Zofunikira Zoyambirira
Mutu 19: Mpingo wa Yesu Khristu Lero


Mutu 19

Mpingo wa Yesu Khristu Lero

Kodi tingaupeze kuti uthenga woona wa Yesu Khristu masiku ano?

Kwa Dzaka Zambiri Mpingo wa Yesu Khristu kudalibe Padziko Lapansi

Yesu adaukhazikitsa Mpingo Wake pamene Iye adali pa dziko lapansi. Mpingo Wake udali pa dziko lapansi kwa kanthawi Iye atabwelera kumwamba. Pamene anthu adasiya kuphunzitsa ndi kukhulupilira ziphunzitso zake zoona, Yesu adatenga unsembe ndi Mpingo wake kuzichotsa padziko lapansi.

Kwa dzaka zambiri, anthu adakhala opanda Uthenga Wabwino oona ndi Mpingo wa Yesu Khristu. Anthu adayambitsa mipingo yochuluka, potengera maganizo awo komanso ziphunzitso zina za m’Baibulo. Koma mipingo imeneyi idalibe unsembe wa Atate athu Akumwamba. Adalibe ziphunzitso zonse za Yesu. Iwo adalibe vumbulutso lopitilira kuchokera kwa Yesu. Adalibe mphatso zonse za uzimu.

Anthu adayamba kufuna kudziwa zoona zokhudza Atate athu Akumwamba. Iwo adayamba kufufuza choonadi chonena za Atate athu Akumwamba komanso zimene ankaphunzitsa. Ena a iwo adazindikira kuti uthenga woona ndi Mpingo wa Yesu Khristu siudalinso pa dziko lapansi. Atate athu Akumwamba adadziwa kuti nthawi idafika yobwenzeretsa uthenga woona ndi Mpingo wa Yesu Khristu padziko lapansi.

Zokambirana

  • Chifukwa chiyani Yesu adatenga unsembe padziko lapansi?

  • Ndi chifukwa chiyani mipingo imene anthu adayambitsa siudali Mpingo wa Yesu Khristu?

Image
Masomphenya Oyamba, ndi Walter Rane

Atate wathu Akumwamba ndi Yesu adayendera Joseph Smith.

Atate athu Akumwamba Adasunga Lonjezo Lawo Lobwenzeretsa Mpingo Woona

Atate athu Akumwamba amakonda ana ake onse. Iwo amafuna kuti adziŵe zimene ayenela kuchita kuti akakhale ndi Iwo akadzafa ndi kuukitsidwa. Asadachotse Mpingo woona wa Yesu Khristu padziko lapansi, Yesu adauza aneneri ndi Atumwi kuti izi zidzachitika. Adalonjezanso kuti tsiku lina adzabwenzeretsa mpingo padziko lapansi. Adzachita zimenezi pamene padalinso anthu amene adali okonzeka kulandira uthenga woona.

Yesu Wabwenzeretsa Mpingo Wake Padziko Lapansi

Yesu wabwenzeretsa mpingo wake padziko lapansi ndi ulamuliro ndi madalitso ofanana ndi mpingo umene adaukhazikitsa pamene adali padziko lapansi. Munthu aliyense amene ali wokonzeka kumvera malamulo ake akhonza kukhala membala wa mpingo wake.

Atate athu Akumwamba Adasankha Joseph Smith Kuti Athandize Kubwenzeretsa Mpingo

M’chaka cha 1820, Yesu adayamba kubwenzeretsa uthenga woona ndi Mpingo padziko lapansi. Mnyamata wina dzina lake Joseph Smith ankafuna kudziwa kuti ndi mpingo uti umene udali mpingo wa Yesu Khristu. Adawerenga m’Baibulo kuti munthu amene akufuna kudziwa zinthu ayenera kufunsa Atate athu Akumwamba. Adaganiza zofunsa Atate athu Akumwamba ndi mpingo uti omwe akuyenera kulowa. Iye adalowa m’nkhalango pafupi ndi kwawo ndipo adafunsa Atate athu Akumwamba ndi mpingo uti akuyenera alowe. Atate athu Akumwamba ndi Yesu adaonekera kwa Joseph Smith. Atate athu Akumwamba adauza Joseph kuti amvetsere Yesu ndi kumumvera iye. Pamenepo Yesu adauza Joseph kuti asalowe uliwonse mwa mipingoyo. Iye adati Mpingo woona siudali pa dziko lapansi.

