Malembo Oyera
Helamani 5


Mutu 5

Nefi ndi Lehi adzipereka iwo eni ku ulaliki—Maina awo awaitanira iwo kutengera miyoyo yawo pambuyo pa makolo awo akale—Khristu awombola iwo amene amalapa—Nefi ndi Lehi apangitsa ambiri kutembenuka ndipo atsekeredwa m’ndende, ndipo moto uwazinga—Mtambo wa mdima ukuta anthu mazana atatu—Dziko ligwedezeka, ndipo mawu alamula anthu kuti alape—Nefi ndi Lehi ayankhula ndi angelo, ndipo khamu lizingidwa ndi moto. Mdzaka dza pafupifupi 30 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti mu chaka chomwecho, taonani, Nefi adapereka mpando wa chiweruzo kwa munthu amene dzina lake lidali Sezoramu.

2 Pakuti monga malamulo awo ndi maboma awo adakhazikitsidwa ndi mawu a anthu, ndipo iwo amene adasankha zoipa adali wochuluka kuposa iwo amene adasankha chabwino, kotero iwo adali okwanira ku chiwonongeko, pakuti malamulo adali atayipitsidwa.

3 Inde, ndipo izi sizidali zonse; iwo adali anthu osamvera, mwakuti sakadatha kulamuliridwa ndi lamulo kapena chilungamo, kupatula ku kuchiwonongeko chawo.

4 Ndipo zidachitika kuti Nefi adali atatopa chifukwa cha kusaweruzika kwawo; ndipo adapereka mpando wa chiweruzo, ndipo adadzitengera pa iye kuti alalikire mawu a Mulungu mu masiku ake wonse wotsala, ndipo m’bale wake Lehi nayenso, masiku ake wonse wotsala;

5 Pakuti adakumbukira mawu omwe atate awo Helamani adayankhula kwa iwo. Ndipo mawu amene adanena ndi awa:

6 Taonani, ana anga, ndikukhumba; kuti mukumbukire kusunga malamulo a Mulungu; ndipo ndikadakonda kuti mukauze anthu mawu awa. Taonani, ndakupatsani inu maina a makolo athu woyamba amene adaturuka m’dziko la Yerusalemu; ndipo ichi ndachita kuti pamene mukukumbukira maina anu mukakumbukire iwo; ndipo mukawakumbukira mudzakumbukira ntchito zawo; ndipo pamene mukukumbukira ntchito zawo mudzadziwa kuti kwanenedwa, ndiponso kwalembedwa, kuti zidali zabwino.

7 Kotero, ana anga aamuna, ndikufuna kuti mudzichita chimene chili chabwino, kuti icho chikanenedwe cha inu, ndi kulembedwa, inde monga kudanenedwa ndi kulembedwa za iwo.

8 Ndipo tsopano ana anga aamuna, taonani ndili nako kanthu kena ndikukhumbira kwa inu, chokhumba chimene chili, kuti musachite zinthu izi kuti mudzitamandire, koma kuti muchite zinthu izi ku kudzikundikira inu eni chuma kumwamba, inde; chimene chili chamuyaya, ndi chimene sichifota; kuti inu mukathe kukakhala ndi mphatso ya mtengo wapatali ya moyo wamuyaya, imene ife tili nacho chifukwa chakuganizira idaperekedwa kwa makolo athu.

9 O, kumbukirani, kumbukirani, ana anga, mawu amene mfumu Benjamini adayankhula kwa anthu ake; inde, kumbukirani kuti palibe njira ina kapena njira imene munthu angapulumutsidwe nayo, kokha kudzera mu mwazi wotetezera wa Yesu Khristu, amene adzabwera; inde, kumbukirani kuti akudza kudzawombola dziko.

10 Ndipo kumbukiraninso mawu amene Amuleki adayankhula kwa Zeziromu, mu mzinda wa Amoniha; pakuti adati kwa iye kuti Ambuye adzabweradi kudzawombola anthu ake, koma kuti sadzabwera kudzawawombola iwo m’machimo awo, koma kudzawawombola iwo ku machimo awo.

