Malembo Oyera
Helamani 14


Mutu 14

Samueli alosera kuwala usiku ndi nyenyezi yatsopano pa kubadwa kwa Khristu—Khristu awombola anthu ku imfa ya kuthupi ndi yakuuzimu—Zizindikiro za imfa Yake ziphatikizapo masiku atatu a mdima, kung’ambika kwa mathanthwe, ndi kugwedezeka kwakukulu kwa chilengedwe. Mdzaka dza pafupifupi 6 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti Samueli, wa Chilamani, adanenera zinthu zina zambiri zomwe sizingalembedwe.

2 Ndipo taonani, iye adati kwa iwo, Taonani, ndikukupatsani inu chizindikiro; pakuti dzaka zina zisanu zikudza, ndipo taonani, Mwana wa Mulungu adzabwera kudzawombola onse amene adzakhulupilira dzina lake.

3 Ndipo taonani, ichi ndidzakupatsani inu ngati chizindikiro pa nthawi ya kubwera kwake; pakuti taonani, kudzakhala kuwala kwakukulu m’mwamba kotero kuti mu usiku asadadze iye sikudzakhala mdima, kotero kuti kudzaonekera kwa munthu ngati usana.

4 Kotero, padzakhala tsiku limodzi ndi usiku ndi usana, ngati kuti lidali tsiku limodzi ndipo padalibe usiku; ndipo ichi chidzakhala kwa inu chizindikiro; pakuti mudzadziwa za kutuluka kwa dzuwa, ndi kulowa kwake; kotero adzadziwa ndithu kuti padzakhala masiku awiri ndi usiku; komabe usikuwo sudzadetsedwa; ndipo udzakhala usiku iye asadabadwe.

5 Ndipo taonani, idzadzuka nyenyezi yatsopano, imene simudayionepo; ndipo ichinso chidzakhala chizindikiro kwa inu.

6 Ndipo taonani izi sizokhazi, kudzakhala zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri kumwamba.

7 Ndipo zidzachitika kuti inu nonse mudzazizwa, ndi kudabwa, kotero kuti mudzagwa pansi.

8 Ndipo zidzachitika kuti aliyense amene adzakhulupilira pa Mwana wa Mulungu, yemweyo adzakhala nawo moyo wosatha.

9 Ndipo taonani, motero Ambuye adandilamulira ine, mwa mngelo wake, kuti ndibwere kudzakuuzani chinthu ichi; inde, walamula kuti ndinenere zinthu izi kwa inu; inde, wanena kwa ine: Lilira kwa anthu awa, lapani ndi kukonza njira ya Ambuye.

10 Ndipo tsopano, chifukwa ndine wa Chilamani, ndipo ndayankhula ndi inu mawu amene Ambuye adandilamula ine; ndipo chifukwa zidali zovuta motsutsa inu, mwandikwiyira, ndipo mukufuna kundiwononga, ndipo mwandichotsa pakati panu.

11 Ndipo mudzamva mawu anga; pakuti, chifukwa cha ichi ndakwera pa makoma a mzinda uwu, kuti mumve ndi kudziwa za ziweruzo za Mulungu zimene zikudikira inu chifukwa cha mphulupulu zanu, ndiponso kuti mudziwe zikhalidwe za kulapa;

12 Ndiponso kuti mudziwe za kudza kwa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, Atate wa kumwamba ndi dziko lapansi, Mlengi wa zinthu zonse kuyambira pachiyambi; ndipo kuti mudziwe za zizindikiro za kudza kwake, ndicholinga chakuti mukathe kukhulupilira dzina lake.

13 Ndipo ngati mukhulupilira dzina lake mudzalapa ku machimo anu onse, kuti mwa kutero mukathe kukhala ndi chikhululukiro cha iwo kudzera mu ubwino wake.

14 Ndipo taonani, kachiwiri, chizindikiro china ine ndikupatsani kwa inu, inde, chizindikiro cha imfa yake.

15 Pakuti taonani, iye akuyenera kufa ndithu kuti chipulumutso chibwere; inde, zikuyenera iye ndipo zakhala zofunikira kuti afe, kuti achititse chiukitso cha akufa, kuti mwa ichi anthu akabweretsedwe pamaso pa Ambuye.

16 Inde, taonani, imfa iyi ichititsa chiukitso, ndi kuwombola anthu onse kuchokera ku imfa yoyamba—imfa yauzimuyo; kwa anthu onse, mwa kugwa kwa Adamu atadulidwa kuchoka pamaso pa Ambuye, amayesedwa ngati akufa, pa zinthu zakuthupi ndi zakuuzimu.

17 Koma taonani, chiukitso cha Khristu chimawombola mtundu wa anthu, inde, ngakhale mtundu wonse wa anthu, ndipo chimawabweretsanso pamaso pa Ambuye.

