona angelo—Osakhulupilira anena kuti sikuli kwanzeru kukhulupilira mwa Khristu ndi kudza kwake ku Yerusalemu. Mdzaka dza pafupifupi 6–1 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, zidachitika kuti padali ambiri amene adamva mawu a Samueli, wa Chilamani, amene adayankhula pa makoma a mzindawo. Ndipo onse amene adakhulupilira mawu ake adatuluka ndipo adasaka Nefi; ndipo pamene adatuluka ndikumpeza, adavomereza kwa iye machimo awo ndipo sadawakane, nafuna kuti akathe kubatizidwa kwa Ambuye.

2 Koma ambiri amene sadakhulupilire mawu a Samueli adakwiya naye; ndipo adamponya miyala pa khoma, ndiponso ambiri adaponyera mivi pa iye pamene iye adaima pa khoma; koma Mzimu wa Ambuye udali naye, kotero kuti sadathe kumugenda iye ndi miyala yawo, kapena ndi mivi yawo.

3 Tsopano pamene iwo adawona kuti sadathe kumugenda, adalipo ambiri amene adakhulupilira m’mawu ake, kotero kuti adapita kwa Nefi kuti akabatizidwe.

4 Pakuti, taonani, Nefi adali kubatiza, ndi kunenera, ndi kulalikira, kufuula kulapa kwa anthu; naonetsa zizindikiro ndi zodabwitsa, nachita zozizwa mwa anthu, kuti adziwe kuti Khristu akuyenera kudza msanga—

5 Ndikuwauza iwo za zinthu zomwe zikuyenera kudza posachedwa, kuti akathe kudziwa ndi kukumbukira pa nthawi ya kudza kwake kuti zidadziwitsidwa kale kwa iwo, kucholinga chokuti akathe kukhulupilira; kotero ochuluka amene adakhulupilira m’mawu a Samueli adapita kwa iye kuti abatizidwe, pakuti adadza akulapa ndi kuvomereza machimo awo.

6 Koma gawo lalikulu la iwo silidakhulupilire mawu a Samueli; kotero pamene adaona kuti sangathe kumugenda ndi miyala ndi mivi yawo, iwo adafuulira atsogoleri ankhondo awo, kuti: Mtengeni munthu uyu ndi kumumanga iye; pakuti taonani ali ndi mdyerekezi; ndipo chifukwa cha mphamvu ya mdyerekezi imene ili mwa iye sitikutha kumugenda iye ndi miyala yathu ndi mivi yathu; kotero mtengeni, mum’mange, ndipo muchoke naye.

7 Ndipo pamene adaturuka kukaika manja awo pa iye, taonani, iye adadumphira pansi kuchokera pa khoma, ndipo adathawa kuchoka m’maiko awo, inde, ngakhale kupita dziko la kwawo; ndikuyamba kulalikira ndi kunenera mwa anthu a mtundu wake.

8 Ndipo taonani, iye sadamvekenso konse pakati pa Anefi; ndipo momwemo ndi momwe adaliri machitidwe a anthu.

9 Ndipo kotero chidatha chaka cha makumi asanu ndi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

10 Ndipo kotero chidathanso chaka cha makumi asanu ndi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha ulamuliro wa oweruza, gawo lochuluka la anthu lidakhalabe mu kunyada ndi kuipa kwawo, ndipo gawo laling’ono likuyenda mosamalitsa kwambiri pamaso pa Mulungu.

11 Ndipo izi zidali zikhalidwenso, mchaka cha makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi zitatu za ulamuliro wa oweruza.

12 Ndipo padali kusintha pang’ono chabe m’zochitika za anthu, kupatulapo kuti anthu adayamba kuumitsitsa kwambiri mu kusaweruzika, ndi kuchita mochulukira za icho chimene chidali chotsutsana ndi malamulo a Mulungu, m’chaka cha makumi asanu ndi atatu ndi zisanu ndi zinayi za ulamuliro wa oweruza.

13 Koma zidafika pochitika mu chaka cha makumi asanu ndi anayi cha ulamuliro wa oweruza, padali zizindikiro zazikulu zidapatsidwa kwa anthu, ndi zodabwitsa; ndipo mawu a aneneri adayamba kukwaniritsidwa.

14 Ndipo angelo adaonekera kwa anthu, anthu anzeru, ndipo adalalikira kwa iwo uthenga wabwino wa chisangalalo chachikulu; choncho m’chakachi malemba woyera adayamba kukwaniritsidwa.

15 Komabe, anthu adayamba kuumitsa mitima yawo, onse kupatulapo adali gawo lokhulupilira kwambiri la iwo, onse a Anefi ndi a Lamani, ndipo adayamba kudalira mphamvu zawo ndi nzeru zawo, kumati:

16 Zinthu zina zomwe mwina amaziganizira bwino, mwa zambiri; koma taonani, tikudziwa kuti ntchito zazikulu zonse izi ndi zodabwitsa sizingachitike, zomwe zanenedwa.

17 Ndipo adayamba kukambirana ndi kutsutsana wina ndi mzake, kumati:

18 Kuti sikuli kwanzeru kuti munthu wotero ngati Khristu adzabwera; ngati ndichoncho, ndipo iye ali Mwana wa Mulungu, Atate a kumwamba ndi a dziko lapansi, monga kwayankhulidwa, chifukwa chiyani iye sadzadzionetsera yekha kwa ife monga ngati kwa iwo amene adzakhala ku Yerusalemu?

19 Inde, chifukwa chiyani sadzadzionetsera yekha m’dziko lino monga ngati m’dziko la Yerusalemu?

20 Koma taonani, ife tikudziwa kuti uwu uli mwambo woipa, umene udaperekedwa kwa ife ndi makolo athu, kutipangitsa ife kukhulupilira mu chinthu china chachikulu ndi chodabwitsa chimene chikuyenera kuchitika, koma osati pakati pathu, koma mu dziko limene liri kutali, dziko limene sitikulidziwa; kotero amatisunga ife mu umbuli, pakuti sitingathe kuchitira umboni ndi maso athu kuti ndi zoona.

21 Ndipo iwo, mwa kuchenjelera ndi matsenga a woipayo, adzachita chinsinsi china chachikulu chimene sitingathe kuchimvetsa, chimene chidzatisunga ife kukhala akapolo a mawu awo, ndi antchito kwa iwo, chifukwa timadalira pa iwo kuti atiphunzitse mawu; ndipo motero adzatisunga ife mu umbuli ngati ife tidzipereka tokha kwa iwo, masiku onse a moyo wathu.

22 Ndipo zinthu zochuluka kwambiri anthu adazilingalira m’mitima mwawo, zomwe zidali zopusa ndi zopanda pake; ndipo iwo adasokonezedwa kwambiri, pakuti Satana adawautsa iwo kuchita mphulupulu mosalekeza; inde, iye adapita kukafalitsa mphekesera ndi mikangano pa nkhope yonse ya dziko, kuti iye athe kuumitsa mitima ya anthu pa chimene chidali chabwino ndi motsutsa icho chimene chikuyenera kudza.

23 Ndipo osatengera zizindikiro ndi zodabwitsa zimene zidachitidwa pakati pa anthu a Ambuye; ndi zozizwitsa zambiri zimene iwo adazichita, Satana adagwira kwakukulu pa mitima ya anthu pa nkhope yonse ya dzikolo.

24 Ndipo kotero chidatha chaka cha makumi asanu ndi anayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

25 Ndipo motero adamaliza buku la Helamani, molingana ndi zolemba za Helamani ndi ana ake aamuna.