Malembo Oyera
3 Nefi 13


Mutu 13

Yesu aphunzitsa Anefi Pemphero la Ambuye—Iwo akuyenera kudzikundikira chuma kumwamba—Ophunzira khumi ndi awiri muutumiki wawo alamulidwa kusaganizira za zinthu zakuthupi—Fananitsani ndi Mateyu 6. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Indetu, indetu, ndinena kuti ndikufuna kuti muzichita zachifundo kwa osauka; koma samalani kuti musachite zachifundo zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; ngati mutero mulibe mphotho kwa Atate anu a Kumwamba.

2 Kotero pamene mukupereka zachifundo musawombe lipenga pamaso panu, monga amachitira onyenga m’masunagoge ndi m’misewu, kuti alemekezedwe ndi anthu. Indetu ndikunena kwa inu, iwo ali nayo mphotho yawo.

3 Koma pamene mukupereka zachifundo dzanja lako lamanzere lisadziwe chimene lichita dzanja lako lamanja;

4 Kuti mphatso zako zachifundo zikhale zamseri; ndipo Atate ako akuona mseri, adzakupatsa iwe mowonekera.

5 Ndipo pamene mukupemphera musamachite monga onyengawo, pakuti amakonda kupemphera alikuyimilira m’masunagoge, ndi m’mphambano za m’misewu, kuti awonekere kwa anthu. Indetu ndikunena kwa inu, iwo ali nayo mphotho yawo.

6 Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako, ndipo pamene watseka chitseko chako, pemphera kwa Atate ako amene ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona mseri adzakubwenzera iwe mowonekera.

7 Koma pamene mukupemphera, musabwerezebwereze mwachabe, monga achikunja; pakuti amayesa kuti adzamveka chifukwa cha kuyankhula kwawo kochuluka.

8 Kotero musakhale inu monga iwo; pakuti Atate anu akudziwa zimene mukuzisowa, inu musadapemphe kwa Iwo.

9 Kotero pempherani inu motere: Atate athu a Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.

10 Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.

11 Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tikhululukira amangawa athu.

12 Ndipo musatitengere ife kokatiyesa, koma mutipulumutse ife kwa woipayo.

13 Pakuti ufumu ndi wanu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, kwamuyaya. Ameni.

14 Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo Atate anu a Kumwamba adzakhululukira inunso;

15 Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate anunso sadzakukhululukirani zolakwa zanu.

16 Ndiponso, pamene musala kudya musakhale monga onyengawo, a nkhope yachisoni; pakuti amaipitsa nkhope zawo, kuti aonekere kwa anthu kuti akusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, iwo ali nayo mphotho yawo.

17 Koma iwe, posala kudya, dzodza mutu wako, ndi kusamba nkhope yako;

18 Kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya, koma kwa Atate ako amene ali mseri; ndipo Atate ako akuona mseri adzakubwenzera iwe mowonekera.

19 Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga, ndi mbala zimaboola ndi kuba;

20 Koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri sizimawononga, ndipo mbala sizimaboola ndi kuba;

21 Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wakonso udzakhala komweko.

22 Kuunika kwa thupi ndi diso; kotero ngati diso lako liri la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowala.

23 Koma ngati diso lako liri loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodzadza ndi mdima. Kotero ngati kuunika kuli mwa iwe kuli mdima, mdimawo ndi waukulu bwanji!

24 Palibe munthu angathe kutumikira ambuye awiri; pakuti pena adzamuda m’modzi, ndikudzakonda winayo, kapena adzakangamira kwa m’modzi, ndikudzanyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma.

25 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Yesu adanena mawu awa adayang’ana pa khumi ndi awiriwo amene adawasankha, nanena nawo, Kumbukirani mawu amene ndayankhula. Pakuti taonani, inu ndinu amene ndakusankhani kuti mutumikire anthu awa. Kotero ndikunena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?

26 Taonani mbalame za mumlengalenga, pakuti sizimafesa ayi, kapena kukolola, kapena kututira m’nkhokwe; koma Atate anu a Kumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa izo?

27 Ndani wa inu pa kudera nkhawa angathe kuwonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi?

28 Ndipo muderanji nkhawa ndi zovala? Lingalirani za maluwa akuthengo, m’mene amakulira; sagwira ntchito, kapena kupota;

29 Koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo, mu ulemerero wake wonse, sadavale ngati limodzi la amenewa.

30 Chifukwa chake ngati Mulungu amaveka motero maudzu a kuthengo, okhala lero, ndi mawa aponyedwa pamoto, momwemonso adzaveka inu, ngati simuli a chikhulupiliro chochepa.

31 Kotero musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani?

32 Pakuti Atate anu a Kumwamba akudziwa kuti mukusowa zinthu zonsezi.

33 Koma muyambe mwafuna Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake, ndipo zinthu zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.

34 Kotero musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa lidzadzidera nkhawa za zinthu za ilo lokha. Lokwanira liri tsiku ndi zoipa zake.

Print