Malembo Oyera
Yakobo 5


Mutu 5

Yakobo ayankhula mawu Zenosi wokhudzana ndi fanizo la mitengo ya azitona yoweta ndi yakuthengo—Iwo ali chifaniziro cha Israeli ndi Amitundu—Kubalalitsidwa ndi kusonkhanitsidwa kwa Israeli kufaniziridwa—Zolozera zapangidwa kwa Anefi ndi Alamani ndi nyumba yonse ya Israeli—Amitundu adzalumikizanitsidwa mwa Israeli—Potsirizira pake munda wampesawo udzatenthedwa. Mdzaka dza pafupifupi 544–421 Yesu asadabadwe.

1 Taonani, abale anga; simukukumbukira kuti mudawerenga mawu a mneneri Zenosi, amene adayankhula kwa nyumba ya Israeli, kuti:

2 Mvetserani, inu nyumba ya Israeli, ndipo imvani mawu a ine, mneneri wa Ambuye.

3 Pakuti, taonani, akutero Ambuye, ndikufanizira inu; Inu nyumba ya Israeli, ngati mtengo wa azitona oweta, umene munthu adautenga ndikuusamala m’munda wake wampesa; ndipo udakula, ndi kukalamba, ndikuyamba kuvunda.

4 Ndipo zidachitika kuti mwini munda wampesa adapita ndipo adaona kuti mtengo wake wa azitona wayamba kuvunda; ndipo adati: ndidzaudulilira, ndi kuukumbira mouzungulira, ndi kuusamalira; kuti kapena uphuke nthambi zanthete, ndi kuti usawonongeke.

5 Ndipo zidachitika kuti adadulilira, ndi kuukumbara mouzungulira, nausamala molingana ndi mawu ake.

6 Ndipo zidachitika kuti patapita masiku ambiri idayamba kumera pang’ono, nthambi zazing’ono ndi zamthete; koma taonani, pamwamba pake padayamba kuwonongeka.

7 Ndipo zidachitika kuti mwini munda wampesa adaona; nati kwa mtumiki wake: Zimandimvetsa chisoni kuti nditaye mtengo uwu; kotero, pitani, ndipo mukazule nthambi za mtengo wazitona wakuthengo, ndipo mubwere nazo kuno kwa ine; ndipo tidzazula nthambi zazikuluzo zimene zayamba kufota, ndipo tidzaziponya m’moto kuti zipse.

8 Ndipo taonani, atero Ambuye a munda wampesa, ndichotsa zambiri za nthambi izi zazing’ono ndi zanthete, ndipo ndidzazilumikizanitsa kulikonse kumene ndikufuna; ndipo ziribe kanthu kuti ngati muzu wa mtengo uwu uwonongeka; ndidzatha kuteteza zipatso zake kwa ine ndekha; kotero ndidzatenga nthambi zazing’ono ndi zanthete izi, ndipo ndidzazilumikizanitsa kulikonse kumene ndikufuna.

9 Tenga nthambi za mtengo wa azitona wakuthengo; ndi kuzilumikizanitsa izo m’malo mwake; ndipo izi ndidazizula ndidzaziponya pamoto, ndi kuzitentha; kuti zingalemeletse munda wanga wampesa.

10 Ndipo zidachitika kuti mtumiki wa Ambuye a munda wampesayo adachita molingana ndi mawu a Ambuye a munda wampesayo ndi kulumikizanitsa m’nthambi za mtengo wa azitona wakuthengo.

11 Ndipo Ambuye a munda wampesa adachititsa kuti ikumbilidwe, ndi kudulilidwa, ndi kusamalidwa, kunena kwa mtumiki wake; Zimandimvetsa chisoni kuti nditaye mtengo uwu; kotero kuti kapena ndikateteze mizu yake kuti isawonongeke, kuti ndiiteteze kwa ine ndekha, ndachita ichi.

12 Kotero, pita; uyang’anire mtengowo, ndi kuusamala iwo, molingana ndi mawu anga.

13 Ndipo izi ndidzaika kunsi kwenikweni kwa munda wanga wampesa, kulikonse kumene ndikufuna; zilibe kanthu kwa iwe; ndipo ndichita icho kuti ndikateteze kwa inemwini nthambi zachilengedwe za mtengo; komanso, kuti ndikadzisungire chipatso chake motsutsana ndi nyengo yake; pakuti zimandimvetsa chisoni ine kuti nditaye mtengo uwu ndi chipatso chake.

