Malembo Oyera
Yakobo 7


Mutu 7

Sheremu akana Khristu, akangana ndi Yakobo, afuna chizindikiro, ndipo akanthidwa ndi Mulungu—Aneneri onse adayankhula za Khristu ndi Chitetezero Chake—Anefi adakhala masiku awo ngati oyendayenda, obadwa m’chisautso, ndi odedwa ndi Alamani. Mdzaka dza pafupifupi 544–421 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti patapita dzaka zingapo, kudadza munthu pakati pa anthu a Nefi, amene dzina lake adali Sheremu.

2 Ndipo zidachitika kuti adayamba kulalikira pakati pa anthu, ndi kulengeza kwa iwo kuti sipakuyenera kukhalapo Khristu. Ndipo adalalikira zinthu zambiri zosyasyalika kwa anthu; ndipo izi adazichita kuti athe kugwetsa chiphunzitso cha Khristu.

3 Ndipo adagwira ntchito mwakhama kuti atsogoze kutali mitima ya anthu, kotero kuti adasokeretsa mitima yambiri; ndipo iye podziwa kuti ine, Yakobo, ndidali ndi chikhulupiliro mwa Khristu amene ali nkudza, iye adafunafuna mwayi kwambiri kuti abwere kwa ine.

4 Ndipo iye adali ophunzira, kuti iye adali ndi chidziwitso chonse cha chinenero cha anthu; kotero, adatha kugwiritsa ntchito kusyasyalika zambiri, ndi mphamvu zambiri za kuyankhula, molingana ndi mphamvu ya mdyerekezi.

5 Ndipo adali ndi chiyembekezo chakundigwedeza ine ku chikhulupiliro; posatengera za mavumbulutso ochuluka ndi zinthu zambiri zimene ndidaziona zokudzana ndi zinthu izi; pakuti ndidaonadi angelo, ndipo adatumikira kwa ine. Komanso, ndidamva mawu a Ambuye akuyankhula kwa ine m’mawu ake omwe, ku nthawi ndi nthawi; kotero, sindikadatha kugwedezeka.

6 Ndipo zidachitika kuti adadza kwa ine, ndipo mwa njira iyi adayankhula kwa ine, kuti: M’bale Yakobo, ndafunafuna mwayi wochuluka kuti ndiyankhule kwa inu; pakuti ndamva, ndipo ndikudziwanso kuti umayendayenda kwambiri, kulalikira chimene umachitcha uthenga wabwino, kapena chiphunzitso cha Khristu.

7 Ndipo mwatsogolera ambiri a anthu awa kuti apotoze njira yolungama ya Mulungu, ndipo kuti asasunge chilamulo cha Mose chimene chiri njira yoyenera; ndi kutembenuza chilamulo cha Mose kukhala kupembedza kwa munthu amene inu mukuti adzabwera dzaka mazana ambiri kuchokera pano. Ndipo tsopano taonani, ine, Sheremu, ndikukuuzani inu kuti uwu ndi mwano; pakuti palibe munthu amadziwa za zinthu zotere; pakuti sanganena zinthu ziri nkudza. Ndipo moteremu Sheremu adanditsutsa ine.

8 Koma taonani, Ambuye Mulungu adatsanulira Mzimu wake mu moyo wanga, kotero kuti ndidamugonjetsa m’mawu ake onse.

9 Ndipo ine ndidati kwa iye: Kodi iwe ukukana Khristu amene akudzabwera? Ndipo adati: Ngati pangakhale Khristu, ine sindikadakana iye; koma ndikudziwa kuti kulibe Khristu, ngakhale sadakhaleko, ndipo sidzakhalaponso.

10 Ndipo ine ndidati kwa iye: Kodi iwe umakukhulupilira malembo? Ndipo adati: Inde.

11 Ndipo ndidati kwa iye: Ndiye siumawamvetsetsa iwo; pakuti amachitiradi umboni za Khristu. Taonani, ine ndikunena kwa iwe kuti palibe mmodzi wa aneneri amene adalemba, kapena kunenera, koma iwo adayankhula za Khristu ameneyu.

12 Ndipo izi si zonse—zadaonetsedwa kwa ine, pakuti ndidamva ndi kuona; ndipo zidaonetseredwanso kwa ine mwa mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero, ndikudziwa ngati sipakhala chitetezero anthu onse akuyenera kutaika.

13 Ndipo zidachitika kuti iye adati kwa ine: Ndionetse ine chizindikiro mwa mphamvu iyi ya Mzimu Woyera, momwe iwe ukudziwira zambiri.

