Malembo Oyera
Mosiya 2


Mutu 2

Mfumu Benjamini idayankhula ndi anthu ake—Iyo isimba za kusasiyanitsa, chilungamo, ndi uzimu wa kulamulira kwake—Iyo ilangiza iwo kutumikira Mfumu Yawo ya Kumwamba—Amene amawukira motsutsana ndi Mulungu adzazunzika ndi zowawa ngati moto osazimitsika. Mdzaka dza pafupifupi 124 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti Mosiya atachita monga atate ake adamulamulira, ndipo adalengeza m’dziko lonselo, kuti anthu asonkhane pamodzi m’dziko lonselo, kuti apite ku kachisi kuti akamve mawu amene mfumu Benjamini ikuyenera kukayankhula kwa iwo.

2 Ndipo padali chiwerengero chachikulu, ngakhale ambiri kuti sadawawerenge; pakuti adachulukana kwambiri, ndipo adakulirakulira m’dzikomo.

3 Ndipo adatenganso ana oyamba kubadwa a ziweto zawo kuti akapereke nsembe ndi zopereka zopsereza molingana ndi chilamulo cha Mose;

4 Komanso kuti akayamike Ambuye Mulungu wawo, amene adawatulutsa m’dziko la Yerusalemu, amene adawalanditsa m’manja mwa adani awo, ndipo adaika anthu olungama kuti akhale aphunzitsi awo, ndiponso munthu olungama kuti akhale mfumu yawo, amene adakhazikitsa mtendere m’dziko la Zarahemula, ndipo amene adawaphunzitsa kusunga malamulo a Mulungu, kuti athe kusangalala ndi kudzadzidwa ndi chikondi kwa Mulungu ndi anthu onse.

5 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adafika ku kachisi, iwo adamanga mahema awo mozungulira, aliyense molingana ndi banja lake, lopangidwa ndi mkazi wake, ndi ana ake aamuna, ndi ana ake aakazi, ndi ana awo aamuna, ndi ana awo aakazi, wamkulu mpaka wamng’ono, banja lirilonse kukhala mosiyana lina ndi linzake.

6 Ndipo adakhoma mahema awo mozungulira kachisi, munthu aliyense kukhala ndi chihema chake ndipo khomo lake litaloza ku kachisi, kuti mwa kutero iwo athe kukhala m’mahema awo ndi kumva mawu amene mfumu Benjamini idayenera kuyankhula kwa iwo;

7 Pakuti unyinjiwu pakukhala waukulu kwambiri kuti mfumu Benjamini sidathe kuwaphunzitsa iwo onse mkati mwa makoma a kachisi, choncho idapangintsa nsanja kuimitsidwa, kuti mwa kutero anthu ake akamve mawu amene iyo ikayamkhula kwa iwo.

8 Ndipo zidachitika kuti idayamba kuyankhula ndi anthu ake ali pansanja; ndipo sadathe onse kumva mawu ake chifukwa cha kuchuluka kwa khamu la anthu; kotero iyo idapangitsa kuti mawu amene iyo idayankhula adzilembedwa ndi kutumizidwa pakati pa iwo amene sadali pansi pa kumveka kwa mawu ake, kuti iwonso akalandire mawu ake.

9 Ndipo awa ndi mawu amene iyo idayankhula ndikuchititsa kuti alembedwe, kuti: Abale anga, inu nonse amene mwasonkhana mwanokha, inu amene mungathe kumva mawu anga amene ine nditayankhule kwa inu lero; pakuti sindidakulamulireni inu kuti mubwere kuno kuti mudzasewere ndi mawu amene ndidzayankhula, koma kuti mundimvere ine, ndi kutsegula makutu anu kuti mumve, ndi mitima yanu kuti mumvetsetse, ndi nzeru zanu kuti zinsinsi za Mulungu zithe kuululidwa kwa maonedwe anu.