18 Inde, ndipo chimachititsa chikhalidwe cha kulapa, kuti aliyense walapa yemweyo sadulidwa ndi kuponyedwa kumoto; koma aliyense amene salapa adzadulidwa ndi kuponyedwa kumoto; ndipo pamenepo pakudzanso pa iwo imfa yauzimu, inde, imfa yachiwiri, pakuti iwo adulidwa kachiwiri mokhudzana ndi zinthu za chilungamo.

19 Kotero lapani inu, lapani inu, kuopa kuti podziwa zinthu izi ndi kusazichita izo inu mudzadzilora nokha kuti mubwere pansi pa kuweruzidwa, ndipo inu mukubweretsedwa pansi ku imfa iyi yachiwiri.

20 Koma taonani, monga ndidanena kwa inu zokhudza chizindikiro china, chizindikiro cha imfa yake; taonani, m’tsiku limenelo limene adzavutika imfa, dzuwa lidzadetsedwa ndi kukana kupereka kuwala kwake kwa inu; komanso mwezi ndi nyenyezi; ndipo sipadzakhala kuwala pa nkhope ya dziko ili, ngakhale kuyambira nthawi imene iye adzalora kufa, kwa nthawi ya masiku atatu, mpaka nthawi imene iye adzauka kwa akufa.

21 Inde, pa nthawi imene iye adzapereka mzimu padzakhala mabingu ndi mphezi kwa nthawi ya maola ambiri, ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka ndi kunjenjemera; ndipo miyala yomwe ili pa nkhope ya dziko lapansi lino, yonse yomwe ili pamwamba pa dziko lapansi ndi pansi, yomwe mukuidziwa pa nthawi ino kuti ndi yolimba, kapena mbali yake yaikulu ndi imodzi yolimba, idzaphwanyidwa;

22 Inde, idzang’ambika pakati; ndipo idzidzapezeka m’misoko ndi m’ming’alu, ndi m’zidutswa pankhope pa dziko lonse lapansi; inde, ponse pamwamba pa dziko lapansi ndi pansi.

23 Ndipo taonani, kudzakhala namondwe wamkulu, ndipo padzakhala mapiri ambiri otsitsidwa, ngati chigwa, ndipo padzakhala malo ambiri amene tsopano amatchedwa zigwa amene adzakhala mapiri, amene kutalika kwake kuli kwakukulu.

24 Ndipo misewu yambiri ikuluikulu idzapasulidwa, ndipo mizinda yambiri idzakhala mabwinja.

25 Ndipo manda ambiri adzatsegulidwa; ndipo adzapereka ambiri a akufa awo; ndipo woyera mtima ambiri adzawonekera kwa ambiri.

26 Ndipo taonani, motere mngelo wayankhula ndi ine; pakuti adanena kwa ine kuti padzakhala mabingu ndi mphezi kwa nthawi ya maora ambiri.

27 Ndipo adanena kwa ine kuti pamene mabingu ndi mphezi zatha, ndi namondwe, kuti izi zikadzakhala, ndi kuti mdima udzaphimba nkhope ya dziko lonse lapansi kwa nthawi ya masiku atatu.

28 Ndipo mngelo adanena kwa ine kuti ambiri adzaona zinthu zazikulu kuposa izi, ndi cholinga chakuti akakhulupilire kuti zizindikiro izi ndi zodabwitsa izi zikuyenera kuchitika pa nkhope yonse ya dziko lino, ndi cholinga chakuti pasakakhale chifukwa cha kusakhulupilira pakati pa ana a anthu—

29 Ndipo ichi kucholinga chakuti aliyense amene wakhulupilira apulumutsidwe, ndi kuti amene sadzakhulupilira, chiweruzo cholungama chikafike pa iwo; ndiponso ngati atsutsidwa adzabweretsere pa iwo wokha kutsutsidwa kwawo.

30 Ndipo tsopano kumbukirani, kumbukirani, abale anga, kuti yense amene atayike, atayika kwa iye yekha; ndipo yense wakuchita mphulupulu, amadzichitira yekha; pakuti taonani, muli mfulu; inu muli woloredwa kudzichitira nokha; pakuti taonani, Mulungu wapereka kwa inu chidziwitso ndipo wakumasulani.

31 Iye wakupatsani inu kuti mukathe kudziwa zabwino ndi zoipa, ndipo wakupatsani inu kuti mukathe kusankha moyo kapena imfa; ndipo mutha kuchita chabwino ndi kubwenzeretsedwa kwa icho chimene chili chabwino, kapena kukhala nacho chimene chili chabwino kubwenzeretsedwa kwa inu; kapena mutha kuchita choipa, ndi kubwenzeretsedwa kwa icho chimene chili choipa.

Print