Malembo Oyera
Helamani 8


Mutu 8

Oweruza achinyengo afuna kusonkhezera anthu kutsutsana ndi Nefi—Abrahamu, Mose, Zenosi, Zenoki, Eziya, Yesaya, Yeremiya, Lehi, ndi Nefi onse adachitira umboni za Khristu—Mwa kutsogozedwa kwakudzodzedwa Nefi alengeza kuphedwa kwa oweruza wamkulu. Mdzaka dza pafupifupi 23–21 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Nefi adanena mawu awa, taonani, padali amuna amene adali oweruza, amenenso adali a gulu lachinsinsi la Gadiyantoni, ndipo iwo adakwiya, ndipo adafuula motsutsa iye, kunena kwa anthu: Chifukwa chiyani simukumugwira munthu uyu ndi kumubweretsa iye, kuti akaweruzidwe monga mwa kulakwa kumene wakuchita?

2 Chifukwa chiyani mukumuona munthu uyu, ndipo mukumva akunyoza anthu awa ndi malamulo athu?

3 Pakuti, taonani, Nefi adali atayankhula kwa iwo zokhudzana ndi chinyengo cha lamulo lawo; inde, zithu zambiri Nefi adayankhula zomwe sizingalembedwe; ndipo sadayankhule kanthu kotsutsana ndi malamulo a Mulungu.

4 Ndipo oweruza aja adamukwiyira chifukwa adayankhula zomveka kwa iwo zokhudzana ndi ntchito zawo zobisika zamdima; komabe, iwo sadayerekeze kuika manja awo pa iye, pakuti iwo ankaopa anthu kuti angafuule motsutsa iwo.

5 Kotero iwo adafuulira kwa anthu, kuti: Chifukwa chiyani inu mukulora munthu uyu kuti atinyoze ife? Pakuti taonani iye akuwatsutsa anthu onse awa, ngakhale kuchiwonongeko; inde, ndiponso kuti iyi mizinda yathu ikuluikulu idzalandidwa kwa ife, kuti ife sitidzakhala ndi malo mwa iyo.

6 Ndipo tsopano tikudziwa kuti izi sizingatheke, pakuti taonani, ife ndife amphamvu, ndipo mizinda yathu ndi yaikulu, kotero adani athu sangakhale ndi mphamvu pa ife.

7 Ndipo zidachitika kuti motero iwo adasonkhezera anthu ku mkwiyo motsutsa Nefi, ndipo adautsa mikangano pakati pawo; pakuti padali ena amene adafuula, Mulekeni munthu uyu, pakuti ndi munthu wabwino, ndipo zinthu zimene akunena zidzachitika pokhapokha ngati ife titalapa;

8 Inde, taonani, ziweruzo zonse zidzafika pa ife zimene iye wachitira umboni kwa ife; pakuti tikudziwa kuti iye wachitira umboni zoona kwa ife za mphulupulu zathu. Ndipo taonani izo ndi zochuluka, ndipo akudziwa bwino lomwe zinthu zonse zimene zidzatichitikira ife monga iye akudziwira za mphulupulu zathu;

9 Inde, ndipo taonani, akadapanda kukhala mneneri iye sakadachitira umboni zokhudzana ndi zinthu zimenezo.

10 Ndipo zidachitika kuti anthu awo amene adafuna kuwononga Nefi adakakamizika chifukwa cha kuopa kwawo, kuti iwo sadaike manja awo pa iye; kotero adayambanso kuyankhula nawo, poona kuti adalandira chisomo pamaso pa ena, kotero kuti otsalawo adachita mantha.

11 Kotero iye adakakamizika kuyankhula zambiri kwa iwo kuti: Taonani, abale anga, inu simudawerenge kuti Mulungu adapatsa mphamvu kwa munthu m’modzi, ngakhale Mose, kukantha pa madzi a Nyanja Yofiira, ndipo iwo adalekana uku ndi uko, kotero kuti ana a Israeli, amene adali makolo athu, adaoloka pa nthaka youma, ndipo madzi adamiza ankhondo a Aigupto, ndikuwameza?

12 Ndipo tsopano taonani, ngati Mulungu adapereka kwa munthu uyu mphamvu yoteroyo, ndiye chifukwa chiyani inu mukukangana pakati panu, ndi kumanena kuti iye sadapereke kwa ine mphamvu iliyonse imene ine ndingathe kudziwa zokhudza ziweruzo zomwe zidzadze pa inu pokhapokha inu mutalapa?

13 Koma, taonani, simukungokana mawu anga okha, koma inunso mukumakana mawu onse amene adayankhulidwa ndi makolo athu, ndiponso mawu amene adanenedwa ndi munthu ameneyu, Mose, amene adali ndi mphamvu yaikulu yotero yoperekedwa kwa iye, inde, mawu amene iye adayankhula zokhudza kubwera kwa Mesiya.

14 Inde, kodi sadachitire umboni kuti Mwana wa Mulungu adzabwera? Ndipo monga iye adakweza njoka yamkuwa m’chipululu, ngakhale motero iye adzakwezedwa amene ali nkudza.

