Malembo Oyera
Yakobo 2


Mutu 2

Yakobo adzudzula kukonda chuma, kunyada, ndi kusadzisunga—Anthu atha kufunafuna chuma kuti athandize anthu anzawo—Ambuye alamula kuti palibe mwamuna pakati pa Anefi amene angakhale ndi mkazi wopitilira m’modzi—Ambuye amakondwera m’kudzisunga kwa akazi. Mdzaka dza pafupifupi 544–421 Yesu asadabadwe.

1 Mawu amene Yakobo, m’bale wake wa Nefi, adayankhula kwa anthu a Nefi, patadutsa imfa ya Nefi:

2 Tsopano, abale anga okondedwa, ine, Yakobo, molingana ndi udindo umene ndiri nawo kwa Mulungu, kuti ndikulitse udindo wanga ndi kutsimikiza mtima, ndi kuti ndingachotse machimo anu m’zovala zanga, ndikubwera ku kachisi lero kuti ndingalalikire inu mawu a Mulungu.

3 Ndipo inu nokha mukudziwa kuti ine ndakhala wodzipereka mu udindo wa maitanidwe anga; koma ine lero ndalemedwa ndi chikhumbo chachikulu ndi kudera nkhawa za ubwino wa miyoyo yanu kuposa momwe ndakhalira kumbuyoku.

4 Pakuti, taonani, nthawi yonseyi, mwamvera mawu a Ambuye, amene ndakupatsani.

5 Koma taonani, mvetserani inu kwa ine, ndipo dziwani kuti mwa chithandizo cha Mlengi wamphamvu zonse wa kumwamba ndi dziko lapansi ine ndingathe kukuuzani inu za maganizo anu, mmene inu mukuyambira kugwira tchito mu uchimo, uchimo umene umaonekera wonyansa kwambiri kwa ine; inde, ndi wonyansa kwa Mulungu.

6 Inde, zikumvetsa chisoni moyo wanga ndipo zikundipangitsa ine kuchepa ndi manyazi pamaso pa Mlengi wanga, kuti ndikuyenera kuchitira umboni kwa inu za kuipa kwa mitima yanu.

7 Ndiponso zikundimvetsa chisoni kuti ndiyenera kuyankhula molimba mtima kwambiri zokhudza inu pamaso pa akazi anu ndi ana anu, ambiri a amene kumvelera kwawo kuli kofatsa ndi koyera ndi kofewa pamaso pa Mulungu, chinthu chimene chiri chokondweretsa kwa Mulungu;

8 Ndipo ndikuganiza ine kuti iwo abwera kuno kudzamva mawu osangalatsa a Mulungu, inde, mawu amene amachiritsa moyo wovulazidwawo.

9 Kotero, zikulemetsa moyo wanga kuti ndikakamizidwe, chifukwa cha lamulo lokhwima limene ndidalandira kwa Mulungu, kukuchenjezani molingana ndi zolakwa zanu, kukulitsa mabala a iwo ovulazidwa kale, m’malo mwa kutonthoza ndi kuchiritsa zilonda zawo; ndipo iwo amene sadavulazidwe, m’malo mokuti apange mphwando pa mawu okondweretsa a Mulungu, ali ndi mipeni yoikidwa kuti ibaye m’mitima mwawo ndi kuvulaza maganizo awo osankhwima.

10 Koma, pakusatengera za ukulu wa ntchitoyi, ndikuyenera kuchita monga mwa malamulo okhwima a Mulungu, ndi kukuuzani za kuipa kwanu ndi zonyansa zanu, pamaso pa oyera mtima, ndi osweka mtima, ndipo pansi pa kuyang’ana kwa kulasa kwa diso la Mulungu Wamphamvu zonse.

11 Kotero, ndikuyenera kukuuzani choonadi molingana ndi kumveka bwino kwa mawu a Mulungu. Pakuti, taonani, monga ndidafunsira kwa Ambuye, adadza mawu kwa ine, kuti: Yakobo, dzuka ndikupita ku kachisi mawa, ndikukanena mawu amene ndidzakupatsa iwe kwa anthu awa.

12 Ndipo tsopano taonani, abale anga, awa ndi mawu amene ndikukuuzani, kuti ambiri a inu mwayamba kufunafuna golidi, ndi siliva, ndi mitundu yonse ya miyala ya mitengo yapatali, imene dziko ili, limene liri dziko la lonjezano kwa inu ndi kwa mbewu zanu ichuluka mochuluka koposa.

13 Ndipo dzanja lopereka lidakumwetulirani mokondweretsa, kuti mwapeza chuma chambiri; ndipo chifukwa ena a inu mwalandira zochulukirapo kuposa za abale anu, mwakuzika m’kunyada kwa mitima yanu, ndi kuvala makosi owuma ndi mitu yokwezeka chifukwa cha mtengo wake wa chobvala chanu, ndipo mukuzunza abale anu chifukwa mumadziyesa muli bwino kuposa iwo.

14 Ndipo tsopano, abale anga, kodi mukuganiza kuti Mulungu amakuyesani olungama mu chinthu ichi? Taonani, ndikunena kwa inu, Ayi. Koma iye akutsutsa inu, ndipo ngati mukhala mu izi ziweruzo zake zikuyenera kubwera kwa inu msanga.

15 O kuti akadakuonetsani kuti akhoza kulasa inu; ndipo ndi kuyang’ana kumodzi kwa diso lake akhoza kukukanthani inu ku fumbi!

