Malembo Oyera
Yakobo 6


Mutu 6

Ambuye adzapulumutsa Israeli m’masiku omaliza—Dziko lidzatenthedwa ndi moto—Anthu akuyenera kutsatira Khristu kuti apewe nyanja ya moto ndi sulufure. Mdzaka dza pafupifupi 544–421 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, taonani, abale anga, monga ndidanena kwa inu kuti ndidzamemera, taonani, uwu uli uneneri wanga—kuti zinthu zimene mneneri Zenosi adayankhula, zokhudzana ndi nyumba ya Israeli, m’mene iye adawafanizira iwo ndi mtengo wa azitona oweta, zikuyenera kuchitikadi.

2 Ndipo tsiku limene adzabwenzeretsanso dzanja lake kachiŵiri kupulumutsa anthu ake; ndi tsiku, inde, ngakhale nthawi yotsiriza, kuti atumiki a Ambuye adzapita mu mphamvu yake; kusamala ndi kudulira munda wake wampesa; ndipo zikadzatha izi chimaliziro chidza msanga.

3 Ndipo odala ali iwo amene agwira ntchito mwakhama m’munda wake wampesa; ndipo ndiotembeleredwa motani nanga amene adzataidwa kumalo awo! Ndipo dziko lapansi lidzatenthedwa ndi moto.

4 Ndipo Mulungu wathu ndi wachifundo chotani kwa ife, pakuti amakumbukira nyumba ya Israeli, mizu ndi nthambi zomwe; ndipo amatambasulira manja ake kwa iwo tsiku lonse; Ndipo iwo ndi anthu osamva ndi otsutsa; koma ochuluka amene sadzaumitsa mitima yawo adzapulumutsidwa mu ufumu wa Mulungu.

5 Kotero, abale anga okondedwa, ndikukupemphani m’mawu a kutsimikiza kuti mulape, ndi kubwera ndi cholinga chonse cha mtima, ndi kumamatira kwa Mulungu monga amamatilira kwa inu. Ndipo pamene mkono wachifundo chake watambasulidwa kwa inu m’kuwala kwa usana, musaumitse mitima yanu.

6 Inde, lero, ngati mumva mawu ake, musaumitse mitima yanu; pakuti mudzaferanji?

7 Pakuti, taonani, mutadyetsedwa ndi mawu abwino a Mulungu tsiku lonse, kodi mudzabala zipatso zoipa, kuti mukuyenera kudulidwa ndi kuponyedwa pamoto?

8 Taonani, kodi inu mukukana mawu awa? Kodi mudzakana mawu a aneneri; ndipo kodi mudzakana mawu onse amene adayankhulidwa zokhudzana ndi Khristu; ochuluka atayankhula zokhudza iye; ndi kukana mawu abwino a Khristu, ndi mphamvu ya Mulungu, ndi mphatso ya Mzimu Woyera, ndi kuzimitsa Mzimu Woyera, ndi kunyoza dongosolo lalikulu la chiwombolo, limene laikidwa kwa inu?

9 Simukudziwa kodi kuti ngati muchita zinthu izi, kuti mphamvu ya chiwombolo ndi chiukitsiro, yomwe iri mwa Khristu, idzakubweretsani inu kuti muyime ndi manyazi ndi kulakwa kwakukulu pamaso pa bwalo la Mulungu?

10 Ndipo malingana ndi mphamvu ya chilungamo, pakuti chilungamo sichingakanidwe; mukuyenera kupita m’nyanja ya moto ndi sulufure, imene malawi ake sazimitsidwa, ndipo utsi wake umakukwera m’mwamba kwa muyaya ndi muyaya, nyanja ya moto ndi sulufule imene iri kuzunzika kosatha.

11 O ndiye, abale anga okondedwa, lapani inu, ndipo lowani pa chipata chopapatiza, ndipo pitirizani m’njira yolunjika, kufikira mutalandira moyo wamuyaya.

12 Inu khalani anzeru; ndinenenso chiyani ine?

13 Pomaliza, ndikukutsanzikani, mpaka ndidzakumana nanu pamaso pa bwalo lokondweretsa la Mulungu, bwalo limene limakantha oipa ndi mantha owopsa. Ameni.

Print