Zofunikira Zoyambirira
Mutu 34: Mileniyamu


Mutu 34

Mileniyamu

Kodi Mileniyamu ndi chiyani? Kodi moyo padziko lapansi udzakhala wotani m’kati mwa Mileniyamu?

Anthu Olungama Adzakhala Padziko Lapansi mu Mileniyamu

Yesu akadzabweranso, adzalamulira dziko lapansi kwa dzaka 1,000. Nthawi imeneyi idzatchedwa Mileniyamu.

Mileniyamu idzakhala nthawi ya mtendere ndi chilungamo. Yesu adzayeretsa dziko lapansi ku uchimo Mileniyamu isadayambe. Anthu onse oipa adzawonongedwa. Anthu olungama okha ndi amene adzapulumuke kuti adzakhale padziko lapansi pa nthawiyo. Satana sadzakhalanso ndi mphamvu pa anthu mpaka kumapeto kwa Mileniyamu.

Mneneri Joseph Smith adanena kuti anthu ochokera kumwamba adzayendera dziko lapansi nthawi zambiri mu Mileniyamu. Adzathandiza pa ntchito yochitidwa m’kachisi ndi ntchito yaumishonale.

Zokambirana

  • Kodi Mileniyamu ndi chiyani?

  • Kodi ndani amene adzakhala padziko lapansi mu Mileniyamu?

  • Taganizirani mmene zingakhalire kukhala m’malo amene mulibe zoipa.

Ntchito Ziŵiri Zazikulu Zidzachitika m’Mileniyamu

Ntchito yaikulu yoyamba kuchitidwa ndiyo kuchita miyambo mu kachisi kwa anthu amoyo ndi akufa. Anthu amene adzaukitsidwa adzathandiza anthu amene adzakhale padzikoli kuti apeze mayina a achibale awo amene adamwalira ndiponso kuti akonze zolakwika zimene zili m’mabuku.

Miyambo yonse yofunikira kuti atsindikize mabanja pamodzi idzachitidwa mu makachisi. Mabanja adzalumikizana kuchokera ku mbadwo umodzi kwa wina kufikira kwa Adamu.

Ntchito ina yaikulu ndi kulalikira uthenga wabwino. Aliyense adzamva uthenga wabwino ndikuulandira. Anthu ena abwino amene si mamembala a Mpingo wa Yesu adzakhalabe ndi moyo padziko lapansi Ulamuliro wa Mileniyamu ukadzayamba. Koma pamapeto pake, anthu onse adzadziwa ndi kunena kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wa dziko lapansi.

Zokambirana

  • Kodi ndi ntchito zazikulu ziŵiri ziti zimene zidzachitidwa mu Mileniyamu?

Kodi Moyo Udzakhala Wotani m’Mileniyamu

M’kati mwa Mileniyamu, dziko lapansi lidzakhala monga mmene lidaliri pamene Adamu ndi Hava ankakhala m’munda wa Edeni. Sipadzakhala nkhondo. Yesu adzalamulira mpingo ndi boma. Malamulo onse adzazikidwa pa mfundo zoona ndi zolungama. Padzakhala mizinda ikuluikulu iwiri. Umodzi udzakhala mu Yerusalemu. Likulu lina lidzakhala Yerusalemu Watsopano, ku Mmawa kwa America.

Anthu adzakhala pamodzi mwa mtendere ndi mwa chikondi. Nyama zonse, ngakhale zimene panopa ndi adani, zidzakhalira limodzi mwamtendere. Sizidzamenyananso wina ndi mnzake.

Sipadzakhala matenda, ndipo sipadzakhalanso imfa. Anthu akadzakalamba sadzafa ngati mmene timachitira panopa. Adzasintha m’kamphindi kuchokera mmene tilili tsopano kupita ku mkhalidwe wosafa, kutanthauza kuti sadzafanso.

Udzakhala mwayi waukulu kukhala ndi moyo mkati mwa Mileniyamu. Zinthu zimene sitikuzimvetsa tsopano zidzamveka bwino kwa ife. Moyo udzakhala monga momwe uliri tsopano, kupatula kuti zonse zidzachitidwa mwa chikondi ndi mwa mtendere. Anthu adzapitiriza kukhala ndi ana ndi kulera, kubzala ndi kukolola mbewu, ndi kumanga nyumba.

Zokambirana

  • Kodi dziko lapansi lidzakhala lotani m’kati mwa Mileniyamu?

Kulimbana Komaliza Kumodzi Kudzachitika Chakumapeto kwa Mileniyamu

Chakumapeto kwa Mileniyamu, Satana adzayambanso kukhala ndi mphamvu padziko lapansi. Anthu ena adzamukhulupilira. Satana ndi amene amamutsatira adzamenyana ndi anthu amene amatsatira Yesu. Pankhondo imeneyi, Satana ndi amene amam’tsatira adzagonjetsedwa kwamuyaya. Pambuyo pa nkhondo imeneyi, anthu adzaweruzidwa, ndipo onse adzapatsidwa mwayi wokhala m’maufumu amene adakonzekera.

Zokambirana

  • Kodi ndi chiyani chidzachitike kumapeto kwa Mileniyamu?

Print