Zofunikira Zoyambirira
Mutu 9: Aneneri


Mutu 9

Aneneri

Kodi ndani amene amalankhula m’malo mwa Atate athu Akumwamba padziko lapansi masiku ano ndipo angatiuze zimene Atate athu Akumwamba akufuna kuti tidziwe ndi kuchita?

Mneneri Ndi Munthu Amene Amayankhulira Atate athu Akumwamba

Atate athu Akumwamba amasankha munthu woti adziwayankhulira padziko lapansi. Munthu ameneyu amatchedwa mneneri. Mneneriyu amakonda Atate athu Akumwamba ndipo amachita zinthu zimene Atate athu Akumwamba amafuna kuti adzichita. Atate athu Akumwamba amaphunzitsa mneneri zinthu zimene tiyenera kudziwa ndi kuchita. Mneneri ndiye amatiuza zinthu zimenezo. Pamene mneneri akuyankhula m’malo mwa Atate athu a Kumwamba, amanena zimene Atate athu Akumwamba Eniwake anganene ngati Atate athu Akumwamba akuyankhula nafe.

Izi ndi zina mwa zinthu zimene mneneriyu amatiuza:

  • Iye amatiuza kuti Yesu ndi Mwana wa Atate athu Akumwamba, kuti Yesu ndi Mpulumutsi wathu, ndi kuti zimene Yesu adaphunzitsa n’zoona.

  • Iye amatiphunzitsa zinthu zimene Atate athu Akumwamba adatiuza kuti tizichita.

  • Iye amatiuza kuti tisiye kuchita zoipa.

  • Iye amatiuza zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo.

Atate athu Akumwamba wokha ndi amene angasankhe mneneri. Anthu sangasankhe mneneri. Munthu sangadzisankhe yekha kukhala mneneri. Atate athu Akumwamba amapatsa mneneriyu ulamuliro wochita ntchito Yake ndi kuwayankhulira. Munthu sangayimire Atate athu Akumwamba ngati alibe ulamuliro umenewu.

Zokambirana

  • Mneneri amalankhula za yani?

  • Kodi zina mwa zinthu zimene mneneri amatiuza ndi ziti?

Atate athu Akumwamba Amatumiza Aneneri Kuti Adzatithandize

Atate athu Akumwamba nthawi zonse amasamala za ana awo padziko lapansi. Kuyambila nthawi ya Adamu, akhala akutumiza aneneri kuti athandize ana awo. Amatumiza aneneri kuti akachenjeze anthu za ngozi. Iwo amawatumiza kuti akachotse anthu ku mavuto. Amawatuma kuti akathandize anthu kukonzekera zochitika zazikulu. Awa ndi ena mwa aneneri amene Atate athu Akumwamba adawatuma:

  1. Nowa: Adachenjeza anthu kuti Atate athu Akumwamba adzatumiza chigumula kuti chiwawononge ngati sasiya kuchita zoipa.

  2. Abrahamu: Iye adamvera Atate athu Akumwamba ndipo adaphunzitsa ana ake kumvera Atate athu Akumwamba. Atate athu Akumwamba adalonjeza kuti adzapereka zinthu zambiri kwa Abrahamu ndi mibadwa yake.

  3. Mose: Adatsogolera anthu a Israyeli kutuluka mu Igupto kupita ku dziko limene Atate athu Akumwamba adawakonzera.

M’masiku athu anonso, Atate athu Akumwamba amatumiza aneneri. M’modzi mwa aneneri amene adakhalako kalekale adali munthu wina dzina lake Joseph Smith. Iye ankakhala ku United States of America. Mu 1820 Joseph Smith adali ndi zaka 14. Pa nthawiyo, anthu ambiri adalowa m’mipingo yosiyanasiyana n’kumafunafuna mpingo woona. Yosefe ankafuna kukhala munthu wabwino ndi kupeza mpingo weniweni wa Atate athu Akumwamba.

Tsiku lina Joseph ankawerenga buku lopatulika lotchedwa Baibulo. Adawerenga kuti ngati mukufuna kudziwa kanthu, muyenera kufunsa Atate athu Akumwamba, ndipo Atate athu Akumwamba adzakuuzani. Adakhulupira kuti Atate athu Akumwamba adzamuuzadi zinthu zimene akuyenera kuchita. Adaganiza zokamba pemphero lapadera kwa Atate athu Akumwamba.

