Malembo Oyera
Helamani 11


Mutu 11

Nefi akakamiza Ambuye kuti aike m’malo mwa nkhondo yawo ndi njala—Anthu ambiri awonongeka—Alapa, ndipo Nefi apempha Ambuye mvula—Nefi ndi Lehi alandira mavumbulutso ambiri—Achifwamba a Gadiyantoni akhazikika molimba m’dzikolo. Mdzaka dza pafupifupi 20–6 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika m’chaka cha makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri cha ulamuliro wa oweruza kuti mikangano idakula, kotero kuti kudali nkhondo m’dziko lonselo pakati pa anthu onse a Nefi.

2 Ndipo lidali gulu lachinsinsi la achifwambali limene lidachita ntchito imeneyi ya chiwonongeko ndi kuipa. Ndipo nkhondoyi idakhala chaka chonsecho; ndipo m’chaka cha makumi asanu ndi awiri mphambu zitatu chidathanso.

3 Ndipo zidachitika kuti mu chaka chimenechi Nefi adalilira kwa Ambuye, kuti:

4 O Ambuye, musalore kuti anthu awa awonongeke ndi lupanga; koma O Ambuye, koma lorani mukhale njala m’dziko, kuti iwautse m’chikumbukiro cha Ambuye Mulungu wawo, ndipo kuti mwina kapena angalape ndi kutembenukira kwa Inu.

5 Ndipo zidachitika, molingana ndi mawu a Nefi. Ndipo padali njala yaikulu pa dziko, pakati pa anthu onse a Nefi. Ndipo motero m’chaka cha makumi asanu ndi awiri mphambu zinayi njalayo idapitilirabe, ndipo ntchito yowononga idatha ndi lupanga, koma njala idakula kwambiri.

6 Ndipo ntchito yowonongayi idapitiliranso m’chaka cha makumi asanu ndi awiri ndi zisanu. Pakuti dziko lidakanthidwa mpaka lidauma, ndipo silidabalitse chimanga pa nyengo ya chimanga; ndipo dziko lonse lapansi lidakanthidwa, ngakhale pakati pa Alamani komanso pakati pa Anefi, kotero kuti adakanthidwa mpaka kuti iwo adawonongeka ndi mazikwi mu madera woipa kwambiri a dzikolo.

7 Ndipo zidachitika kuti anthu adaona kuti adali pafupi kufa ndi njala, ndipo adayamba kukumbukira Ambuye Mulungu wawo; ndipo adayamba kukumbukira mawu a Nefi.

8 Ndipo anthu adayamba kuchondelera ndi akulu oweruza awo ndi atsogoleri awo, kuti akanene kwa Nefi: Taonani, ife tikudziwa kuti iwe ndiwe munthu wa Mulungu, ndipo kotero lilira kwa Ambuye Mulungu wathu kuti achotse kwa ife njala iyi, kuopa kuti mawu onse udanena zokhudzana ndi chiwonongeko chathu akwaniritsidwa.

9 Ndipo zidachitika kuti oweruza adanena kwa Nefi, monga mwa mawu amene adafunidwa. Ndipo zidachitika kuti pamene Nefi adaona kuti anthu adalapa ndipo adadzichepetsa okha mu chiguduli, iye adaliranso kwa Ambuye, kuti:

10 O Ambuye, taonani anthu awa alapa; ndipo asesa gulu la Gadiyantoni kuchoka pakati pawo mpaka kuti latheratu; Ndipo iwo abisa ziwembu zawo padziko lapansi.

11 Tsopano, O Ambuye, chifukwa cha kudzichepetsa kwawoku kodi mudzabwenza mkwiyo wanu, ndipo mulore mkwiyo wanu ukhutitsidwe mu chiwonongeko cha anthu oipa omwe mudawawononga kale.