14 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesa adapita; ndikukabisa nthambi zake za mtengo wa azitona oweta ku tsinde la munda wampesa; ina mwa wina ndi ina mwa mzake, monga mwa chifuniro chake ndi chikondwelero chake.

15 Ndipo zidachitika kuti nthawi yaitali idapita, ndipo Ambuye a mundawo adati kwa mtumiki wake: Tiyeni, titsikire kumunda wampesa, kuti tikagwire ntchito m’munda wampesa.

16 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesa, ndi mtumikiyo, adatsikira kumunda wampesa kukagwira ntchito. Ndipo zidachitika kuti mtumikiyo adati kwa mbuye wake: Onani, taonani; onani mtengowu.

17 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesa adayang’ana, ndikuona mtengo umene nthambi za azitona zakuthengo zidalumikizanitsidwa; ndipo idaphuka ndikuyamba kubala zipatso. Ndipo adaona kuti zidali zabwino; ndipo zipatso zake zidali ngati zipatso zachibadwa.

18 Ndipo adati kwa mtumikiyo: Taona, nthambi za mtengo wakuthengo zagwira chinyontho cha muzu wake, kuti muzu wake wabweretsa mphamvu zambiri; ndipo chifukwa cha mphamvu ya mizu yake, nthambi zakuthengo zidabala zipatso zoweta. Tsopano, ngati ife tikadati tisalumikizanitse mu nthambi izi, mtengo wake ukadawonongeka. Ndipo tsopano, taonani, ndidzasunga zipatso zambiri, zimene mtengo wake udabala; ndipo zipatso zake ndidzasunga motsutsana ndi nyengo, kwa ine ndekha.

19 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesa adati kwa mtumiki: Tiyeni, tiyeni tipite ku mapeto a munda wampesa, ndipo taonani, ngati nthambi zachilengedwe za mtengo sizidabale zipatso zambiri; kuti ine ndikasunge zipatso zake motsutsana ndi nyengo, kwa ine ndekha.

20 Ndipo zidachitika kuti adapita kumene mbuye adabisa nthambi zachilengedwe za mtengo, ndipo adati kwa mtumikiyo: Taonani iyi; ndipo adaona yoyamba kuti idabala zipatso zambiri; ndipo adaonanso kuti zidali zabwino. Ndipo iye adati kwa mtumikiyo: Tenga zipatso zake, ndipo uzisunge motsutsana ndi nyengoyo, kuti ine ndingathe kuteteza izo kwa ine ndekha; pakuti taona, adati, nthawi iyi yaitali ndazisamala, ndipo zidabala zipatso zambiri.

21 Ndipo zidachitika kuti mtumikiyo adati kwa mbuye wake: Iwe wabwera bwanji kuno kudzabzala mtengo uwu, kapena nthambi iyi ya mtengo? Pakuti taonani, adali malo osauka kwambiri m’malo onse a munda wanu wampesa.

22 Ndipo Ambuye a munda wampesawo adati kwa iye: Osandilangiza. Ndidadziwa kuti adali malo a nthaka yosalongosoka; kotero, ndidati kwa iwe, ndausamala nthawi yaitali yonseyi; ndipo taona, wabala zipatso zambiri.

23 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesayo adati kwa mtumiki wake: Tapenya kuno; taona ndadzala nthambi ina ya mtengowo; ndipo ukudziwa kuti malo a nthaka iyi idali yosauka kuposa yoyamba ija. Koma, taona mtengowo. Ndausamala nthawi yaitali yonseyi, ndipo udabala zipatso zambiri; kotero, sonkhanitsa, ndipo uisunge motsutsana ndi nyengo yake; kuti ndiiteteze kwa ine ndekha.

24 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesa adatinso kwa mtumiki wake: Tayang’ana kuno, ndipo taona nthambi inanso, imene ine ndadzala; taona ndausamalanso, ndipo udabala zipatso.

25 Ndipo adati kwa mtumiki: Yang’ana kuno, nuwone otsirizawo. Taonani, iyi ndaidzala pa malo a nthaka yabwino; ndipo ndaisamala nthawi yaitali, ndipo gawo limodzi lokha la mtengo lidabala zipatso zoweteka; ndi gawo lina la mtengo lidapereka zipatso zakuthengo; taonani, ndasamala mtengo uwu monga ina ija.

26 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesawo adati kwa mtumikiyo: Zula nthambi zimene sizidabale zipatso zabwino, ndi kuziponya pamoto.

