Nefi aona m’masomphenya mpingo wa mdyerekezi utayikidwa pakati pa Amitundu, Kutulukira ndi kulamulira dziko la Amerika, kutayika kwa zigawo zomveka komanso zamtengo wapatali za mu Baibulo, zotsatila zake za mpatuko wa amitundu, kubwenzeretsedwa kwa uthenga wabwino, Kubwera kwa malembo oyera a masiku otsiriza, ndi kumangidwa kwa Ziyoni. Mdzaka dza pafupifupi 600–592 Yesu asadabadwe.