Zofunikira Zoyambirira
Mutu 21: Miyambo


Mutu 21

Miyambo

Kodi abambo ndi anyamata angachite chiyani ndi unsembe?

Ndi Unsembe, Amuna Ali ndi Ulamuliro womwewo Wochita Miyambo imene Yesu Adachita

Miyambo ndi zochitika zopatulika zochitidwa ndi iwo amene apatsidwa ulamuliro wa unsembe. Ubatizo, chitsimikiziro, kusanjika manja pa odwala kuti awachiritse, ndi kudalitsa ndi kupereka m’gonero ndi zina mwa miyambo.

Pamene Yesu adali padziko lapansi, adachita miyambo yothandiza anthu. Iye adachiritsa odwala ndi kuchititsa akhungu kuona. Iye adachititsa ogontha kuti amve ndipo ngakhale kubwezeretsa akufa kukhalanso ndi moyo. Iye adapereka mgonero kwa otsatira ake.

Yesu wapereka kwa amuna amene ali ndi unsembe mphamvu ndi ulamuliro wochita miyambo. Azibambo ndi anyamata oyenelera omwe ali ndi unsembe akhonza kuchititsa miyambo. Amachita miyamboyi kuti atidalitse ndi kutithandiza kukhala ngati Atate athu Akumwamba. Miyambo imatithandiza kukonzekera kubwelera ndi kukakhala ndi Iye.

Chifukwa Yesu wapereka unsembe kwa anthu padziko lapansi masiku ano, tikhonza kulandira madalitso ambiri pa moyo wathu. Tikhonza kubatizidwa, kulandira mphatso ya Mzimu Woyera, ndikutsindikizidwa ndi mabanja athu kwa muyaya.

Ma pulezidenti a makolamu akuyenera kuphunzitsa mamembala awo momwe angachitire miyambo. Ngati mwamuna amene ali ndi unsembe akuyenera kuchita mwambo ndipo sakudziwa m’mene angachitire, afunse pulezidenti wakolamu yake kuti amuphunzitse.

Zokambirana

  • N’chifukwa chiyani miyambo imachitidwa?

Image
Mgonero otsiliza, wolemba Carl Heinrich Bloch

Yesu adayambitsa mgonero pa M’gonero Wotsiliza ndi Atumwi Ake.

Miyambo Imachitidwa Kuti Tithandizidwe

Ubatizo

Ubatizo ndi mwambo oyamba mu Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu. Anthu asadabatizidwe ayenera kukhulupilira Yesu, kulapa machimo awo komanso kuchita zimene Yesu adaphunzitsa.

Ndi munthu yekhayo amene ali ndi unsembe akhonza kubatiza ena. Kuti abatize munthu aliyense, ayenera kukhala ndi chilolezo kuchokera kwa bishopu kapena pulezidenti wa nthambi. Munthu amene akubatiza amalowa m’madzi ndi munthu woti abatizidwe. Munthu amene akubatiza amatchula dzina la wobatizidwayo n’kupemphera pemphero lalifupi. Kenako amalowetsa munthu amene akubatizidwayo kwathunthu pansi pa madzi ndi kumutulutsa m’madzimo.

Pemphero limene munthuyo amanena ndilakuti: “Popatsidwa ulamuliro ndi Yesu Khristu, ndikukubatiza mu dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera. Ameni.”

Zokambirana

  • Kodi mwambo oyamba mu Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu ndi chiyani?

Kupereka mphatso ya Mzimu Woyera

Munthu akabatizidwa, azibambo amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki amaika manja pa Mutu wamunthuyo, ndipo mmodzi waiwo amapemphera mwapadera. M’pemphero limenelo, iwo amatsimikizira munthuyo kukhala membala wa Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza ndi kunena kwa iye kuti, “Landirani Mzimu Woyera.” Izi zikutanthauza kuti munthuyo amalandira ufulu wokhala ndi chitsogozo cha Mzimu Woyera nthawi zonse, pamene munthuyo amayesetsa moona mtima kumvera malamulo a Yesu. Kupereka uku kwa mphatso ya Mzimu Woyera ndi mwambo wachiwiri mu Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu. Ndiye amene akuchita mwambowu amamupatsa munthuyo madalitso amene adzodzedwa ndi Mzimu Woyera. Amuna ayenera kukhala ndi chilorezo cha bishopu wawo kapena pulezidenti wa nthambi kuti apatse munthu mphatso ya Mzimu Woyera.