27 Koma taonani, mtumikiyo adati kwa iye: Tiyeni tiudulire, ndipo tikumbire mouzungulira, ndi kuusamala pang’ono, kuti kapena ubala zipatso zabwino kwa inu, kuti mungazisunge motsutsana ndi nyengo yake.

28 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesa ndi mtumiki wa Ambuye wa munda wampesa adasamala zipatso zonse za munda wampesawo.

29 Ndipo zidachitika kuti nthawi yaitali idapita, ndipo Ambuye a munda wampesa adati kwa mtumiki wake: Tiyeni, tipite kumunda wampesa, kuti tikagwirenso ntchito m’munda wampesa. Pakuti taonani, nthawi yayandikira, ndipo mapeto afika posachedwa; kotero ine ndiyenera kudzisungira chipatso motsutsana ndi nyengo yake, kwa ine ndekha.

30 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesa ndi mtumiki adatsikira kumunda wampesa; ndipo adabwera ku mtengowo umene nthambi zake zachilengedwe zidathyoledwa; ndipo nthambi zakuthengo zidalumikizanitsidwa; ndipo taonani, zipatso zamitundumitundu zidasokoneza mtengowo.

31 Ndipo zidachitika kuti Mbuye wa munda wampesayo adalawa zipatso, zamtundu uliwonse monga mwa kuchuluka kwake. Ndipo Ambuye a mundawo wampesayo adati: Taonani, nthawi yaitali iyi tasamalira mtengo uwu, ndipo ndadzisungira kwa ine ndekha motsutsana ndi nyengoyi zipatso zambiri.

32 Koma taonani, nthawi ino wabala zipatso zambiri, ndipo palibe chabwino. Ndipo taonani, pali mitundu yonse ya zipatso zoipa; ndipo sizindipindulira kanthu, pakusatengera ntchito yathu yonse; ndipo tsopano zikundimvetsa chisoni kuti nditaye mtengo uwu.

33 Ndipo Ambuye wa munda wampesayo adati kwa kapoloyo: Tichite chiyani ndi mtengowo, kuti ndikatetezerenso chipatso chabwino kwa ine ndekha?

34 Ndipo mtumikiyo adati kwa mbuye wake: Taonani, popeza mudalumikizanitsa nthambi za mtengo wa azitona wakuthengo, zidadyetsera mizu; kuti ili ndi moyo ndipo siidawonongeke; kotero mukuona kuti zikadali zabwino.

35 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesa adati kwa mtumiki wake: Mtengowo sundipindulira ine kalikonse, ndi mizu yake sindipindula ine kanthu pemene udzabala zipatso zoipa.

36 Komabe, ndikudziwa kuti mizu ndi yabwino, ndipo chifukwa cha cholinga changa ndaiteteza; ndipo chifukwa cha mphamvu zawo zambiri idabala kufikira tsopano; kuchokera ku nthambi zakuthengo, zipatso zabwino.

37 Koma taonani, nthambi zakuthengo zakula ndipo zapitilira mizu yake; ndipo chifukwa kuti nthambi zakuthengo zidagonjetsa mizu yake kotero idabala zipatso zambiri zoipa; ndipo chifukwa yabala zipatso zoipa zochuluka iwe ukuona kuti ukuyamba kuwonongeka; ndipo posachedwapa udzapsa; kuti ukaponyedwe kumoto, kupatula ngati tichitepo kanthu kuti tiuteteze.

38 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesawo adati kwa mtumiki wake: Tiyeni titsikire kumunsi kwenikweni kwa munda wampesawo, ndipo tikaone, ngati nthambi za chibadwidwe zidabalanso chipatso choipa.

39 Ndipo zidachitika kuti adatsikira kumunsi kwa munda wampesawo. Ndipo zidachitika kuti adaona kuti chipatso cha nthambi zachilengedwe zidavundanso; inde, zoyamba ndi zachiwiri, ndi zotsiriza; ndipo zonse zidavunda.

40 Ndipo zipatso zakuthengo za yotsiriza zidagonjetsa gawo la mtengo wobala zipatso zabwino; ngakhale kuti nthambiyo idafota ndi kufa.

41 Ndipo zidachitika kuti Mbuye wa munda wampesa adalira, nati kwa mtumikiyo: Ndikadachita chiyani chinanso ku munda wanga wampesa?

42 Taonani, ndidadziwa kuti zipatso zonse za m’munda wampesa, kupatula izi, zidali zovunda. Ndipo tsopano iyo imene adabala zipatso zabwino, yavundanso; ndipo tsopano mitengo yonse ya m’munda wanga wampesa njopanda pake, pokhapokha kuidulidwa ndi kuiponya pamoto.