10 Sindidakulamulireni kubwera kuno kuti mundiwope, kapena kuti muganiza kuti ine ndine woposa munthu wachivundi.

11 Koma ine ndili ngati inu, wogonjetsedwa ndi zofooka zonse za thupi ndi maganizo; koma ine ndasankhidwa ndi anthu awa, ndipo ndidapatulidwa ndi atate anga, ndipo ndidalolezedwa ndi dzanja la Ambuye kuti ndikhale wolamulira ndi mfumu pa anthu awa; ndipo ndasungidwa ndi kusamalidwa ndi mphamvu yake yosayerekezeka, kuti ndikutumikireni ndi mphamvu zonse, malingaliro ndi nyonga zimene Ambuye adapereka kwa ine.

12 Ndikunena kwa inu kuti monga ndaloledwa kukhala masiku anga mu utumiki wanu, ngakhale mpaka nthawi ino, ndipo sindidafune golide kapena siliva kapena mtundu uli wonse wa chuma cha inu;

13 Kapena sindidakulolereni kuti mutsekeledwe m’ndende, kapena kulolera kuti mupangane akapolo wina ndi mzake, kapena kupha, kapena kuwononga, kapena kuba, kapena kuchita chigololo; kapena ngakhale sindidalore kuti muchite mtundu uli wonse wa kuipa, ndipo ndakuphunzitsani kuti musunge malamulo a Ambuye, m’zinthu zonse zimene adakulamulirani—

14 Ndipo ngakhale ine, ine mwini, ndagwira ntchito ndi manja anga omwe kuti ndikutumikireni, ndi kuti musalemedwe ndi misonkho, ndi kuti pasakhale chinthu chirichonse chodzabwera pa inu chimene chidali chowawa kunyamulidwa—ndipo pa zinthu zonsezi zimene ndayankhula, inu nokha ndinu mboni lero.

15 Koma, abale anga, sindidachite izi kuti ndidzitamandire; kapena ndikukuuzani zinthu izi kotero kuti ine ndithe kukuimbani inu mulandu; koma ndikukuuzani zinthu izi kuti mudziwe kuti ndikhonza kuyankha ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu lero.

16 Taonani, ndinena kwa inu kuti chifukwa ndidati kwa inu kuti ndidathera masiku anga mu utumiki wanu, sindikufuna kudzitamandira, pakuti ndakhala ndili mu utumiki wa Mulungu wokha.

17 Ndipo taonani, ndikukuuzani zinthu izi kuti muphunzire nzeru; kuti muphunzire kuti pamene mukutumikira anthu anzanu muli kutumikiranso Mulungu wanu.

18 Taonani, mwanditcha Ine mfumu yanu; ndipo ngati ine, amene mumanditcha mfumu yanu, ndimagwira ntchito kukutumikirani, simukuyenera inunso kutumikirana wina ndi mzake?

19 Ndipo taonaninso, ngati ine, amene inu mumamutcha mfumu yanu, amene wathera masiku ake mu utumiki wanu, ndipo komabe wakhala mu utumiki wa Mulungu, ndikuyenera kuyamikidwa kulikonse kuchokera kwa inu, O momwe muyenelera kuthokoza Mfumu yanu yakumwamba!

20 Ndikunena kwa inu, abale anga, kuti ngati mupereka mathokozo ndi matamando onse omwe moyo wanu wonse uli ndi mphamvu zokhala nawo, kwa Mulungu amene adakulengani, ndipo wakusungani ndi kukusamalani, ndipo wapangitsa kuti mudzisangalala; ndipo wapereka kuti muzikhala mu mtendere wina ndi mzake—

21 Ndikunena kwa inu kuti ngati mukutumikira iye amene adakulengani kuyambira pa chiyambi, ndipo akukusungani tsiku ndi tsiku, pa kukubwerekani mpweya, kuti mukhale ndi moyo ndikuyenda ndi kuchita monga mwa kufuna kwanu, ngakhale kukuthandizani kuyambira ku mphindi imodzi kufikira ku imzake—ndikunena, ngati mumtumikira ndi moyo wanu wonse koma mudzakhalabe atumiki opanda phindu.

