Zofunikira Zoyambirira
Mutu 35: Moyo Pambuyo pa Imfa


Image
Mzinda Wamuyaya, ndi Keith Larson

Khristu adapangitsa kukhala kotheka kuti ife tidzakhale ndi moyo tikadzafa.

Mutu 35

Moyo Pambuyo pa Imfa

Kodi tingakonzekere bwanji moyo wotsatira?

Mizimu Yathu Imakhala Ndi Moyo Ife Tikafa

Ndife ana auzimu a Atate athu Akumwamba. Pamene tidali kukhala nawo kumwamba monga mizimu, tidalibe matupi amnofu. Lidali gawo la dongosolo lawo kuti ife tibadwe padziko lino lapansi ndi kuti mizimu yathu ilandire matupi a mnofu ndi mafupa. Mizimu yathu ndi imene imapereka moyo ku matupi athu amnofu pamene tikukhala padziko lapansi.

Monga momwe kubadwa kudali gawo la dongosolo la Atate athu Akumwamba kwa ife, gawo lina la dongosolo Lawo ndi lakuti ife tidzifa. Tikafa, mizimu yathu imachoka m’matupi athu. Popanda mzimu, thupi lilibe moyo ndipo limaikidwa m’manda.

Koma mizimu yathu idali ndi moyo tisadabadwe, ndipo idzapitilirabe kukhala ndi moyo tikadzamwalira. Tikafa, mizimu yathu imapita kudziko la mizimu kukayembekezera chiukitso, pamene thupi limakhalabe m’manda.

M’dziko la mizimu mizimu yathu idzakhala ndi maonekedwe ofanana ndi pamene tidali kukhala padziko lapansi ndi matupi a mnofu ndi mafupa. Tidzaonana momwe tikuchitira pano. Tidzaganiza mofanana ndi kukhulupilira zinthu zofanana ndi zimene tinkachitira kuno. Amene ali olungama m’moyo uno adzakhalabe olungama. Amene adali osalungama adzakhalabe osalungama. Tidzakhala ndi zilakolako zomwezo tikadzamwalira monga momwe tidaliri tili padziko lapansi pano.

Zokambirana

  • Kodi matupi athu auzimu adachokera kuti?

  • Nanga n’chiyani chimachitika kwa iwo tikafa?

  • Kodi matupi auzimu ndi otani?

Dziko Lauzimu Ndi Malo Ogwilira Ntchito, Kuphunzira, ndi Kudikilira

Aneneri a Atate athu Akumwamba amatiuza zinthu zambiri zokhudza dziko la mizimu. Malo amodzi amatchedwa paradiso. Munthu akafa amene walandira uthenga wabwino ndi kukhala wotsatira wokhulupirika wa Yesu, mzimu wa munthuyo umapita ku paradiso. Kumeneku ndi malo amene anthu amakhala osangalala komanso amtendere. Kumeneko amamasuka ku mavuto, chisoni, ndi zowawa. Angathe kuchita zinthu zambiri zaphindu, monga kuphunzitsa ena za uthenga wabwino kapena kuphunzira zambiri za iwo eni.

Malo ena amatchedwa ndende ya mizimu. Mitundu itatu ya anthu idzakhala kumeneko. Padzakhala iwo amene adali oipa m’moyo uno, amene adakhala ndi moyo wabwino koma osavomereza Uthenga Wabwino, ndi amene sadakhale ndi mwayi wakumva uthenga wabwino.

Aneneri a Atate athu Akumwamba adatiuza kuti mamishonale adzatumizidwa kuchokera pakati pa olungama mu dziko la mizimu kukaphunzitsa uthenga wabwino kwa mizimu yonse ya anthu akufa. Ambiri adzavomereza uthenga wabwino ndi kulapa. Miyambo yopulumutsa yofunikira adzawachitira ndi anthu amoyo mu makachisi a Atate athu a Kumwamba. Achibale kapena mamembala ena a Mpingo amawachitira iwo miyamboyi. Pamenepo adzatha kutuluka m’ndende ya mizimu. Mwanjira imeneyi, Atate athu Akumwamba amapereka mwayi kwa ana ake onse kuti alandire madalitso a uthenga wabwino mosasamala kanthu za nthawi imene adakhala padziko lapansi.

Pamapeto pake onse a m’dziko la mizimu adzaukitsidwa. Pakuuka kwa akufa, mzimu ndi thupi zidzalumikizananso. Ngakhale kuti thupi lavunda ndi kukhala fumbi pamene lidali m’manda, lidzakhala thupi lokuti silidzafa ndi langwiro. Malemba amanena kuti palibe ngakhale tsitsi limodzi la m’Mutu mwathu limene lidzatayike ndi kuti zinthu zonse zidzabwenzeretsedwa m’chimake choyenera ndi changwiro.

Pakuuka kwa akufa thupi ndi mzimu zidzalumikizana, sizidzalekanitsidwanso. Kudzera m’chikondi chake ndi nsembe Yake yaikulu yotetezera ife, Yesu adapereka mphatso yabwino kwambiri imeneyi ya chiukitso kwa munthu aliyense amene adzakhalapo pa dziko lapansi.

Zokambirana

  • Ndi magawo awiri ati amene alipo mu dziko la mizimu?

  • Kodi ndi ndani adzakhala m’paradiso? Kodi mizimu m’paradiso imachita chiyani?

  • Ndi ndani adzakhale mu ndende ya mizimu? Chimachitika ndi chiyani kumeneko?

