Zofunikira Zoyambirira
Mutu 23: Nsembe


Mutu 23

Nsembe

Kupereka china chake kuti tithandize wina ndi gawo la dongosolo la Atate athu Akumwamba kutithandiza ife kukhala monga Iwo. Kodi mudayamba mwakhalapo ndi chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chosiya chinachake kuti muthandize wina?

Yesu adapereka Nsembe Moyo Wake Chifukwa Cha ife

Kuti timvere Atate athu Akumwamba, nthawi zambiri tiyenera kupereka nsembe. Kupereka nsembe ndiko kusiya chinthu kuti uthandize wina. Yesu adapereka nsembe yaikulu kwambiri. Adavutika chifukwa cha machimo athu. Kenako adapereka moyo wake chifukwa cha ife.

Chifukwa chakuti Yesu adapereka moyo wake chifukwa cha ife, aliyense adzakhalanso ndi moyo pambuyo pa imfa. Tonse tidzakhala ndi thupi langwiro limene silidzafanso. Ichi chimatchedwa chiukitso. Ndiponso, amene ali ndi chikhulupiliro mwa Yesu, kulapa machimo awo onse, adzakhululukidwa machimo awo chifukwa cha zimene Yesu adachita ndipo adzakhoza kubwelera kwa Atate athu Akumwamba.

Kuyambira pa nthawi imene Adamu adakhala ndi moyo mpaka nthawi ya Yesu Khristu, anthu ankapereka nsembe za nyama kwa Atate athu Akumwamba. Anthu ankasankha nyama zabwino kwambiri pa nkhosa kapena ng’ombe zawo kuti azipereke nsembe. Nthawi zonse zidali zoyamba kubadwa zazimuna. Pambuyo posankha nyama zoyenera, anthu ankazipha ndi kuotcha magawo ena a nyamazo monga nsembe kwa Atate wathu Akumwamba.

Anthu adapereka nsembe zimenezi kuti amvere lamulo la Atate athu Akumwamba. Mwanjira imeneyi, iwo ankasonyeza kufunitsitsa kwawo kumvera Atate athu Akumwamba ngakhale pamene zimenezo zidatanthauza kusiya chinthu chimene chidali chofunika kwa iwo. Atate athu Akumwamba adawauza kuti adzipereka nsembe nyama kuti adziwakumbutsa kuti adzapereka Mwana wawo nsembe m’malo mwawo. Yesu, Mwana woyamba kubadwa, wa Atate athu Akumwamba, adzabwera padziko lapansi ndipo adzakhala wangwiro m’njira iliyonse. Iye adzalola kuti aperekedwe nsembe chifukwa cha machimo athu.

Yesu atapereka moyo wake, adalamula anthu kuti asamaperekenso nsembe ya nyama. Adatipatsa mgonero kuti tizikumbukira nsembe yaikulu imene adapereka chifukwa cha ife. Mkate ndi madzi za mgonero zimaimira thupi ndi mwazi wa Yesu, zimene adapeleka chifukwa cha ife pamene adafa.

Zokambirana

  • Kodi nsembe za nyama kalelo zinkaimira chiyani?

Nsembe Ndi Gawo la dongosolo la Atate athu Akumwamba Kwa Ife

Atate athu Akumwamba tsopano amafuna kuti tidzipereka nsembe m’njira ina. Amatilamula kuti tidzipereka nsembe ya mtima wosweka ndi mzimu wolapa. Izi zikutanthauza kusiya machimo athu ndi kunyada kwathu. Kumatanthauza kukhala wofunitsitsa kukumbukira Yesu nthaŵi zonse ndi kusunga malamulo Ake, pakusaona za mtengo wake. Izi zikutanthauza kuti:

  1. Tiri ndi chikhulupiliro mwa Yesu, timalapa machimo athu, tidabatizidwa, ndipo timasunga malamulo a Yesu.

  2. Timauza anthu ena za chikhulupiliro chathu mwa Yesu kuti akhale otsatira ake ndi kulowa mpingo wake.

  3. Ndife okonzeka kuchita ntchito iliyonse mu mpingo wa Yesu imene iye akufuna kuti tichite.

  4. Amuna ndi okonzeka kulandira unsembe ndi kuthandiza banja lawo ndi anthu ena kukhala munjira yoti akonzekere kubwelera kwa Atate athu Akumwamba m’moyo wotsatira.