12 O Ambuye, kodi mudzabweza mkwiyo wanu, inde, mkwiyo wanu waukali, ndi kupangitsa kuti njala iyi ithe m’dziko lino.

13 O Ambuye, kodi mudzandimvetsera ine, ndi kuchititsa kuti kuchitidwe monga mwa mawu anga, ndi kutumiza mvula pa nkhope ya dziko lapansi, kuti iye abweretse zipatso zake, ndi chimanga chake pa nyengo ya chimanga.

14 O Ambuye, mudamvetsera mawu anga pamene ndidati, Pakhale njala, kuti mliri wa lupanga uthe; ndipo ine ndikudziwa mupanga, ngakhale pa nthawi ino, mumvetsera mawu anga, pakuti inu mudanena kuti: Ngati anthu awa alapa ndiwapulumutsa iwo.

15 Inde, O Ambuye, ndipo mwaona kuti alapa chifukwa cha njala ndi mliri ndi chiwonongeko chimene chadza kwa iwo.

16 Ndipo tsopano, Ambuye, kodi mubwenza mkwiyo wanu, ndi kuyesanso ngati iwo adzakutumikireni? Ndipo ngati ndi choncho, O Ambuye, inu mutha kuwadalitsa iwo molingana ndi mawu anu amene mwanena.

17 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha makumi asanu ndi awiri ndi zisanu ndi chimodzi Ambuye adabwenza mkwiyo wawo kuchoka kwa anthu, ndipo adachititsa kuti mvula igwe pa dziko lapansi, kotero kuti idabweretsa chipatso chake mu nyengo ya chipatso chake. Ndipo zidachitika kuti idatulutsa mbewu zake mu nyengo ya mbewu zake.

18 Ndipo taonani, anthu adakondwera, ndi kulemekeza Mulungu, ndi nkhope yonse ya dziko idadzala ndi chimwemwe; ndipo sadafunenso kuwononga Nefi, koma adamutenga ngati mneneri wamkulu, ndi munthu wa Mulungu, wokhala ndi mphamvu zazikulu ndi ulamuliro wopatsidwa kwa iye kuchokera kwa Mulungu.

19 Ndipo taonani, Lehi, m’bale wake, sadali kumbuyo kwake olo pang’ono pa zinthu zokhudzana ndi chilungamo.

20 Ndipo motero zidachitika kuti anthu a Nefi adayamba kuchitanso bwino m’dzikolo, ndipo adayamba kumanga malo awo opasuka, ndipo adayamba kuchulukana ndi kufalikira, ngakhale mpakana adakuta dziko lonselo, konse kumpoto ndi kum’mwera komwe, kuyambira kunyanja kumadzulo kufikira kunyanja kum’mawa.

21 Ndipo zidachitika kuti chaka cha makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi chidatha mwamtendere. Ndipo chaka cha makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri chidayamba mu mtendere; ndipo mpingo udafalikira pankhope yonse ya dziko lonse; ndipo mbali yochuluka ya anthu, onse Anefi ndi Alamani, adali a mumpingo; ndipo iwo adali ndi mtendere wochuluka kwambiri m’dzikomo; ndipo motero chidatha chaka cha makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri.

22 Ndiponso adali ndi mtendere m’chaka cha makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi zitatu, kupatulapo kudali zokangana pang’ono zokhudzana ndi mfundo za chiphunzitso zimene zidaikidwa ndi aneneri.

23 Ndipo m’chaka cha makumi asanu ndi awiri kudza zisanu ndi zinayi kudayamba mikangano yambiri. Koma zidachitika kuti Nefi ndi Lehi, ndi ambiri a abale awo omwe ankadziwa za mfundo zoona za chiphunzitso, pokhala ndi mavumbulutso ambiri tsiku ndi tsiku, kotero adalalikira kwa anthu, kotero kuti adathetsa mikangano yawo m’chaka chomwecho.

24 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha makumi asanu ndi atatu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, padali chiwerengero china cha opanduka ochokera kwa anthu a Nefi, amene dzaka zingapo m’mbuyomo adapita kwa Alamani, ndipo adatenga pa iwo okha dzina la Alamani, komanso chiwerengero cha ena omwe adali zidzukulu zenizeni za Alamani, atautsidwa ku mkwiyo ndi iwo, kapena ndi opandukawo, kotero adayamba nkhondo ndi abale awo.