11 Ndipo ali ndi mphamvu yopatsidwa kwa iye yochokera kwa Atate kuwawombola iwo ku machimo awo chifukwa cha kulapa; kotero watumiza angelo ake kukalengeza uthenga wa ndondomeko za kalapidwe, zomwe zimabweretsa ku mphamvu ya Muwomboli, ku chipulumutso cha miyoyo yawo.

12 Ndipo tsopano, ana anga, kumbukirani, kumbukirani kuti ndi pa thanthwe la Muwomboli wathu, amene ali Khristu, Mwana wa Mulungu, kuti mukuyenera kumanga maziko anu; kuti pamene mdyerekezi adzatumiza mphepo zake zamphamvu, inde, mivi yake mu kamvuluvulu, inde, pamene matalala ake wonse ndi namondwe wake wamkulu adzagwera pa inu, sizidzakhala ndi mphamvu pa inu kukukokerani inu pansi ku phompho la chisoni ndi tsoka losatha, chifukwa cha thanthwe limene mudamangidwapo, limene lili maziko okhazikika, maziko amene anthu akamanga sangagwe.

13 Ndipo zidachitika kuti awa adali mawu amene Helamani adaphunzitsa kwa ana ake aamuna; inde, iye adawaphunzitsa iwo zinthu zambiri zimene sizidalembedwe, ndiponso zinthu zambiri zimene zidalembedwa.

14 Ndipo iwo adakumbukira mawu ake; ndipo chifukwa chake adapita patsogolo, akusunga malamulo a Mulungu, kukaphunzitsa mawu a Mulungu pakati pa anthu wonse a Nefi, kuyambira ku mzinda wa Chuluka;

15 Ndipo kuchokera pamenepo ku mzinda wa Gidi; ndi kuchokera ku mzinda wa Gidi mpaka ku mzinda wa Muleki;

16 Ndipo ngakhale kuchokera mumzinda umodzi ku wina, mpaka iwo adali atapita pakati pa anthu wonse a Nefi womwe adali m’dziko lakummwera; ndipo kuchokera pamenepo kupita m’dziko la Zarahemula, pakati pa Alamani.

17 Ndipo zidachitika kuti iwo adalalikira ndi mphamvu yaikulu, kufikira kuti adasokoneza ambiri a opandukirawo amene adali atapita kuchokera kwa Anefi, kufikira kuti adabwera ndipo adavomereza machimo awo ndipo adabatizidwa mu kulapa, ndipo mwamsanga adabwelera kwa Anefi kuti ayesere kukonzanso kwa iwo zoipa zomwe adazichita.

18 Ndipo zidachitika kuti Nefi ndi Lehi adalalikira kwa Alamani ndi mphamvu yaikulu yotero ndi ulamuliro, pakuti iwo adali ndi mphamvu ndi ulamuliro zopatsidwa kwa iwo kuti akayankhule, ndipo iwonso adali kupatsidwa kwa iwo chimene adayenera—

19 Kotero iwo adayankhula mozwizwitsa kwambiri kwa Alamani, m’kuwatsimikizira iwo, kotero kuti padali zikwi zisanu ndi zitatu za Alamani amene adali m’dziko la Zarahemula ndi m’madera ena ozungulira adabatizidwa mu kulapa, ndipo adatsimikizirika za kuipa kwa miyambo ya makolo awo.

20 Ndipo zidachitika kuti Nefi ndi Lehi adapitilira kuchokera kumeneko kupita ku dziko la Nefi.

21 Ndipo zidachitika kuti iwo adatengedwa ndi gulu lankhondo la Alamani ndi kuponyedwa m’ndende; inde, ngakhale mu ndende yomweyo yomwe Amoni ndi abale ake adaponyedwa ndi antchito a Limuhi.