Kuti tibwelere kwa Atate athu Akumwamba, tiyenera kukhala okonzeka kupereka chirichonse chimene Yesu watipempha. Mtumwi Paulo adanena kuti tiyenera kugwiritsa ntchito nthawi yathu yapadziko lapansi kuchita zonse zimene tingathe kuti tithandize pa ntchito ya Yesu.

Zokambirana

  • Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakumbukira nsembe ya Yesu masiku ano?

Munthu wina wachuma adam’funsa Yesu zimene ayenera kuchita kuti akakhale ndi Atate athu Akumwamba kwamuyaya. Yesu adamuuza kuti amvere malamulo onse a Atate athu Akumwamba. Munthu wachumayo adayankha kuti adamvera malamulowo kuyambira ali wamng’ono. Yesu adamuuza kuti pali chinthu chinanso chimene ayenera kuchita. Ayenera kugulitsa zonse zomwe adali nazo. Kenako ayenera kupereka ndalamazo kwa osauka ndi kutsatira Yesu. Munthu wachuma uja atamva zimenezi adamva chisoni. Sadafune kusiya zinthu zonse zimene adali nazo ndi kutsatira Yesu.

Munthu wachumayo adali munthu wabwino. Iye adayesetsa ndi mtima wonse kumvera malamulo. Koma Yesu atamupempha kuti apereke zinthu zonse zimene adali nazo ndi kumutsatira, sadachite zimenezo.

Atumwi aŵiri a Yesu, Petro ndi Andileya, adalolera kusiya zonse zimene adali nazo kuti atsatire Yesu. Yesu atawapempha kuti amutsatire, adasiya ntchito yawo n’kumutsatira.

Abrahamu adalinso wololera kupereka chirichonse chimene adali nacho kwa Atate athu Akumwamba. Abrahamu adakhala padziko lapansi Yesu asadabadwe. Pa nthawiyo, Atate athu Akumwamba ankafunabe kuti anthu adzipereka nsembe nyama. Iye adalamula Abrahamu kuti apereke nsembe mwana wake, kuti aone ngati angamvere. Abrahamu adali wofunitsitsa kumvera. Adamanga guwa lansembe n’kuikapo mwana wake wamwamuna. Abrahamu adali wokonzeka kupha mwana wake, pamene mngelo adamuletsa. Mngeloyo adauza Abrahamu kuti sayenela kupereka nsembe mwana wake. Atate athu Akumwamba ankadziwa kuti Abrahamu adali wokonzeka kupereka zonse zimene Atate athu Akumwamba adamulamula kuti apereke, ngakhale mwana wake yemwe. Abrahamu ankakonda kwambiri Atate athu Akumwamba moti adali wokonzeka kuchita zonse zimene Atate athu Akumwamba adalamula. Atate athu Akumwamba adadalitsa Abrahamu chifukwa adali wokonzeka kupereka chiriconse chifukwa cha Iwo.

Zokambirana

  • Kodi ndani amene adali chitsanzo cha munthu amene sadalole kupereka chilichonse chimene Yesu adamulamula?

  • Kodi ndani amene adali chitsanzo cha munthu amene adalolera kupereka chilichonse chimene Atate athu Akumwamba adamulamula?

  • Kodi mukadatani mu nyengo zimenezi?

Image
Khristu ndi Wolamulira Wachinyamata Wolemera, wolembedwa ndi Heinrich Hofmann

Wolamulira wachinyamata wachumayo adalibe chikhulupiliro chopereka nsembe yachuma chake ndi kutsatira Yesu.

Tingafunike Kupereka Nsembe Zinthu pa Ntchito ya Yesu

Mabanja athu angatikane ngati titsatira Yesu. Anthu ena angatiseke kapena kutikhumudwitsa tikamamvera malamulo ake. Tikhonza kutaya ntchito chifukwa cholowa mpingo wa Yesu Khristu.

