Zofunikira Zoyambirira
Mutu 4: Ndife Omasuka Kusankha


Mutu 4

Ndife Omasuka Kusankha

Tonsefe timasankha zochita tsiku lirilonse. Atate athu Akumwamba adatipatsa ufulu wosankha tokha. Ndichifukwa chiyani tiyenela kuyesetsa kupanga zosankha zabwino?

Atate athu Akumwamba Amatipatsa Ufulu Wosankha

Kumwamba tidali ndi ufulu wosankha. Tidali omasuka kutsatira Yesu kapena kutsatira Satana. Ambiri mwa ana a Atate athu Akumwamba adasankha kutsatira Yesu. Enanso adasankha kutsatira Satana. Atate athu Akumwamba adalora ana ake onse kusankha okha.

Atate athu Akumwamba amatipatsanso mwayi wodzisankhira tokha pano pa dziko lapansi. Pamene tidabwera pa dziko lapansi, Iwo adatipangitsa kuiwala moyo wathu ndi Iwo. Tidafunika kuphunzira kusankha tokha pamene sitidali nawo.

Zokambirana

  • Kodi mumamva bwanji mukakakamizidwa kuchita zina zake?

  • Kodi mumamva bwanji munthu wina akakulorani kusankha zimene mukufuna kuchita?

Dongosolo la Atate athu Akumwamba Litha Kugwira Ntchito Pokhapokha Ngati Ndife Omasuka Kusankha

Mbali ina ya dongosolo la Atate athu Akumwamba idali kutitumiza ku dziko lapansi kumene kudzakhala zinthu zabwino ndi zoipa. Iwo amafuna kuti tizisankha zabwino. Satana amayesa kutinyengelera kuti tisankhe zoipa. Tiri ndi ufulu wosankha pakati pa chabwino ndi choipa.

Pamene tapanga zisankho chabwino, timakhala okhonza kuchita zinthu zimene Atate athu Akumwamba amafuna. Tikamachita zinthu zimene Atate athu Akumwamba amafuna kuti tichite, timakhala ngati Iwo. Timadzipezera tokha zisankho zabwino kwambiri zoti tisankhe. Timamvetsa bwino zinthu zimene zimatisangalatsa komanso zimene zimatikhumudwitsa.

Tikadapanda kusankha mwatokha, sitikadakwanitsa kukhala ngati Atate athu Akumwamba. Sitikadatha kuphunzira tokha zinthu zabwino kwambiri zimene tingasankhe. Sitikadatha kuwonetsa Atate athu Akumwamba kuti timawakonda komanso timafunitsitsa kuwatsatira.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani tikuyenera kukhala ndi ufulu wosankha?

Kusankha Kumvera Atate athu Akumwamba Kumatipangitsa Kusangalala

Zisankho zabwino zimabweretsa zotsatira zabwino; zisankho zolakwika zimabweretsa zotsatira zoipa. Tikasankha kumvera Atate athu Akumwamba, tidzakhala anthu osangalala komanso abwino. Ngati tisankha kusawamvera, tidzakhala achisoni ndipo sitidzakhala abwino.

Pamene tapanga zisankho zoyenera, timaona kuti timakhala osangalala chifukwa cha zimenezi. Timaphunzira kuti tikuyenera kuchita zinthu zambiri zabwino. Tikamaona kuti kusankha bwino kumatipatsa chimwemwe, timafuna kusankha zinthu zoyenera zochuluka. Timalakalaka mochulukira kukhala abwino. Tikhonza kupanga zisankho zolondola mosavuta chifukwa tikudziwa kuti zotsatira zake zidzakhala zabwino kwa ife. Timaphunzira zinthu zimene tikuyenera kudziwa ndi kuchita, kuti tikhale ngati Atate athu Akumwamba.

Pamene tapanga zisankho zolakwika, timamva chisoni komanso kuchita manyazi. Tikapitiriza kuchita zoipa, Satana amayamba kukhala ndi mphamvu pa ife. Kusankha kuchita zabwino kumakhala kovuta kwambiri. Timasiya kuyesa kutsatira dongosolo la Atate athu Akumwamba.

Zokambirana

  • Ganizilani zisankho zimene mudapanga. Kodi chotsatira chirichonse cha zisankhozo chidali chotani?

  • Kodi mungasankhe bwanji kukhala osangalala ndikubwelera kukakhala ndi Atate athu Akumwamba?

  • Kodi kupanga chisankho choyenera kungakuthandizeni bwanji kupanga zisankho zoyenera zochuluka?

  • Kodi kusankha zinthu zolakwika kumakulepheretsani bwanji kusankha zinthu zabwino m’tsogolo?

Atate athu Akumwamba Adzatithandiza Kupanga Zisankho Zabwino

Atate athu Akumwamba amafuna kuti tizisankha zinthu mwanzeru kuti tiphunzire zimene iwo amadziŵa, kuchita zimene amachita, ndikukhala ndi zinthu zimene alinazo. Iwo amadziwa kuti tidzakhala osangalala ndipo tidzatha kubwelera kukakhala nawo ngati titasankha kuchita zabwino.

Atate athu Akumwamba amafuna kutithandiza kupanga zisankho zabwino. Ndi thandizo lawo, tithe kusankha kuchita chirichonse chimene atiuza. Tikamawapempha, adzatithandiza kulimbana ndi mayesero a Satana. Iwo adzatipatsa mphamvu kuti tisankhe chabwino. Iwo adzatithandiza kutsatira dongosolo lawo ndi kukhala monga Iwo.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani Atate athu Akumwamba amafuna kuti tidzipanga zisankho zabwino?

  • Kodi Iwo angadzatikakamize kuchita zabwino? Chifukwa chiyani?

Print