43 Ndipo taonani iyi yomaliza, imene nthambi yake idafota, ndidaidzala pa malo a nthaka yabwino; inde, ngakhale iyo imene idali yosankhika kwa ine kuposa madera ena onse a malo a munda wanga wampesa.

44 Ndipo waona kuti ine ndidadulanso zomwe zidali zovuta pa malo a nthaka iyi; kuti ine ndikabzale mtengo uwu m’malo mwake.

45 Ndipo udaona kuti gawo lina lidabala zipatso zabwino, ndipo gawo lina lidabala zipatso zakuthengo; ndipo chifukwa sindidazule nthambi zake ndi kuziponya pamoto, taonani, zagonjetsa nthambi yabwino imene idafota.

46 Ndipo tsopano, taonani, posatengera kusamala konse kumene tidapereka m’munda wanga wampesa, mitengo yake yavunda; kuti sidabale zipatso zabwino; ndipo iyi ndidayembekezera kuiteteza, kuti ndisunge zipatso zake motsutsana ndi nyengo yake, kwa ine ndekha. Koma taonani, yakhala ngati mtengo wazitona wakuthengo, ndipo ulibe phindu, koma kuti udulidwe ndi kuponyedwa pamoto; ndipo zikundiwawa ine kuti ndiutaye iwo.

47 Koma ndikadachitanso chiyani m’munda wanga wampesa? Kodi ndachepetsa dzanja langa, kuti sindidausamalire? Ayi, ine ndausamalira, ndipo ndakumba mouzungulira, ndipo ndaudulira, ndipo ndauthira ndowe; ndipo ndatambasula dzanja langa pafupifupi tsiku lonse, ndipo chimaliziro chikuyandikira. Ndipo zikundimvetsa chisoni kuti ndidzagwetse mitengo yonse ya m’munda wanga wampesa, ndi kuiponya pamoto kuti ipse. Ndani amene wawononga munda wanga wampesa?

48 Ndipo zidachitika kuti mtumiki adati kwa mbuyake: Kodi si kudzikweza kwa munda wanu wampesa—kodi nthambi zake sizidagonjetse mizu yomwe ili yabwino? Ndipo popeza nthambizo zagonjetsa mizu yake, taonani, zidakula nsanga kuposa mphamvu ya mizu, ndi kudzilimbitsa zokha. Taonani, ine ndikuti, kodi ichi sichochititsa kuti mitengo ya m’munda wanu wampesa ikhale yovunda?

49 Ndipo zidachitika kuti Ambuye a munda wampesa adati kwa mtumikiyo: Tiyeni tipite, tikadule mitengo ya m’munda wampesa, ndi kuiponya kumoto, kuti ingakwiyitse nthaka ya munda wanga wampesa, pakuti ndachita zonse. Ndikadachitanso chiyani m’munda wanga wampesa?

50 Koma, taonani, mtumikiyo adati kwa Ambuye a munda wampesa: Usiyeni pang’ono.

51 Ndipo Ambuye adati: Inde, ine ndidzausiya pang’ono, pakuti zikundimvetsa chisoni kuti nditaye mitengo ya m’munda wanga wampesa.

52 Kotero, tiyeni titengeko nthambi ya iyi imene, ndidadzala kumunsi kwenikweni kwa munda wanga wampesa, ndipo tiilumikizanitse ku mtengo umene idachokera; ndipo tiyeni tizule pamtengowo nthambi zimene zipatso zake ziri zowawa koposa; ndi kulumikizanitsa ku nthambi zachilengedwe za mtengo m’malo mwake.

53 Ndipo ichi ndidzachita kuti mtengo usawonongeke, kuti, mwinamwake, ine ndikateteze kwa ine ndekha mizu yake ku cholinga changa.

54 Ndipo taonani, mizu ya chibadwa ya nthambi za mtengo umene ndidadzala kuli konse ndinkafuna, ukadali ndi moyo; kotero, kuti inenso ndikaitetenzenso pa cholinga changa, ndidzatenga nthambi za mtengo uwu, ndipo ndidzailumikizanitsa kwa iyo. Inde, ndidzailumikizanitsa mwa iwo nthambi za mtengo wa manthu wawo, kuti ndikateteze mizuyonso kwa ine ndekha, kuti pamene idzakhala yamphamvu mokwanira, mwina ingathe kubala chipatso chabwino kwa ine, ndipo ndikakhale ndi ulemelero mu zipatso za munda wanga wampesa.

