Zofunikira Zoyambirira
Mutu 24: Tsiku Lopembedza


Mutu 24

Tsiku Lopembedza

Atate athu Akumwamba adatiuza kuti tidziwalambira tsiku limodzi pamlungu. Timalandila madalitso ambiri tikapanga tsiku limenelo kukhala lopatulika.

Atate athu Akumwamba Adatipatsa Tsiku Lopembedza Kuti Atithandize

Atate athu Akumwamba amadziwa kuti tili ndi mavuto ambiri. Tikuyenera kuchita zinthu zambiri tsiku lirilonse. Tikuyenera kugwira ntchito kuti tipeze chakudya ndi zovala. Tikuyenera kukonza chakudya chathu ndi kugwira ntchito zina zapakhomo tsiku lirilonse.

Ndi zinthu zonsezi, n’zosavuta kuiwala za Atate athu Akumwamba. N’zosavutanso kuiwala zinthu zimene Atate athu Akumwamba amafuna kuti tizichita. Timaganizira kwambiri za zosowa zathu za tsiku ndi tsiku kuposa mmene timaganizira za Atate athu Akumwamba.

Atate athu Akumwamba amadziwa kuti timafunika nthawi yoganizira za iwo. Timafunika nthawi kuti tiphunzire zimene iwo amafuna kuti tichite. Chifukwa cha zimenezi, atiuza kuti tizikwanitsa tsiku limodzi pa masiku asanu ndi awiri aliwonse kuti tipume ku ntchito yathu ndi kuphunzira za Iwo.

Atate athu Akumwamba adalenga dziko lapansi kudzera mwa Yesu Khristu m’nyengo zisanu ndi imodzi. Adazitcha nyengozi zimenezi masiku. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, adapuma pa ntchito yolenga dziko lapansi. Iwo atiuza kuti tizipuma tsiku limodzi pamlungu ku ntchito yathu ya tsiku ndi tsiku.

Atate athu Akumwamba Atiuza Kuti Ndi Tsiku Liti Lopembedza

Atate athu Akumwamba adauza anthu m’nthawi zakale kuti azigwiritsira ntchito tsiku lachisanu ndi chiŵili la mlungu pa tsiku la kulambila. Tsikuli lidali lothandiza anthu kukumbukira kuti atalenga dziko lapansi adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiwiri.

Yesu atamwalira, adaukitsidwa pa tsiku loyamba la mlungu. Otsatira a Yesu ankagwiritsa ntchito tsiku loyamba la mlungu monga tsiku la kulambira pothandiza anthu kukumbukira ndi kulemekeza tsiku la kuuka kwa Yesu. Ili timalitcha tsiku la Ambuye. (Nthaŵi zina Yesu amatchedwa Ambuye.) Limenelinso timalitchula kuti tsiku la Sabata.* Ngakhale liri tsiku losiyana ndi tsiku la pa mlungu lomwe ankagwiritsa ntchito kalekale polambira, nditsikube limodzi kwa asanu ndi awiri. Timagwirabe ntchito yathu wamba masiku asanu ndi limodzi pamlungu. Ndiye pa tsiku lachisanu ndi chiwiri timalambira Atate athu Akumwamba.

Masiku ano, anthu ambiri amagwiritsa ntchito tsiku loyamba la mlungu, lomwe ndi Lamlungu monga tsiku la kulambira. Nthawi zingapo Atate athu Akumwamba anauza mneneri wawo kuti anthu ake m’mayiko ena angagwiritse ntchito tsiku lina ngati tsiku la kulambira.

Image
anthu akuimba ku Mpingo

Lamlungu ndi tsiku la kupembedza.

Tikhonza Kusunga Tsiku la Ambuye Lopatulika

Pali zinthu zambiri zimene tikuyenera kuchita pa tsiku la Ambuye. Chinthu chofunika kwambiri chimene tingachite ndi kuganizira za Atate athu Akumwamba komanso Yesu mkati mwa tsiku. Tikuyenera kuganizira zinthu zimene iwo amafuna kuti tidziwe ndi kuchita. Zina mwa zinthu zimene tingachite pa tsiku la kulambira zimene zingatithandize kukumbukira ndi kuphunzira za Atate athu Akumwamba ndi:

  1. Kuwerenga malemba amene amaphunzitsa za Atate athu Akumwamba ndi Yesu.

  2. Kuthandiza anthu ena kuphunzira za Mpingo.

  3. Kuphunzitsa mabanja athu za Atate athu a Kumwamba ndi Yesu ndi zimene amafuna kuti ife tichite.

  4. Kupita kumisonkhano yampingo ndi makalasi komwe tingaphunzire pamodzi za uthenga wabwino. Tingaphunzire nkhani za Yesu ndi ziphunzitso zina za uthenga wabwino, ndipo tikhoza kuuzana wina ndi mnzake za zinthu zimene Atate athu Akumwamba ndi Yesu adatichitira.

