Malembo Oyera
Helamani 13


Uneneri wa Samueli, Mlamani, kwa Anefi.

Zophatikizidwa mu Mitu 13 mpaka 15.

Mutu 13

Samueli Mlamani anenera za chiwonongeko cha Anefi pokhapokha atalapa—Iwo ndi chuma chawo ndi chotembeleredwa—Iwo akana ndi kuponya miyala aneneri, azingidwa ndi dziwanda, ndipo afunafuna chimwemwe pakuchita mphulupulu. Mdzaka dza pafupifupi 6 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano izo zidachitika mu chaka cha makumi asanu ndi atatu ndi chisanu ndi chimodzi, Anefi adakhalabe m’zoipa, inde, mu kuipa kwakukulu, pamene Alamani adatsatira mosamalitsa kusunga malamulo a Mulungu, monga mwa chilamulo cha Mose.

2 Ndipo zidachitika kuti m’chaka chimenechi kudali Samueli wina, wachilamani, adadza m’dziko la Zarahemula, ndipo adayamba kulalikira kwa anthu. Ndipo zidachitika kuti iye adalalikira kulapa masiku ambiri kwa anthu, ndipo iwo adamuponyera iye kunja, ndipo iye adali pafupi kubwelera ku dziko lake.

3 Koma taonani, mawu a Ambuye adadza kwa iye, kuti abwelerenso, ndipo anenere kwa anthu zinthu zilizonse zimene zingabwere mu mtima mwake.

4 Ndipo zidachitika kuti iwo sadalore kuti iye alowe mu mzindamo; kotero adapita ndikukakwera pa khoma lake, ndikutambasula dzanja lake, ndikufuula ndi mawu aakulu, ndi kunenera kwa anthu zinthu zilizonse Ambuye adaziika mu mtima mwake.

5 Ndipo adati kwa iwo: taonani, ine, Samueli, wachilamani, ndikuyankhula mawu a Ambuye amene awaika mu mtima mwanga; ndipo taonani awaika iwo mu mtima mwanga kuti ndinene kwa anthu awa kuti lupanga la chilungamo lalendewera pa anthu awa; ndipo dzaka mazana anayi sizidzapita koma lupanga la chilungamo lidzagwera pa anthu awa.

6 Inde, chiwonongeko chachikulu chikuyembekezera anthu awa, ndipo ndithudi zikudza kwa anthu awa, ndipo palibe chimene chingapulumutse anthu awa kupatula kulapa ndi chikhulupiliro mwa Ambuye Yesu Khristu, amene ndithudi adzabwera m’dziko lapansi, ndipo adzazunzika zinthu zambiri ndipo adzaphedwa chifukwa cha anthu ake.

7 Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye walengeza kwa ine, ndipo adabweretsa uthenga wabwino ku moyo wanga. Ndipo taonani, ndidatumidwa kwa inu kudzalalikira kwa inunso, kuti mukakhale nawo uthenga wabwino; koma taonani simudandilandire ine.

8 Kotero, motere akutero Ambuye: Chifukwa cha kuuma kwa mitima ya anthu Achinefi, pokhapokha iwo alape, ndidzachotsa mawu anga kwa iwo, ndipo ndidzachotsa Mzimu wanga kwa iwo, ndipo sindidzawaloranso, ndipo ndidzatembenuza mitima ya abale awo pa iwo.

9 Ndipo dzaka mazana anayi sizidzapita ndisadachititse kuti akanthidwe; inde, ndidzawayendera ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri.

10 Inde, ndidzawayendera mu mkwiyo wanga waukali, ndipo padzakhala iwo a m’badwo wachinayi amene adzakhala ndi moyo, mwa adani anu, kuti aone chiwonongeko chanu; ndipo ichi chidzabweradi pokhapokha inu mulape, akutero Ambuye; ndipo iwo a m’badwo wachinayi adzayendera chiwonongeko chanu.

11 Koma ngati mulapa ndi kubwelera kwa Ambuye Mulungu wanu ndidzabweza mkwiyo wanga, akutero Ambuye; inde, motere akutero Ambuye, odala ali iwo amene alapa ndi kutembenukira kwa ine, koma tsoka kwa iye amene salapa.

12 Inde, tsoka kwa mzinda waukulu uwu wa Zarahemula; pakuti taonani, ndi chifukwa cha wolungama kuti umapulumutsidwa; inde, tsoka kwa mzinda waukulu uwu, pakuti ndikuona, akutero Ambuye, kuti alipo ambiri, inde; ngakhale gawo lalikulu la mzinda waukulu uwu, amene adzaumitsa mitima yawo motsutsana ndi ine, akutero Ambuye.

