Malembo Oyera
Yakobo 4


Mutu 4

Aneneri onse ankalambira Atate m’dzina la Khristu—Kupereka kwa Abrahamu kwa Isaki kunali m’chifaniziro cha Mulungu ndi Wobadwa Wake Yekha—Anthu ayenera kudziyanjanitsa iwo okha kwa Mulungu kudzera mwa Chitetezero—Ayuda adzakana mwala wa maziko. Mdzaka dza pafupifupi 544–421 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano taonani, zidachitika kuti ine, Yakobo, nditatumikira mochuluka kwa anthu anga m’mawu, (ndipo sindingathe kulemba koma mawu anga ochepa chabe, chifukwa cha kuvuta kwa kuzokota mawu athu pa mapale) ndipo tikudziwa kuti zinthu zimene timalemba pa mapale zikuyenera kukhala;

2 Koma zimene timalemba pa chirichonse kupatula pa mapale zikuyenera kuwonongeka ndikuzimilirika; koma tikhoza kulemba mawu ochepa pa mapale, zimene zidzapatsa ana athu, ndiponso abale athu okondedwa, chidziwitso chochepa chokhudza ife, kapena zokhudza makolo awo—

3 Tsopano mu chinthu ichi timakondwera; ndipo tikugwira ntchito modzipereka kuzokota mawu awa pa mapale, kuyembekezera kuti abale athu okondedwa ndi ana athu adzawalandira iwo ndi mitima ya chiyamiko, ndi kuyang’ana pa iwo kuti iwo angathe kuphunzira ndi chisangalalo osati ndi chisoni, kapena monyoza, zokhudzana ndi makolo awo oyamba.

4 Pakuti pa chifukwa ichi talemba zinthu izi; kuti adziwe kuti tidadziwa za Khristu, ndipo tidali ndi chiyembekezo cha ulemelero wake dzaka mazana ambiri asadabwere; ndipo si ife tokha amene tidali ndi chiyembekezo cha ulemelero wake, komanso aneneri oyera onse amene adakhalapo ife tisadakhaleko.

5 Taonani, adakhulupilira mwa Khristu ndi kulambira Atate m’dzina lake, ndipo ifenso timalambira Atate m’dzina lake. Ndipo chifukwa cha ichi timasunga chilamulo cha Mose, chomwe chimalozera miyoyo yathu kwa iye; ndipo pa chifukwa ichi chayeretsedwa kwa ife mu chilungamo, inde monga chidawerengedwa kwa Abrahamu m’chipululu kukhala womvera malamulo a Mulungu mukupereka nsembe mwana wake Isaki, chimene chiri chifaniziro cha Mulungu ndi Mwana wake Wobadwa Yekha.

6 Kotero, timafufuza aneneri, ndipo tiri ndi mavumbulutso ambiri ndi mzimu wa uneneri; ndipo pokhala ndi mboni zonsezi timapeza chiyembekezo, ndipo chikhulupiliro chathu chimakhala chosagwedezeka, kotero kuti tingathedi kulamulira mu dzina la Yesu ndi mitengo yomwe imatimvera ife, kapena mapiri, kapena mafunde a nyanja.

7 Komabe, Ambuye Mulungu amationetsa ife kufooka kwathu kuti tidziwe kuti ndi mwa chisomo chake, ndi kudzichepetsa kwake kwakukulu kwa ana a anthu, kuti tiri ndi mphamvu yakuchita zinthu izi.

8 Taonani, zazikulu ndi zodabwitsa ndi ntchito za Ambuye. Ndi kosasanthulika bwanji, ndi kuya kwa zinsinsi za iye; ndipo nzosatheka kuti munthu adziwe njira zake zonse. Ndipo palibe munthu akudziwa za njira zake pokhapokha ziululidwe kwa iye; kotero, abale, musapeputse mavumbulutso a Mulungu.