Vumbulutso lotere kuchokera kwa Atate athu Akumwamba silidalandiridwe popeza uthenga woona ndi Mpingo wa Yesu Khristu udachotsedwa padziko lapansi. Kuchokera pa vumbulutso limenelo, mavumbulutso ena ambiri abwera. Atate athu Akumwamba adasankha Joseph Smith kuti amuyimire Iye padziko lapansi. Yesu adabwenzeretsa uthenga woona ndi Mpingo wa Yesu Khristu kudzera mwa Joseph Smith.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani Joseph Smith adawona masomphenya?

Unsembe Udabwenzeretsedwa

Unsembe udabwenzeretsedwa kudziko lapansi mu 1829. Yohane M’batizi adabwera kuchokera kumwamba ndipo adapereka wina mwa ulamuliro wa unsembe kwa Joseph Smith posanjika manja ake pa Mutu wa Joseph. Ulamuliro wa unsembe uwu umatchedwa Unsembe wa Aroni. Yohane M’batizi, amene adabwenzeretsa ulamuliro wa unsembe uwu, adali munthu yemweyo amene adabatiza Yesu. Petro, Yakobo, ndi Yohane, atatu a Atumwi a Yesu oyambirira, nawonso adabwera ndipo adapatsa Joseph mphamvu zochuluka za unsembe. Ulamuliro wa unsembe uwu umatchedwa Unsembe wa Melkizedeki.

Aneneri ena, kuphatikizapo Mose ndi Eliya, adabweranso ndipo adapereka kwa Joseph Smith ulamuliro wochita ntchito zina zopatulika. Ulamuliro wochokera kwa Atate athu Akumwamba wophunzitsa uthenga wabwino, kuchita ntchito zopatulika, ndi kutsogolera mpingo uli pa dzikola pansi kachiwiri.

Zokambirana

  • Kodi Joseph Smith adalandira bwanji unsembe poyamba?

Yesu Adakhazikitsanso Mpingo Wake

Kudzera mu vumbulutso, Yesu adatsogolera Joseph Smith kuti akhazikitsenso Mpingo Wake, pa 6 April 1830. Yesu adali Mutu wa Mpingo Wake pamene Iye adali kukhala padziko lapansi. Iye ali Mutu wa Mpingo Wake tsopano lino. Mamembala a Mpingo Wake akadali kutchedwa Oyera mtima.

Yesu adatchula Mpingo Wake lero Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera mtima M’masiku Otsiriza. Mawu akuti Masiku Otsiriza amasonyeza kuti uwu ndi Mpingo wa Yesu Khristu mu nthawi yotsiriza yadziko lapansi. Yesu adanena kuti mpingo uwu ndi mpingo woona wokha pa dziko lonse lapansi ndipo amasangalala nawo.

Yesu amasankha mneneri kuti atsogolere mpingo padziko lapansi. Yesu amatsogolera mneneri ameneyu. Iye amamupatsa mneneri ameneyu ulamuliro otsogolera mpingo. Joseph Smith adali mneneri woyamba wa Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera mtima M’masiku Otsiriza. Mneneri wa Mpingo amatchedwanso Pulezidenti wa Mpingo. Pulezidenti ali ndi anthu omwe amamuthandiza. Iwo amatchedwa Alangizi. Mneneri akamwalira, Yesu amasankha mneneri watsopano kuti alowe m’malo mwake.

Yesu amasankhanso atumwi khumi ndi awiri kuti athandize kutsogolera mpingo. Amuna osankhidwa kukhala mamembala a Magulu a Makumi Asanu ndi Awiri amathandiza Atumwi ndi Pulezidenti. Azibambo ndi anyamata ena abwino amalandiranso unsembe ndi kutumikira mu mpingo. Amatchedwa akulu a nsembe, akulu, mabishopu, ansembe, aphunzitsi, ndi madikoni, monga momwe adatchulidwira mu Mpingo woyambilira wa Yesu Khristu.

Yesu adauza Joseph Smith momwe Mpingo Wake uyenera kukhazikitsiridwa. Pamene mpingo wakhazikitsidwa kwathunthu mu dera, dera limenelo limadziwika ngati Siteki.* Pulezidenti amatsogolera Siteki. Amakhala ndi alangizi awiri oti azimuthandiza.

Siteki imagawidwa m’madera ang’onoang’ono. Madera amenewa amadziwika kuti ma wodi.* Mtsogoleri wa unsembe wotchedwa bishop amatsogolera wodi. Amakhala ndi alangizi awiri azimuthandiza.

