Malembo Oyera
Helamani 7


Uneneri wa Nefi, mwana wa Helamani—Mulungu awopseza anthu a Nefi kuti adzawayendera mu mkwiyo wake, ku kuwawononga kotheratu pokhapokha atalapa zoipa zawo. Mulungu akantha anthu a Nefi ndi mliri; alapa ndi kubwelera kwa iye. Samueli, Mlamani, anenera kwa Anefi.

Zophatikizidwa mu Mitu 7 mpaka 16.

Mutu 7

Nefi akanidwa kumpoto ndipo abwelera ku Zarahemula—Iye apemphera pansanja yake ya kumunda ndipo kenako aitana anthu kuti alape kapena kuwonongeka. Mdzaka dza pafupifupi 23–21 Yesu asadabadwe.

1 Taonani, tsopano zidachitika mu chaka cha makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu ndi zinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Anefi, kuti Nefi, mwana wa Helamani, adabwelera ku dziko la Zarahemula kuchokera ku dziko la kumpoto.

2 Pakuti iye adali atapita pakati pa anthu amene adali m’dziko la kumpoto, ndipo adalalikira mawu a Mulungu kwa iwo, ndipo adanenera zinthu zambiri kwa iwo;

3 Ndipo iwo adakana mawu ake onse, kotero kuti iye sakadatha kukhala pakati pawo, koma kubweleranso ku dziko la kubadwa kwake.

4 Ndipo poona anthu mu mkhalidwe wa kuipa koopsya kotero, ndi achifwamba a Gadiyantoni aja akukhala m’mipando ya chiweruzo—atalanda mphamvu ndi ulamuliro wa dziko; kuika pambali malamulo a Mulungu, ndipo osalungama pamaso pake ngakhale pang’ono; osachitira chilungamo ana a anthu;

5 Kutsutsa olungama chifukwa cha kulungama kwawo; kuwaleka olakwa ndi oipa apite osalangidwa chifukwa cha ndalama zawo; ndipo kuwonjezera apo kukhazikidwa pa udindo pa mutu wa boma, kulamulira ndi kuchita monga mwa kufuna kwawo, kuti apeze phindu ndi ulemelero wa dziko lapansi, ndipo, kuwonjezera apo, kuti iwo azitha kuchita chigololo mosavuta, ndi kuba, ndi kupha, ndi kuchita monga mwa zifuniro zawo—

6 Tsopano kusaweruzika kwakukuru kumeneku kudadza pa Anefi, munthawi ya dzaka zosachuluka; ndipo pamene Nefi adachiona ichi, mtima wake udafufuma ndi chisoni mkati mwa chifuwa chake; ndipo adafuula m’kuwawa kwa moyo wake:

7 O, kuti ine ndikadakhala nawo masiku anga m’masiku amene atate anga Nefi adabwera kuchokera m’dziko la Yerusalemu, kuti ndikadasangalala ndi iwo m’dziko lolonjezedwa; pamenepo anthu ake adali osavuta kuphunzitsidwa, osagwedezeka posunga malamulo a Mulungu, ndi ochedwa kutsogozedwa kuchita mphulupulu; ndipo iwo adali achangu kumvetsera mawu a Ambuye—

8 Inde, ngati masiku anga akadakhala m’masiku amenewo, pamenepo moyo wanga ukadakondwera m’kulungama kwa abale anga.

9 Koma taonani, ndaikidwa kuti awa ndi masiku anga, ndi kuti moyo wanga udzadzazidwa ndi chisoni chifukwa cha kuipa kwa abale anga.

10 Ndipo taonani, tsopano zidachitika kuti padali pa nsanja, imene idali m’munda wa Nefi, imene idali pafupi ndi njira yaikulu yopita ku msika waukulu, umene udali mu mzinda wa Zarahemula; kotero, Nefi adadzigwaditsa pa nsanja imene idali m’munda wake, nsanjayo idalinso pafupi ndi chipata cha m’munda chimene chimatsogolera njira yaikuluyo.

11 Ndipo zidachitika kuti padali anthu ena akudutsapo ndipo adaona Nefi pamene adali kutsanulira moyo wake kwa Mulungu pa nsanjapo; ndipo adathamanga ndikukauza anthu zomwe adaziona, ndipo anthu adasonkhana pamodzi mwa unyinji kuti adziwe chifukwa cha kulira kwakukulu kotero chifukwa cha kuipa kwa anthu.

12 Ndipo tsopano, pamene Nefi adanyamuka iye adaona unyinji wa anthu amene adasonkhana pamodzi.

13 Ndipo zidachitika kuti adatsekula pakamwa pake, ndipo adati kwa iwo, Taonani, mwasonkhanilananji pamodzi? Kuti ndikuuzeni za mphulupulu zanu?

