Malembo Oyera
Yakobo 3


Mutu 3

Oyera mu mtima alandira mawu osangalatsa a Mulungu—Kulungama kwa Alamani kuposa kwa Anefi—Yakobo achenjeza motsutsana ndi dama, kutayilira, ndi uchimo uliwonse. Mdzaka dza pafupifupi 544–421 Yesu asadabadwe.

1 Koma taonani, ine, Yakobo, ndiyankhula kwa inu amene muli oyera mtima. Yang’anani kwa Mulungu ndi kukhazikika kwa maganizo, ndipo pempherani kwa iye ndi chikhulupiliro chopambana, ndipo iye adzakutonthozani inu m’masautso anu, ndipo iye adzakuikirani kumbuyo pa mlandu wanu, ndi kutsitsa chilungamo pa amene akufuna chiwonongeko chanu.

2 O nonse amene muli oyera mu mtima, kwezani mitu yanu ndi kulandira mawu okondweretsa a Mulungu, ndipo mudye pa chikondi chake; pakuti mukhoza kutero, ngati maganizo anu ali okhazikika, kwamuyaya.

3 Koma, tsoka, tsoka, kwa inu amene simuli oyera mtima, amene muli odetsedwa lero pamaso pa Mulungu; pakuti kupatula kuti mulape dzikolo litembeleredwa chifukwa cha inu; ndi Alamani, amene sali onyansa ngati inu, komabe iwo ali otembeleredwa ndi thembelero lowawa, adzakwapula inu ngakhale mpaka ku chiwonongeko.

4 Ndipo nthawi ikubwera mwachangu, kuti pokhapokha mulape iwo adzalandira dziko la cholowa chanu; ndipo Ambuye Mulungu adzachotsa olungama pakati panu.

5 Tawonani, abale anu Alamani, amene mumawada chifukwa cha chidetso chawo, ndi thembelero limene lidagwera pakhungu lawo, ali olungama koposa inu; pakuti sadaiwale lamulo la Ambuye; limene lidaperekedwa kwa atate athu—kuti akhale ndi mkazi mmodzi, ndi akazi ena asakhale nawo, ndi kuti pasakhale zachiwerewere pakati pawo.

6 Ndipo tsopano, lamulo ili amatsatira kusunga; kotero, chifukwa cha kusunga uku, mu kusunga lamulo ili, Ambuye Mulungu sadzawaononga iwo, koma adzakhala wachifundo kwa iwo; ndipo tsiku lina adzakhala anthu odalitsika.

7 Taonani, amuna awo amakonda akazi awo, ndipo akazi awo amakonda amuna awo; ndipo amuna awo ndi akazi awo amakonda ana awo; Ndipo Kusakhulupilira kwawo ndi udani wawo pa inu uli chifukwa cha kusaweruzika kwa makolo awo; kotero, inu muposa iwo bwanji, pamaso pa Namalenga wanu wamkulu?

8 Abale anga, ine ndikuopa kuti pokhapokha mutalapa machimo anu, kuti khungu lawo lidzakhala loyera kuposa lanu, pamene mudzabweretsedwa pamodzi nawo kumpando wachifumu wa Mulungu.

9 Chifukwa chake, lamulo ine ndikupereka kwa inu, limene liri mawu a Mulungu, kuti inu musanyozenso motsutsana ndi iwo chifukwa cha kuda kwa khungu lawo; ndipo musawanyozenso chifukwa cha chidetso chawo; koma mudzakumbukira chidetso chanu, ndi kukumbukira kuti chidetso chawo chidabwera chifukwa cha makolo awo.

10 Kotero, mudzikumbukira ana anu, kuti mudamvetsa chisoni mitima yawo chifukwa cha chitsanzo mudawaikira; komanso, kumbukirani kuti mutha, chifukwa cha chidetso chanu, chibweretsa ana anu ku chiwonongeko, ndipo machimo awo adzawunjikidwa pa mitu yanu patsiku lomaliza.

11 O abale anga, mvetserani mawu anga; dzutsani mphamvu za moyo wanu; dzigwedezeni nokha kuti mudzuke ku tulo ta imfa; ndipo dzimasureni inu eni ku zowawa za gahena kuti musakhale angelo kwa mdyerekezi, kuti mudzaponyedwe m’nyanja ya moto ndi sulufure yomwe ili imfa yachiwiri.

12 Ndipo tsopano ine, Yakobo, ndidayankhula zinthu zina zambiri kwa anthu a Nefi, kuwachenjeza motsutsana ndi za dama ndi zotayilira; ndi tchimo la mtundu uliwonse, kuwauza zotsatira zoipa za izo.

13 Ndipo gawo zana la zochitika za anthu awa, zimene tsopano zidayamba kukhala zochuluka, sizingalembedwe pa mapale awa; koma zambiri za zochitika zawo zidalembedwa pa mapale akuluakulu, ndi nkhondo zawo, ndi mikangano yawo, ndi maulamuliro a mafumu awo.

14 Mapale amenewa akutchedwa mapale a Yakobo, ndipo adapangidwa ndi dzanja la Nefi. Ndipo ndikumaliza kuyankhula mawu awa.