13 Koma odala ali iwo amene adzalapa, pakuti ine ndidzawapulumutsa. Koma taonani, pakadapanda kukhala olungama amene ali mu mzinda waukulu uwu, taonani, ndikadachititsa kuti moto utsike kuchokera kumwamba ndi kuwuwononga.

14 Koma taonani, ndi chifukwa cha olungama kuti wapulumutsidwa. Koma taonani, ikudza nthawi, akutero Ambuye, pamene mudzaponyera kunja olungama pakati panu; pamenepo mudzayenera chiwonongeko; inde, tsoka liri ku mzinda waukulu uwu, chifukwa cha kuipa ndi zonyansa zomwe zili mwa iye.

15 Inde, ndipo tsoka likhale kwa mzinda wa Gideoni, chifukwa cha zoipa ndi zonyansa zili mwa iye.

16 Inde, ndipo tsoka mizinda yonse yozungulira dzikolo; yomwe idatengedwa ndi Anefi, chifukwa cha zoipa ndi zonyansa zomwe zili mwa iwo.

17 Ndipo taonani, thembelero lidzafika pa dzikoli, atero Ambuye wa makamu, chifukwa cha anthu amene ali pa dzikoli, inde, chifukwa cha kuipa kwawo ndi zonyansa zawo.

18 Ndipo zidzachitika, atero Ambuye wa makamu, inde, Mulungu wathu wamkulu ndi oona, kuti aliyense amene adzabisa chuma padziko lapansi sadzachipezanso, chifukwa cha thembelero lalikulu la dzikolo, kupatula iye akhale munthu wolungama ndipo adzachibisa kwa Ambuye.

19 Pakuti ndidzachita, atero Ambuye, kuti adzachibisa chuma chawo kwa ine; ndipo adzakhala otembeleredwa iwo amene sadzabisa chuma chawo kwa ine; pakuti palibe amene amabisa chuma chawo kwa ine kupatula atakhala olungama; ndipo iye amene samabisira chuma chake kwa ine, otembeleredwa iye, ndiponso chuma chake, ndipo palibe amene adzachiwombola chifukwa cha thembelero la dzikoli.

20 Ndipo tsikulo lidzafika limene adzabisa chuma chawo, chifukwa adaika mitima yawo pa chuma; ndipo chifukwa iwo adaika mitima yawo pa chuma chawo, ndipo adzabisa chuma chawo pamene iwo adzathawa pamaso pa adani awo; chifukwa sadzachibisa icho kwa ine, otembeleredwa iwo ndi chuma chawochonso; ndipo tsiku limenelo adzakanthidwa, atero Ambuye.

21 Taonani inu, anthu a mzinda waukulu uwu, ndipo mvetserani mawu anga; inde, mvetserani mawu amene Ambuye anena; pakuti taonani, anena kuti ndinu wotembeleredwa chifukwa cha chuma chanu; ndiponso chuma chanu n’chotembeleredwa, chifukwa mudaika mitima yanu pa icho; ndipo simudamvetsere mawu a iye amene adakupatsani inu.

22 Simukumbukira Ambuye Mulungu wanu mu zimene adakudalitsani nazo, koma mumakumbukira chuma chanu munthawi zonse, osayamika Ambuye Mulungu wanu; inde, mitima yanu siidayandikire kwa Ambuye, koma imakula ndi kunyada kwakukulu; ndi kudzitamandira, ndi kudzitukumula kwakukulu, njiru, mikangano, dumbo, kuzunza, ndi kupha, ndi mitundu yonse ya kusaweruzika.

23 Pa chifukwa ichi Ambuye Mulungu achititsa kuti thembelero libwere pa dziko, ndiponso pa chuma chanu, ndipo ichi chifukwa cha mphulupulu zanu.

24 Inde, tsoka kwa anthu awa, chifukwa cha nthawi iyi yafika, kuti mukuwaponya kunja aneneri, ndi kuwatonza, ndi kuwaponya miyala, ndi kuwapha, ndi kuwachitira zoipa zamtundu uliwonse, monga adachitira nthawi yakale.

25 Ndipo tsopano pamene mukuyankhula, mukuti, Masiku athu akadakhala m’masiku a makolo athu akale, sitikadapha aneneri; sitikadawaponya miyala, ndi kuwaponya kunja.