22 Ndipo ataponyedwa m’ndende masiku ambiri osadya, taonani, adaturuka kupita kundende kuwatenga kuti akawaphe.

23 Nefi ndi Lehi adazingidwa monga ngati moto, ngakhale kufikira kuti sadayerekeze kuyika manja awo pa iwo kuwopa kuti angawotchedwe. Komabe, Nefi ndi Lehi sadatenthedwe; ndipo adaimilira pakati pa moto ndipo sadawotchedwe.

24 Ndipo pamene adaona kuti adazingidwa ndi mzati wamoto, ndi kuti sudawawotche, mitima yawo idalimbika.

25 Pakuti iwo adaona kuti Alamani sadayese kuika manja awo pa iwo; kapena sadalimbe mtima kuyandikira kwa iwo, koma adaima monga ngati kuti adadzidzimutsidwa ndi kuzizwa.

26 Ndipo zidachitika kuti Nefi ndi Lehi adaimilira ndipo adayamba kuyankhula kwa iwo, kuti: Musawope, chifukwa taonani, ndi Mulungu amene wasonyeza kwa inu chinthu chodabwitsa ichi, chimene chasonyeza kwa inu kuti simungaike manja anu pa ife kuti mutiphe ife.

27 Ndipo taonani, pamene iwo adanena mawu awa dziko lidagwedezeka kwambiri, ndipo makoma a ndende adagwedezeka ngati kuti adali pafupi kugwa pansi; koma taonani, sadagwe. Ndipo taonani, iwo amene adali m’ndende adali Alamani ndi Anefi womwe adali opanduka.

28 Ndipo zidachitika kuti adaphimbidwa ndi mtambo wamdima, ndipo mantha aakulu adawagwera.

29 Ndipo zidachitika kuti kudadza mawu ngati ali pamwamba pa mtambo wa mdima, akunena: Lapani inu, lapani inu, ndipo musafunenso kuwononga atumiki anga amene ndawatumiza kwa inu kuti alengeze uthenga wabwino.

30 Ndipo zidachitika pamene iwo adamva mawu awa, ndipo adaona kuti sadali mawu a bingu, kapena sadali mawu a phokoso loopsya kwambiri, koma taonani, adali mawu odekha a kufatsa kwangwiro, ngati kuti adali mawu a kunong’ona, ndipo adapyoza kufikira kumoyo—

31 Ndipo mosaona za kufatsa kwa mawu, taonani dziko lidagwedezeka kwambiri, ndipo makoma a ndende adanjenjemera kachiwiri, ngati kuti adali pafupi kugwetsedwa pansi; ndipo taonani mtambo wamdima, umene udawaphimba, sudabalalike—

32 Ndipo taonani mawu adadza kachiwiri, kuti: Lapani inu, lapani inu, pakuti ufumu wa kumwamba uli pafupi; ndipo musafunenso kuwononga atumiki anga. Ndipo zidachitika kuti dziko lidagwedezeka kachiwiri, ndipo makoma adanjenjemera.

33 Komanso kenanso kwa nthawi yachitatu mawu adadza, ndipo adayankhula kwa iwo mawu odabwitsa amene sangathe kunenedwa ndi munthu; ndipo makomawo adanjenjemeranso, ndipo dziko lidagwedezeka ngati lidali pafupi kugawikana pakati.

34 Ndipo zidachitika kuti Alamani sakadatha kuthawa chifukwa cha mtambo wa mdima umene udawaphimba iwo; inde, komanso adali osasunthika chifukwa cha mantha womwe adawagwera.

35 Tsopano padali m’modzi pakati pawo amene adali Mnefi mwa kubadwa, amene poyamba adali wa mpingo wa Mulungu koma adapanduka kuchoka kwa iwo.

36 Ndipo zidachitika kuti adatembenuka, ndipo taonani, adaona kudzera mumtambo wa mdima nkhope za Nefi ndi Lehi; ndipo taonani, izo zidawala kwambiri, monga ngati nkhope za angelo. Ndipo iye adaona kuti iwo adakweza maso awo kumwamba; ndipo amaoneka ngati kuti akuyankhula kapena kukweza mawu awo kwa munthu wina yemwe amamuona.

