Zofunikira Zoyambirira
Mutu 32: Kukhala Monga Mabanja Kwamuyaya


Image
Kachisi ya Portland Oregon

Kachisi ku Portland, Oregon, USA.

Mutu 32

Kukhala Monga Mabanja Kwamuyaya

Kodi mabanja angakhale bwanji pamodzi kwamuyaya, angakhale moyo wa padziko lapansi utatha?

Mulungu Adakonza Zoti Mabanja Azikhala Pamodzi Mpaka Kalekale

Banja ndi gulu lofunika kwambiri la anthu padziko lapansi. Banja lathu lapadziko lapansi limatengera chitsanzo cha banja lathu lakumwamba. Tonse tidali abale ndi alongo kumwamba. Tidali ana a Mulungu. Mulungu adali mtsogoleri wa nyumba yathu yakumwamba. Tidalandira chikondi chachisamaliro ndi chitsogozo kuchokera kwa makolo athu akumwamba.

Mulungu adatumiza aliyense wa ife ku banja lapadziko lapansi. Iye wapatsa makolo udindo wosamalira mwana wake aliyense pamene ali padziko lapansi. Makolo akuyenera kukonda ana awo ndi kuwapatsa chakudya, zovala, ndi nyumba. Akuyenera kuphunzitsa ana awo za Mulungu ndi m’mene angakhalire ngati iye.

Mulungu adachititsa kuti mabanja akhale pamodzi kwamuyaya. Iye wapatsa atsogoleri a mpingo wake ulamuliro womanga mabanja pamodzi kwamuyaya. Kumanga pamodzi kumeneku kumatchedwa kutsindikiza. Kutsindikiza kumeneku kungachitike m’kachisi mokha. Makachisi ndi nyumba zopatulika kumene mamembala okhulupirika a Mpingo angapiteko. Pamene mwamuna ndi mkazi atsindikizidwa m’kachisi ndi munthu amene ali ndi unsembe ndipo ali ndi mphamvu yapadera yotsindikiza, ukwati wawo sudzatha akadzamwalira. Ukwati wawo udzakhalapo mpaka kalekale ngati adzasunga malonjezo amene adalonjeza m’kachisi. Izi zimatchedwa ukwati wamuyaya.

Ngati mwamuna ndi mkazi sanatsindikizidwe m’kachisi, ukwati umatha pamene mmodzi wa iwo amwalira. Ngati tasindikizidwa mu kachisi, ndipo ngati titsatira Yesu Khristu mokhulupirika mpaka mapeto a moyo wathu, mabanja athu akhonza kukhala pamodzi kwamuyaya.

Banja lokwatirana lingapite kukachisi kukatsindikizidwa ngati ali otsatira okhulupirika a Yesu. Kumeneko, wansembe amene ali ndi ulamuliro wapadera akhonza kutsindikiza iwo kwa wina ndi mzake. Akhozanso kutsindikiza ana awo kwa iwo. Akatsindikizidwa kwa wina ndi mzake, akhonza kukhala pamodzi kwamuyaya, monga ngati kuti adakwatirana m’kachisi pachiyambi.

Mulungu akufuna kuti ana ake onse akonze zoti atsindikizidwe m’kachisi ndi kukuza banja lomvera. Makolo akuyenera kutsogolera ana awo kuti adzakhale okonzeka kupita kukachisi kuti akamangitse banja lawo. Ngati mwamuna ndi mkazi atsindikidwa mu kachisi, ana onse obadwa kwa iwo pambuyo potsindikiza, adzatsindikizidwa kwa iwo nthawi yomweyo.

Zokambirana

  • Kodi Mulungu wakonza bwanji kuti tikhale ndi mabanja athu kwamuyaya?

  • Nchifukwa chiyani tifunika kutsindikizidwa mu kachisi?

Ndi mamembala Okhulupirika okha a Mpingo omwe Angalowe mu Kachisi

Makachisi ndi malo opatulika. Ndi mamembala okha a Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera Mtima Mmasiku Otsiriza omwe asonyeza chikhulupiliro chawo mwa Yesu Khristu pomvera malamulo Ake ndi omwe amaloledwa kulowamo. Anthu amenewa akhala oyenera kulowa m’kachisi. Munthu asadalowe m’kachisi akuyenera kuti adali membala wa mpingo kwa chaka chimodzi. Amuna akuyenera kukhala kuti adalandira Unsembe wa Melkizedeki.

