Zofunikira Zoyambirira
Mutu 6: Adamu ndi Hava


Mutu 6

Adamu ndi Hava

Kodi Adamu ndi Hava adali ndani? Kodi iwo adachita chiyani kuti atithandize?

Adamu ndi Hava Adali Anthu Oyamba Kubwera Pa dziko Lapansi

Atate athu Akumwamba adatchula anthu oyamba pa dziko lapansi kuti Adamu ndi Hava. Iwo adali awiri a ana Awo amphamvu kwambiri. Iwo adachititsa kuti tonsefe tibwere pa dziko lapansi.

Kumwamba, Adamu ankatchedwa Mikayeli. Adali mmodzi wa atsogoleri athu. Iye adatitsogolera pa nkhondo yolimbana ndi Satana. Mikayeli adali munthu wabwino. Iye adachita zimene Atate athu Akumwamba ankafuna kuti achite. Iye adakhala munthu woyamba kukhala pa dziko lapansili.

Hava adali mwana wabwino kwambiri wa Atate athu Akumwamba. Atate athu Akumwamba adatumiza Hava ku dziko lapansi ndi Adamu kuti akhale mkazi wake ndi omuthandizila. Atate athu Akumwamba ankadziwa kuti sibwino kuti Adamu akhale yekha. Adamu, mwa iye yekha, sakadatipangitsa kubwera pa dziko lapansi. Gawo la Hava mu dongosololi lidali lofunika monga la Adamu.

Zokambirana

  • Asadabwere pa dziko lapansi, kodi Adamu ankatchedwa ndani ndipo adachita chiyani?

  • Ndi chifukwa chiyani Atate athu Akumwamba adatumiza Hava kuti akakhale ndi Adamu?

Munda wa Edeni Udali Nyumba Yoyamba ya Adamu ndi Hava

Atate athu Akumwamba adalenga malo okongola pa dziko lapansi kuti Adamu ndi Hava azikhalamo. Adautcha Munda wa Edeni. Pamene Adamu ndi Hava adali m’munda wa Edeni, aliyense adali ndi thupi la mnofu ndi mafupa limene silikadafa. Adalibe ana. Sadafunikire kubzala ndi kukolola kapena kugwira ntchito zimene adafunikira. Sadakumbukire moyo wawo wakumwamba. Iwo sankadziwa chimene chidali chabwino ndi choipa.

M’munda wa Edeni, Adamu ndi Hava amatha kuyenda ndi kuyankhulana ndi Atate athu Akumwamba. Adawauza zinthu zimene adayenera kuchita. Adawauza kuti asamalire mundawo kuti ukhale wokongola. Adawauza kuti akhale ndi ana. Adawauzanso kuti adye zipatso za mtengo uliwonse wam’munda mwaufulu, kupatulapo umodzi. Atate athu Akumwamba adawauza kuti asadye chipatso cha mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Adawachenjeza kuti akadya chipatso cha mtengowo adzafa.

Zokambirana

  • Kodi moyo wa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni udali wosiyana bwanji ndi wa masiku ano?

  • Kodi Atate athu Akumwamba adawauza Adamu ndi Hava kuti achite chiyani?

Image
Adamu ndi Hava, wolemba Lowell Bruce Bennett

Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni.

Adamu ndi Hava Adalekanitsidwa ndi Atate athu Akumwamba

Satana adaganiza kuti akhonza kuwononga dongosolo la Atate athu Akumwamba. Iye adafika m’munda wa Edeni n’kumunyengelera Hava kuti adye chipatso cha mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Adamuuza kuti akadya chipatsocho sadzafa. Iye adati adzadziwa kusiyanitsa chabwino ndi choipa, monga m’mene Atate athu Akumwamba amachitira. Hava adakhulupilira Satana, ndipo adadya chipatsocho. Pamene Hava adauza Adamu kuti wadya chipatsocho, iye adadziŵa kuti achoka m’mundamo. Adadyanso zina mwazipatsozo kuti akhale pamodzi.

Moyo wa Adamu ndi Hava udasintha atadya chipatso chimene Atate athu Akumwamba adawauza kuti asadye. Atate athu Akumwamba adawatulutsa m’munda wa Edeni. Sadathenso kuyenda ndi kuyankhula ndi Iwo. Kuyambira pamenepo anthu adalekanitsidwa ndi pamaso pa Atate athu Akumwamba. Kulephera kukhala ndi Atate athu Akumwamba kumatchedwa imfa yauzimu.* Adafunika kugwira ntchito kuti apeze zinthu zofunika.

Matupi awo adasintha. Tsopano akadatha kukhala ndi ana. Iwo akadatha kudwala ndi kumva ululu ndi chisoni, ndipo tsiku lina nkudzafa. Kusintha kumene kudadza kwa Adamu ndi Hava kumatchedwa Kugwa kwa Adamu.

Kusintha kumeneku kumakhudza mibadwo yonse ya Adamu ndi Hava. Mofanana ndi iwo, ifenso tiri ndi mphamvu zokhala ndi ana; ndimatenda, zowawa, chisoni, ndi imfa zimabweranso kwa ife.

Zokambirana

  • Kodi Satana adachita chiyani pofuna kuwononga dongosolo la Atate athu Akumwamba?

  • Kodi moyo wa Adamu ndi Hava udasintha bwanji atadya chipatso cha mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa?

  • Kodi imfa yauzimu ndi chiyani?

  • Kodi Kugwa kwa Adamu Ndi chiyani?

Kugwa kwa Adamu Kunali Gawo Lofunikira Kwambiri pa Dongosolo la Atate athu Akumwamba

Atate athu Akumwamba adakonza zoti ana awo abwere pa dziko lapansi kuti adzalandire matupi a mnofu ndi mafupa. Atatulutsa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni, adayamba kubala ana. Kenako ana awo adakwatira n’kukhala ndi ana. Mwanjira imeneyi ana auzimu a Atate athu Akumwamba amene adali kukhala ndi Iwo adayamba kubwera ku dziko lapansi monga momwe adakonzera. Chifukwa cha zimene Adamu ndi Hava adachita, aliyense wa ife akadatha kubwera pa dziko lapansi n’kulandira thupi la mnofu ndi mafupa.

Atate athu Akumwamba adakonzeranso ana Awo kuti azigwira ntchito kuti apeze zinthu zomwe ankafuna ndi zomwe amafunikira. Kuchokela pamene Adamu ndi Hava adachoka m’munda wa Edeni, ana a Atate athu Akumwamba pa dziko lapansi adafunika kugwira ntchito kuti apeze zinthu zimene amafuna ndi zosowa.

Adamu ndi Hava atadya chipatso chimene Atate athu Akumwamba adawauza kuti asadye, adaphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Tsopano, aliyense wa ife pa dziko lapansi atha kuphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choipa ndi kusankha yekha kuchita zabwino kapena zoipa.

Pamene Atate athu Akumwamba adatulutsa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni, iwo adayesetsa kuphunzira zinthu zimene Iwo adafuna kuti azichita. Iwo ankawamvera ndipo ankaphunzitsa ana awo kuti azimvera Iwo. Aliyense wa ife ayeneranso kuphunzira zinthu zimene Atate athu Akumwamba amafuna kuti tidzichita, ndipo tidziwamvera ndi kuphunzitsa ana athu kuti azimvera Iwo.

Zokambirana

  • Kodi Satana adawononga dongosolo la Atate athu Akumwamba?

  • Ndi chifukwa chiyani tikuyenera kuyamikira zimene Adamu ndi Hava adachita?

Print