Zofunikira Zoyambirira
Mutu 7: Mzimu Woyera


Mutu 7

Mzimu Woyera

Atate athu Akumwamba adasankha munthu woti atiuze zinthu zimene iye amafuna kuti tidziwe. Kodi munthu ameneyu ndani, ndipo tingaphunzire bwanji kumvetsa uthenga wa Atate athu Akumwamba?

Mzimu Woyera Umagwira Ntchito ndi Atate athu Akumwamba ndi Yesu Kuti Utithandize

Mzimu Woyera umagwira ntchito limodzi ndi Atate athu Akumwamba ndi Yesu. Umachitira umboni kwa ife kuti ali ndi moyo ndipo amatikonda ife. Umawathandiza kuti azitiphunzitsa zinthu zimene tiyenera kudziwa ndi kuchita komanso kutithandiza kumvera malamulo awo. Iye alibe thupi la mnofu ndi mafupa monga momwe Atate athu Akumwamba ndi Yesu alili. Iye ndi mzimu. Umawoneka ngati mwamuna.

Atate athu Akumwamba, Yesu Khristu, ndi Mzimu Woyera ndi anthu atatu osiyana. Iwo amagwira ntchito limodzi kutithandiza kuphunzira zinthu zimene tiyenera kudziwa ndi kuchita. Pamene tilandira mauthenga kuchokera kwa Atate athu a Kumwamba kapena Yesu, kawirikawiri ndi Mzimu Woyera umene umatibweretsera kwa ife. Umatithandizanso kumvera malamulo Awo.

Zokambirana

  • Kodi Mzimu Woyera umagwira ntchito ndi ndani?

  • Kodi Mzimu Woyera ndi wosiyana bwanji ndi Atate athu Akumwamba ndi Yesu?

Ntchito ya Mzimu Woyera

Mzimu Woyera umatiphunzitsa za Atate athu Akumwamba ndi Yesu. Umatiuza kuti ndi Ali ndi moyo ndipo Amatikonda. Umatiuza kuti Atate athu Akumwamba ndi Atate a mizimu yathu. Umatiuzanso kuti Yesu ndi Mpulumutsi wathu.

Mzimu Woyera umatithandiza kumvetsetsa za Atate athu Akumwamba ndi Yesu komanso zinthu zimene tiyenera kuchita kuti tibwelere kumwamba. Umatithandizanso kuphunzira ndi kumvetsa choonadi chonse.

Mzimu Woyera umatipatsanso mphamvu kuti tidzimvera malamulo a Atate athu Akumwamba ndi Yesu. Iwo umatha kutithandiza kuti tisankhe bwino tikamasankha pakati pa zinthu ziwiri. Iwo umatha kutipatsa mtendere pa nthawi ya mavuto.

Zokambirana

  • Kodi ntchito ya Mzimu Woyera ndi chiyani?

  • Kodi Mzimu Woyera ungatithandize kudziwa chiyani?

  • Kodi Mzimu Woyera ungatithandize kuchita chiyani?

Mzimu Woyera Umatiphunzitsa mu Njira Yamphamvu

Mzimu Woyera umatiphunzitsa ife chimene chili chabwino ndi chimene chili cholakwika. Chiphunzitsochi ndi champhamvu kwambiri moti sitidzaiwala. Mzimu Woyera nthawi zambiri sulankhula kwa ife mwanjira yomwe tingamve ndi makutu athu. M’malo mwake, umatichititsa kuganiza kapena kumva ngati zimene timawerenga kapena kumva zili zoona. Maganizo amenewa ndi amphamvu kwambiri.

Mphamvu ya Mzimu Woyera imatha kumveka ndi anthu ambiri nthawi imodzi. Kuti timvetse bwino zimenezi, taganizirani za dzuwa. Pali dzuŵa limodzi lokha, koma kuwala ndi kutentha kwake zimamvedwa ndi anthu m’madera ambiri nthawi imodzi. Mzimu Woyera ukhonza kuganiziridwa mwanjira yomweyo. Mphamvu zake zikhonza kumveka ndi anthu m’malo ambiri nthawi imodzi ngakhale kuti Iwo mwini uli pamalo amodzi pa nthawi ina iliyonse.

Zokambirana

  • Kodi Mzimu Woyera umatiuza bwanji zinthu zimene tiyenera kudziwa?

  • Kodi Mzimu Woyera ungathandize bwanji anthu ambiri nthawi imodzi?

Mzimu Woyera Udzathandiza Aliyense wa Ife

Atate athu Akumwamba atatulutsa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni, iwo adapemphera ndi kuwafunsa chimene ayenera kuchita. Atate athu Akumwamba adatumiza Mzimu Woyera kuti uwaphunzitse za Iwo ndi Yesu komanso za zinthu zimene Adamu ndi Hava amayenera kuchita. Mzimu Woyera udawauza kuti ziphunzitso za Atate athu Akumwamba zidali zoona. Adawapatsa mphamvu kuti achite zinthu zimene Atate athu Akumwamba ankafuna kuti iwo adzichita.

Adawathandizanso kukhala odzichepetsa komanso oyamikira zinthu zimene Atate athu Akumwamba adawachitira.

Kudzera mu chitsogozo cha Mzimu Woyera, Adamu ndi Hava adaphunzira kuti akhonza kukhalanso ndi Atate athu Akumwamba tsiku lina ngati adzatsatire Yesu nthawi zonse ndi kumvera malamulo Ake. Chitsogozo cha Mzimu Woyera chidawapangitsa iwo kukhala osangalala kwambiri.

Atate athu Akumwamba amakonda aliyense wa ife. Amatumiza Mzimu Woyera kuti atitsogolere ndi kutiphunzitsa choonadi. Komabe, Mzimu Woyera udzatithandiza pokhapokha ngati tiyesetsa mowona mtima kutsatira malamulo ndi malangizo amene umatibweretsera kuchokera kwa Atate athu Akumwamba ndi Yesu. Ngati sitiyesetsa mowona mtima kumvera malamulo awo, kapena ngati sitikufuna kuti Mzimu Woyera utiphunzitse ife, Iwo sudzatiuza ife kalikonse. Tidzakhala ndi moyo wabwino ngati titsatira ziphunzitso za Mzimu Woyera.

Zokambirana

  • Kodi Mzimu Woyera udathandiza bwanji Adamu ndi Hava?

  • Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tilandire thandizo kuchokera kwa Mzimu Woyera?

Print