55 Ndipo zidachitika kuti iwo adatenga kuchokera ku mtengo wachibadwa umene udasandulika wakuthengo, nalumikizanitsamo ku mitengo yachibadwa, imenenso idasandulika yakuthengo.

56 Ndipo adatenganso mwa mitengo yachilengedwe imene idasanduka yakuthengo, nailumikizanitsa ku mtengo wake.

57 Ndipo Mbuye wa munda wampesayo adati kwa mtumikiyo: Usazule nthambi zakuthengo za mitengo, kupatula imene ili yowawa koposa; ndipo m’menemo mudzalumikizanitsa monga ndanenera.

58 Ndipo tidzasamalanso mitengo ya m’munda wampesa, ndipo tidzadulilira nthambi zake; ndipo tidzazula m’mitengomo nthambizo zimene zapsa, zimene zikuyenera kuwonongeka, ndi kuponyedwa m’moto.

59 Ndipo ichi ndikuchita kuti, kapena, mizu yake ikhale yolimba chifukwa cha ubwino wawo; ndi chifukwa cha kusintha kwa nthambi, kuti zabwino zigonjetse zoipa.

60 Ndipo chifukwa choti ndateteza nthambi zachilengedwe ndi mizu yake, ndi kuti ndalumikizanitsanso mu nthambi zachilengedwe ku mtengo wawo; ndipo ndateteza mizu ya mtengo wawo, kuti, kapena mitengo ya m’munda wampesa ikabalenso chipatso chabwino; ndipo kuti ndikakhalenso ndi chisangalalo m’chipatso cha munda wanga wampesa, ndipo, mwinamwake, kuti ndisangalale mopambana kuti ndateteza mizu ndi nthambi za chipatso choyamba—

61 Kotero, pitani, ndipo itanani atumiki, kuti tikagwire ntchito modzipereka ndi mphamvu zathu m’munda wampesa, kuti tikakonze njira, kuti ndikabweretsenso chipatso chachibadwa, chimene chipatso chachibadwa chiri chabwino ndi cha mtengo wapatali kuposa chipatso china chirichonse.

62 Kotero, tiyeni ndi kukagwira ntchito ndi mphamvu zathu nthawi yotsiriza ino, pakuti taonani mapeto akuyandikira, ndipo ino ndi nthawi yotsiriza yomwe ine ndidzadulira munda wanga wampesa.

63 Lumikizanitsani mu nthambi; muyambe pa zotsiriza, kuti zikhale zoyamba, ndi kuti zoyamba zikhale zotsiriza; ndipo kumbani mbali mwa mitengo, yaikulu ndi yaing’ono, yoyamba ndi yotsiriza; ndi yotsiriza ndi yoyamba, kuti yonse akasamalidwenso kamodzinso nthawi yotsiriza.

64 Kotero, ikumbireni, iduleni, ndi kuithira ndowe kamodzinso, kwa nthawi yotsiriza, pakuti chimaliziro chikuyandikira. Ndipo ngati kudzakhala kotero kuti malumikizanidwe otsiriza awa adzakula, ndi kubala chipatso chachibadwa, ndiye inu mudzawakonzera iwo njira, kuti iwo akakule.

65 Ndipo pamene iyamba kukula mudzachotsa nthambi zobala zipatso zowawa, molingana ndi mphamvu ya yabwino ndi ukulu wake; ndipo simudzachotsa kuipa konseko nthawi imodzi, kuopa kuti mizu yake ingakhale yolimba kwambiri ku kulumikizanitsa, ndi kulumikizanitsa kwake kudzawonongeka, ndipo ndidzataya mitengo ya munda wanga wampesa.

66 Pakuti zimandimvetsa chisoni kuti nditaye mitengo ya m’munda wanga wampesa; kotero muchotse yoipayo monga momwe yabwino idzakulira; kuti muzu ndi pamwamba zikhale zofanana mu mphamvu; kufikira zabwino chidzagonjetsa zoipa, ndi zoipa zidzadulidwa, ndi kuponyedwa pamoto; kuti zisadetse nthaka ya munda wanga wampesa; ndipo motero ndidzachotsa zoipa m’munda wanga wampesa.

67 Ndipo nthambi za mtengo wachibadwidwe ndidzazilumikizanitsanso mu mtengo wachibadwidwe;

68 Ndipo nthambi za mtengo wachibadwidwe ndidzazilumikizanitsa mu nthambi zachilengedwe za mtengowo; ndipo motero ndidzazibweretsa izo pamodzi kachiwiri, kuti zidzabale chipatso chachibadwa, ndipo zidzakhala zimodzi.