Kuti awone ngati ali oyenera kupita ku kachisi, onse amuna ndi akazi akuyenera kulankhula ndi bishopu kapena pulezidenti wa nthambi. Ngati bishopu kapena pulezidenti wa nthambi apeza kuti munthuyo ndi woyenera, adzapatsa munthuyo pepala losaina lotchedwa chiphaso cha m’kachisi. Kenako membala wa pulezidenti wa siteki kapena pulezidenti wa mishoni akuyeneranso kufunsa munthuyo. Adzasainanso chiphaso cha m’kachisi ngati apeza kuti munthuyo ndi woyenerera. Munthuyo akuyenera kutenga chiphaso cha m’kachisi kukachisi kuti alowemo.

Otsatirawa ndi mafunso ofanana ndi amene bishopu kapena pulezidenti wa nthambi adzafunsa kuti apange chiganizo ngati membala wa Mpingo ali woyenera kupita ku kachisi:

  1. Kodi mumakhulupilira mwa Mulungu; mwa Mwana Wake, Yesu Khristu; ndi mwa Mzimu Woyera?

  2. Kodi mumavomereza Pulezidenti wa Mpingo wa Yesu Khristu wa Oyera mtima M’masiku Otsiriza monga mneneri, oona, ndi wovumbulutsa? Kodi mumamuvomereza iye monga munthu yekha padziko lapansi amene ali ndi mphamvu zogwiritsira ntchito mfungulo zonse zaunsembe?

  3. Kodi mumapereka gawo limodzi mwa magawo khumi a zomwe mumapeza ku mpingo?

  4. Kodi mumamvera Mawu a Nzeru?

  5. Kodi mumayesetsa kukhala oona mtima ndi anthu ena?

  6. Kodi mumayesetsa kuchita ntchito yanu mu Mpingo popita kumisonkhano yanu ndi kumvera malamulo?

  7. Kodi mumamvera lamulo la kudzisunga?

  8. Kodi mudayamba mwachitapo tchimo lalikulu osaulula kwa atsogoleri otenelera a unsembe?

Kulowa m’kachisi ndi mwayi wopatulika. Tikuyenera kukhala oyenera ndi okonzeka kumvera lonjezano lirilonse lopatulika limene timapanga ndi Mulungu mu kachisi. Tikuyenera kukumbukira kuti kutsindikiza kwa muyaya kochitidwa mu makachisi ndi kopatulika. Ndi njira yokhayo imene tingakhalire pamodzi monga mabanja mpaka kalekale. Ndi njira yokhayo yopezera madalitso onse amene Mulungu watipatsa. Ndikofunikira kwambiri kuti tipeze chisangalalo chamuyaya kuti tiyese kupita ku kachisi kukatsindikizidwa.

Zokambirana

  • Ndani angalowe m’kachisi?

  • Kodi munthu akuyenera kuchita chiyani kuti akhale woyenera kulowa m’kachisi?

  • Ndi chifukwa chiyani tikuyenera kupita ku kachisi kuti tikatsindikizidwe?

Kukonzekeretsa Banja Lanu Kukhala Limodzi Kwamuyaya

Kutsindikizidwa mu kachisi kumapangitsa kukhala kotheka kukhala pamodzi kwamuyaya monga banja, koma pali zinthu zina zomwe tikuyenera kuchita ngati tikufuna kulandira dalitso lalikululi. Tikuyenera kupitiriza kutsatira Yesu mokhulupirika. Tikuyenera kusunga malonjezo amene timapanga m’kachisi. Tikuyenera kuphunzira kukhala achibale abwino okondana ndi kutumikirana. Tikuyenera kupemphera kwa Mulungu kuti Mzimu Woyera atithandize kupanga zisankho zoyenera mu chilichonse chomwe tichita. Nthawi zonse tiziyesetsa kuthandiza mabanja athu kukhala oyenera kukhala ndi Mulungu.

Zokambirana

  • Pambali pa kutsindikizidwa m’kachisi, kodi banja liyenera kuchita chiyani kuti likhale limodzi kwamuyaya?

Mulungu Wapangitsa Kuti Zikhale Zotheka Kuti Tipulumutse Makolo Athu

Miyanda ya ana a Mulungu amwalira osamva uthenga wake. Sadalandire miyambo yoyenera kuti akhululukidwe machimo awo ndi kukhalanso ndi moyo ndi Mulungu. Mulungu amakonda ana ake onse ndipo amafuna kuti onse abwelere kwa Iye, choncho wapereka njira yoti miyambo ya uthenga wabwino achitidwe kwa iwo. Ntchito imeneyi ikuyenera kuchitikira m’kachisi.