22 Ndipo taonani, zonse zimene amafuna kwa inu ndi kusunga malamulo ake; ndipo wakulonjezani kuti ngati mungasunge malamulo ake mudzapambana m’dziko; Ndipo sasintha zimene wanena; kotero, ngati inu mukasunga malamulo ake amakudalitsani ndi kukuchititsani bwino.

23 Ndipo tsopano, poyamba, iye adakulengani inu, ndipo adakupatsani inu moyo wanu, umene inu muli nawo mangawa kwa iye.

24 Ndipo kachiwiri, iye akufuna kuti inu muchite monga adakulamulirani inu; pakuti ngati mutero, adzakudalitsani pomwepo; ndipo kotero wakulipirani inu. Ndipo muli ndi mangawa kwa iye, ndipo muli, ndipo mudzakhala, kunthawi za nthawi; kotero, muli nacho chiyani chodzitamandilira?

25 Ndipo tsopano ndikufunsa, kodi munganene kanthu za inu nokha? Ndikuyankhani, Ayi. Simungathe kunena kuti muli olingana monga fumbi la dziko lapansi; koma inu mudalengedwa ndi fumbi lapansi; koma taonani, ndi la iye amene adakulengani.

26 Ndipo ine, ngakhale ine, amene inu munditcha mfumu yanu, sindili wabwino kuposa inu nokha mulili; pakuti inenso ndine wa ku fumbi. Ndipo taonani, ndakalamba, ndipo ndatsala pang’ono kupereka thupi lachivundi ili ku make dziko lapansi.

27 Kotero, monga ndidakuwuzani kuti ndakutumikirani, pakuyenda ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu, kotero kuti ine pa nthawi ino ndachititsa kuti inu musonkhane inu nokha pamodzi, kuti ine ndipezeke wopanda cholakwa, ndi kuti mwazi wanu usakhale pa ine, pamene ine ndidzaima kuti ndiweruzidwe ndi Mulungu pa zinthu zimene adandilamulira ine zokhudza inu.

28 Ndikunena kwa inu kuti ndachititsa kuti musonkhane inu nokha pamodzi kuti ndichotse mwazi wanu mu zovala zanga, pa nthawi iyi pamene ndatsala pang’ono kupita kumanda anga, kuti nditsikire mu mtendere, mzimu wanga osafa uthe kugwirizana ndi oimba akumwamba m’kuimba matamando a Mulungu wolungama.

29 Komanso, ndikunena kwa inu kuti ndapangitsa kuti musonkhane pamodzi nokha; kuti ine ndilengeze kwa inu kuti sindingathe kukhalanso mphunzitsi wanu, kapena mfumu yanu;

30 Pakuti ngakhale pa nthawi ino, thupi langa lonse likunjenjemera kwambiri poyesera kuyankhula ndi inu; koma Ambuye Mulungu akundithandizira, ndipo wandilora ine kuti ndiyankhule kwa inu, ndipo wandilamulira ine kuti ndinene kwa inu lero, kuti mwana wanga Mosiya ndi mfumu ndi wolamulira pa inu.

31 Ndipo tsopano, abale anga, ndikufuna kuti muchite monga mwachitira mpaka pano. Monga inu mwasungira malamulo anga, ndiponso malamulo a atate anga, ndipo mwachita bwino, ndipo mwasungidwa kuti musagwe m’manja mwa adani anu, ngakhale kotero ngati mudzasunga malamulo a mwana wanga wamwamuna, kapena malamulo a Mulungu amene adzaperekedwa kwa inu ndi iye, mudzachita bwino m’dziko, ndipo adani anu sadzakhala ndi mphamvu pa inu.

32 Koma, O anthu anga, chenjerani kuwopa kuti pangabuke mikangano pakati panu, ndipo inu mudzasankha kumvera mzimu woipa, umene udanenedwa ndi atate anga Mosiya.