M’madera amene masiteki sanakonzedwebe, Kumatha kukhala zigawo,* zomwe zimapangidwa ndi nthambi. Nthambi zimatsogozedwa ndi pulezidenti ndi alangizi awiri. Madera amene kuli mamishonale ambiri ophunzitsa uthenga wabwino amatchedwa mamishoni.*

Amuna Amene Ali ndi Unsembe Amakhazikitsidwa M’makoramu

Amuna omwe ali ndi unsembe amakhazikitsidwa m’magulu otchedwa makoramu. Koramu ya unsembe ndigulu la amuna omwe ali ndi udindo ofanana mu unsembe. Amalumikizana pamodzi kuti azithandizana wina ndi mnzake komanso anthu ena.

Zokambirana

  • Kodi mtsogoleri wa Mpingo wa Yesu Khristu ndi ndani masiku ano?

  • Kodi amuna amene amathandiza kutsogolera mpingo amatchedwa chiyani?

Mpingo Lerolino Wakhazikitsidwa chimodzimodzi ndi Mpingo Umene Yesu Adaukhazikitsa Pamene Adali Padziko Lapansi

Yesu Akutsogolerabe Mpingo Wake ndi Chivumbulutso

Kudzera mwa Mzimu Woyera, Yesu amauza mneneri momwe akuyenera kutsogolera mpingo. Iye amavumbulutsa kwa Atumwi ndi atsogoleri ena a Mpingo zimene iye akufuna kuti iwo achite. Kudzera mu chivumbulutso, Yesu mosalekeza amatsogolerabe mamembala a Mpingo Wake.

Aliyense Akhonza Kukhala membala wa Mpingo

Aliyense akhonza kukhala membala wa Mpingo wa Yesu Khristu tsopano monga momwe anthu adalowa mu Mpingo Wake pamene Iye anali pa dziko lapansi. Munthuyo akuyenera kukhala ndi chikhulupiliro mwaYesu ndikulapa. Munthuyo akuyenera kubatizidwa. Munthu akabatizidwa, iye amalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Zokambirana

  • Kodi tikuyenera kuchita chiyani kuti tilowe mu Mpingo wa Yesu Khristu tsopano?

Mamembala a Mpingo Masiku Ano Amalandira Mphatso Za uzimu

Yesu nthawi zonse amapereka mphatso za uzimu kwa mamembala a mpingo wake. Mphamvu zonse zauzimuzi ziri mu Mpingo lero.

Zokambirana

  • Kodi zina mwa mphatso za uzimu ndi ziti? (Onani Mutu 16.)

Yesu Adabwenzeretsa Ziphunzitso Zake Zoona

Yesu wabwenzeretsanso ziphunzitso zimene Iye ndi Atumwi Ake adaphunzitsa. Ziphunzitso zoyambirira ndi chikhulupiliro mwa Yesu Khristu, kulapa, ubatizo, ndi mphatso ya Mzimu Woyera. Zoona zina zofunika zomwe Yesu wapereka kwa mpingo wake ndi izi:

  1. Atate athu Akumwamba ali ndi thupi la mnofu ndi mafupa.

  2. Ndife ana auzimu a Atate athu Akumwamba. Tidakhala Nawo kumwamba ngati mizimu tisadabadwe padziko lapansi.

  3. Tidzalangidwa chifukwa cha machimo athu okha osati chifukwa cha zimene Adamu adachita. Anthu ambiri amakhulupilira kuti chifukwa chakuti Adamu ndi Hava adadya chipatso choletsedwa, ifeyo, ana awo ndife ochimwa pamene tikubadwa. Izi sizowona. Ana siali ochimwa pamene abadwa. Iwo ndiosalakwa. Choncho, siofunikira kubatizidwa mpaka atakwanitsa zaka zisanu ndi zitatu.

  4. Mwamuna akuyenera kukhala ndi unsembe kuti achititse miyambo* (onani Mutu 21) ya Mpingo wa Yesu Khristu.

Zokambirana

  • Kodi zina mwa ziphunzitso za Yesu zimene wapelekanso kwa anthu ndi ziti?

Mpingo wa Yesu Khristu siudzachotsedwanso padziko lapansi

Tsopano pamene Mpingo woona wa Yesu Khristu, ulamuliro wa unsembe, ndi uthenga wabwino zabwenzeretsedwa kudziko lapansi, sizidzachotsedwanso padziko lapansi. Atate athu Akumwamba adanena kuti adzakhazikitsa ufumu umene siudzawonongedwa. Ufumu umenewu ndi Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza. Udzapitilira mpaka muyaya.

Anthu ambiri alowa mu Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza. Pali mamembala ampingo m’maiko ambiri padziko lapansi. Anthu ambiri adzapitiriza kulowa mu mpingo. Ana onse a Atate athu Akumwamba adzamva uthenga wabwino ndikukhala ndi mwayi woulandira.

Zokambirana

  • Kodi mungatani kuti muthandize ena kumva za Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu kuti alowe Mpingo Wake?

Print