Malembo Oyera
Helamani 12


Mutu 12

Anthu ndi wosakhazikika ndi wopusa ndi achangu kuchita zoipa—Ambuye amalanga anthu ake—Kupanda pake kwa munthu kuyerekezedwa ndi mphamvu ya Mulungu—M’tsiku la chiweruzo, anthu adzalandira moyo wosatha kapena chiwonongeko chosatha. Mdzaka dza pafupifupi 6 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo motero tikuona bodza lake, ndiponso kusakhazikika kwa mitima ya ana a anthu; inde, titha kuona kuti Ambuye muubwino wake waukulu wopanda malire amadalitsa ndi kuchititsa bwino iwo amene amamukhulupilira.

2 Inde, ndipo titha kuona pa nthawi yomweyo imene amachititsa bwino anthu ake, inde, m’kuchuluka kwa minda yawo, nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo, ndi golide, ndi siliva, ndi mu mitundu yonse ya zinthu za mtengo wapatali za mtundu uliwonse ndi maluso; kupulumutsa miyoyo yawo, ndi kuwawombotsa kuchoka m’dzanja la adani awo; kufewetsa mitima ya adani awo kuti asawamenye nkhondo; inde, mwachidule, kuchita zinthu zonse pa chithandizo ndi chisangalalo cha anthu ake; inde, imeneyo ndi nthawi yakuti iwo amaumitsa mitima yawo, ndipo amaiwala Ambuye Mulungu wawo, ndi kupondereza pansi pa mapazi awo Woyerayo—inde, ndipo izi chifukwa cha kumasulidwa kwawo, ndi kuchita bwino kwawo kwakukulu.

3 Ndipo motero ife tikuona kuti pokhapokha Ambuye alangize anthu ake ndi masautso ambiri, inde, pokhapokha atawayendera ndi imfa ndi chiopsezo, ndi njala ndi mliri yamtundu uliwonse, iwo sadzamkumbukira.

4 O ndi wopusa motani, ndi achabechabe motani, ndi woipa motani, ndi aumdyerekezi, ndi achangu bwanji kuchita mphulupulu, ndi kuzengereza bwanji kuchita zabwino, ndi ana a anthu; inde, ndi achangu chotani nanga kumvetsera mawu a woipayo, ndi kuika mitima yawo pa zinthu zopanda pake za dziko!

5 Inde, ndi a changu chotani pa kudzikuza m’kunyada; inde, ndi achangu chotani m’kudzitama; ndi kuchita mitundu yonse ya zimene zili mphulupulu; ndipo ndi ochedwa motani iwo kuti amukumbukire Ambuye Mulungu wawo, ndi kutchera makutu ku uphungu wake, inde, ndi ochedwa motani nanga m’kuyenda m’njira za nzeru!

6 Taonani, iwo safuna kuti Ambuye Mulungu wawo, amene adawalenga iwo, kuti adziwalamulira ndi kulamulira pa iwo; pakusatengera ubwino wake waukulu ndi chifundo chake pa iwo, iwo amapeputsa malangizo ake, ndipo iwo safuna kuti iye akhale chitsogozo chawo.

7 O, ndi waukulu motani nanga uchabechabe wa ana a anthu; inde, ngakhale iwo ndi ocheperapo kuposa fumbi la dziko lapansi.

8 Pakuti, taonani, fumbi la dziko lapansi limayenda uku ndi uko, mpaka kugawanikana pakati, mwa lamulo la Mulungu wathu wamkulu ndi wosatha.

9 Inde, taonani, pa mawu ake zitunda zimanjenjemera, ndipo mapiri amagwedezeka.

10 Ndipo ndi mphamvu ya mawu ake iwo amasweka, ndi kukhala osalala, inde, ngakhale ngati chigwa.

11 Inde, ndi mphamvu ya mawu ake dziko lonse lapansi limagwedezeka;

12 Inde, ndi mphamvu ya mawu ake, maziko amagwedezeka, ngakhale mpakana pakati.

13 Inde, ndipo ngati anena kwa dziko lapansi—Suntha—limasuntha.

14 Inde, ngati anena kwa dziko lapansi—Udzabweleranso, kuti litalikitse tsiku kwa maola ambiri—zimachitika;

15 Ndipo motero, monga mwa mawu ake dziko lapansi limabwelera m’mbuyo, ndipo zimaoneka kwa munthu kuti dzuwa laima; inde, ndipo taonani, izi zili chomwecho; pakuti ndithu, ndi dziko limene limayenda osati dzuwa.

16 Ndipo taonani, komanso, ngati anena kwa madzi akuya kwakukulu—Khala ouma—zimachitika.

17 Taonani, ngati ati kwa phiri ili—Dzuka iwe, ndipo bwera ndi kugwera pamzinda umenewo, kuti udzakwilirike, taonani—zimachitika.

18 Ndipo taonani, ngati munthu wabisa chuma m’nthaka, ndipo Ambuye adzati—Chikhale chotembeleredwa, chifukwa cha mphulupulu ya iye amene adachibisa—taonani chidzakhala chotembeleredwa.

19 Ndipo ngati Ambuye adzanena—Khala chotembeleredwa, kuti palibe munthu adzakupeza iwe kuyambira tsopano mpaka muyaya—taonani, palibe munthu adzachipeza kuyambira pano mpaka muyaya.

20 Ndipo taonani, ngati Ambuye adzanena kwa munthu—chifukwa cha mphulupulu zako, iwe udzatembeleredwa kwamuyaya—chidzachitika.

21 Ndipo ngati Ambuye adzanena—Chifukwa cha mphulupulu zako iwe mudzadulidwa kuchoka pamaso panga—adzachititsa kuti zikhale chomwecho.

22 Ndipo tsoka kwa iye amene adzamunenera izi, pakuti kudzakhala kwa iye amene adzachita mphulupulu, ndipo iye sangathe kupulumutsidwa; kotero, pa chifukwa ichi, kuti anthu athe kupulumutsidwa, kulapa kwalengezedwa.

23 Chotero, odala ali iwo amene adzalapa ndi kumvetsera mawu a Ambuye Mulungu wawo; pakuti iwo ndiwo amene adzapulumutsidwa.

24 Ndipo Mulungu apereke, mu chidzalo chake chachikulu, kuti anthu athe kubweretsedwa ku kulapa ndi ntchito zabwino, kuti athe kubwenzeretsedwa ku chisomo kwa chisomo, monga mwa ntchito zawo.

25 Ndipo ndikadakonda kuti anthu onse adzapulumutsidwe. Koma timawerenga kuti mu tsiku lalikulu ndi lomaliza kuli ena amene adzaponyedwa kunja, inde, amene adzachotsedwa kuchoka pamaso pa Ambuye;

26 Inde, amene adzaperekedwa ku mkhalidwe wachisoni chosatha, kukwaniritsa mawu akuti: Iwo amene adachita zabwino adzakhala nawo moyo wosatha; ndipo amene adachita zoipa adzakhala nacho chilango chosatha. Ndipo izi zili motero. Ameni.

Print