16 O kuti akadakuchotserani mphulupulu ndi zonyansazi. Ndipo, O kuti mukadamvera mawu a malamulo ake, ndipo osalora kudzikuza kwa mitima yanu kuwononge miyoyo yanu!

17 Ganizanirani za abale anu monga inu eni, ndipo khalani ochezeka ndi onse ndi omasuka ndi chuma chanu, kuti akhale olemera ngati inu.

18 Koma musadayambe kufunafuna chuma, funani Ufumu wa Mulungu.

19 Ndipo mutalandira chiyembekezo mwa Khristu, mudzapeza chuma ngati muchifunafuna; ndipo mudzachifunafuna ndi cholinga cha kuchita zabwino—kuveka amaliseche, ndi kudyetsa anjala, ndi kumasula andende, ndi kupereka chithandizo kwa odwala ndi osautsika.

20 Ndipo tsopano, abale anga, ndayankhula ndi inu za kunyada; ndipo amene mwa inu mudasautsa mnansi wanu, ndi kumuzunza chifukwa mudadzikuza m’mitima mwanu, pa zinthu zimene Mulungu wakupatsani, mukuti chiyani za izo?

21 Kodi simukuganiza kuti zinthu zoterozo nzonyansa kwa iye amene adalenga zamoyo zonse? Ndipo munthu mmodzi ndi wamtengo wapatali pamaso pake ngati wina. Ndipo zamoyo zonse zichokera kufumbi; ndipo chifukwa cha chitsiriziro chomwechi adazilenga izo, kuti asunge malamulo ake ndi kulemekeza Iye kosatha.

22 Ndipo tsopano ine ndikumaliza kuyankhula kwa inu za kunyada kumeneku. Ndipo pakadapanda kuti ine sindikuyenera kuyankhula kwa inu zokhudza cholakwa choipitsitsa, mtima wanga ukadakondwera kopambana chifukwa cha inu.

23 Koma mawu a Mulungu akundilemetsa chifukwa cha zolakwa zanu zazikulu. Pakuti taonani, akutero Ambuye: Anthu awa ayamba kukula mu kusaweruzika; iwo samamvetsa malemba, pakuti akafuna kudzimasula okha pochita zachiwerewere, chifukwa cha zinthu zimene zidalembedwa zokhudza Davide ndi Solomoni mwana wake.

24 Taonani, Davide ndi Solomoni zoona adali ndi akazi ambiri ndi adzakazi ambiri, chimene chidali chonyansa pamaso panga, akutero Ambuye.

25 Kotero, akutero Ambuye, ndawatsogolera anthu awa kuchokera m’dziko la Yerusalemu, ndi mphamvu ya mkono wanga, kuti ndithe kukwezera kwa ine nthambi yolungama kuchokera ku chipatso cha m’chiuno mwa Yosefe.

26 Kotero, ine Ambuye Mulungu sindidzalora kuti anthu awa achite monga kwa iwo akale.

27 Kotero, abale anga, ndimvereni ine, ndipo mvetserani mawu a Ambuye: Pakuti palibe munthu mwa inu adzakhale naye, koma mkazi mmodzi yekha; ndipo sadzakhala ndi akazi apambali;

28 Pakuti ine, Ambuye Mulungu, ndimakondwera ndi kudzisunga kwa akazi. Ndipo zachiwerewere ndi zonyansa pamaso panga; akutero Ambuye wa makamu.

29 Kotero, anthu awa adzasunga malamulo anga, atero Ambuye wa makamu, kapena lotembeleredwa likhala dziko chifukwa cha iwo.

30 Pakuti ngati ndikufuna, atero Ambuye wa makamu, kuutsa mbewu kwa ine, ndidzalamulira anthu anga; mu zina zonse adzamvera zinthu izi.

31 Pakuti, taonani, ine, Ambuye, ndidaona chisoni, ndipo ndidamva kulira kwa ana aakazi a anthu anga m’dziko la Yerusalemu, inde, ndi m’maiko onse a anthu anga, chifukwa cha kuipa ndi zonyansa za amuna awo.

32 Ndipo sindidzalora, akutero Ambuye wa makamu, kuti kulira kwa ana aakazi okongola a anthu awa, amene ndidawatsogolera kuchokera m’dziko la Yerusalemu, kudzakwere kwa ine motsutsana ndi amuna a anthu anga, atero Ambuye wa makamu.

33 Pakuti sadzatsogolera ku ukapolo ana aakazi a anthu anga chifukwa cha kufatsa kwawo, pokhapokha ine ndidzawalanga ndi thembelero lowawa, ngakhale ku chiwonongeko; pakuti sadzachita zachiwerewere, monga iwo akale, akutero Ambuye wa makamu.

34 Ndipo tsopano taonani, abale anga, mukudziwa kuti malamulo awa adapatsidwa kwa atate athu, Lehi; kotero, mudawadziwa kale; ndipo mwafika ku kutsutsidwa kwakukulu; pakuti mudachita zinthu izi zimene simukuyenera kuzichita.

35 Taonani, inu mwachita mphulupulu zazikulu kuposa Alamani, abale athu. Inu mwaswa mitima ya akazi anu ofatsa, ndipo mudataya chidaliro cha ana anu, chifukwa cha zitsanzo zanu zoipa pamaso pawo; ndipo kulira kwa mitima yawo kukwera kwa Mulungu pa inu. Ndipo chifukwa cha kunkhwima kwa mawu a Mulungu, amene amatsika motsutsa inu, mitima yambiri idafa yolasidwa ndi mabala akuya.