69 Ndipo zoipa zidzatayidwa, inde, ngakhale m’malo onse a munda wanga wampesa; pakuti taonani, kamodzi kokhaka ndidzadulira munda wanga wampesa.

70 Ndipo zidachitika kuti Ambuye wa munda wampesa adatuma mtumiki wake; ndipo mtumikiyo adapita ndikuchita monga Ambuye adamuuzira; ndikukabwera nawo atumiki ena; ndipo iwo adali ochepa.

71 Ndipo Ambuye a munda wampesawo adati kwa iwo, Pitani, kagwireni ntchito m’munda wampesa ndi mphamvu zanu. Pakuti, taonani, ino ndi nthawi yotsiriza imene ndidzasamala munda wanga wampesa; pakuti chimaliziro chiri pafupi, ndi nyengo ikudza msanga; ndipo ngati mugwira ntchito ndi mphamvu yanu pamodzi ndi ine mudzasangalala ndi zipatso zimene ndidzadzisungira ndekha motsutsana ndi nthawi yomwe ikubwera posachedwa.

72 Ndipo zidachitika kuti atumiki adamuka ndikukagwira ntchito ndi mphamvu zawo; ndipo Ambuye wa munda wampesawo adagwira nawo ntchito; ndipo iwo adamvera malamulo a Ambuye wa munda wampesa mu zinthu zonse.

73 Ndipo apo padayamba kukhala chipatso chachibadwa kachiwiri m’munda wampesa; ndipo nthambi zachilengedwe zidayamba kukula ndi kuchita bwino kwambiri; ndipo nthambi zakuthengo zidayamba kuzulidwa ndi kutaidwa; ndipo adasunga muzu ndi pamwamba pake mofanana, molingana ndi mphamvu yake.

74 Ndipo kotero iwo adagwira ntchito, ndi khama lonse, monga mwa malamulo a Ambuye a munda wampesa, ngakhale mpakana yoipawo itataidwa kunja kwa munda wampesa; ndipo Ambuye adatetezera kwa iyemwini kuti mitengoyo idakhalanso chipatso chachibadwa; ndipo idakhala ngati thupi limodzi; ndipo zipatso zidali zofanana; ndipo Ambuye a munda wampesa adadzisungira kwa iye yekha chipatso chachibadwa, chimene chidali cha mtengo wapatali kwa iye kuyambira pa chiyambi.

75 Ndipo zidachitika kuti pamene Ambuye a munda wampesa adaona kuti zipatso zake zidali zabwino, ndi kuti munda wake wampesa si wovundanso; adaitana atumiki ake, ndipo adati kwa iwo: Taonani, kwa nthawi yotsiriza iyi ife tasamala munda wanga wampesa; ndipo mwaona kuti ndachita monga mwa kufuna kwanga; ndipo ndateteza chipatso chachibadwa, kuti chil chabwino, monga chidali pachiyambi. Ndipo wodala ndi ine; pakuti mwakhala wodzipereka mu kugwilira ntchito limodzi ndi ine m’munda wampesa wanga, ndipo mwasunga malamulo anga, ndipo mwabweretsanso kwa ine chipatso chachibadwa, kuti munda wanga wampesa sudzavundanso, ndipo yoipawo yataidwa, taonani mudzakhala ndi chisangalalo ndi ine chifukwa cha zipatso za m’munda wanga wampesa.

76 Pakuti, taonani, kwa nthawi yaitali ndidzadzisungira zipatso za m’munda wanga wampesa kwa ine ndekha motsutsana ndi nyengo; imene irinkudza msanga; ndipo ndidasamala munda wanga wampesa kotsiriza; ndikuwudulilira, ndikuwukumbira mouzungulira, nauthilira ndowe; kotero ndidzadzisungira ndekha zipatso, kwa nthawi yaitali, molingana ndi zomwe ndayankhula.

77 Ndipo ikafika nthawi kuti zipatso zoipa zidzabweranso m’munda wanga wampesa, pamenepo ndidzasonkhanitsa zabwino ndi zoipa; ndipo zabwino ndidzadzisungira ndekha, ndipo zoipa ndidzadzitaya m’malo mwake. Kenako ikudza nyengo ndi mapeto; ndipo munda wanga wampesa ndidzautentha ndi moto.

Print