14 Inde, chifukwa ndakwera nsanja yanga, kuti nditsanulire moyo wanga kwa Mulungu wanga; chifukwa cha chisoni chachikulu cha mtima wanga, chimene chili chifukwa cha mphulupulu zanu!

15 Ndipo chifukwa cha chisoni changa ndi kulira kwanga mwasonkhana pamodzi, ndipo mukudabwa; inde, ndipo muli nako kufunika kwakukulu kuti mudabwe; inde, inu mukuyenera kudabwa chifukwa inu mwaperekedwa kuti mdyerekezi wakugwirani kwakukulu koposa pa mitima yanu.

16 Inde, mudaperekeranji njira yonyengelera ya iye amene akufuna kutaya miyoyo yanu ku chisoni chosatha ndi tsoka losatha?

17 O Lapani, lapani! Mudzaferanji? Tembenukani inu, tembenukirani kwa Ambuye Mulungu wanu. Chifukwa chiyani adakusiyani inu?

18 Ndi chifukwa chakuti mwaumitsa mitima yanu; inde, simukumvetsera mawu a m’busa wabwino; inde, mwautsa iye mumkwiyo otsutsa inu.

19 Ndipo taonani, m’malo mwa kukusonkhanitsani, pokhapokha mudzalape, taonani, adzakubalalitsani kuti mudzakhale chakudya cha agalu ndi zilombo zakuthengo.

20 O, kodi mudaiwala bwanji Mulungu wanu pa tsiku lomwelo limene iye adakuwombolani?

21 Koma taonani, ndiko kupeza phindu, kuyamikiridwa ndi anthu, inde, ndipo kuti mupeze golidi ndi siliva. Ndipo mwaika mitima yanu pa chuma ndi zinthu zopanda pake za dziko lino, zimene mukuphera, ndi kulanda, ndi kuba, ndi kuchita umboni wonama motsutsana ndi mnansi wanu, ndi kuchita kusaweruzika kwa mtundu uliwonse.

22 Ndipo chifukwa cha ichi tsoka lidzafika kwa inu pokhapokha mulape. Pakuti ngati simulapa, taonani, mzinda waukulu uwu, ndiponso mizinda ikuluikulu yonse yozungulira, imene ili m’kati mwa dziko lathu, idzatengedwa kuti musakhale ndi malo m’menemo; pakuti taonani, Ambuye sadzakupatsani mphamvu, monga wakhala akuchitira, kuti mupambane potsutsana ndi adani anu.

23 Pakuti, taonani, motere akutero Ambuye: Sindidzaonetsa woipa mphamvu yanga; kwa wina kuposa wina, kupatula kwa iwo amene alapa machimo awo, ndi kumvetsera mawu anga. Tsopano kotero, ndikufuna kuti muone, abale anga, kuti kudzakhala bwino kwa Alamani kuposa inu kupatula kuti mulape.

24 Pakuti, taonani, iwo ali olungama kwambiri kuposa inu, chifukwa iwo sadachimwire pa chidziwitso chachikulucho chimene inu mwalandira; kotero Ambuye adzakhala wachifundo kwa iwo; inde, adzatalikitsa masiku awo ndi kuonjezera mbewu zawo, ngakhale pamene inu mudzawonongedwa kotheratu pokhapokha inu mutalapa.

25 Inde, tsoka kwa inu chifukwa cha chonyansa chachikulu icho chimene chadza pakati panu; ndipo inu mwadzigwirizanitsa nokha kwa icho, inde, kwa gulu lachinsinsi lija lomwe lidakhazikitsidwa ndi Gadiyantoni!

26 Inde, tsoka lidzadza kwa inu chifukwa cha kunyada uko kumene mudalora kulowa m’mitima yanu, kumene kwakukuzani inu kupitilira icho chimene chili chabwino chifukwa cha chuma chanu chochuluka kwambiri!

27 Inde, tsoka kwa inu chifukwa cha kuipa ndi zonyansa zanu!

28 Ndipo pokhapokha mulape mudzawonongeka; inde, ngakhale maiko anu adzalandidwa kwa inu, ndipo mudzawonongeka kuchoka pankhope ya dziko lapansi.

29 Taonani tsopano, sindikunena kuti zinthu izi zidzakhala, mwa ine ndekha, chifukwa sikuli kwa ine ndekha kuti ndikudziwa zinthu izi; koma taonani, ndikudziwa kuti zinthu izi ndizoona chifukwa Ambuye Mulungu wadziwitsa izo kwa ine, kotero ndikuchitira umboni kuti zidzakhala.

Print