Malembo Oyera
Helamani 15


Mutu 15

Ambuye adadzudzula Anefi chifukwa adawakonda—Alamani otembenuka mtima ali wosagwedezeka ndi wokhazikika m’chikhulupiliro—Ambuye adzakhala wachifundo kwa Alamani m’masiku otsiriza. Mdzaka dza pafupifupi 6 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, taonani, ine ndikulengeza kwa inu kuti pokhapokha mulape nyumba zanu zidzasiyidwa kwa inu pululu.

2 Inde, pokhapokha mutalapa, akazi anu adzakhala ndi chifukwa chachikulu chakulira tsiku limene adzayamwitsa; pakuti mudzayesera kuthawa, ndipo sipadzakhala pothawira; inde, ndipo tsoka kwa iwo amene ali ndi pakati, pakuti adzalemedwa ndipo sadzatha kuthawa; kotero, iwo adzaponderezedwa pansi ndipo adzasiyidwa kuti awonongeke.

3 Inde, tsoka kwa anthu awa amene akutchedwa anthu a Nefi pokhapokha kuti alape, pamene iwo adzaona zizindikiro zonse izi ndi zodabwitsa zomwe zidzaonetsedwa kwa iwo; pakuti taonani, iwo akhala anthu wosankhidwa a Ambuye; inde, anthu a Nefi adawakonda, komanso adawadzudzula; inde, m’masiku a mphulupulu zawo adawadzudzula chifukwa adawakonda.

4 Koma taonani abale anga, Alamani wawada chifukwa zochita zawo zakhala zoipa mopitilira, ndipo izi chifukwa cha mphulupulu za miyambo ya makolo awo. Koma taonani, chipulumutso chidadza kwa iwo kudzera mu kulalikira kwa Anefi; ndipo chifukwa cha ichi Ambuye watalikitsa masiku awo.

5 Ndipo ine ndikufuna kuti inu muthe kuona kuti ochuluka a iwo ali m’njira ya udindo wawo, ndipo amayenda mosamala pamaso pa Mulungu, ndipo amatsatira kusunga malamulo ake ndi malamulo olembedwa ake ndi ziweruzo zake mogwirizana ndi chilamulo cha Mose.

6 Inde, ndinena kwa inu, kuti ochuluka a iwo akuchita izi, ndipo akulimbikira ndi khama losatopa kuti abweretse otsala a abale awo ku chidziwitso cha choonadi; kotero pali ambiri omwe akuwonjezera chiwerengero chawo tsiku ndi tsiku.

7 Ndipo taonani, mukudziwa inu nokha; pakuti mudachitira umboni pamene ambiri a iwo omwe abweretsedwa ku chidziwitso cha choonadi, ndi kudziwa za miyambo yoipa ndi yonyansa ya makolo awo, ndipo atsogozedwa kuti akhulupilire malemba woyera, inde, mauneneri a aneneri woyera, amene alembedwa, amene amawatsogolera iwo ku chikhulupiliro mwa Ambuye, ndi ku kulapa, chimene chikhulupiliro ndi kulapa kumabweretsa kusintha kwa mtima kwa iwo—

8 Kotero, pamene ambiri omwe abwera pa ichi, mukudziwa mwa inu nokha ndi osagwedezeka ndi okhazikika m’chikhulupiliro, ndi mu chinthu chimene iwo adamasulidwa nacho.

9 Ndipo inu mukudziwanso kuti akwilira zida zawo zankhondo, ndipo akuopa kuzinyamula kuti angachimwe; inde, mukuona kuti akuopa kuchimwa—pakuti taonani iwo adzadzilolera kuti apondedwe pansi ndi kuphedwa ndi adani awo, ndipo sadzanyamula malupanga awo motsutsana nawo, ndipo izi chifukwa cha chikhulupiliro chawo mwa Khristu.

10 Ndipo tsopano, chifukwa cha kukhazikika kwawo pamene iwo akukhulupilira m’chinthu chimene iwo amakhulupilira, pakuti chifukwa cha kusagwedezeka kwawo pamene iwo adaunikiridwapo kamodzi, taonani, Ambuye adzawadalitsa iwo ndikutalikitsa masiku awo, posatengera za kusaweruzika kwawo—

11 Inde, ngakhale ngati angacheperechepere m’kusakhulupilira Ambuye adzatalikitsa masiku awo, mpaka nthawi idzafika imene idanenedwa ndi makolo athu, ndiponso ndi mneneri Zenosi, ndi aneneri ena ambiri, zokudza kubwenzeretsedwa kwa abale athu, Alamani; kachiwiri ku chidziwitso cha choonadi—

12 Inde, ndikunena kwa inu, kuti mu nthawi zotsiriza malonjezano a Ambuye adzaperekedwa kwa abale athu, Alamani; ndipo pakusatengera masautso ambiri amene iwo adzakhala nawo, ndipo pakusatengera iwo kudzathamangitsidwa uku ndi uko pa nkhope ya dziko lapansi, ndi kudzasakidwa, ndi kudzakanthidwa ndi kubalalitsidwa, kukhala opanda pothawirapo, Ambuye adzawachitira chifundo.

13 Ndipo izi zili molingana ndi uneneri, kuti iwonso adzabweretsedwa ku chidziwitso choona, chimene chili chidziwitso cha Muwomboli wawo, ndi m’busa wawo wamkulu ndi woona, ndi kuwerengedwa m’kati mwa nkhosa zake.

14 Kotero ndikunena kwa inu, zidzakhala zabwino kwa iwo kuposa inu pokhapokha mutalapa.

15 Pakuti, taonani, ngati ntchito zamphamvu zikadaonetsedwa kwa iwo zimene zidaonetsedwa kwa inu, inde, kwa iwo amene adacheperachepera mu kusakhulupilira chifukwa cha miyambo ya makolo awo, inu mukhonza kuona mwa inu nokha kuti iwo sakadakhala konse ocheperachepera mu kusakhulupilira.

16 Kotero, akutero Ambuye: Sindidzawawononga konse, koma ndidzawachititsa kuti tsiku la nzeru zanga abwelere kwa Ine, akutero Ambuye.

17 Ndipo tsopano taonani, akunena Ambuye, zokhudzana ndi anthu a Anefi: Ngati iwo salapa, ndi kutsatira kuchita chifuniro changa, ndidzawawononga iwo kotheratu, akutero Ambuye, chifukwa cha kusakhulupilira kwawo posatengera za ntchito zazikulu zimene ndachita pakati pawo; ndipo mongadi Ambuye ali wamoyo zinthu izi zidzakhala, akutero Ambuye.