Malembo Oyera
3 Nefi 18


Mutu 18

Yesu akhazikitsa mgonero pakati pa Anefi—Iwo alamulidwa kupemphera nthawi zonse mu dzina Lake—Amene amadya thupi lake ndi kumwa mwazi wake mosayenera atembeleredwa—Ophunzira apatsidwa mphamvu ya kupereka Mzimu Woyera. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 34.

1 Ndipo zidachitika kuti Yesu adalamulira ophunzira ake kuti abweretse mkate ndi vinyo kwa iye.

2 Ndipo pamene iwo adapita kukafuna mkate ndi vinyo, iye adalamulira khamulo kuti iwo akhale pansi pa dothi.

3 Ndipo pamene ophunzira adadza ndi mkate ndi vinyo, iye adatengako mkate ndi kuunyema ndi kuudalitsa iwo; ndipo adapereka kwa ophunzira ndi kuwalamulira kuti iwo adye.

4 Ndipo pamene adadya ndi kukhutira, adalamulira kuti apereke kwa khamulo.

5 Ndipo pamene khamulo lidadya ndi kukhutira, adati kwa ophunzira ake: Taonani, m’modzi adzadzozedwa pakati panu, ndipo kwa iye ndidzampatsa mphamvu kuti adzinyema mkate, ndi kuudalitsa, ndi kuupereka kwa anthu a mpingo wanga; kwa onse amene akhulupilira ndi kubatizidwa m’dzina langa.

6 Ndipo izi mudzaonetsetsa kuchita nthawi zonse; ngakhale monga ndachitira, ngakhale monga ndanyema mkate ndi kuudalitsa ndi kuupereka kwa inu.

7 Ndipo izi mudzazichita pokumbukira thupi langa, limene ndalionetsa kwa inu. Ndipo udzakhala umboni kwa Atate kuti mumandikumbukira ine nthawi zonse. Ndipo ngati mundikumbukira nthawi zonse mudzakhala ndi Mzimu wanga kukhala ndi inu.

8 Ndipo zidachitika kuti pamene adanena mawu awa, adalamulira ophunzira ake kuti atengeko vinyo wa m’chikho ndi kumwamo, ndipo kutinso apereke kwa khamulo kuti amweko.

9 Ndipo zidachitika kuti iwo adachita momwemo, ndipo adamwako ndipo adakhutila; ndipo adapereka kwa khamulo, ndipo adamwa, ndipo adakhutira.

10 Ndipo pamene ophunzirawo adachita ichi, Yesu adati kwa iwo, Wodala muli inu chifukwa cha chinthu ichi chimene mwachita; pakuti uku kuli kukwaniritsa malamulo anga, ndipo ichi chikuchitira umboni kwa Atate kuti muli kulolera kuchita chimene ine ndakulamulirani inu.

11 Ndipo izi mudzazichita nthawi zonse kwa iwo amene alapa ndi kubatizidwa m’dzina langa; ndipo mudzazichita m’chikumbukiro cha mwazi wanga, umene ndakhetsa chifukwa cha inu, kuti mukachitire umboni kwa Atate kuti mumandikumbukira ine nthawi zonse. Ndipo ngati mundikumbukira nthawi zonse mudzakhala ndi Mzimu wanga kukhala nanu.

12 Ndipo ine ndikukupatsani inu lamulo kuti inu mudzachita zinthu izi. Ndipo ngati inu nthawi zonse mudzachita zinthu izi wodala ndi inu, pakuti mwamangidwa pa thanthwe langa.

13 Koma amene mwa inu adzachita zambiri kapena zochepa kuposa izi sadamangidwe pa thanthwe langa, koma amangidwa pa maziko amchenga; ndipo pamene mvula itsika, ndipo madzi osefukira adzabwera, ndi mphepo zikuwomba, ndi kuwomba pa iwo, iwo adzagwa, ndipo zipata za gahena zakonzeka kuti ziwalandire iwo.

14 Kotero odala muli inu ngati musunga malamulo anga, amene Atate andilamulira ine kuti ndidzapereke kwa inu.

15 Indetu, indetu, ndinena kwa inu, mukuyenera kukhala tcheru ndi kupemphera nthawi zonse, kuti mungayesedwe ndi mdyerekezi, ndipo ndikutsogozedwa ukapolo ndi iye.

16 Ndipo monga ndapemphera pakati pa inu inde kotero inu mudzapemphera mu mpingo wanga, pakati pa anthu anga amene alapa ndi kubatizidwa m’dzina langa. Taonani, ine ndine kuwala; ndakupatsani chitsanzo.

17 Ndipo zidachitika kuti pamene Yesu adayankhula mawu amenewa kwa ophunzira ake, iye adatembenukiranso kwa khamulo ndipo adati kwa iwo:

18 Taonani, indetu, indetu, ndikunena kwa inu, mukuyenera kukhala tcheru ndi kupemphera nthawi zonse kuti mungalowe m’kuyesedwa; pakuti Satana akufuna kuti akhale nanu, kuti akupeteni ngati tirigu.