  5. Kupumula ku ntchito zomwe timachita masiku ena a pamlungu.

  6. Kupemphera.

  7. Kuyendera anthu odwala ndi kuwathandiza kuti adzimverako bwino.

  8. Kulemba zinthu zina zimene zimachitikira mabanja athu kuti tidzathe kuzikumbukira m’tsogolo.

Mamembala ampingo wa Yesu Khristu akuyenera kudya mgonero pa tsiku la kupembedza. Iwo angathe kukonzekera kuti adye nawo pa kuganizira za Yesu ndi zinthu zimene adatichitira ife. Ayenera kupempha Atate athu Akumwamba kuti awathandize kukumbukira Yesu. Pamene atenga mgonero, ayenera kukumbukira malonjezo opatulika amene adapanga. Ayenera kuganizira zinthu zimene Atate athu Akumwamba awalonjeza ngati angamvere Yesu.

Pali zinthu zambiri zimene sitiyenera kuchita pa tsiku la kulambira. Sitikuyenera kugwira ntchito. Sitikuyenera kuchititsa mabanja athu, antchito athu kapena ziweto zathu kugwira ntchito. Sitikuyenera kuŵerenga zinthu, kuonera mapulogalamu a pa TV, kapena kumvetsera nyimbo zimene zingatilepheretse kuganizira za Atate athu Akumwamba ndi Yesu. Sitikuyenera kupita ku zochitika zamasewera. Sitikuyenera kugula kapena kugulitsa zinthu. Zinthu zimenezi zingaoneke ngati zofunika, koma sizingatithandize kuganizira za Atate athu Akumwamba ndi Yesu pa tsiku lopatulikali.

Pamatha kukhala nthawi zina pamene tiyenera kugwira ntchito pa tsiku la kulambira, koma tiyenera kuyesetsa kuti tisatero. Pamene kugwira ntchito kuli kofunikira, tiyenera kuganizira za Atate athu Akumwamba ndi Yesu pamene tikugwira ntchito.

Zokambirana

  • Kodi tikuyenera kuchita chiyani pa tsiku la Ambuye?

  • Kodi sitikuyenera kuchita chiyani pa tsiku la kupembedza?

Atate athu Akumwamba Amatidalitsa Chifukwa Chosunga Tsiku la Ambuye Lopatulika

Cholinga cha tsiku la kupembedza chimakhala chofanana nthawi zonse. Ndi tsiku lopuma ku ntchito zomwe timagwira tsiku lirilonse. Ndi tsiku lophunzira za Atate athu Akumwamba ndi kukonzekera moyo ndi Iwo. Ndi tsiku loti tikhale ndi moyo wabwino pophunzira zambiri zimene Atate athu Akumwamba amafuna kuti tidzichita.

Tsikuli ndilabwino kwa ife. Zimatithandiza kukumbukira Atate athu Akumwamba komanso chifukwa chimene tilili padziko lapansi. Tikamachita zinthu zimene Atate athu Akumwamba amafuna kuti tichite pa tsiku la Ambuye, timalandila madalitso. Mabanja athu amakhala osangalala. Matupi athu amafewetsedwa. Timayandikira kwa Atate athu Akumwamba ndi ziphunzitso Zawo. Tidzakhala okhonza kumva chikoka cha Mzimu Woyera mwamphamvu kwambiri mkati mwa sabata. Chifukwa chakuti takhala omvera, Atate athu Akumwamba adzatithandiza kupeza chakudya, zovala ndi zinthu zina zimene timafunikira. Adzatithandiza kuphunzira zambiri za Iwo ndi kukhala osangalala.

Zokambirana

  • Ndi zifukwa ziti zimene tikuyenera kusunga tsiku la kupembedza monga tsiku lopatulika?

Print