Tonse Tidzaweruzidwa pa Chiweruzo Chomaliza

Timaweruzidwa nthawi zambiri pa moyo wathu wamuyaya. Tidaweruzidwa pamene tidali kukhala ndi Atate athu Akumwamba kuti tiwone ngati tidali oyenelera kubwera pa dziko lapansi ndi kutenga matupi. Tikuweruzidwa tili pano kuti tiwone ngati ndife oyenera kubatizidwa. Amuna amaweruzidwa kuti awone ngati ali oyenera kupatsidwa unsembe. Timaweruzidwa kuti tiwone ngati ndife oyenera kulowa m’kachisi kuti tilandire madalitso apadera. Tikafa, timaweruzidwa, ndipo mphoto imene tidzalandira idzadalira mmene tidakhalira padziko lapansi.

Tikadzaukitsidwa, tidzabweretsedwa pamaso pa Atate athu Akumwamba kuti tidzaweruzidwe komaliza. Ichi chimatchedwa Chiweruzo Chomaliza. Chiweruzo chomalizachi chidzasankha kumene tipite kukakhala kosatha. Tidzaweruzidwa ndi zimene tidalankhula, kuchita ndi kuganiza m’moyo uno. Tidzaweruzidwa ndi mmene tidatsatira bwino chiphunzitso cha Yesu. Tidzaweruzidwa ndi zolemba zomwe zasungidwa padziko lapansi komanso kumwamba. Atate Athu a Kumwamba adzauza Yesu kuti atiweruze.

Yesu amatikonda kwambiri, koma ndi woweruza wachilungamo ndipo ayenera kutiweruza potengera moyo umene tinkakhala. Zonse zimene taganiza, kunena kapena kuchita, zimalembedwa m’maganizo mwathu komanso m’zolembedwa zimene zasungidwa. Yesu amadziwa ntchito zathu zonse, ndipo tikaima pamaso pake tidzazikumbukiranso.

Zokambirana

  • Tchulani nthawi zina pamene timaweruzidwa.

  • Ndi zinthu zina ziti zimene tidzaweruzidwe nazo?

Timasankha mwa Zochita Zathu Zatsiku ndi Tsiku Zomwe Zidzatichitikira Tikadzafa

Ngati tichita zabwino m’moyo wathu, tidzadzikonzekeretsa kukakhala kosatha ndi Atate athu Akumwamba ndi anthu abwino a padziko lapansi. Ngati sitinatsatire malamulo a Atate athu Akumwamba, tidzamva chisoni kwambiri tikaimilira pamaso pa Yesu kuti atiweruze.

Aneneri adanena kuti mawu athu, malingaliro athu, ndi ntchito zathu zonse zidzatitsutsa ngati zakhala zoipa. Iwo anena kuti oipa adzaima pamaso pa Yesu ndi manyazi ndi kulakwa kwakukulu ndipo adzafuna kubisala pamaso pawo.

Kwa munthu aliyense amene wakhala pa dziko lapansi, ndiye kuti tsiku lachiweruzo lidzakhala losangalatsa kapena lachisoni. Tiyenera kukonzekera mnyengo yamtsogolo iyi kuti tsiku lathu lidzakhale losangalatsa. Tikufuna kudzakwanitsa kuima pamaso pa Atate athu Akumwamba mopanda manyazi ndi kuwamva akunena kuti avomereza zimene tidachita pa moyo wathu.

Tikuyenera kuganizira za chiweruzo chomalizachi. Tikuyenera kukhala okhulupirika mwa Yesu Khristu ndi kulapa machimo athu mpaka mapeto a moyo wathu kuti tikhale okonzeka. Ndi njira yokhayo imene tingakhalire omasuka ku machimo onse ikadzakwana nthawiyo. Ngati tikhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu Khristu ndi kulapa machimo athu onse, Atate athu a Kumwamba adzatikhululukira machimo athu ndi kutithandiza kukhala opanda uchimo kotheratu. Ngati tikhala okhulupirika kwa Yesu Khristu, tidzakhala m’moyo wathu wochita zabwino, kulingalira zinthu zabwino, ndi kulankhula mawu abwino. Tidzapewa anthu, mabuku, ndi malo amene angatichititse kuganiza zoipa kapena kuchita zinthu zopanda chilungamo m’njira iliyonse.

Atate athu Akumwamba amatikonda aliyense wa ife ndipo amafuna kuti tikhale oyenelera kubwelera pamaso pawo. Ngati tikufuna kukhala ndi iwo ndi anthu abwino amene timawakonda, tikuyenela kukhala ndi chikhulupiliro mwa Yesu Khristu ndi kuchita zimene amatilamula kuchita. Tikuyeneranso kuthandiza mabanja athu kukhala ndi moyo wabwino. Atate athu Akumwamba adzatithandiza. Iwo adatipatsa uthenga wabwino kuti utisonyeze njira ndipo atiuza kuti tidzipemphera kwa iwo nthawi zonse kuti atithandize.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani maganizo ndi zochita zathu za tsiku ndi tsiku zili zofunika kwambiri?

  • Kodi mungatani kuti muwongolere maganizo anu, mawu, ndi zochita zanu?

  • Ndi chifukwa chiyani tikufunikira thandizo la Atate athu Akumwamba kuti tikhale amngwilo?

  • Kodi ndi chifukwa chiyani kudzera mwa chikhulupiliro mwa Yesu Khristu mokha ndipamene tingaweruzidwe kukhala oyenera kukhala ndi Atate athu Akumwamba?

Print