15 Ndipo onse amene angayang’ane pa njoka imeneyo adzakhala ndi moyo, ngakhale kotero kuti onse amene angayang’ane pa Mwana wa Mulungu ndi chikhulupiliro, pokhala nawo mzimu wolapa, akhonza kukhala ndi moyo, ngakhale ku moyo umenewo umene uli wamuyaya.

16 Ndipo tsopano taonani, Mose sadachitire umboni wa zinthu izi zokha, komanso aneneri woyera onse, kuyambira masiku ake ngakhale mpaka masiku a Abrahamu.

17 Inde, ndipo taonani, Abrahamu adaona za kudza kwake, ndipo adadzazidwa ndi chisangalaro, ndipo adakondwera.

18 Inde, ndipo taonani ndikunena kwa inu, kuti si Abrahamu yekha adadziwa za zinthu izi, koma adalipo ambiri asadafike masiku a Abrahamu amene adaitanidwa mwa dongosolo la Mulungu; inde, ngakhale pambuyo pa dongosolo la Mwana wake; ndipo ichi kuti chikaonetsedwe kwa anthu, dzaka zikwi zambirimbiri iye asadabwere, kuti ngakhale chiwombolo chidzathe kudza kwa iwo.

19 Ndipo tsopano ndikufuna kuti mudziwe, kuti ngakhale kuyambira masiku a Abrahamu padali aneneri ambiri amene adachitira umboni zinthu izi; inde, taonani, mneneri Zenosi adachitira umboni molimba mtima; n’chifukwa chake chimene iye adaphedwera.

20 Ndipo taonani, ndiponso Zenoki, komanso Eziya, nayenso Yesaya, ndi Yeremiya, (Yeremiya pokhala mneneri yemweyo amene adachitira umboni za chiwonongeko cha Yerusalemu) ndipo tsopano ife tikudziwa kuti Yerusalemu adawonongedwa monga mwa mawu a Yeremiya. O nanga ndiye bwanji sangabwere Mwana wa Mulungu, molingana ndi uneneri wake?

21 Ndipo tsopano kodi inu mungatsutse kuti Yerusalemu adawonongedwa? Kodi mukunena kuti ana aamuna a Zedekiya sadaphedwe, onse kupatulapo Muleki? Inde, ndipo simukuona kuti a mbewu ya Zedekiya ali ndi ife, ndipo adathamangitsidwa m’dziko la Yerusalemu? Koma taonani, izi sizokhazi—

22 Atate athu Lehi adathamangitsidwa kuchokera ku Yerusalemu chifukwa adachitira umboni za zinthu izi. Nefi nayenso adachitira umboni za zinthu izi, ndiponso pafupifupi makolo athu onse, ngakhale kufikira nthawi ino; inde, iwo adachitira umboni za kudza kwa Khristu, ndipo adayang’ana kutsogolo, ndi kukondwera m’tsiku lake limene lirinkudza.

23 Ndipo taonani, iye ndi Mulungu, ndipo ali ndi iwo, ndipo adadzionetsera yekha kwa iwo, kuti iwo adawomboledwa ndi iye; ndipo adampatsa iye ulemelero, chifukwa cha ichi chimene chilinkudza.

24 Ndipo tsopano, pakuona inu mukudziwa zinthu izi ndipo simungathe kuzikana izo pokhapokha mudzaname, kotero mu ichi inu mwachimwa, pakuti inu mwakana zinthu zonsezi; posatengera za maumboni ochuluka omwe mwalandira; inde, ngakhale inu mudalandira zinthu zonse; zinthu zonse za kumwamba, ndi zinthu zonse za padziko lapansi, ngati umboni kuti ndi zoona.

25 Koma taonani, inu mwakana choonadi, ndi kupandukira Mulungu wanu woyera; ndipo ngakhale pa nthawi ino, m’malo modzikundikira nokha chuma kumwamba, kumene kulibe kanthu kangachivunditse, ndipo kumene sikungafike chinthu chodetsedwa, mukudzikundikira nokha mkwiyo wotsutsa tsiku la chiweruzo.

26 Inde, ngakhale nthawi ino mukucha, chifukwa cha kupha kwanu ndi dama ndi kuipa kwanu, ku chiwonongeko chosatha; inde, ndipo pokhapokha mutalapa, lidzafika kwa inu posachedwa.

27 Inde, taonani, liri tsopano pakhomo panu; inde, pitani inu ku mpando oweruzira, ndipo kafufuzeni; ndipo taonani, oweruza wanu waphedwa, ndipo wagona m’mwazi wake; ndipo adaphedwa ndi m’bale wake, amene akufuna kukhala pampando wa chiweruzo.

28 Ndipo taonani, onsewo ndi a gulu lanu lachinsinsi, lomwe oyambitsa wake ndi Gadiyantoni ndi oipa amene akufuna kuwononga miyoyo ya anthu.

Print