9 Pakuti, taonani, ndi mphamvu ya mawu ake munthu adadza pa nkhope ya dziko lapansi, dziko lapansi limene lidalengedwa ndi mphamvu ya mawu ake. Kotero, ngati Mulungu ali wotha kuyankhula ndipo dziko lidakhalapo, ndi kuyankhula ndipo munthu adalengedwa, nanga bwanji asathe kulamulira dziko lapansi, kapena zopangidwa za manja ake pamaso pake, molingana ndi chifuniro chake ndi chisangalaro chake?

10 Kotero, abale, musafune kulangiza Ambuye, koma kutenga uphungu kuchokera m’manja mwake. Pakuti, taonani, mukudziwa inu nokha kuti amapereka malangizo mwa nzeru, ndi mwa chilungamo, ndi mwa chifundo chachikuru, pa ntchito zake zonse.

11 Kotero, abale okondedwa, yanjanitsidwani naye kudzera mwa chitetezero cha Khristu; Mwana Wake Wobadwa Yekha, ndipo mudzalandira chiukitso; monga mwa mphamvu ya chiukitso imene ili mwa Khristu; ndi kuperekedwa kwa Mulungu ngati zipatso zoyamba za Khristu; kukhala ndi chikhulupiliro, ndipo adalandira chiyembekezo chabwino cha ulemelero mwa iye asadadzionetsere yekha kuthupi.

12 Ndipo tsopano, okondedwa, musadabwe kuti ndikunena kwa inu zinthu izi; pakuti chifukwa chani osayankhula za chitetezero cha Khristu, ndi kupeza chidziwitso chonse cha iye, kuti tipeze chidziwitso cha chiukitso ndi dziko lirinkudza?

13 Taonani, abale anga, iye wakulosera, alosere munkuzindikira kwa anthu; pakuti Mzimu umayankhula choonadi, ndipo sumanama. Kotero, umayankhula za zinthu momwe ziliri, ndi zinthu momwe zidzakhalire; kotero, zinthu izi zaonetseledwa kwa ife poyera, kwa chipulumutso cha miyoyo yathu. Koma taonani, ife sitiri mboni tokha mu zinthu izi; pakuti Mulungu adayankhulanso izo kwa aneneri akale.

14 Koma taonani, Ayuda adali anthu osamva; ndipo iwo adanyoza mawu omveka, ndikupha aneneri, ndikufunafuna zinthu zimene sakadatha kuzimvetsa. Kotero, chifukwa cha kusaona kwawo, kusaona komwe kudabwera poyang’ana mopitilira chizindikirocho, akuyenera kugwa; pakuti Mulungu wachotsa kumveka kwake kwa iwo; napereka kwa iwo zinthu zambiri zimene sakadazimvetsa; chifukwa iwo adakhumba izo. Ndipo popeza adazikhumba, Mulungu adazichita, kuti apunthwe.

15 Ndipo tsopano ine, Yakobo, ndatsogozedwa ndi Mzimu ku kulosera; pakuti ndipenya mwa ntchito za Mzimu uli mwa ine, kuti mwa kupunthwa kwa Ayuda adzakana nthathwe limene angathe kumangapo ndi kukhala ndi maziko okhazikika.

16 Koma taonani, molingana ndi malembo, mwala uwu udzakhala waukulu, ndi wotsiriza, ndi maziko okhawo okhazikika, pamene Ayuda akhoza kumanga.

17 Ndipo tsopano, okondedwa anga, zingatheke bwanji kuti awa, atakana maziko okhazikika, akhoza kumangapo, kuti ukhale mutu wa ngodya yawo?

18 Taonani, abale anga okondedwa, ndidzaululira chinsinsi ichi kwa inu; ngati, mwanjira iliyonse, sindidzagwedezeka konse, kuchoka mukukhazikika kwanga mu Mzimu, ndi kupunthwa chifukwa cha nkhawa yanga ya chifukwa cha inu.

Print