Malembo Oyera
Helamani 6


Mutu 6

Alamani wolungama alalikira kwa Anefi oipa—Mitundu yonse iwiri ya anthu ichita bwino mu nthawi ya mtendere ndi zochuluka—Lusifara, oyambitsa wa tchimo, awutsa mitima ya oipa ndi achifwamba a Gadiyantoni mu kupha ndi kuipa—Achifwamba alanda boma la Anefi. Mdzaka dza pafupifupi 29–23 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti pamene chaka cha makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri cha ulamuliro wa oweruza chidatha, zinthu zonsezi zidali zitachitika, ndipo Alamani adakhala, ochuluka a iwo, anthu olungama, kotero kuti chilungamo chawo chidaposa cha Anefi, chifukwa cha kulimba ndi kukhazikika kwawo m’chikhulupiriro.

2 Pakuti, taonani, padali ambiri a Anefi amene adakhala ouma mtima ndi osalapa ndi oipa kwambiri, kotero kuti iwo adakana mawu a Mulungu ndi ulaliki ndi uneneri wonse umene udabwera pakati pawo.

3 Komabe, anthu a mpingo adali ndi chisangalalo chachikulu chifukwa cha kutembenuka kwa Alamani, inde, chifukwa cha Mpingo wa Mulungu, umene udakhazikitsidwa pakati pawo. Ndipo iwo adatumikilana wina ndi mzake, ndipo adasangalala wina ndi mzake, ndipo adali ndi chisangalalo chachikulu.

4 Ndipo zidachitika kuti ambiri a Alamani adabwera m’dziko la Zarahemula, ndipo adalengeza kwa anthu a Anefi njira ya kutembenuka kwawo, ndipo adawalimbikitsa iwo ku chikhulupiliro ndi kulapa.

5 Inde, ndipo ambiri adalalikira ndi mphamvu yopambana ndi ulamuliro, kwa kutsitsitsa ambiri a iwo m’kuya kwa kudzichepetsa, kukhala otsatira wodzichepetsa a Mulungu ndi a Mwana wa Nkhosa.

6 Ndipo zidachitika kuti ambiri a Alamani adapita ku dziko la kumpoto; ndiponso Nefi ndi Lehi adapita ku dziko la kumpoto, kukalalikira kwa anthu. Ndipo kotero chidatha chaka cha makumi asanu ndi limodzi ndi zitatu.

7 Ndipo taonani, mudali mtendere m’dziko lonse, mwakuti Anefi adapita gawo lirilonse la dziko limene iwo angafune, kaya pakati pa Anefi kapena Alamani.

8 Ndipo zidachitika kuti Alamani nawonso adapita kulikonse kumene akadafuna, kaya kudali pakati pa Alamani kapena pakati pa Anefi; ndipo kotero adayenderana momasuka wina ndi mzake, kugula ndi kugulitsa, ndi kupeza phindu, monga mwa kufuna kwawo.

9 Ndipo zidachitika kuti adalemera kwambiri, wonse Alamani ndi Anefi; ndipo iwo adali ndi golide wochuluka, ndi siliva, ndi mitundu yonse ya zitsulo zamtengo wapatali, konse m’dziko lakummwera ndi m’dziko la kumpoto.

10 Tsopano dziko lakummwera lidatchedwa Lehi, ndipo dziko la kumpoto lidatchedwa Muleki, limene lidali pambuyo pa mwana wamwamuna wa Zedekiya; pakuti Ambuye adabweretsa Muleki m’dziko la kumpoto, ndipo Lehi odalowa m’dziko lakummwera.

11 Ndipo taonani, padali golide wamitundu yonse m’maiko onsewa, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wapatali yamitundumitundu; ndipo padalinso amisili aluso, amene adamanga mitundu yonse ya miyala, ndi kumaiyenga; ndipo kotero iwo adakhala olemera.

12 Adalima tirigu wambiri, kumpoto konse ndi kummwera; ndipo iwo adakula kwambiri, konse kumpoto ndi kummwera. Ndipo iwo adachulukana ndi kukula mumphamvu kwambiri m’dzikolo. Ndipo iwo adaweta nkhosa zambiri ndi ng’ombe, inde, zonenepa zambiri.

13 Taonani akazi awo adagwira ntchito ndi kupota, ndi kupanga mitundu yonse ya nsalu, za bafuta wopota wabwino ndi nsalu za mtundu uliwonse, kuti aveke maliseche awo. Ndipo kotero chaka cha makumi asanu ndi limodzi mphambu zinayi chidapita mu mtendere.

