Malembo Oyera
Yakobo 1


Buku la Yakobo
m’bale wa Nefi

Mawu a ulaliki wake kwa abale ake. Iye asokoneza munthu amene akufuna kuwononga chiphunzitso cha Khristu. Mawu ochepa okhudza mbiri yakale ya anthu a Nefi.

Mutu 1

Yakobo ndi Yosefe afuna kukopa anthu kuti akhulupilire Khristu ndi kusunga malamulo Ake—Nefi amwalira—Kuipa kupambana pakati pa Anefi. Mdzaka dza pafupifupi 544–421 Yesu asadabadwe.

1 Pakuti, taonani, zidachitika kuti zaka makumi asanu ndi zisanu zidali zitapita kuchokera pamene Lehi adachoka ku Yerusalemu; kotero, Nefi adandipatsa ine, Yakobo, lamulo lokhudza mapale aang’ono, pamene zinthu izi zalembedwapo.

2 Ndipo iye adandipatsa ine, Yakobo, lamulo lakuti ndilembe pa mapale awa zinthu zingapo zimene ndidaziona kukhala zamtengo wapatali; kuti sindikuyenera kugwira, pokhapokha kuti zidali zopepuka, za mbiri ya anthu awa omwe amatchedwa anthu a Nefi.

3 Pakuti adanena kuti mbiri ya anthu ake ikuyenera kulembedwa pa mapale ake ena, ndipo kuti nditeteze mapalewa ndi kuwapereka kwa mbewu yanga, kuchokera ku m’badwo kupita ku m’badwo.

4 Ndipo ngati padali ulaliki umene udali wopatulika, kapena vumbulutso limene lidali lalikulu, kapena kulosera, kuti ine ndizokote mitu yake pa mapale awa, ndi kuwakhudza monga momwe ndingathere, chifukwa cha Khristu, ndi chifukwa cha anthu athu.

5 Pakuti chifukwa cha chikhulupiliro ndi nkhawa yaikulu, izo ndithudi zidali zitaonetseredwa kwa ife zokhuda anthu athu, zinthu zimene zikuyenera kuchitika kwa iwo.

6 Ndipo ifenso tidali nawo mavumbulutso ambiri, ndi mzimu wa kunenera kwambiri; kotero, tidadziwa za Khristu ndi ufumu wake, womwe ukuyenera kudza.

7 Kotero tidagwira ntchito modzipereka pakati pa anthu athu; kuti tiwakope kuti abwere kwa Khristu, ndi kugawana nawo za ubwino wa Mulungu, kuti akalowe mumpumulo wake, kuti kapena mu njira iliyonse angalumbire kuti asalowemo mu mkwiyo wake; monga m’kuputa m’masiku a mayesero pamene ana a Israeli adali muchipululu.

8 Kotero, tikufuna kwa Mulungu kuti tikope anthu onse kuti asapandukire Mulungu, kumukwiyitsa; koma kuti anthu onse akhulupilire mwa Khristu, ndi kuona imfa yake, ndi kuvutikira mtanda wake ndi kunyamula manyazi a dziko; kotero, ine, Yakobo, ndadzitengela pa ine kuti ndikwaniritse lamulo la m’bale wanga Nefi.

9 Tsopano Nefi adayamba kukalamba, ndipo adaona kuti akuyenera kufa posachedwa; kotero, iye adadzoza munthu kukhala mfumu ndi olamulira pa anthu ake tsopano, molingana ndi kulamulira kwa mafumu.

10 Anthu pokhala omukonda Nefi kwambiri, iye pokhala wotetezera wamkulu kwa iwo, atagwira lupanga la Labani m’chitetezo chawo, ndipo atagwira ntchito m’masiku ake onse chifukwa cha ubwino wawo—

11 Kotero, anthu ankafunitsitsa kuti adzikumbukira dzina lake. Ndipo amene adayenera kulamulira m’malo mwake adatchedwa ndi anthu, Nefi wachiwiri, Nefi wachitatu, ndi mwina motero, malingana ndi maulamuliro a mafumu; ndipo motero iwo adatchedwa ndi anthu, asiyeni iwo akhale a dzina lirilonse limene iwo afuna.

12 Ndipo zidachitika kuti Nefi adafa.

13 Tsopano anthu amene sadali Alamani adali Anefi; kotero, iwo ankatchedwa Anefi, Ayakobe, Ayosefe, Azoramu, Alamani, Alemueli, ndi Aismayeli.

14 Koma ine, Yakobo, kuyambila pano sindidzawasiyanitsa iwo ndi maina awa, koma ndidzawatcha iwo Alamani amene amafuna kuwononga anthu a Nefi, ndipo iwo amene ali aubwenzi kwa Nefi ndidzawatcha Anefi, kapena anthu a Nefi, monga mwa maulamuliro a mafumu.

15 Ndipo tsopano zidachitika kuti anthu a Nefi, pansi pa ulamuliro wa mfumu yachiwiri, adayamba kuuma m’mitima mwawo, ndipo amadziloŵetsa m’machitidwe oipa, monga ngati Davide wakale kumakhumba akazi ambiri ndi adzakazi, ndiponso Solomoni mwana wake.

16 Inde, ndipo iwonso adayamba kufunafuna golidi ndi siliva wochuluka, ndipo adayamba kudzikweza penapake m’kunyada.

17 Kotero ine, Yakobo, ndidapereka kwa iwo mawu awa pamene ndinkawaphunzitsa iwo m’kachisi, nditalandira choyamba mawu anga kuchokera kwa Ambuye.

18 Pakuti ine, Yakobo, ndi m’bale wanga Yosefe tidapatulidwa kukhala ansembe ndi aphunzitsi a anthu awa, ndi dzanja la Nefi.

19 Ndipo tidakulitsa udindo wathu kwa Ambuye, kutenga pa ife udindo, kuyankha machimo a anthu pa mitu yathu ngati sitidawaphunzitse mawu a Mulungu ndi khama lonse; kotero, pogwira ntchito ndi mphamvu zathu mwazi wawo sungabwere pa zovala zathu; kukapanda kutero, mwazi wawo ukadabwera pa zovala zathu, ndipo sitikadapezeka opanda banga patsiku lomaliza.