Ina mwa miyambo yomwe imachitidwa mkachisi kwa iwo amene adamwalira ndi ubatizo, kupereka mphatso ya Mzimu Woyera, ndi kutsindikiza kwa mabanja kwa muyaya. Popeza kuti miyamboyi ndi yofunika kwa onse amene akufuna kukhalanso ndi Mulungu, tingagwire ntchito imeneyi kwa makolo athu akale.

Zokambirana

  • Kodi iwo amene adafa osamva uthenga angalandire bwanji miyambo yofunikira kuti abwelere kwa Mulungu?

  • Ndi ndani ali ndi udindo woonetsetsa kuti miyambo yofunikira ikuchitidwa kwa akufa?

Amoyo Amachita Miyambo mmalo mwa Akufa

Pali zinthu zina zimene tingachite kuti miyambo ichitidwe kwa achibale athu amene adamwalira. Tifunika kuwadziŵa bwino ndi dzina lawo, tsiku ndi malo amene adabadwira ndi kumwalira. Ngati sitingapeze chidziŵitso chimenechi, tingachizindikirebe mwa kulemba monga momwe tikudziŵira za gulu la banja (bambo, amayi, ndi ana awo).

Ntchito yofufuza mayina a makolo athu amene adamwalira ndiponso zinthu zina zonse zokhudza iwowo imatchedwa kuti mibadwo ya makolo athu kapena mbiri ya banja.

Pali ma fomu awiri, omwe amatchedwa tchati cha makolo ndi zolemba zagulu la banja, zomwe mungalembepo izi. Mutha kupeza mafomu awa kuchokera kwa mtsogoleri wanu wa unsembe. Adzakhala ndi wina wokuthandizani kulemba nkhaniyi. Ndiye mukhonza kutenga kapena kutumiza uthenga ku kachisi, kumene miyambo idzachitidwe.

Ngati palibe wachibale wathu wamoyo amene ali ndi chidziwitso chimene tikufuna, tingachipeze m’zolembedwa za boma, m’zolemba za mipingo imene makolo athu angakhalemo, kumanda, kapena kumalo aliwonse kumene chidziwitsocho chilipo.

Ngati ndife oyenera, titha kupita ku kachisi kukachita miyambo mmalo mwa achibale athu. Ngati sitingathe kupita ku kachisi, ena adzawachitira miyamboyo. Tikuyenera kupita kukachisi nthawi zambiri kukachita miyambo kwa akufa.

Zokambirana

  • Kodi tikuyenera kuchita chiyani tisadachite miyambo mu kachisi kwa makolo athu amene adamwalira?

  • Kodi ndi uthenga wotani omwe ukufunika kuti miyamboyi achitidwe?

  • Ndi ndani angachitire miyambo mmalo mwa makolo athu amene adamwalira?

Mbiri Yaumwini Ndi Yofunika

Tikamawerenga zimene munthu wina wa m’banja lathu adalemba zokhudza iyeyo, timamudziwa komanso kumukonda kwambiri. Kuwonjezera pa kuphunzira za achibale athu amene adamwalira ndi kuwachitira miyambo, tikuyenera kusunga mbiri ya moyo wathu. Tikuyenera kulemba za makolo athu, kubadwa kwathu, ndi zinthu zimene zatichitikira pa moyo wathu. Tikuyeneranso kulemba maganizo athu kuti ana athu ndi adzukulu athu adziwe zambiri za ife ndi kulimbikitsidwa kuchita zinthu zabwino zomwe tidachita.

Mulungu adauza Adamu kuti alembe mbiri ya moyo wake kaamba ka ana ake. Aneneri nawonso adalemba zolemba zoterozo, ndipo ifenso tikuyenera kuchita zimenezo. Tikamawerenga nkhani imene Adamu ndi aneneri ena adalemba, timaphunzira za madalitso ndi malamulo amene Mulungu adawapatsa. Zimenezi zimatithandiza kuchita zabwino. Tikuyenera kuthandiza ana athu posunga mbiri ya moyo wathu.

Zokambirana

  • Ndi chifukwa chiyani Mulungu adauza anthu ake kuti adzisunga zolembedwa za umoyo wawo?

  • Kodi ndi madalitso otani amene angadze kwa ana anu ndi adzukulu kuchokera m’zolemba zanu zaumwini?

Print