Koriho, wotsutsa Khristu, anyoza Khristu, chitetezero, ndi mzimu wa uneneri—Iye aphunzitsa kuti kulibe Mulungu, kulibe kugwa kwa munthu, kulibe chilango cha tchimo, ndipo kulibe Khristu—Alima achitira umboni kuti Khristu adzabwera ndipo zinthu zonse zimasonyeza kuti kuli Mulungu—Koriho apempha chizindikiro ndipo akanthidwa ndikukhala wosayankhula—Mdyerekezi adaonekera kwa Koriho monga mngelo ndipo adam’phunzitsa zoti anene—Koriho apondedwa pansi ndipo amwalira. Mdzaka dza pafupifupi 76–74 Yesu asadabadwe.