19 Kotero mukuyenera kupemphera nthawi zonse kwa Atate m’dzina langa;

20 Ndipo china chili chonse chimene mudzapempha Atate m’dzina langa, chimene chili cholondola, mukukhulupilira kuti mudzalandira, taonani, chidzapatsidwa kwa inu.

21 Pempherani m’mabanja anu kwa Atate, nthawi zonse m’dzina langa, kuti akazi anu ndi ana anu adalitsidwe.

22 Ndipo taonani, mudzakumana pamodzi kawiri kawiri; ndipo inu simudzaletsa aliyense kubwera kwa inu pamene mudzakumana, koma aloleni iwo kuti abwere kwa inu, ndipo musawaletse;

23 Koma inu mudzawapemphelera, ndipo simudzawaponya kunja; ndipo ngati kutero kuti abwera kwa inu kawiri kawiri mudzawapemphelera iwo kwa Atate, m’dzina langa.

24 Kotero, nyamulani kuwala kwanu kuti kuunikire ku dziko lapansi. Taonani, ine ndine kuwala kumene mudzakunyamula—icho chimene mwandiona ndikuchita. Taonani mukuona kuti ndapemphera kwa Atate, ndipo inu nonse mwachitira umboni.

25 Ndipo mukuona kuti ndakulamulirani kuti palibe m’modzi wa inu akuyenera adzipita kutali, koma makamaka ndalamulira kuti mudze kwa ine, kuti mukamvelere ndi kuona; ngakhale momwemonso mudzachitira dziko lapansi; ndipo amene amphwanya lamulo ili adzilolera yekha kutsogozedwa m’mayesero.

26 Ndipo tsopano zidachitika kuti Yesu atanena mawu amenewa, adatembenuziranso maso ake kwa ophunzira amene iye adawasankha, nanena nawo.

27 Taonani indetu, indetu, ndikunena kwa inu, ndikupereka kwa inu lamulo lina, ndipo kenako ine ndikuyenera kupita kwa Atate anga kuti ndikakwaniritse malamulo ena amene iwo adandipatsa ine.

28 Ndipo tsopano taonani, ili ndi lamulo limene ine ndikupereka kwa inu, kuti inu musadzalore wina aliyense modziwa kuti atenge thupi ndi mwazi wanga mosayenera, pamene inu mudzaperekera izo;

29 Pakuti yense wakudya ndi kumwa thupi ndi mwazi wanga mosayenera, akudya ndi kumwera chiwonongeko cha moyo wake; kotero ngati mukudziwa kuti munthu sali woyenera kudya ndi kumwa thupi langa ndi mwazi wanga, inu mudzamuletsa.

30 Komabe, inu simudzamuchotsa pakati panu, koma inu mudzatumikira kwa iye ndi kumupemphelera iye kwa Atate, m’dzina langa; ndipo ngati atakhale kuti alapa ndipo abatizidwa m’dzina langa, pamenepo inu mudzamulandira iye, ndipo mudzaperekera kwa iye thupi ndi mwazi wanga.

31 Koma ngati iye salapa iye sadzawerengedwa pakati pa anthu anga, kuti asawononge anthu anga, pakuti taonani ndikudziwa nkhosa zanga, ndipo zimawerengedwa.

32 Komabe, inu musadzamtulutse iye m’masunagoge anu, kapena malo anu opembedzerapo, pakuti kwa oterowo mudzapitiriza kutumikira; pakuti inu simudziwa koma chimene iwo adzabwelera ndi kulapa, ndi kudza kwa ine ndi cholinga chonse cha mtima, ndipo ndidzawachiritsa iwo; ndipo inu mudzakhala njira yowabweretsera ku chipulumutso.

33 Kotero, sungani mawu awa amene ndakulamulirani inu kuti musabwere pansi pa kutsutsidwa; pakuti tsoka kwa iye amene Atate amutsutsa.

34 Ndipo ndikukupatsani malamulo awa chifukwa cha mikangano imene yakhala pakati panu. Ndipo muli wodala ngati mulibe mikangano pakati panu.

35 Ndipo tsopano ndipita kwa Atate, chifukwa ndikofunikira kuti ndipite kwa Atate chifukwa cha inu.

36 Ndipo zidachitika kuti, pamene Yesu adamaliza mawu awa, adawakhudza ndi dzanja lake ophunzira amene adawasankha, m’modzim’modzi, ngakhale mpakana atawakhudza iwo onse, ndipo adayankhula nawo pamene ankawakhudza iwo.

37 Ndipo khamulo silidamve mawu amene iye adayankhula, kotero iwo sadachitire umboni; koma ophunzirawo adachitira umboni kuti iye adawapatsa iwo mphamvu ya kupereka Mzimu Woyera. Ndipo ine ndidzakuonetsani inu kutsogoloku kuti umboni uwu uli woona.

38 Ndipo zidachitika kuti, pamene Yesu adawakhudza iwo onse, kudadza mtambo ndipo udaphimba khamu la anthulo, kotero kuti iwo sadathe kumuona Yesu.

39 Ndipo pamene iwo adaphimbidwa, iye adawachokera, ndipo adakwera kumwamba. Ndipo ophunzira adaona ndipo adachitira umboni kuti adakweranso kumwamba.

Print