37 Ndipo zidachitika kuti munthu uyu adalirira kwa khamulo, kuti iwo atembenuke ndi kuyang’ana. Ndipo taonani, padali mphamvu yopatsidwa kwa iwo kuti adatembenuka ndi kuyang’ana; ndipo iwo adaona nkhope za Nefi ndi Lehi.

38 Ndipo adati kwa munthuyo: Taona, zinthu zonsezi zikutanthauza chiyani? Ndipo ndindani amene akuyankhula ndi anthu awa?

39 Tsopano dzina la munthuyo lidali Aminadabu. Ndipo Aminadabu adati kwa iwo: Iwo amayankhulana ndi angelo a Mulungu.

40 Ndipo zidachitika kuti Alamani adati kwa iye: Tichite chiyani, kuti mtambo wamdima uwu uchotsedwe kuti usatiphimbe?

41 Ndipo Aminadabu adati kwa iwo: Mukuyenera kulapa, ndi kulilira ku mawuwo, ngakhale kufikira mudzakhale ndi chikhulupiliro mwa Khristu, amene adaphunzitsidwa kwa inu ndi Alima, ndi Amuleki, ndi Zeziromu; ndipo pamene muchita izi, mtambo wamdima udzachotsedwa pokuphimbani.

42 Ndipo zidachitika kuti iwo wonse adayamba kulilira ku mawu a iye amene adagwedeza dziko lapansi; inde, iwo adalira ngakhale mpaka mtambo wamdima udabalalika.

43 Ndipo zidachitika kuti pamene adaponya maso awo uku ndi uko, ndi kuona kuti mtambo wamdima udabalalika kuchoka powaphimba, taonani, iwo adawona kuti adazingidwa, inde wina aliyense, ndi mzati wa moto.

44 Ndipo Nefi ndi Lehi adali pakati pawo; inde, adazingidwa; inde, adali ngati ali pakati pa malawi a moto, koma sudawavulaze, kapena kugwira makoma a ndende; ndipo adadzadzidwa ndi chisangalalo chosaneneka, chodzala ndi ulemerero.

45 Ndipo taonani, Mzimu Woyera wa Mulungu udatsika kuchokera kumwamba, ndipo udalowa m’mitima yawo, ndipo iwo adadzadzidwa monga ngati ndi moto, ndipo adatha kuyankhula mawu wodabwitsa.

46 Ndipo zidachitika kuti kudadza mawu kwa iwo, inde, mawu wosangalatsa, ngati kuti onong’ona, okuti:

47 Mtendere, mtendere ukhale ndi inu, chifukwa cha chikhulupiliro chanu mwa Okondedwa wanga, amene adali wochokera ku maziko a dziko.

48 Ndipo tsopano, pamene adamva izi adakweza maso awo, ngati kuti akuyang’ana kumene mawu adachokera; ndipo taonani, adaona thambo litatsekuka; ndipo angelo adatsika kuchokera kumwamba ndi kuwatumikira iwo.

49 Ndipo padali anthu mazana atatu amene adaona ndi kumva izi; ndipo adaitanidwa kuti apite chitsogolo ndipo asadabwe, kapena asakayike.

50 Ndipo zidachitika kuti iwo adapita patsogolo, ndipo adatumikira kwa anthu, kulalika mozungulira madera wonse ozungulira zinthu zonse zimene adamva ndi kuziona, kotero kuti gawo lochuluka la Alamani lidatsimikizika ndi iwo, chifukwa cha kukula kwa maumboni omwe iwo adali atalandira.

51 Ndipo wochuluka amene adatsimikizika adaika pansi zida zawo zankhondo, ndiponso udani wawo ndi miyambo ya makolo awo.

52 Ndipo zidachitika kuti iwo adapereka kwa Anefi maiko awo.