Zofunikira Zoyambirira
Mfundo za Chikhulupiliro


Mfundo za Chikhulupiliro

M’chaka cha 1842, Mneneri Joseph Smith adatumiza kalata kwa John Wentworth, yemwe adali mkonzi wa nyuzipepala yotchedwa Chicago Democrat. Kalata iyi idali ndi mbiri ya zochitika zambiri za mbiri ya Mpingo zoyambilira. Chikalatacho chidalinso ndi mfundo 13 zofotokoza zikhulupiliro za Oyera Mtima M’masiku Otsiriza. Izi zafika podziwika kuti ndi Mfundo za Chikhulupiliro, zomwe zaperekedwa pansipa.

Mfundo za Chikhulupiliro ndi chiphunzitso chovomerezeka cha Mpingo ndipo chavomerezedwa ngati gawo la malemba amasiku otsiriza. Ndi mawu omveka bwino a chikhulupiliro omwe amathandiza mamembala kumvetsetsa zikhulupiliro zoyambilira za Mpingo ndi kufotokozera zikhulupiliro izi kwa ena. Komabe izo sichidule chathunthu cha ziphunzitso za Mpingo. Kudzera mwa aneneri amoyo, Mpingo umatsogozedwa ndi vumbulutso lopitilira ndi kudzoza.

  1. Timakhulupilira mwa Mulungu, Atate Amuyaya, ndi mwa Mwana Wawo, Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu Woyera.

  2. Timakhulupilira kuti anthu adzalangidwa chifukwa cha machimo awo, osati chifukwa cha kulakwa kwa Adamu.

  3. Timakhulupilira kuti kudzera mu Chitetezero cha Khristu, anthu onse akhonza kupulumutsidwa, pomvera malamulo ndi miyambo ya Uthenga Wabwino.

  4. Timakhulupilira kuti mfundo zoyamba ndi miyambo ya Uthenga Wabwino ndi: choyamba, Chikhulupiliro mwa Ambuye Yesu Khristu; chachiwiri, Kulapa; chachitatu, Ubatizo womizidwa mmadzi ku chikhululukiro cha machimo; chachinayi, Kusanjika manja kuti ulandire mphatso ya Mzimu Woyera.

  5. Timakhulupilira kuti munthu akuyenera kuyitanidwa ndi Mulungu, mwa uneneri, ndi kusanjika manja ndi iwo amene ali ndi ulamuliro, kuti alalikire Uthenga Wabwino ndikuchita mwa miyambo yake.

  6. Timakhulupilira mu ndondomeko yomwe idalipo mu Mpingo Woyamba, maina ake, atumwi, aneneri, abusa, aphunzitsi, alaliki, ndi ena otero.

  7. Timakhulupilira mu mphatso ya malirime, uneneri, vumbulutso, masomphenya, machiritso, kutanthauzira kwa malirime, ndi zina zotero.

  8. Timakhulupilira kuti Baibulo ndi Mau a Mulungu kufikira ngati lidamasuliridwa molondola; timakhulupiliranso kuti Buku la MormoniMormoni ndi mawu a Mulungu.

  9. Timakhulupilira zonse zimene Mulungu wavumbulutsa, zonse zimene Iye akuvumbulutsa tsopano, ndipo timakhulupirira kuti Iye adzavumbulutsa zinthu zazikulu ndi zofunika zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu.

  10. Timakhulupilira mu kusonkhanitsidwa kwenikweni kwa Israeli ndi kubwezeretsedwa kwa mafuko Khumi; kuti Ziyoni (Yerusalemu Watsopano) adzamangidwa pa kontinenti ya Amerika; kuti Khristu adzalamulira yekha padziko lapansi; ndi, kuti dziko lapansi lidzakonzedwanso ndi kulandira ulemerero wake wa paradiso.

  11. Timadzinenera kuti tili ndi mwayi wolambira Mulungu Wamphamvu zonse motsatira chikumbumtima chathu, ndipo timalora anthu onse kukhala ndi mwayi wofanana, kuwalola kuti alambire momwe, komwe, kapena zomwe angachite.

  12. Timakhulupilira kumvera mafumu, mapulezidenti, olamulira, ndi oweruza, mu kumvera, kulemekeza, ndi kusunga malamulo.

  13. Timakhulupilira kukhala owona mtima, achilungamo, oyera, okoma mtima, odzisunga, ndi kuchita zabwino kwa anthu onse; ndithu, tinganene kuti timatsatira malangizo a Paulo akuti—Timakhulupilira zinthu zonse, timayembekeza zinthu zonse, tapilira zinthu zambiri, ndipo tikuyembekeza kuti tidzatha kupilira zinthu zonse. Ngati pali chinthu chabwino, chokondeka, kapena cha mbiri yabwino kapena chotamandika, timafunafuna zinthu zimenezi.

Print