Malembo Oyera
2 Nefi 2


Mutu 2

Chiwombolo chimabwera kudzera mwa Mesiya Oyera—Ufulu wa kudzisankhira (Upangiri) ndi ofunika mu kukhalapo ndi kupita patsogolo—Adamu adagwa kuti anthu akhale—Anthu ali omasuka kusankha ufulu ndi moyo wamuyaya. Mdzaka dza pafupifupi 588–570 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, Yakobo, ndiyankhula ndi iwe: Iwe ndi mwana wanga oyamba m’masiku anga amasautso m’chipululu. Ndipo taona, mu ubwana wako iwe udamva zowawa ndi chisoni chachikulu, chifukwa cha mwano wa abale ako.

2 Komabe, Yakobo, mwana wanga woyamba m’chipululu, ukudziwa ukulu wa Mulungu; ndipo adzakupatulira masautso ako kuti akupindulire.

3 Kotero, moyo wako udzadalitsika, ndipo udzakhala motetezeka ndi m’bale wako, Nefi; ndipo masiku ako adzathera potumikira Mulungu wako. Kotero, ndikudziwa kuti iwe ndi owomboledwa, chifukwa cha chilungamo cha Muwomboli wako; pakuti iwe udaona kuti mu chidzalo cha nthawi alinkudza kubweretsa chipulumutso kwa anthu.

4 Ndipo iwe waona m’chinyamata chako ulemelero wake; kotero, iwe ndi odala ngakhale ngati iwo amene iye adzawatumikire mu thupi; pakuti Mzimu ndi omwewo, dzulo, lero ndi kunthawi zonse. Ndipo njira yakonzedwa kuchokera mu kugwa kwa munthu, ndipo chipulumutso ndichaulere.

5 Ndipo anthu amalangizidwa mokwanira kuti adziwe chabwino ku choipa. Ndipo lamulo lapatsidwa kwa anthu. Ndipo ndi lamulo, palibe munthu amene angayesedwe kuti ndiolungama; kapena mwa lamulo anthu amadulidwa. Inde, pa chilamulo cha kuthupi iwo adadulidwa; ndiponso, pa lamulo lauzimu iwo amawonongeka kuchokera ku chomwe chili chabwino, ndikukhala achisoni kwa muyaya.

6 Kotero, chiwombolo chimabwera ndi kudzera mwa Mesiya Oyera; pakuti iye ali odzadza ndi chisomo ndi choonadi.

7 Taonani, adzipereka yekha nsembe ya uchimo, kuti ayankhe mathero a chilamulo, kwa onse amene ali ndi mtima osweka ndi mzimu olapa; ndipo palibe pa aliyense yemwe mathero a chilamulo angayankhidwe.

8 Kotero, n’kwakukulu bwanji kufunika kodziwitsa zinthu izi kwa anthu okhala mu dziko lapansi, kuti iwo adziwe kuti palibe thupi lomwe lingakhale pamaso pa Mulungu, pokhapokha kudzera mwa zabwino, ndi chifundo, ndi chisomo cha Mesiya Oyera, amene wapereka moyo wake monga mwa thupi, ndikuutenganso mwa mphamvu ya Mzimu, kuti apangitse kutheka kwa chiukitso cha akufa, iye okhala oyamba kuukitsidwa.

9 Kotero, Iye ndi zipatso zoyamba kwa Mulungu, makamaka popeza iye adzapembedzera ana onse a anthu, ndipo iwo amene akhulupilira mwa iye adzapulumutsidwa.

10 Ndipo chifukwa cha mapembedzero a onse, anthu onse amabwera kwa Mulungu; kotero, iwo ayima pamaso pake, kuti aweruzidwe ndi iye molingana ndi choonadi ndi chiyero chimene chili mwa iye. Kotero, mathero a lamulo limene Oyerayo adapereka, kwa kuperekedwa kwa chilango chimene chaikidwa, chilango chimene chaikidwacho chiri chotsutsana ndi icho cha chisangalalo chimene chaikidwa, kuyankha mathero a chitetezero—

11 Pakuti ndikoyenera, kuti padzikhala kutsutsana pa zinthu zonse. Ngati sichoncho, mwana wanga oyamba m’chipululu, chilungamo sichikadachitika, ngakhale kuipa, ngakhale chiyero kapena chisoni, ngakhale chabwino kapena choipa. Kotero, zinthu zonse zikuyenera kukhala zophatikizika mu chimodzi; kotero, ngati lingakhale thupi limodzi, likuyenera kukhalabe monga lakufa, lopanda moyo ngakhale imfa, kapena chivundi kapena chisavundi, chimwemwe kapena chisoni, ngakhale kuzindikira kapena kusazindikira.

12 Kotero, chidakayenera kukhala chilengedwe chopanda phindu; kotero pakadakhala popanda cholinga kumathero a chilengedwe chake. Kotero, chinthu ichi chikadaononga nzeru ya Mulungu ndi cholinga chake chamuyaya, ndiponso mphamvu, ndi chifundo, ndi chilungamo cha Mulungu.

13 Ndipo ngati mudzanene kuti palibe lamulo, inu mudzatinso palibe tchimo. Ngati mudzanene kuti palibe tchimo, inu mudzanenanso palibe chilungamo. Ndipo ngati palibe chilungamo, palibe chimwemwe. Ndipo ngati palibe chilungamo kapena chimwemwe sipadzakhala chilango kapena chisoni. Ndipo ngati zinthu izi palibe, palibe Mulungu. Ndipo ngati palibe Mulungu ife palibe, kapena dziko lapansi; pakuti sikukadakhala chilengedwe cha zinthu, kapena zochita kapena zakuchitidwa; kotero, zinthu zonse ziyenera kukhala kulibe.