Tikhoza kufuna kugwiritsa ntchito ndalama zathu komanso nthawi yathu kuti tipite kukaphunzitsa anthu za Yesu. Tikhoza kugwiritsa ntchito nthawi yathu kuthandiza atsogoleri a mpingo kuchita ntchito yake. Tikhoza kufuna kugwiritsa ntchito nthawi ndi ndalama zathu pothandiza ena m’banja lathu pamene akugwira ntchito ya Yesu. Atate athu Akumwamba Akhoza kufuna kuti tipereke moyo wathu m’malo mokana umboni wathu wa Yesu.

Zokambirana

  • Kodi mungamve bwanji mutauzidwa kuti musiye chinthu chimene mumakonda kwambiri?

  • Kodi ndinu okonzeka kupeleka nsembe pa ntchito ya Yesu?

Image
Nsembe ya Isaki, yolembedwa ndi Jerry Harston

Abrahamu anali ndi chikhulupiriro chachikulu kotero kuti anali wokonzeka kupereka mwana wake Isake nsembe mwa lamulo la Ambuye.

Nsembe Imabweretsa Madalitso Omwe Sangabwere Mwa Njira Ina

Nsembe imatithandiza kukhala osadzikonda. Timaphunzira kutumikira Atate athu Akumwamba ndi kuthandiza anthu ena. Timaphunzira kuti kuchitira ena zinthu kumatithandiza kukhala osangalala. Timaphunzila kuti kuchita zimene Yesu adatilamula n’kofunika kwambili kuposa chilichonse chimene tingakhale nacho padziko lapansi. Timaphunzira kuti kutumikira ena n’kwabwino kuposa kudziganizira tokha. Tikamapereka nsembe mofunitsitsa, timapezanso kuti Atate athu Akumwamba amatipatsa madalitso abwino kwambiri kuposa chirichonse chimene tasiya.

Kupereka nsembe chifukwa cha ena kumatithandiza kumvetsa bwino zimene Yesu adatichitira. Iye adatikonda kwambiri moti adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Pamene tipereka zinthu kwa Atate athu Akumwamba kapena anthu ena, timawakonda kwambiri. Timayamba kukhala achikondi komanso ngati Yesu komanso Atate athu Akumwamba.

Kukhala ndi katundu wambiri sikuli koipa. Atate athu Akumwamba nthawi zina amatipatsa zinthu zimenezi kuti tithandize ena. Koma n’zovuta kusakonda katundu wathu ndi ndalama. Timayesetsa kugwira ntchito kuti tizipeze. Zina mwa zinthu zimenezi n’zofunika kuti tikhale ndi moyo. Komabe, sitiyenera kusamala kwambiri za zinthu zimenezi mpakana kusadzasiya chirichonse chimene Atate athu Akumwamba angafune kuti athandize ana ake ena.

Mamembala onse a Mpingo wa Yesu Khristu ayenera kupanga kutumikira Atate athu Akumwamba ndi Yesu kukhala chinthu chofunika kwambiri m’miyoyo yawo. Timasonyeza kuti timakonda Atate athu Akumwamba ndi Yesu kuposa mmene timakondera chuma chathu tikamachita zimene atsogoleri a Mpingo wa Yesu Khristu amatipempha. Tikuyenera kupeleka nsembe nthawi yathu kuti tiziwathandiza kuphunzitsa ndi kutumikira ena. Kuti tikhale oyenelera kukhala ndi Atate athu Akumwamba, tikuyenera kukhala okonzeka kupereka chirichonse chimene tiri nacho kuti tithandize ntchito ya Yesu ngati ndi zimene Iye amafuna kwa ife.

Yesu walonjeza madalitso aakulu kwa anthu amene amamumvera ndi kumutumikira. Iye adanena kuti sitingathe kulingalira za zinthu zodabwitsa zimene tidzalandire m’tsogolo ngati tidzipereka nsembe yathu pa ntchito yake panopa.

Print