14 Ndipo m’chaka cha makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu adalinso ndi chisangalalo chachikulu ndi mtendere, inde, kulalikira kochuluka ndi mauneneri ambiri okhudza zomwe zidali nkudza. Ndipo kotero chidapita chaka cha makumi asanu ndi limodzi ndi zisanu.

15 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza, taonani, Sezoramu adaphedwa ndi dzanja losadziwika pamene adakhala pa mpando wa chiweruzo. Ndipo zidachitika kuti m’chaka chomwecho, kuti mwana wake, amene adasankhidwa ndi anthu m’malo mwake, nayenso adaphedwa. Ndipo motero chidatha chaka cha makumi asanu ndi limodzi ndi zisanu ndi chimodzi.

16 Ndipo kumayambiliro kwa chaka cha makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu ndi ziwiri anthu adayambanso kukula mukuipa moipitsitsa.

17 Pakuti, taonani, Ambuye adawadalitsa nthawi yaitali ndi chuma cha dziko lapansi kotero kuti sadautsidwe ku mkwiyo, kunkhondo, kapena kukhetsa mwazi; choncho adayamba kuika mitima yawo pa chuma chawo; inde, iwo adayamba kufunafuna phindu kuti iwo akazikuze wina kuposa nzake; kotero adayamba kupha anthu mwachinsinsi, ndi kuba ndi kulanda, kuti apeze phindu.

18 Ndipo tsopano taonani, awo okupha ndi olanda adali gulu lomwe lidapangidwa ndi Kishkumeni ndi Gadiyantoni. Ndipo tsopano zidali zitachitika kuti adali ambiri, ngakhale pakati pa Anefi, a gulu la Gadiyantoni. Koma taonani, iwo adali wochuluka kwambiri pakati pa gawo loipa kwambiri la Alamani. Ndipo ankatchedwa achifwamba ndi okupha a Gadiyantoni.

19 Ndipo ndi amene adapha oweruza wamkulu Sezoramu, ndi mwana wake wamwamuna, pamene adali pa mpando wa chiweruzo; ndipo taonani, sadapezedwe.

20 Ndipo tsopano zidachitika pamene Alamani adapeza kuti padali achifwamba pakati pawo iwo adali achisoni chopambana; ndipo iwo adagwiritsa ntchito njira iliyonse mu mphamvu zayo kuti awawononge padziko lapansi.

21 Koma taonani, Satana adautsa mitima ya gawo lochuluka la Anefi, moti adalumikizana ndi magulu a achifwamba aja, ndipo adalowa m’mapangano awo ndi malumbiro awo, kuti akatetezane ndi kusungana wina ndi mnzake m’makhalidwe ovuta aliwonse angaikidwe, kuti asavutike chifukwa cha kupha kwawo, ndi kulanda kwawo, ndi kuba kwawo.

22 Ndipo zidachitika kuti iwo adali ndi zizindikiro zawo, inde, zizindikiro zawo zachinsinsi, ndi mawu awo achinsinsi; ndipo ichi kuti akasiyanitse m’bale amene adalowa m’pangano, kuti choipa chilichonse m’bale wake angachite iye asavulazidwe ndi m’bale wake, kapena ndi iwo amene adali a gulu lake, amene adatenga pangano ili.

23 Ndipo kotero akhonza kupha, ndi kulanda, ndi kuba, ndi kuchita zadama ndi mtundu uliwonse wa kuipa, kotsutsana ndi malamulo a dziko lawo komanso malamulo a Mulungu wawo.

24 Ndipo aliyense wa iwo amene adali a gulu lawo akawululira ku dziko kuipa kwawo ndi zonyansa zawo, akuyenera kuweruzidwa, osati molingana ndi malamulo a dziko lawo, koma monga mwa malamulo a kuipa kwawo, amene adaperekedwa ndi Gadiyantoni ndi Kishkumeni.

25 Tsopano taonani, ndi malumbiro achinsinsi awa ndi mapangano amene Alima adalamulira mwana wake kuti asapite ku dziko, kuopera kuti iwo angakhale njira yogwetsera anthu ku chiwonongeko.

26 Tsopano taonani, malumbiriro achinsinsi awo ndi mapangano sadabwere kwa Gadiyantoni kuchokera mu zolemba zomwe zidaperekedwa kwa Helamani; koma taonani, adaikidwa mu mtima mwa Gadiyantoni ndi munthu yemweyo amene adanyenga makolo athu woyamba kuti adye chipatso choletsedwacho—

27 Inde, munthu yemweyo amene adachita chiwembu ndi Kaini, kuti ngati iye angaphe m’bale wake Abele izo sizidzadziwika ku dziko. Ndipo adachita chiwembu ndi Kaini ndi otsatira ake kuyambira nthawi imeneyo.