Tsiku lina m’mawa, Joseph adapita kutchire kukapemphera. Pamene adali kupemphera, kuwala kowala kwambiri kuposa dzuŵa kudatsika kuchokera kumwamba. M’kuunikaku adaona Atate athu Akumwamba ndi Yesu Khristu. Atate athu Akumwamba adaloza kwa Yesu nati, “Uyu ndiye Mwana Wanga Wokondedwa. Mverani Iye!”

Joseph adamvera zonse zimene Yesu adamuuza, ndipo adatsatira malangizo amene Yesu adamupatsa.

Pamene Joseph ankakula, Atate athu Akumwamba adamusankha kuti akhale mneneri Wawo. Iye adali mneneri wamkulu. Adaphunzitsa anthu zinthu zimene Atate athu Akumwamba ankafuna kuti iwo azichita.

Joseph Smith adamwalira mu 1844. Atamwalira, Atate athu Akumwamba adasankha munthu wina kuti akhale mneneri. Masiku ano, nthawi iliyonse mneneri akamwalira, Atate athu Akumwamba amasankha munthu wina kuti alankhule m’malo mwawo padziko lapansi.

Atate athu Akumwamba atumiza aneneri m’masiku athu ano.

Image
M’neneri Joseph Smith

Joseph Smith

Image
Brigham Young

Brigham Young

Image
John Taylor

John Taylor

Image
Wilford Woodruff

Wilford Woodruff

Image
Lorenzo Snow

Lorenzo Snow

Image
Joseph F. Smith

Joseph F. Smith

Image
Heber J. Grant

Heber J. Grant

Image
George Albert Smith

George Albert Smith

Image
David O. Mckay

David O. McKay

Image
Joseph Fielding Smith

Joseph Fielding Smith

Image
Harold B. Lee

Harold B. Lee

Image
Spencer W. Kimball

Spencer W. Kimball

Image
Ezra Taft Benson

Ezra Taft Benson

Image
Howard W. Hunter

Howard W. Hunter

Image
Gordon B. Hinckley

Gordon B. Hinckley

Image
Thomas S. Monson

Thomas S. Monson

Image
Russell M. Nelson

Russell M. Nelson

Zokambirana

  • Kodi ena mwa aneneri amene Atate athu Akumwamba adasankha ndi ati?

  • Kodi Joseph Smith adachita chiyani?

Pali Mneneri Padziko Lapansi Masiku Ano

Atate athu Akumwamba amakonda ana awo amene ali padziko lapansi lero. Amadziwa kuti tiri ndi mavuto ambiri. Iwo atumiza mneneri kuti atithandize. Iwo amayankhula ndi mneneriyo masiku ano monga mmene adayankhulira ndi aneneri m’nthawi zakale. Atate athu Akumwamba amapereka malangizo kwa mneneriyu a kwa anthu a dziko lonse lapansi. Mneneri ndi munthu yekhayo amene angalandire malangizo kuchokera kwa Atate athu Akumwamba pa dziko lonse lapansi.

Mneneri amene ali ndi moyo masiku ano ndi munthu wamkulu. Iye amakonda Atate athu Akumwamba ndipo amafuna kuwamvera. Atate athu Akumwamba amauza mneneriyo zinthu zimene amafuna kuti tidziwe ndi kuchita.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani Atate athu Akumwamba atumiza mneneri lero?

  • Kodi mneneriyo amalandira malangizo kwa ndani?

  • Ndichifukwa chiyani tingakhulupilire zonse zimene mneneri akutiuza?

Atate athu Akumwamba Amatithandiza Tikamamvera Malangizo Amene Amapereka kwa Mneneri

Atate athu Akumwamba atilamula kuti tizimvera mneneri wawo pamene mneneriyo akuyankhula m’malo mwawo. Tikamamvera malangizo amene Atate athu Akumwamba amapereka kwa mneneri, timaphunzira mmene tingakhalire ngati Atate athu Akumwamba. Timaphunzira zinthu zimene tikuyenera kuchita. Timaphunzira mmene tingathetsere mavuto tikakhala nawo. Atate athu Akumwamba adzatithandiza, ndipo tidzakhala ndi mtendere mu mtima mwathu.

Zokambirana

  • Ndichifukwa chiyani tikuyenera kumvera zimene mneneri akutiuza kuti tichite?

  • Kodi Atate athu Akumwamba adzatithandiza bwanji tikamachita zinthu zimene iwo amalangiza mneneri kuti atiuze?

Print