Zofunikira Zoyambirira
Mutu 31: Udindo Wathu Wolalikira Uthenga Wabwino


Image
Pitani Inu Choncho, wolemba Harry Anderson

Yesu adalamula atumwi ake kuti akaphunzitse uthenga wabwino padziko lonse lapansi.

Mutu 31

Udindo Wathu Wolalikira Uthenga Wabwino

Kodi tingathandize bwanji ana onse a Atate athu Akumwamba kuti amve uthenga wabwino?

Atate athu Akumwamba Amafuna Kuti Ana Ake Onse Adziwe Uthenga Wabwino

Atate athu Akumwamba amakonda ana awo onse. Aliyense wa ife ndi wofunika kwa Iwo, ndipo aliyense akhoza kukhala ngati Iwo. Iwo akufuna kuti ife tibwelere kukakhala ndi Iwo ndi kukhala ndi chisangalaro ndi ulemelero wofanana ndi iwo.

Atate athu Akumwamba ali ndi dongosolo lothandiza aliyense wa ife kubwelera ndi kukakhala ndi Iwo. Ndondomekoyi imatchedwa Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu. Tikamaphunzira uthenga wabwino, timaphunzira za kufunika kwathu. Timaphunzira chifukwa chake tili padziko lapansi pano. Timaphunziranso kumene tidzapita tikamwalira. Timaphunzira zimene tikuyenera kuchita kuti tibwelere kwa Atate athu Akumwamba.

Yesu Khristu ndi m’bale wathu wauzimu. Iye ndi mwana woyamba kubadwa wauzimu wa Atate athu Akumwamba. Iye adabwera ku dziko lapansi monga mwana wa Atate athu Akumwamba wobadwa yekha m’thupi. Iye amatikonda kwambiri moti adavutika ndi kutifera. Iye adaphunzitsa zimene Atate athu Akumwamba amafuna kuti tizidziŵe ndi kuchita. Adakonza mpingo wake kuti utithandize. Adapereka unsembe wake kwa anthu padziko lapansi kuti agwire ntchito yake.

Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima M’masiku Otsiriza ndi mpingo wokhawo umene uli ndi unsembe wa Atate athu Akumwamba ndi dongosolo Lawo lenileni. Atate athu Akumwamba amafuna kuti anthu onse aphunzire za dongosolo lawo ndi kulilandira. Miyambo ya Mpingo woona ndi ofunikira kuti ife tibwelere kukakhala ndi Atate athu Akumwamba.

Atate athu Akumwamba adauza membala aliyense wa mpingo wake kuti auze ena za uthenga wabwino. Aneneri onse kuyambira Adamu akhala akugwiritsa ntchito nthawi yawo yambiri pophunzitsa uthenga wabwino kwa ena. Iwo adatiuza kuti membala aliyense wa mpingo akuyenera kukhala mmishonale. Imeneyi ndi mbali ya lonjezo limene tidapanga pamene tidali kubatizidwa. Tidalonjeza kuti tidzauza anthu za Yesu nthawi iliyonse imene tingathe.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani anthu onse akuyenera kumva uthenga wabwino?

  • Ndi ndani ali ndi udindo wophunzitsa uthenga wabwino kwa anthu onse?

Banja lirilonse mu mpingo likuyenera kumvetsetsa kufunika kophunzitsa uthenga wabwino. Timadziwa kufunika kwa dongosolo la uthenga wabwino. Tikuyenera kusamala kwambiri kuti ena achite chirichonse chofunikira kuwathandiza kumvetsetsa dongosolo la Atate athu Akumwamba.

Achibale angachite zinthu zambiri kuthandiza ena kuphunzira za uthenga wabwino. Zina mwa zinthu izi ndi:

  1. Chitirani ena zabwino.

  2. Kuuza ena kuti ndinu okondwa chifukwa mumamvera chiphunzitso cha uthenga wabwino.

  3. Kufotokoza uthenga wabwino kwa abwenzi ndi anansi. Kuwaitana kuti apite nanu ku misonkhano ya mpingo.

  4. Kuitana anthu kuti abwere kunyumba kwanu kuti akakhale nanu ku banja madzulo panyumba panu kapena pamene mamishonale angawaphunzitse.

  5. Kupereka kwa mamishonale mayina ndi ma adilesi a anzanu kapena achibale omwe angafune kuphunzira za uthenga wabwino.

  6. Kuphunzitsa ana kufunika kotumikira monga mamishonale. Kuwathandiza kusunga ndalama kuti apite kumishoni.

  7. Kupereka chakhumi chanu.

  8. Kupereka ndalama ku thumba la mamishonale.

Zokambirana

  • Ganizirani njira yofotokozera munthu amene siali membala wa mpingo za uthenga wabwino.

  • Kodi banja lanu lingachite chiyani kuti muthandize anthu ena kuphunzira za uthenga wabwino?

Banja Lanu Likhonza Kukhala Gawo la Ntchito Yofunika Yaumishonale wa Mpingo

Mpingo wathu watumiza mamishonale zikwizikwi kukaphunzitsa uthenga wabwino m’mayiko ambiri. Ambiri a iwo ndi achinyamata azaka zapakati pa 18 ndi 25. Okalamba amatumikiranso monga mamishonale. Iwowa ndi mamembala okhulupirika, omvera a Mpingo omwe ali ndi chikhumbo chotumikira Atate athu Akumwamba.

Pakufunika mamishonale ena ambiri. Banja lanu likhonza kutengapo mbali pa ntchito yofunika imeneyi po konzekeretsa achibale anu kupita ku mamishoni. Makolo angathandize ana awo kupeza umboni wa uthenga wabwino ndi kuphunzira mmene angafotokozere uthenga wabwino kwa ena. Iwo angaphunzitse ana awo kukonda anthu amitundu yonse. Makolo akuyeneranso kudzikonzekeretsa okha kupita kumishoni ana awo akadzakula.

Anthu ambiri sadamvebe za uthenga wabwino. Ena a iwo amakhala m’mayiko amene mamishonale sangathe kupitako. Anthuwa akuyenera kukhala ndi mwayi womva ndi kuvomereza uthenga wabwino. Atate athu Akumwamba adzapereka njira yochitira zimenezi. Tikuyenera kupemphera kwa iwo kuti atsogoleri a mayikowa alole kuti mamishonale alowe ndi kuphunzitsa anthu awo.

Zokambirana

  • Kodi mabanja mu mpingo akhala akukwaniritsa bwanji udindo wawo wophunzitsa uthenga wabwino kwa anthu onse?

  • Kodi ndi chifukwa chiyani mamishonale ambiri akufunika masiku ano?

Madalitso Akulu Amadza Kwa Amene Amauza Ena Za Uthenga Wabwino

Atate athu Akumwamba adzatidalitsa ngati tisamala mokwanira za ena kuwauza za uthenga wabwino. Iwo adzatidalitsa ife chifukwa chomvera lamulo Lawo ndi chimwemwe chimene timabweretsa kwa iwo amene alandira uthenga wabwino. Iwo adatiuza kuti tidzakhala osangalala ngati tithandiza mmodzi yekha wa ana awo kuphunzira uthenga wabwino ndi kubwelera kwa Iwo. Chimwemwe chathu chidzakhala chokulirapo ngati tithandiza ambiri a ana awo kubwelera kwa Iwo.

Zokambirana

  • Kodi ndi madalitso otani amene amabwera chifukwa chotengera uthenga wabwino kwa ena?

  • Kodi mwapezapo ena mwa madalitso amenewa?

Print