28 Komanso ndi munthu yemweyo amene adaika izo mu mitima ya anthu kumanga nsanja yaitali mokwanira kuti akafike kumwamba. Ndipo ndiye munthu yemweyo amene adatsogolera anthu adachokera ku nsanja ija kulowa m’dziko lino; amene adafalitsa ntchito za mdima ndi zonyansa pa nkhope yonse ya dziko, mpaka kuwakokera anthu ku chiwonongeko chonse, ndi ku gehena yosatha.

29 Inde, ndi munthu yemweyo amene adachiika icho mu mtima mwa Gadiyantoni kuti apitirizebe ntchito ya mdima, ndi ya kupha mwachinsinsi; ndipo waibweretsa kuyambira pa chiyambi cha munthu kufikira nthawi ino.

30 Ndipo taonani, ndiye amene ali oyambitsa wa uchimo wonse. Ndipo taonani, amapitiriza ntchito zake za mdima ndi kupha mwachinsinsi, ndi kupatsirana ziwembu zawo, malumbiro awo, ndi mapangano awo, ndi malingaliro awo a kuipa koopsya, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo malinga ndi momwe iye angagwilire pa mitima ya ana a anthu.

31 Ndipo tsopano taonani, iye adali atagwira kwakukulu pa mitima ya Anefi; inde, kotero kuti iwo adakhala oipa kwambiri; inde, wochuluka a iwo adali atapatuka panjira ya chilungamo, ndipo adaponda pansi pa mapazi awo malamulo a Mulungu, ndipo adatembenukira ku njira zawo, ndi kudzimangira kwa iwo wokha mafano a golide wawo ndi siliva wawo.

32 Ndipo zidachitika kuti mphulupulu zonsezo zidadza kwa iwo mu nthawi ya dzaka zochepa, kotero kuti gawo lochuluka la izo zidadza kwa iwo mchaka cha makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu ndi ziwiri cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

33 Ndipo iwo adakula mu mphulupulu zawo m’chaka cha makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu ndi zitatu, ku chisoni chachikuru ndi kulira kwa olungama.

34 Ndipo motero tikuona kuti Anefi adayamba kucheperachepera mu kusakhulupilira, ndi kukula mu zoipa ndi zonyansa, pamene Alamani adayamba kukula mopambanitsa m’chidziwitso cha Mulungu wawo; inde, iwo adayamba kusunga malamulo olembedwa ndi malamulo ake, ndi kuyenda m’choonadi ndi m’chilungamo pamaso pake.

35 Ndipo motero tikuona kuti Mzimu wa Ambuye udayamba kuchoka kwa Anefi, chifukwa cha kuipa ndi kuumitsa kwa mitima yawo.

36 Ndipo motero tikuona kuti Ambuye adayamba kutsanulira Mzimu wake pa Alamani, chifukwa cha kufewa kwawo ndi kufuna kwawo kokhulupilira m’mawu ake.

37 Ndipo zidachitika kuti Alamani adasaka gulu la achifwamba a Gadiyantoni; ndipo iwo adalalikira mawu a Mulungu pakati pa gulu loipa kwambiri la iwo, moti gulu ili la achifwamba lidawonongedwa kotheratu kuchokera pakati pa Alamani.

38 Ndipo zidachitika kumbali inayi, kuti Anefi adawalimbitsa iwo ndi kuwathandiza iwo, kuyambira pa gawo loipa kwambiri la iwo, mpaka iwo adafalikira dziko lonse la Anefi, ndipo adanyengelera gawo lochuluka la wolungama mpaka iwo adatsika ndikuyamba kukhulupilira ntchito zawo ndi kutenga nawo mbali ku zofunkha zawo, ndi kugwirizana nawo mu kupha kwawo kwachinsinsi ndi magulu awo.

39 Ndipo kotero iwo adatenga kuyendetsa konse kwa boma, mwakuti iwo adapondereza pansi pa mapazi awo ndi kukantha ndi kung’amba ndi kutembenuzira misana yawo pa wosauka ndi wofatsa, ndi wotsatira wodzichepetsa a Mulungu.

40 Ndipo motero tikuona kuti iwo adali mu chikhalidwe choopsya, ndi oyenelera ku chiwonongeko chosatha.

41 Ndipo zidachitika kuti motero chidatha chaka cha makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zitatu za ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.