14 Ndipo tsopano, ana anga aamuna, ndikuyankhula kwa inu zinthu izi chifukwa cha phindu ndi maphunziro anu; pakuti kuli Mulungu, ndipo iye adalenga zinthu zonse, kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zinthu zonse zomwe ziri mmenemo, zinthu zonse zochita ndi zinthu zoti zichitidwe.

15 Ndipo kuti akwaniritse zolinga zake za muyaya kumapeto kwa munthu, atatha kulenga makolo athu oyamba, ndi zilombo za mtchire, ndi mbalame za mlengalenga, ndipo mnthawi yake, zonse zomwe zidalengedwa, zidayenera kukhala kuti zikutsutsana; ngakhale chipatso choletsedwa kutsutsana ndi mtengo wa moyo; wina kukhala otsekemera ndi winawo kukhala owawa.

16 Kotero, Ambuye Mulungu adapereka kwa munthu kuti adzidzichitira mwayekha. Kotero, munthu sakadatha kudzichitira mwa yekha pokhapokha atakopeka ndi umodzi kapena winawo.

17 Ndipo ine, Lehi, molingana ndi zinthu zimene ndawerenga, ndikuganiza kuti mngelo wa Mulungu, molingana ndi zomwe zalembedwa, adagwa kuchokera kumwamba; kotero, adakhala mdyerekezi, atafuna kuchita zomwe zidali zoipa pamaso pa Mulungu.

18 Ndipo chifukwa adagwa kuchokera kumwamba, ndipo adakhala osasangalala kwa muyaya, adafunafunanso masautso a anthu onse. Kotero, iye adati kwa Hava, inde, ngakhale njoka yakaleyo, amene ali mdyerekezi, amene ali tate wa mabodza onse, kotero adati: Idya chipatso choletsedwacho, ndipo siudzafa, koma udzakhala ngati Mulungu, odziwa chabwino ndi choipa.

19 Ndipo Adamu ndi Hava atatha kudya chipatso choletsedwacho adathamangitsidwa m’munda wa Edeni, kuti adzilima thaka.

20 Ndipo iwo adabala ana; inde, ngakhale banja lonse la dziko lapansi.

21 Ndipo masiku a ana a anthu adatalikitsidwa, molingana ndi chifuniro cha Mulungu, kuti alape adakali mu thupi; kotero, makhalidwe awo adakhala m’khalidwe loyesedwera, ndipo nthawi yawo idatalikitsidwa, molingana ndi malamulo amene Ambuye Mulungu adapereka kwa ana a anthu. Pakuti adapereka lamulo kuti anthu onse akuyenera kulapa; pakuti adaonetsa kwa anthu onse kuti adali otaika, chifukwa cha kulakwitsa kwa makolo awo.

22 Ndipo tsopano, taonani, ngati Adamu akadapanda kulakwa, iye sakadagwa, koma akadakhalabe m’munda wa Edeni. Ndipo zinthu zonse zomwe zidalengedwa zikadakhala momwe zidalili pamene izo zidalengedwa; ndipo zikadakhala choncho kwa muyaya, ndi kopanda malire.

23 Ndipo iwo sakadakhala ndi ana; kotero akadakhalabe mumkhalidwe wosalakwa, opanda chisangalalo, chifukwa sakadadziwa chisoni; osachita zabwino, chifukwa sakadadziwa tchimo.

24 Koma taonani, zinthu zonse zachitika mu mzeru za iye amene amadziwa zonse.

25 Ndipo Adamu adagwa kuti anthu akhale; ndipo anthu ali, kuti akathe kukhala ndi chisangalalo.

26 Ndipo Mesiya adzabwera mu chidzalo cha nthawi, kuti adzawombole ana a anthu kuchokera m’kugwa. Ndipo chifukwa chakuti awomboledwa kuchoka m’kugwa, iwo akhala omasuka kwa muyaya, odziwa chabwino ku choipa; kuti adzichitire wokha ndipo osati kuchitiridwa, pokhapokha ndi chilango cha lamulo pa tsiku lalikulu ndi lomaliza, molingana mwa malamulo amene Mulungu wapereka.

27 Kotero, anthu ali ndi ufulu molingana ndi thupi; ndipo zinthu zonse zaperekekedwa zomwe zili zofunikira kwa munthu. Ndipo ndi omasuka kusankha ufulu ndi moyo wamuyaya, kudzera mwa Mkhalapakati wamkulu wa anthu onse, kapena kusankha ukapolo ndi imfa, molingana ndi ukapolo ndi mphamvu ya mdyerekezi; pakuti iye amafuna kuti anthu onse akhale osasangalala ngati m’mene iye aliri.

28 Ndipo tsopano, ana anga aamuna, ndidzafuna kuti inu muyang’ane kwa Mkhalapakati wamkulu, ndi kumvetsera malamulo ake aakulu; ndi kukhulupirika ku mawu ake, ndikusankha moyo wamuyaya, molingana ndi chifuniro cha Mzimu wake Oyera.

29 Ndipo musasankhe imfa ya muyaya, molingana ndi chifuniro cha thupi ndi choipa chiri m’menemo, chimene chimapereka kwa mzimu wa mdyerekezi mphamvu yakumanga, ndikukubweretsani pansi ku gahena, kuti akulamulireni inu mu ufumu wake.

30 Ndayankhula mawu ochepa awa kwa inu nonse, ana anga aamuna, m’masiku otsiriza akuyesedwa kwanga; ndipo ndasankha gawo labwino, molingana ndi mawu a mneneri. Ndipo ine ndilibe china chilichonse kupatula kufuna ubwino wamuyaya wa miyoyo yanu. Ameni.

Print