Malembo Oyera
Helamani


Mutu 2

Helamani, mwana wa Helamani, akhala mkulu wa oweruza—Gadiyantoni atsogolera gulu la Kishkumeni—Wantchito wa Helamani apha Kishkumeni, ndipo gulu la Gadiyantoni lithawira m’chipululu. Mdzaka dza pafupifupi 50–49 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika m’chaka cha makumi anayi ndi ziwiri cha ulamuliro wa oweruza, Moroniha atakhazikitsanso mtendere pakati pa Anefi ndi Alamani, taonani padalibe wina okhala pa mpando wa chiweruzo; kotero kudayambikanso mkangano pakati pa anthu okhudzana ndi yemwe akuyenera kukhala pa mpando wachiweruzo.

2 Ndipo zidachitika kuti Helamani, amene adali mwana wa Helamani, adasankhidwa kuti akhale pa mpando wa chiweruzo, ndi mawu a anthu.

3 Koma onani, Kishkumeni, amene adapha Pahorani, adadikilira kuti awonongenso Helamani; ndipo adathandizidwa ndi gulu lake, limene lidalowa mu pangano kuti palibe amene akuyenera kudziwa kuipa kwake.

4 Pakuti padali wina Gadiyantoni, amene adali katswiri kwambiri mu mawu ochuluka, ndiponso mu luso lake, kuti apitirize ntchito yachinsinsi ya kupha ndi ya umbava; kotero adakhala mtsogoleri wa gulu la Kishkumeni.

5 Kotero iye adawanyengelera iwo, ndiponso Kishkumeni, kuti ngati angamuike iye mu mpando wa chiweruzo iye akapereka kwa iwo amene adali a gulu lake kuti iwo aikidwe mu mphamvu ndi ulamuliro pakati pa anthu; kotero Kishkumeni adafuna kuwononga Helamani.

6 Ndipo zidachitika pamene iye adapita patsogolo kuyandikira mpando wachiweruzo kuti amuwononge Helamani, taonani m’modzi wa antchito a Helamani, atatuluka kunja usiku, ndipo atalandira, kudzera mu kudzibisa, chidziwitso cha madongosolo amenewo amene adaikidwa ndi gulu ili kuti awononge Helamani—

7 Ndipo zidachitika kuti adakumana naye Kishkumeni, ndipo adampatsa iye chizindikiro; kotero Kishkumeni adadziwitsa kwa iye cholinga cha chikhumbo chake, chokhumba kuti amutsogolere kumpando wa chiweruzo kuti akaphe Helamani.

8 Ndipo pamene wantchito wa Helamani adadziwa mtima wonse wa Kishkumeni, ndi m’mene chidaliri cholinga chake chakupha, ndiponso kuti chidali cholinga cha anthu wonse amene adali a gulu lake cha kupha, ndi kuba, ndi kupeza mphamvu, (ndipo ili lidali dongosolo lawo la chinsinsi, ndi gulu lawo) wantchito wa Helamani adati kwa Kishkumeni: Tiyeni tipite ku mpando wa chiweruzo.

9 Tsopano izi zidakondweretsa Kishkumeni mopambana, pakuti adaganiza kuti akwaniritse cholinga chake; koma taonani, wantchito wa Helamani, pamene adali kupita ku mpando wa chiweruzo, adalasa Kishkumeni ngakhale pamtima, mpaka adagwa ndikufa opanda kubuula. Ndipo adathamanga ndi kukamuuza Helamani zinthu zonse zimene adaziona, ndi kuzimva, ndi kuchita.

10 Ndipo zidachitika kuti Helamani adatumiza kuti atenge gulu ili la achifwamba ndi lokupha mwachinsinsi, kuti akathe kuphedwa monga mwa lamulo.

11 Koma taonani, pamene Gadiyantoni adapeza kuti Kishkumeni sadabwelere adaopa kuti angawonongedwe; kotero iye adapangitsa kuti gulu lake limutsatire iye. Ndipo iwo adathawa kuchokera mu dzikolo, mwa njira yachinsinsi, kupita mu chipululu; ndi motero pamene Helamani adatumiza kuti akawatenge iwo sadapezeke pena paliponse.

12 Ndipo zambiri za Gadiyantoni uyu zidzayankhulidwa patsogolo pake. Ndipo motero chidatha chaka cha makumi anayi ndi chiwiri cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

13 Ndipo taonani, pa mapeto a buku ili mudzaona kuti Gadiyantoni uyu adatsimikizira kugwetsa, inde, pafupifupi chiwonongeko chonse cha anthu a Nefi.

14 Taonani ine sindikutanthauza mapeto a buku la Helamani, koma ine ndikutanthauza mapeto a buku la Nefi, kumene ine ndidatenga nkhani yonse yomwe ine ndidalemba.

Print