Mutu 10
Ambuye amupatsa Nefi mphamvu yotsindikizira—Iye apatsidwa mphamvu kuti amange ndi kumasula padziko lapansi ndi kumwamba—Iye awalamulira anthu kuti alape kapena kuwonongeka—Mzimu umunyamula kuchokera ku unyinji kufikira ku unyinji. Mdzaka dza pafupifupi 21–20 Yesu asadabadwe.
1 Ndipo zidachitika kuti kudayamba kugawikana pakati pa anthu, mokuti adagawanikana uku ndi uko ndipo adapita njira zawo, kusiya Nefi yekha, pamene iye adaima pakati pawo.
2 Ndipo zidachitika kuti Nefi adapita njira yake molunjika ku nyumba yake, akusinkhasinkha pa zinthu zimene Ambuye adaonetsa kwa iye.
3 Ndipo zidachitika pamene adali kulingalira motero—pokhala wokhumudwa kwambiri chifukwa cha kuipa kwa anthu Achinefi, ntchito zawo zachinsinsi za mdima, ndi kupha kwawo, ndi kulanda kwawo, ndi mitundu yonse ya kuipa—ndipo zidachitika pamene iye adali kusinkhasinkha motere mumtima mwake, taonani, mawu adadza kwa iye, nanena:
4 Ndiwe odala, Nefi, chifukwa cha zinthu zimene iwe wazichita; pakuti ndaona momwe iwe walalikira mopanda kutopa mawu amene ndapereka kwa iwe, kwa anthu awa. Ndipo sudawaope, ndipo sudafune moyo wako, koma udafuna chifuniro changa, ndi kusunga malamulo anga.
5 Ndipo tsopano, chifukwa wachita ichi ndi kusatopa, taona, ndidzakudalitsa iwe kwamuyaya; ndipo ndidzakupanga iwe wamphamvu m’mawu ndi m’zochita, m’chikhulupiliro ndi m’ntchito; inde, ngakhale kuti zonse zidzachitidwa kwa iwe monga mwa mawu ako, pakuti sudzapempha chimene chili chotsutsana ndi chifuniro changa.
6 Taona, iwe ndiwe Nefi, ndipo ine ndine Mulungu. Taona, ine ndikulengeza kwa iwe pamaso pa angelo anga, kuti udzakhala ndi mphamvu pa anthu awa, ndipo udzakantha dziko lapansi ndi njala, ndi mliri, ndi chiwonongeko, molingana ndi kuipa kwa anthu awa.
7 Taona, ndikupereka kwa iwe mphamvu, kuti chilichonse chimene iwe udzatsindikize pa dziko lapansi chidzakhala chotsindikizidwa kumwamba; ndipo chilichonse udzamasule pa dziko lapansi chidzamasulidwa Kumwamba; ndipo motero udzakhala ndi mphamvu pakati pa anthu awa.
8 Ndipo motero, ngati iwe ungadzanene kwa kachisi iyi kuti idzang’ambike pawiri, zidzachitika.
9 Ndipo ngati iwe udzanena kwa phiri iri, Ugwe pansi ndi kukhala posalazika, zidzachitika.
10 Ndipo taona, ngati iwe udzanene kuti Mulungu adzakanthe anthu awa, zidzachitika.
11 Ndipo tsopano taonani, ine ndikulamulira iwe, kuti udzapita ndi kukalengeza kwa anthu awa, kuti motere akutero Ambuye Mulungu, yemwe ali Wamphamvu zonse: Pokhapokha mulape inu mudzakanthidwa, ngakhale kufikira chiwonongeko.
12 Ndipo taonani, tsopano zidachitika kuti pamene Ambuye adayankhula mawu awa kwa Nefi, adaima ndipo sadapite ku nyumba yake, koma adabwelera kwa makamu amene adabalalikana pa nkhope ya dzikolo, ndipo adayamba kulengeza kwa iwo mawu a Ambuye omwe adayankhulidwa kwa iye, za chiwonongeko chawo ngati salapa.
13 Tsopano taonani, pakusatengera za chozizwitsa chachikulucho chimene Nefi adachita powauza iwo za imfa ya mkulu wa oweruza, iwo adaumitsa mitima yawo ndipo sadamvetsere mawu a Ambuye.
14 Kotero, Nefi adalalika kwa iwo mawu a Ambuye, kuti: Pokhapokha mulape, motere akutero Ambuye, mudzakanthidwa mpaka ku chiwonongeko.
15 Ndipo zidachitika kuti pamene Nefi adalalikira kwa iwo mawu, taonani, iwo adaumitsabe mitima yawo ndipo sadamvetsere mawu ake; kotero adamunyoza ndipo adafuna kuika manja awo pa iye kuti akamponye m’ndende.
16 Koma taonani, mphamvu ya Mulungu idali ndi iye, ndipo iwo sakadatha kumutenga iye kuti amuponye iye mu ndende, pakuti iye adatengedwa ndi Mzimu ndipo adatengedwa kuchoka pakati pawo.
17 Ndipo zidachitika kuti motero iye adapita patsogolo mu Mzimu, kuchokera ku unyinji kwa unyinji, akumalengeza mawu a Mulungu, ngakhale mpaka iye atawalengeza iwo kwa onse, kapena kuwatumiza iwo pakati pa anthu onse.
18 Ndipo zidachitika kuti iwo sadamvetsere mawu ake; ndipo kudayamba kukhala mikangano, kotero kuti adagawanikana motsutsana okhaokha ndipo adayamba kuphana wina ndi mnzake ndi lupanga.
19 Ndipo kotero chidatha chaka cha makumi asanu ndi awiri ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.