Zokambirana

  • Kodi ndindani amene angapereke mphatso ya Mzimu Woyera?

Kudzodzedwa ku Unsembe

Kupereka kwa munthu unsembe ndi mwambo. Izi ziyenera kuchitidwa ndi amuna ena omwe ali ndi unsembe. Iwo ayenera kukhala ndi chilolezo cha bishopu kapena pulezidenti wa nthambi kuti apereke Unsembe wa Aroni, ndi wa pulezidenti wa siteki kuti apereke Unsembe wa Melkizedeki. Ndi ulemu waukulu kwa mzibambo kapena mnyamata kulandira unsembe. Amene amasunga malonjezo amene apanga pamene alandira unsembe adzakhala ndi unsembe kwa muyaya.

Zokambirana

  • Ndi ndani angapereke unsembe kwa ena?

Mgonero

Munthu amene ali ndi unsembe amanena pemphero kuti adalitse mkate ndi madzi. Kenako iye kapena munthu wina amene ali ndi unsembe amapereka kwa mamembala a Mpingo chidutswa cha mkate kuti adye ndi madzi kuti amwe. Izi zimatchedwa mgonero. Mgonero ndi mwambo.

Mkate ndi madzi ndi zifaniziro za thupi ndi mwazi wa Yesu. Zimatithandiza kukumbukira kuti Iye adapereka nsembe* moyo wake chifukwa cha ife. Tiyenera kukumbukira chikondi chake pa ife. Tiyenera kuyamikira kuti wapanga kuthekera kuti tikhululukidwe machimo athu ndi kudzakhalanso ndi Atate athu Akumwamba.

Nthawi iliyonse imene timatenga mgonero, timapanganso malonjezo amene tidapanga kwa Atate athu Akumwamba pamene tidabatizidwa. Timalonjezanso kuti tidzakumbukira nthawi zonse Yesu, kuti ndife ofunitsitsa kutchedwa ndi dzina lake, ndi kuti tidzamvera malamulo ake nthawi zonse. Tisanatenge mgonero, tiyenera kulapa zoipa zimene tachita ndi kuganizira malonjezo amene tidalonjeza.

Atate athu Akumwamba amatilonjeza kuti tikachita zinthu zimene tidalonjeza kuti tidzazichita, adzatumiza Mzimu Woyera kuti ukhale nafe nthawi zonse.

Kudalitsa Mkate

Yesu watipatsa mapemphero apadera a mgonero. Ili ndi pemphero la mkate:

“O Mulugu, Atate Wamuyaya, tikukupemphani mu dzina la Mwana wanu, Yesu Khristu, kuti mudalitse ndi kuyeretsa mkate uwu kwa miyoyo yonse imene idye, kuti adye pokumbukira thupi la Mwana wanu, ndi kuchitira umboni kwa inu, O Mulungu, Atate Wamuyaya, kuti iwo ali kulolera kutenga paiwo dzina la Mwana wanu, ndi kumukumbukira iye nthawi zonse ndi kusunga malamulo amene adawapereka kwa iwo; kuti akhale nao Mzimu wake nthawi zonse. Ameni.”

Kudalitsa madzi

Ili ndi pemphero la madzi:

“O Mulungu, Atate Wamuyaya, tikukupemphani mu dzina la Mwana wanu Yesu Khristu, kuti mudalitse ndi kuyeretsa madzi awa kumiyoyo ya onse amene amwe madzi awa, kuti achite ichi pokumbukira mwazi wa Mwana wanu, umene udakhetsedwa chifukwa cha iwo; kuti achitire umboni kwa Inu, O Mulungu, Atate Wamuyaya; kuti azimukumbukira iye nthawi zonse, kuti akhale nawo Mzimu wake. Ameni.”

Zokambirana

  • Kodi mgonero ndi chiyani?

  • Kodi tiyenera kuganizira chiyani pamene ansembe akudalitsa ndi kupereka m’gonero?

  • Kodi timalonjeza chiyani tikamalandira m’gonero?