14 Ndipo ine ndidati kwa iye: Ndine ndani ine kuti ndimuyese Mulungu kuti akuonetse iwe chizindikiro mu chinthu chimene iwe ukuchidziwa kukhala choona? Koma udzakana, chifukwa uli wa mdyerekezi. Komabe, osati kufuna kwanga kuchitidwe; komabe ngati Mulungu akukantha iwe, chimenecho chikhale chizindikiro kwa iwe kuti ali nayo mphamvu, konse kumwamba ndi pa dziko lapansi; ndiponso kuti Khristu adzabwera. Ndipo kufuna kwanu kuchitidwe, O Ambuye, osati kwanga.

15 Ndipo zidachitika kuti pamene ine, Yakobo, nditayankhula mawu amenewa, mphamvu ya Ambuye idafika pa iye, kotero kuti adagwa pansi. Ndipo zidachitika kuti iye adadyetsedwa kwa nthawi ya masiku ambiri.

16 Ndipo zidachitika kuti iye adati kwa anthu: Sonkhanani pamodzi mawa, pakuti ndidzafa; kotero, ndikufuna kuyankhula ndi anthu ndisadafe.

17 Ndipo zidachitika kuti m’mawa mwake khamulo lidasonkhana; ndipo adayankhula nawo momveka, ndikukana zinthu zimene adawaphunzitsa, ndipo adavomereza Khristu; ndi mphamvu ya Mzimu Woyera, ndi utumiki wa angelo.

18 Ndipo adayankhula momveka kwa iwo, kuti adanyengedwa ndi mphamvu ya mdyerekezi. Ndipo iye adayankhula za gahena, ndi za muyaya, ndi za chilango chamuyaya.

19 Ndipo adati: Ndikuopa kuti mwina ndachita tchimo losakhululukidwa, pakuti ndanamiza Mulungu; pakuti ndidakana Khristu, ndipo ndidanena kuti ndidakhulupilira malembo; ndipo amamuchitira umboni ndithu. Ndipo chifukwa ine ndidanama motere kwa Mulungu ine ndikuopa kwakukulu kuti mwina mlandu wanga ungakhale woipa; koma ndivomereza machimo anga kwa Mulungu.

20 Ndipo zidachitika kuti pamene adanena mawu amenewa sadathe kuyankhulanso, ndipo adapereka mzimu wake.

21 Ndipo pamene unyinji udachitira umboni kuti adanena izi pamene ankafuna kupereka mzimu; adadabwa kwambiri; kotero kuti mphamvu ya Mulungu idatsikira pa iwo, ndipo adagonjetsedwa kuti adagwa pansi.

22 Tsopano, chinthu ichi chidali chondikomera ine, Yakobo, pakuti ine ndidapempha izo kwa Atate anga amene adali Kumwamba; pakuti adamva kulira kwanga, ndikuyankha pemphero langa.

23 Ndipo zidachitika kuti mtendere ndi chikondi cha Mulungu chidabwenzeretsedwanso pakati pa anthu; ndipo adasanthula malembo, ndipo sadamverenso mawu a munthu woipa uyu.

24 Ndipo zidachitika kuti njira zambiri zidalinganizidwa kuti titengenso ndi kubwenzeretsa Alamani ku chidziwitso cha choonadi; koma zonse zidali chabe, pakuti iwo amakondwera mu nkhondo ndi kukhetsa mwazi, ndipo iwo adali ndi udani wamuyaya wotsutsana ndi ife, abale awo. Ndipo adafunafuna ndi mphamvu ya manja awo kuti atiwononge kosalekeza.

25 Kotero, anthu a Nefi adalimba kumenyana nawo ndi manja awo, ndi mphamvu zawo zonse, kukhulupilira Mulungu ndi thanthwe la chipulumutso chawo; kotero, adakhalabe ogonjetsa adani awo.

26 Ndipo zidachitika kuti ine, Yakobo, ndidayamba kukalamba; ndipo mbiri ya anthu awa ikusungidwa pa mapale ena a Nefi, kotero, ndimaliza zolemba izi, ndikulengeza kuti ndalemba molingana ndi chidziwitso changa, ponena kuti nthawi idapita nafe, komanso miyoyo yathu idapita monga ngati adali maloto kwa ife, ife okhala osungulumwa komanso anthu aulemu, osokera, otaidwa ku Yerusalemu, obadwa m’masautso, m’chipululu, ndi odedwa ndi abale athu, amene adayambitsa nkhondo ndi mikangano; kotero, tidalira masiku athu.

27 Ndipo ine, Yakobo, ndidaona kuti ndikuyenera kutsikira kumanda anga; kotero, ndidanena kwa mwana wanga Enosi: Tenga mapalewa. Ndipo ndidamuuza iye zinthu zimene m’bale wanga Nefi adandilamulira ine, ndipo adalonjeza kumvera malamulowo. Ndipo ine ndikupanga mapeto a kulemba kwanga pa mapale awa, omwe kulemba kwakhala kochepa; ndipo kwa wowerenga nditsanzikana naye, ndikuyembekezera kuti ambiri a abale anga adzawerenga mawu anga. Abale, tsalani mwa Ambuye.

Print