25 Ndipo iwo adachita zophana ndi umbanda; ndipo kenako iwo amakhonza kubwelera ku mapiri, ndi ku chipululu ndi kumalo obisika, kudzibisa okha kuti iwo asathe kudziwika, kulandira tsiku ndi tsiku kuwonjezeredwa kwa chiwerengero chawo, pamene padali ogalukira amene adapita kwa iwo.

26 Ndipo motero m’kupita kwa nthawi, inde, ngakhale mu nthawi ya dzaka dzochepa, iwo adakhala gulu lalikulu kwambiri la achifwamba; ndipo iwo adafufuza madongosolo onse achinsinsi a Gadiyantoni; ndipo motero iwo adakhala achifwamba a Gadiyantoni.

27 Tsopano taonani, achifwambawa adachita chisokonezo chachikulu, inde, ngakhale chiwonongeko chachikulu pakati pa anthu a Nefi, komanso pakati pa anthu a Alamani.

28 Ndipo zidachitika kuti kudali koyenera kuti pakhale kuimitsidwa kwa ntchito ya chiwonongekoyi; kotero iwo adatumiza gulu lankhondo la amuna amphamvu m’chipululu ndi pamapiri kukafufuza gulu la achifwambali, ndi kukawawononga.

29 Koma taonani, zidachitika kuti m’chaka chimenecho iwo adabwenzedwa ngakhale ku maiko awo. Ndipo motero chidatha chaka cha makumi asanu ndi atatu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

30 Ndipo zidachitika kumayambiliro kwa chaka cha makumi asanu ndi atatu ndi chimodzi iwo adapitanso motsutsana ndi gulu ili la achifwamba, ndipo lidawononga ambiri; ndipo adayenderedwanso ndi chiwonongeko chachikulu.

31 Ndipo iwo adakakamizikanso kubwelera kuchoka m’chipululu ndi kuchoka m’mapiri kupita kumalo awo, chifukwa cha kuchuluka kwakukulu kwa chiwerengero cha achifwamba amene adadzadza m’mapiri ndi m’chipululu.

32 Ndipo zidachitika kuti motero chakacho chidatha. Ndipo achifwamba adachulukirabe ndipo adakula mphamvu, motero kuti adanyazitsa magulu ankhondo onse a Anefi, ndiponso a Alamani; ndipo iwo adachititsa mantha aakulu kuti adze kwa anthu pa nkhope yonse ya dzikolo.

33 Inde, pakuti iwo adayendera madera ambiri a dzikolo, ndikuchita kuwononga kwakukulu kwa iwo; inde, adapha ambiri, ndipo adatenga ena ukapolo mu chipululu, inde, ndipo makamaka akazi awo ndi ana awo.

34 Tsopano choipa chachikuluchi, chimene chidadza kwa anthu chifukwa cha mphulupulu zawo; chidawautsanso m’chikumbutso cha Ambuye Mulungu wawo.

35 Ndipo motero chidatha chaka cha makumi asanu ndi atatu ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza.

36 Ndipo m’chaka cha makumi asanu ndi atatu kudza ziwiri adayambanso kuiwala Ambuye Mulungu wawo. Ndipo m’chaka cha makumi asanu ndi atatu kudza zitatu iwo adayamba kukula m’mphamvu mu mphulupulu. Ndipo m’chaka cha makumi asanu ndi atatu mphambu zinayi sadakonze njira zawo.

37 Ndipo zidachitika m’chaka cha makumi asanu ndi atatu ndi zisanu iwo adakulira kulira mphamvu mu kunyada kwawo, ndi mu kuipa kwawo; ndipo motero iwo adali akuchanso ku chiwonongeko.

38 Ndipo motero chidatha chaka cha makumi asanu ndi atatu ndi zisanu.