33 Pakuti, taonani, pali tsoka lonenedwa pa iye amene asankha kumvera mzimu umenewo; pakuti ngati akufuna kumvera iye, nakhalabe ndi kufa m’machimo ake, yemweyo adzimwera nacho chiwonongeko cha moyo wake; pakuti alandira mphotho yake chilango chosatha, ataphwanya lamulo la Mulungu motsutsana ndi chidziwitso chake.

34 Ndikunena kwa inu, kuti palibe wina mwa inu; kupatula ngati ali ana anu aang’ono amene sadaphunzitsidwe zokhudzana ndi izi; koma mukudziwa kuti muli ndi mangawa osatha kwa Atate anu a kumwamba? kuwabwenzera zonse muli, ndi muli nazo; komanso mwaphunzitsidwa zokhudza zolembedwa zomwe zili ndi mauneneri omwe adayankhulidwa ndi aneneri oyera; ngakhale mpaka ku nthawi atate athu, Lehi, adachoka ku Yerusalemu;

35 Komanso, zonse zimene makolo athu adanena mpaka pano. Ndipo taonani, iwonso adayankhula chimene chidalamulidwa iwo ndi Ambuye; kotero, ali olungama ndi woona.

36 Ndipo tsopano, ndikunena kwa inu, abale anga, kuti mutadziwa ndi kuphunzitsidwa zinthu zonsezi, ngati mulakwira ndi kupita motsutsana ndi zimene zanenedwa, kuti inu mudzipatule nokha kwa Mzimu wa Ambuye; kuti usakhale ndi malo mwa inu okutsogolerani m’njira zanzeru kuti mudalitsidwe, kuchita bwino, ndi kusungidwa—

37 Ine ndikunena kwa inu, kuti munthu amene achita izi, yemweyo atulukira poyera pakupandukira Mulungu; kotero asankha kumvera mzimu woipa, ndikukhala m’dani wa chilungamo chonse; kotero, Ambuye alibe malo mwa iye, pakuti sakhala m’makachisi osayera.

38 Kotero ngati munthu ameneyo salapa, ndikukhalabe ndi kufa ngati m’dani wa Mulungu, zofuna za chilungamo chaumulungu zimadzutsa mzimu wake wosafa ku malingaliro amoyo a kulakwa kwake, komwe kumamupangitsa kuti achepe kuchoka pamaso pa Ambuye, nadzadzidwa pachifuwa chake ndi zolakwa, ndi zowawa, ndi kuzunzika, zomwe ziri ngati moto osazimitsika, umene lawi lake limakwera m’mwamba kwamuyaya.

39 Ndipo tsopano ndikunena kwa inu, kuti chifundo chilibe mphamvu yodzinenelera pa munthu ameneyo; kotero chilango chake chomaliza ndicho kupilira mazunzo osatha.

40 O, inu abambo achikulire nonse, ndiponso inu anyamata achichepere, ndi inu ana aang’ono amene mungathe kumvetsa mawu anga, pakuti ine ndayankhula momveka kwa inu kuti mumvetsetse, ine ndikupemphera kuti inu mudzuke ku kukumbukira za mkhalidwe woopsya wa iwo amene adagwa mukulakwitsa.

41 Komanso, ndidakakonda mukadaganizira za mkhalidwe wodalitsika ndi wokondwa wa iwo amene amasunga malamulo a Mulungu. Pakuti taonani, iwo amadalitsidwa muzinthu zonse, zonse zakuthupi ndi zauzimu; ndipo ngati iwo akhala okhulupirika kufikira chimaliziro iwo amalandiridwa m’mwamba, kuti mwa kutero akakhale ndi Mulungu mu mkhalidwe wa chimwemwe chosatha. O kumbukirani, kumbukirani kuti zinthu izi ndi zoona; pakuti Ambuye Mulungu wazinena.

Print