Zofunikira Zoyambirira
Mawu Oyamba


Mawu Oyamba

Bukhuli lidzakuthandizani kuphunzira ndi kuphunzitsa mfundo zoyambilira za uthenga wabwino wa Yesu Khristu. Kudziwa mfundo zimenezi kudzakuthandizani kumvetsetsa cholinga cha moyo komanso m’mene mungakhalire osangalala. Mfundo zomwe zafotokozedwa mubukuli ndizoona. Pamene mukuwerenga mfundo izi ndi kusinkhasinkha ndi kupemphera za izo, mudzazidziwa mwanokha, ndipo Mzimu Woyera udzachitira umboni kwainu, kuti ndizoona.

Mutha kugwiritsa ntchito bukuli pazifukwa zosiyanasiyana. Mukhonza kugwiritsa ntchito powerenga ndi kuphunzira panokha. Mungaligwiritse ntchito pokonzekera kulalikira kapena pofotokozera ena uthenga wabwino.

Mutha kugwiritsa ntchito bukuli powerenga mawu pabanja ndi kunyumba madzulo pabanja. Phunziro lirilonse liri ndimafunso amene inuyo monga kholo kapena mphunzitsi mungafunse kwa ana aang’ono kuti muwone m’mene akumvera.

Mukamaphunzitsa za m’bukuli, mutha kuphunzitsa mitu yoposa umodzi m’kalasi kapena kuthera nthaŵi yochuluka m’kalasi pa Mutu umodzi. Onetsetsani kuti ophunzira anu amvetsetsa bwino mfundo musadapitilire ku Mutu wina. Ngati muli ndi malemba amene adawamasulira kale, yang’anani malembawo ndi kukambirana.

Monga mphunzitsi, kumbukirani kuti mutha kukhala ndi magawo 21 mpaka 25 okha pa chaka kuphunzitsa kalasi. Izi zikutanthauza kuti mutha kuphatikiza maphunziro 10 kapena kupitilira apo. Ganizirani zosowa za kalasi yanu ndikusankha maphunziro omwe mungaphatikize komanso maphunziro omwe mungafune kutherapo nthawi yochulukirapo.

Chakumapeto kwa chaka mukhonza kufuna kuthera kalasi imodzi kapena awiri kukambirana za Mfundo za Chikhulupiliro, zomwe zikuwonekanso m’buku lino. Mukhonzanso kugwiritsa ntchito Mfundo za Chikhulupiliro pounikira maphunziro.

Makolo ndi aphunzitsi, pemphelerani chitsogozo pamene mukukonzekera ndikuphunzitsa maphunzirowa. Lolani Mzimu Woyera ukutsogolereni mu kumvetsa kwanu ndi mu chiphunzitso chanu. Membala aliyense amene angakwanitse awerenge mituyo ndi kubwera wokonzeka kugawana ndi anthu ena pazokambirana.

Mukawona liwu lolembedwa ndi *, mutha kupeza tanthauzo lake pagawo la “Mawu Oyenera Kudziwa” kumapeto kwa bukuli. Mawu ena aphatikizidwanso m’menemo kuti akuthandizeni kumvetsa tanthauzo lake.

Mulungu akudalitseni pamene mukuwerenga mwapemphero zoona za m’bukuli.

Print