26 Taonani inu muli oipa koposa iwo; pakuti monga Ambuye ali wamoyo, ngati mneneri adza pakati pa inu, ndikudzakuuzani inu mawu a Ambuye; amene akuchitira umboni za machimo anu ndi mphulupulu zanu, inu mumamukwiyira iye, ndi kumuponyera kunja ndi kufunafuna njira zonse zomuwonongera; inde, mudzanena kuti ali mneneri wonyenga, ndi kuti iye ndi ochimwa, ndi wa mdyerekezi, chifukwa akuchitira umboni kuti ntchito zanu ndi zoipa.

27 Koma taonani, ngati munthu adzabwera pakati panu ndikudzati: Chitani ichi, ndipo palibe mphulupulu; chitani icho ndipo simudzavutika; inde, adzanena: Yendani mwa kunyada kwa mitima yanu; inde, yendani mwa kunyada kwa maso anu, ndipo chitani chimene mtima wanu ukufuna—ndipo ngati munthu adzabwera pakati panu oti adzanena izi, mudzamulandira, ndi kunena kuti iye ndi mneneri.

28 Inde, mudzamukweza; ndipo mudzampatsa chuma chanu; mudzampatsa golidi wanu ndi siliva wanu, ndipo mudzamuveka zovala za mtengo wake wapatali; ndipo chifukwa akuyankhula nanu mawu osyasyalika, ndipo akuti zonse zili bwino, pamenepo simudzampezera chifukwa.

29 O inu a m’badwo woipa ndi wopotoka; inu anthu amakani ndipo inu osamvera, mpaka liti mukuganiza kuti Ambuye adzakulolerani inu? Inde, mpaka liti mudzadzilora kutsogozedwa ndi atsogoleri opusa ndi akhungu? Inde, kodi mudzasankha mdima m’malo mwa kuwala mpaka liti?

30 Inde, taonani, mkwiyo wa Ambuye wakuyakirani kale motsutsana nanu; taonani, watembelera dziko chifukwa cha mphulupulu zanu.

31 Ndipo taonani, ikudza nthawi kuti atembelere chuma chanu, kuti chikhale chotelera, kuti simungathe kuchigwira; ndipo m’masiku a umphawi wanu simungathe kuchisunga.

32 Ndipo m’masiku a umphawi wanu mudzalilira kwa Ambuye; ndipo mudzalilira pachabe, pakuti chipululutso chanu chafikira kale pa inu, ndipo chiwonongeko chanu chatsimikizika; ndipo pamenepo mudzalira ndi kubuula m’tsiku limenelo, akutero Ambuye wa makamu. Ndipo pamenepo mudzalira, ndi kuti:

33 O ndikadalapa, ndi kusapha aneneri, ndi kuwaponya miyala, ndi kuwaponya kunja. Inde, tsiku limenelo mudzati: O kuti tidakumbukila Ambuye Mulungu wathu tsiku lija adatipatsa chuma chathu, ndiye pamenepo sichikadakhala chotelera kuti chitaike; pakuti taonani, chuma chathu chachoka kwa ife.

34 Taonani, timaika chida pano ndipo mawa chapita; ndipo taonani, malupanga athu achotsedwa kwa ife tsiku limene tikuwafuna kunkhondo.

35 Inde, tabisa chuma chathu ndipo chatelera kuchoka kwa ife chifukwa cha thembelero la dzikolo.

36 O kuti ife tikadalapa mu tsiku limene mawu a Ambuye adadza kwa ife; pakuti taonani dziko ndi lotembeleredwa, ndipo zinthu zonse zakhala zoterera, ndipo sitingathe kuzigwira.

37 Taonani, tazingidwa ndi ziwanda, inde, tili ozunguliridwa ndi angelo a iye amene akufuna kuwononga miyoyo yathu. Taonani, mphulupulu zathu ndi zazikulu. O Ambuye, kodi simungachotse mkwiyo wanu kutali ndi ife? Ndipo ichi chidzakhala chiyankhulo chanu masiku amenewo.

38 Koma taonani, masiku a kuyesedwa kwanu apita; mwazengereza tsiku la chipulumutso chanu mpaka kuchedwa kosatha, ndipo chiwonongeko chanu chakhazikika; inde, pakuti mwafunafuna masiku onse a moyo wanu chimene simudachipeze; ndipo mwafunafuna chimwemwe pochita mphulupulu; chinthu chimene chili chotsutsana ndi chikhalidwe cha chilungamo chimenecho chimene chili mu Mutu wathu waukulu ndi Wamuyaya.

39 O inu anthu a m’dzikoli, kuti mumve mawu anga! Ndipo ndikupemphera kuti mkwiyo wa Ambuye uchoke kwa inu, ndipo kuti mulape ndi kupulumutsidwa.