Madalitso a Ana

Azibambo omwe ali ndi unsembe akhonza kudalitsa ana, kawirikawiri masabata angapo ana atabadwa. Ayenera kukhala ndi chilorezo cha bishopu kapena pulezidenti wa nthambi kuti achite izi. Bambo wamwanayo akhonza kudalitsa mwanayo ngati ali ndi Unsembe wa Melkizedeki. Ngati alibe Unsembe wa Melkizedeki, sangadalitse mwanayo kapena kukhala pabwalo ndi azibambo omwe akudalitsa mwanayo. Akhonza kupempha munthu amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki kuti adalitse mwanayo. Bamboyo, ngati ali ndi Unsembe wa Melkizedeki ndipo ali woyenera, kapena munthu wina amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki, amanyamula mwanayo m’manja mwake, mothandizidwa ndi ena amene ayeneranso kukhala ndi Unsembe wa Melkizedeki, ndipo amanena pemphero. M’pempherolo, amatchula Atate athu Akumwamba, ndikunena kuti akuchita mwambowu mwa ulamuliro wa Unsembe wa Melkizedeki, ndipo amapatsa mwanayo dzina limene makolo ake alisankha. Kenako amadalitsa mwanayo monga Mzimu Woyera amukhudzira iye.

Zokambirana

  • Kodi munthu amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki amachita chiyani akamadalitsa mwana?

Madalitso a Anthu Odwala

Pamene anthu adwala, akhonza kufunsa azibambo omwe ali ndi Unsembe wa Melkizedeki kuti awadalitse. Choyamba, mmodzi wa ansembe amadzodza munthu wodwala. Amachita zimenezi potsanulira mafuta opatulika pang’ono pa mutu pa munthuyo, kenako n’kuika manja ake pa mutu pa munthuyo ndi kupemphera pemphero lapadera. Zikatha izi, ansembe amaika manja awo paMutu wa munthuyo, ndipo mmodzi waiwo amatsindikiza kudzodza ndi kudalitsa munthuyo monga momwe wauzidwira ndi Mzimu Woyera. Anthu ambiri amapeza bwino kapena amachilitsidwa kumatenda awo atalandira dalitso la unsembe. Madalitso a odwala ndi mwambo.

Mafuta amene amagwiritsidwa ntchito podzodza odwala amapatulidwa ku ntchito imeneyi pa mwambo wina. Kuti ayeretse mafutawo, mzibambo wina amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki amanyamula mafuta ochepa muchotengela chotsegula ndikunena pemphero lapadera.

Mzibambo amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki sachita kufunika chilorezo kuchokera kwa bishopu, pulezidenti wa nthambi, kapena pulezidenti wa siteki kuti achite miyamboyi.

Zokambirana

  • Ndi ndani angadalitse anthu akadwala?

Bambo Akhonza kudalitsa Anthu a Banja Lake

Bambo amene ali ndi Unsembe wa Melkizedeki akhonza kudalitsa mamembala a banja lake. Angachite zimenezi ngati wachibale akudwala kapena akufunika thandizo lapadera. Iye sachita kufunikira chilorezo kuchokera kwa bishopu, pulezidenti wa nthambi, kapena pulezidenti wa siteki kuti achite izi. Bamboyo amaika manja ake pa mutu pa munthuyo ndi kupemphera. Mu pempherolo, amapatsa munthuyo madalitso amene Mzimu Woyera umamuuza m’maganizo mwake kuti apereke. Kudalitsa achibale ndi mwambo.

Zokambirana

  • Kodi ndi nthawi yanji yomwe bamboo angadalitse anthu a m’banja lake?

Miyambo ina Ndi Yofunika Kwambiri Kwa kuti Aliyense Ayenera Kuilandira

Miyambo ina ya unsembe ndi yofunikira kuti munthu abwelere ndi kukakhala ndi Atate athu Akumwamba. Iwiri ya miyambo imeneyi ndi ubatizo ndi kulandira mphatso ya Mzimu Woyera. Azibambo ndi anyamatana akuyeneranso kulandira unsembe. Miyambo ina, madalitso amene bambo amapereka kwa banja lake, amachitidwa pamene tifunikira chithandizo ndi chitonthozo.

Zokambirana

  • Miyambo ina ndi iti?

  • Kodi madalitso ati amane iliyonse mwa iyo imabweretsa?

Print